Mayi wa Zaka Zoposa 100 Ali ndi Cholinga Pamoyo
ELIN ndi mmodzi mwa anthu 60 a ku Sweden amene posachedwapa aikidwa pa m’ndandanda wa anthu omwe akwanitsa zaka 105 kapena kuposa. Elin ali ndi zaka 105. Ngakhale kuti amakhala ku nyumba yosungirako anthu okalamba, iye akutumikirabe monga Mboni ya Yehova yachangu, ndipo anakhala wa Mboni za Yehova zaka zoposa 60 zapitazo.
Polalikira kwa ena, Elin amatsatira chitsanzo cha mtumwi Paulo ali pa ukaidi wosachoka panyumba. Paulo ankalalikira kwa anthu onse omwe ankabwera kudzamuona. (Machitidwe 28:16, 30, 31) Mofanana ndi zimenezi, Elin amagwiritsa ntchito mpata uliwonse wolalikira anthu okonza m’nyumba, madokotala amano ndi amatenda ena, okonza tsitsi, manesi, ndi ena amene amakumana nawo kunyumbako, ndipo amawauza uthenga wabwino wa m’Baibulo. Nthawi ndi nthawi, okhulupirira anzake a mu mpingo umodzi ndi Elin amauza ophunzira Baibulo awo kuti akamuchezere kuti apindule ndi nzeru zake ndi zimene wakumana nazo pamoyo wake.
Anthu a mu mpingo wa Elin amayamikira mtima wake wansangala ndi wofuna kudziwa zinthu zatsopano. Mboni inzake inati: “Amandichititsa chidwi kwambiri chifukwa amadziwa zinthu zonse zomwe zikuchitika mumpingo. Amakumbukira mayina a ana onse ndi a anthu amene asamukira kumene mu mpingo wathu.” Elin amadziwikanso bwino monga munthu wochereza alendo, wokonda kuseka, ndiponso wosadandauladandaula ndi mavuto apamoyo.
Kodi n’chiyani chimamuthandiza Elin kuti akhalebe wachimwemwe ndiponso aziganizira kwambiri cholinga chake pamoyo? Amawerenga lemba la m’Baibulo tsiku lililonse kuchokera m’kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku, kofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Amawerenganso Baibulo tsiku lililonse pogwiritsa ntchito galasi lokuzira zilembo. Elin amakonzekera misonkhano ya mlungu ndi mlungu ya Mboni za Yehova, ndipo ngakhale kuti sangathe kupita ku misonkhanoyi, amamvera matepi a nkhani zokambidwa pa misonkhano imeneyi. Kaya tikhale ndi zaka zingati, tikhoza kukhala ndi moyo wokhutiritsa ndi watanthauzo ngati timawerenga Baibulo ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo nthawi zonse, ndiponso ngati sitiphonya misonkhano yachikhristu.—Salmo 1:2; Aheberi 10:24, 25.