Inali Nzeru Yothandiza
ABALE achinyamata atatu ku Central Africa ankafuna kupita ku msonkhano wachigawo. Kuti akafike ku msokhanowu, anafunikira kuyenda mtunda wa makilomita pafupifupi 90, m’misewu yokumbikakumbika komanso yafumbi. Iwo analibenso choyendera. Ndiyeno kodi akanayenda bwanji? Anyamatawa anaganiza kuti abwereke njinga zitatu koma njinga zabwino sizinapezeke.
Mkulu wa mumpingo wawo ataona vuto lawolo anawabwereka njinga yake, yomwe inali yakale koma yabwino. Mkuluyo anawalongosolera zimene iye ndi anzake ankachita kuti akafike ku msonkhano. Iye anawauza kuti angathe kumasinthana njingayo. Inali njira yosavuta koma anafunika kugwirizana. Kodi zikanatheka bwanji kuti anthu atatu agwiritse ntchito njinga imodzi?
Poopa dzuwa, abalewa anakumana m’mamawa kwambiri n’kumangirira katundu wawo panjingapo. Mmodzi anakwera njingayo n’kutsogola, ndipo enawo ankamutsatira akuyenda ndawala. Woyambayo anapalatsa njingayo mtunda wa mamita pafupifupi 500 ndipo kenako anatsika ndi kuiimika pa mtengo. Koma anafunika kuonetsetsa kuti waimika njingayo pamalo oti anzakewo aione, komanso oti anthu ena asaibe. Ndipo iye anayamba kuyenda pansi popitiriza ulendowo.
Abale awiri aja atafika pamene mnzawoyo anaimika njinga, wachiwiri anakwera njingayo ndipo wachitatu anayendanso mtunda wina wa mamita pafupifupi 500, kenako nayenso anakwera njinga ija. Chifukwa cha kukonzekera bwino komanso kufunitsitsa kuti akapezeke ku msonkhano, abalewa anachepetsa mtunda wa makilomita 90 n’kukhala wa makilomita pafupifupi 60. Khama lawo linapindula. Iwo anakumana ndi abale ndi alongo awo achikhristu kumsonkhanoko ndipo anasangalala kwambiri ndi phwando lauzimu. (Deut. 31:12) Kodi inuyo chaka chino muyesetsa kuti mukapezeke ku msonkhano wachigawo wa kwanuko?