Yesu Amalemekezedwa ndi Anthu Ambiri
“Palibe amene angatsutse kuti Yesu wa ku Nazareti . . . ndiye munthu wotchuka kwambiri m’mbiri yonse.”—Anatero H. G. Wells, katswiri wa mbiri yakale wa ku England.
“Pa anthu onse akale amene anali otchuka, palibe aliyense amene ali otchuka ngati Khristu.”—Anatero Philip Schaff, yemwe ndi katswiri wamaphunziro a zaumulungu ndiponso wa mbiri yakale, wa ku Switzerland.
PA ANTHU onse amene akhalapo ndi moyo, kodi ndani amene tinganene kuti ndi munthu woposa onse? Kodi n’chiyani chimene chimapangitsa munthu kukhala woposa ena? Kodi ndi nzeru zake pankhondo? Mphamvu zake? Kuganiza kwambiri? Kapena kodi ndi chifukwa cha mmene zonena zake ndiponso zochita zake komanso chitsanzo chimene iye amapereka, zimakhudzira anthu ena?
Taonani zimene olemba mbiri, asayansi, akatswiri a maphunziro osiyanasiyana, olemba mabuku, atsogoleri a ndale, ndiponso anthu ena anenapo zokhudza munthu wa ku Nazareti, yemwe ankatchedwa kuti Yesu Khristu:
“Palibe munthu wanzeru zake amene angatsutse mfundo yakuti Yesu wa ku Nazareti ndiye munthu amene wakhudza moyo wa anthu ambiri pa zaka 2,000 zapitazi komanso m’mbiri yonse ya anthu.”—Anatero Reynolds Price, wolemba mabuku wa ku America, yemwenso ndi katswiri wa maphunziro a Baibulo.
“Munthu ameneyu anali wosalakwa ngakhale pang’ono koma anapereka nsembe kuti apindulitse ena, ndi adani ake omwe, ndipo anawombola anthu onse padziko pano. Palibenso wina angachite zinthu ngati zimenezi.”—Anatero Mohandas K. Gandhi, yemwe anali mtsogoleri wandale ndiponso wachipembedzo ku India.
“Ndili mwana ndinaphunzitsidwa mfundo za m’Baibulo ndiponso za mu Talmud. Ndine m’Yuda koma ndimagoma ndi chitsanzo chabwino cha munthu wa ku Nazareti ameneyu.”—Anatero Albert Einstein, wasayansi wa ku Germany.
“Ine ndimaona kuti Yesu Khristu ndi munthu woposa onse m’mbiri yonse ya anthu . . . Chilichonse chimene ananena kapena kuchita n’chofunika kwambiri masiku ano, ndipo palibenso munthu wina amene angafanane ndi Yesu pankhani imeneyi, kaya ali moyo panopa kapena anafa.”—Anatero Sholem Asch, wolemba mabuku wa ku Poland , m’magazini yakuti Christian Herald.
“Kwa zaka 35, sindinkakhulupirira chilichonse pankhani zachipembedzo. Koma ndinasintha maganizo zaka 5 zapitazo. Ndinayamba kukhulupirira ziphunzitso za Yesu Khristu ndipo moyo wanga unasinthiratu.”—Anatero Olemekezeka a Leo Tolstoy, wolemba mabuku ndiponso katswiri wa maphunziro ofufuza nzeru zapamwamba wa ku Russia.
“Mpaka pano, moyo wa [Yesu] umakhudza anthu ambiri padziko pano kuposa moyo wa munthu wina aliyense.”—Anatero Kenneth Scott Latourette, katswiri wa mbiri yakale ndiponso wolemba mabuku wa ku America.
“Kodi tinganene kuti nkhani ya moyo wa Yesu ndi yongopeka? Ayi ndithu, palibe chilichonse chosonyeza zimenezi. Ndipotu ngakhale nkhani ya Socrates, yemwe ndi munthu wotchuka amene ambiri sakayika zoti anakhalako, ilibe umboni weniweni ngati nkhani ya Yesu Khristu.”—Anatero Jean-Jacques Rousseau, katswiri wa maphunziro ofufuza nzeru zapamwamba wa ku France.
Pamenepa n’zoonekeratu kuti palibe munthu wina kuposa Yesu Khristu, yemwe ali wabwino kwambiri kumutsanzira pamoyo wathu. Paulo, anali munthu wophunzira kwambiri ndipo anasankhidwa ndi Yesu kuti akhale wotsatira Wake. Iye anapatsidwa ntchito yokalalikira za Yesu kwa anthu amene sanali Aisiraeli. Ponena za Yesu, Paulo analimbikitsa anthu ‘kuyang’anitsitsa’ Yesuyo. (Aheberi 12:2; Machitidwe 9:3) Kodi Yesu angatiphunzitse chiyani pankhani ya mmene tiyenera kukhalira pamoyo wathu? Kodi moyo wa Yesu ungakuthandizeni bwanji?