Phunzitsani Ana Anu
Paulo Anapulumutsidwa ndi Mwana wa Mlongo Wake
KODI ukudziwa kuti mtumwi Paulo anali ndi abale ake omwenso anali otsatira a Yesu?a— Malemba amasonyeza kuti mlongo wake wa Paulo ndiponso mwana wamwamuna wa mlongo wakeyo anali otsatira a Khristu. Ndipo mnyamatayu anapulumutsa Paulo. Baibulo silitchula dzina la mnyamatayu ndiponso la mayi ake koma limangonena zimene iye anachita. Kodi ungakonde kumva zimene anachitazo?—
Paulo anali atangomaliza ulendo wake wachitatu waumishonale ndipo anapita ku Yerusalemu. Zikuoneka kuti munali m’chaka cha 56 C.E. Panthawiyi, iye anali atamangidwa ndipo amayembekezera kuti azengedwe mlandu. Koma adani ake sankafuna kuti iye akaimbidwe mlandu koma kuti aphedwe basi. Choncho anakonza zoti anthu okwana 40 akamubisalire panjira kuti amuphe.
Koma mwana wa mlongo wa Paulo anamva za chiwembucho. Kodi ukudziwa zimene mnyamatayu anachita?— Iye anakauza Paulo zimene anamvazo. Nthawi yomweyo Paulo anauza msilikali wina kuti: “Pita naye mnyamatayu kwa mkulu wa asilikali, pakuti ali ndi mawu oti amuuze.” Kenako msilikali uja anatenga mnyamatayo n’kupita naye kwa mkulu wa asilikaliwo, yemwe dzina lake linali Klaudiyo Lusiya, n’kumuuza kuti mnyamatayo ali ndi uthenga wofunika kwambiri woti amuuze. Klaudiyo anatengera mnyamatayo pambali, ndipo iye anamuuza zonse zokhudza chiwembucho.
Klaudiyo anachenjeza mnyamatayo kuti: “Usayese kubwetukira aliyense zakuti wandifotokozera zimenezi.” Kenako mkulu wa asilikaliyo anaitanitsa akapitawo awiri a asilikali n’kuwauza kuti aitanitse asilikali wamba 200, asilikali 70 okwera pa akavalo ndiponso asilikali 200 a mikondo kuti apite ndi Paulo ku Kaisareya. Cha m’ma 9 koloko usiku, asilikali onsewo, okwana 470, anyamuka ulendo wopita ndi Paulo ku Kaisareya kwa bwanamkubwa wachiroma dzina lake Felike, ndipo anakam’siya ali bwinobwino. Klaudiyo analembera kalata Felike, yom’fotokozera zonse zokhudza chiwembu chofuna kupha Paulo.
Choncho Ayuda anakakamizika kupita ku Kaisareya kukakumana ndi Paulo m’bwalo la milandu kuti akafotokoze zomwe Paulo analakwa. Komabe iwo analibe umboni uliwonse wosonyeza kuti Paulo anali ndi mlandu. Ngakhale zinali choncho, Paulo anatsekeredwa m’ndende kwa zaka ziwiri. Zimenezi zinachititsa kuti iye apemphe kuti akaweruzidwe ndi Kaisara ku Roma, ndipo anam’tumizadi kumeneko.—Machitidwe 23:16–24:27; 25:8-12.
Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene mnyamatayu anachita?— Tikuphunzirapo kuti tifunika kulimba mtima kuti chilungamo chichitike chifukwa kuchita zimenezi kungapulumutse moyo wa anthu ena. Tiyeneranso kutengera chitsanzo cha Yesu yemwe anapitirizabe kuuza anthu za Ufumu wa Mulungu, ngakhale kuti adani ake “anali kufunitsitsa kumupha.” Kodi chingatithandize n’chiyani kuti tichite zimenezi? Kuti tichite zimenezi tiyenera kulimba mtima ngati mmene anachitikira mwana wamwamuna wa mlongo wake wa Paulo uja.—Yohane 7:1; 15:13; Mateyo 24:14; 28:18-20.
Paulo analangiza mnzake Timoteyo yemwe anali wachinyamata kuti: “Udziyang’anire wekha mosalekeza, ndi kusamalanso zimene umaphunzitsa. Pitiriza kuchita zimenezi, pakuti potero, udzadzipulumutsa iwe mwini ndi aja okumvera iwe.” (1 Timoteyo 4:16) Apatu n’zoonekeratu kuti mwana wamwamuna wa mlongo wa Paulo anagwiritsa ntchito malangizo amenewa. Kodi iweyo udzachita zimenezi?
a Ngati mukuwerenga nkhaniyi ndi mwana wanu, mukapeza pamene pali mzere pakusonyeza kuti muime kaye kuti mwanayo anenepo maganizo ake.