Zimene Owerenga Amafunsa . . .
N’chifukwa chiyani Mulungu analonjeza anthu kuti adzawapatsa mphatso ya moyo wosatha?
▪ Baibulo limati Mulungu akufuna kuti adzatipatse “moyo wosatha.” (Yohane 6:40) Komano, n’chifukwa chiyani akufuna kudzatipatsa mphatso imeneyi? Kapena kodi akufuna kutipatsa mphatsoyi chifukwa choti iye ndi wachilungamo?
Munthu wachilungamo amachita zinthu zabwino ndiponso zoyenera kwa anthu ena. Kodi Mulungu adzatipatsa moyo wosatha chifukwa ndife oyenera kuulandira? Ayi. Baibulo limati: “Kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.” (Mlaliki 7:20) Tonse timafunika kulandira chilango chifukwa ndife ochimwa. Ndipo, Mulungu anachenjeza munthu woyambirira, Adamu, kuti tsiku limene adzachimwe adzafa ndithu. (Genesis 2:17) Patapita nthawi, mtumwi Paulo anauziridwa kulemba kuti: “Malipiro a uchimo ndiwo imfa.” (Aroma 6:23) Ndiyeno, ngati ana onse a Adamu ndi oyenera imfa, n’chifukwa chiyani Mulungu akufuna kuwapatsa moyo wosatha?
Moyo wosatha ndi “mphatso yaulere” ndipo ndi umboni wakuti Mulungu ndi wachikondi ndiponso wokoma mtima kwambiri. Baibulo limati: “Onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu. Ndiponso, kuyesedwa kwawo olungama chifukwa cha kukoma mtima kwa m’chisomo chake kumene wakusonyeza, powamasula ndi dipo lolipiridwa ndi Khristu Yesu.”—Aroma 3:23, 24.
Ngakhale kuti tonse timafunika kulandira chilango cha imfa chifukwa ndife ochimwa, Mulungu anasankha kupereka moyo wosatha kwa anthu amene amamukonda. Kodi zimenezi zikusonyeza kuti Mulungu ndi wopanda chilungamo? Baibulo limati: “Ndiye tinene kuti chiyani? Kodi Mulungu alibe chilungamo? Ayi si zimenezo! Pakuti anati kwa Mose: ‘Ndidzachitira chifundo aliyense amene ndikufuna kum’chitira chifundo, ndipo ndidzamvera chisoni aliyense amene ndikufuna kumumvera chisoni.’ . . . Iweyo ndiwe ndani kuti uziyankhana ndi Mulungu?”—Aroma 9:14-20.
M’mayiko ena, mtsogoleri wadziko kapena woweruza amakhululukira anthu amene akugwira ukaidi chifukwa chopalamula mlandu waukulu. Ngati mkaidiyo akutsatira malamulo amene am’patsa ndiponso akusintha khalidwe lake, woweruzayo kapena pulezidentiyo angasankhe zochepetsa chilango chake kapena kungomukhululukira kumene. Zimenezi zingasonyeze kuti amukomera mtima kwambiri mkaidiyo.
Chimodzimodzinso ndi Yehova. Iye angasankhe kukhululukira anthu ochimwa omwe anafunika kulangidwa. Koma chifukwa cha chikondi, iye amapereka moyo wosatha kwa anthu amene amamukonda ndiponso amatsatira malangizo ake. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu ulionse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”—Machitidwe 10:34, 35.
Yehova anasonyeza kuti amatikonda kwambiri potumiza Mwana wake kudzatifera. Ponena za Atate wake, Yesu anati: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.”—Yohane 3:16.
Yehova amalandira aliyense amene amachita zimene amafuna ndiponso amene amamukonda, ndipo amachita zimenezi mosayang’ana kumene munthuyo akuchokera. Choncho, Mulungu anatilonjeza mphatso ya moyo wosatha chifukwa chakuti ndi wokoma mtima ndiponso amatikonda kwambiri.
[Mawu Otsindika patsamba 29]
Mulungu anatilonjeza mphatso ya moyo wosatha chifukwa chakuti ndi wokoma mtima ndiponso amatikonda kwambiri