Mafunso Ochokera kwa Owerenga
Kodi tingamvetse bwanji ziwerengero za mu lipoti la chaka chautumiki?
Chaka chilichonse timasangalala kulandira lipoti la utumiki limene limalembedwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Zimakhala zosangalatsa kuona zimene gulu la anthu a Yehova lachita padziko lonse m’ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu za Ufumu. Koma kuti tipinduledi ndi lipotili tiyenera kumvetsa zimene zalembedwamo ndiponso ziwerengero zake. Tiyeni tione mbali zina za lipotili.
Chaka chautumiki. Chaka chimenechi chimayamba pa September 1 n’kukathera pa August 31 chaka chotsatira. Mu Utumiki Wathu wa Ufumu mumakhala lipoti la chaka chautumiki chimene chatha. Choncho mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa April 2011 muli lipoti la chaka chautumiki cha 2010 chimene chinayamba pa September 1, 2009, n’kukathera pa August 31, 2010.
Chiwerengero chapamwamba cha ofalitsa ndiponso avereji ya ofalitsa. Mawu akuti “ofalitsa” amanena za Mboni za Yehova zobatizidwa komanso anthu osabatizidwa amene ndi oyenera kulalikira za Ufumu. “Chiwerengero chapamwamba cha ofalitsa” chikuimira chiwerengero cha mwezi umene unali ndi ofalitsa ambiri amene anapereka malipoti kuposa miyezi ina yonse. Chimaphatikizapo malipoti ochedwa amene sanaphatikizidwe m’mwezi wapita. Izi zimachititsa kuti ofalitsa ena awerengedwe kawiri. Koma chiwerengerochi sichiphatikizapo ofalitsa amene analalikira koma n’kuiwala kupereka lipoti. Choncho m’pofunika kuti wofalitsa aliyense azipereka lipoti la mwezi uliwonse pa nthawi yake. “Avereji ya ofalitsa” ndi chiwerengero chimene amapeza akawonkhetsa malipoti a miyezi yonse n’kugawa ndi 12.
Maola. Malinga ndi Utumiki Wathu wa Ufumu wa April, Mboni za Yehova zinalalikira kwa maola 1,604,764,248. Komabe maolawa sakuphatikizapo nthawi imene timachita zinthu zina zokhudza kulambira kwathu monga maulendo aubusa, kusonkhana, kuphunzira Baibulo patokha kapena kusinkhasinkha.
Ndalama zimene zagwiritsidwa ntchito. M’chaka chautumiki cha 2010, Mboni za Yehova zinagwiritsa ntchito ndalama zopitirira madola 155 miliyoni posamalira apainiya apadera, amishonale ndi oyang’anira oyendayenda mu utumiki wawo. Koma chiwerengerochi sichikuphatikizapo ndalama zimene zimagwiritsidwa ntchito posindikiza mabuku athu ofotokoza Baibulo. Sichikuphatikizanso ndalama zimene zimagwiritsidwa ntchito posamalira atumiki a pa Beteli oposa 20,000 amene ali m’maofesi a nthambi padziko lonse.
Akudya pa chikumbutso. Ichi ndi chiwerengero cha padziko lonse cha anthu obatizidwa amene adya zizindikiro pa Chikumbutso. Kodi chimenechi ndi chiwerengero cha odzozedwa onse amene ali padziko lapansi? Sitinganene choncho. Pali zinthu zina zimene zingachititse munthu kuganiza kuti ndi wodzozedwa pomwe sizili choncho. Zinthu zake ndi monga zikhulupiriro za m’chipembedzo chake chakale komanso mavuto kapena matenda ena okhudza maganizo. Choncho sitingadziwe chiwerengero chenicheni cha odzozedwa amene ali padziko lapansi ndipo kudziwa zimenezi si kofunika kwenikweni. Bungwe Lolamulira silisunga mayina a anthu amene adya mkate ndi kumwa vinyo pa Chikumbutso.a
Chomwe tikudziwa n’chakuti “akapolo a Mulungu” odzozedwa ena adzakhala ali padziko lapansi pamene mphepo za chiwonongeko za chisautso chachikulu zidzasiyidwa kuti ziwombe. (Chiv. 7:1-3) Chisautso chachikuluchi chisanafike, Akhristu odzozedwa adzapitiriza kutsogolera ntchito imene imalembedwa mu lipoti la pachaka. Ntchito imeneyi ndi yolalikira ndi kuphunzitsa anthu ndipo ikugwiridwa kwambiri masiku ano kuposa kale lonse.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Mdindo Wokhulupirika ndi Bungwe Lake Lolamulira,” mu Nsanja ya Olonda ya June 15, 2009, tsamba 24.