NKHANI YA PACHIKUTO | KODI UFUMU WA MULUNGU UDZAKUCHITIRANI CHIYANI?
N’chifukwa Chiyani Muyenera Kudziwa za Ufumu wa Mulungu?
Anthu ambiri amakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetse mavuto padzikoli. Amatsanzira Yesu yemwe anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.”—Mateyu 6:10, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.
N’zodabwitsa kuti ngakhale kuti anthu ambiri amaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika, zipembedzo zambiri siziphunzitsa kwenikweni zokhudza Ufumuwu. Pa nkhaniyi, katswiri wina wa mbiri yakale, dzina lake H. G. Wells, ananena kuti ngakhale kuti mfundo yaikulu ya zimene Yesu ankaphunzitsa inali Ufumu wakumwamba, masiku ano matchalitchi ambiri saphunzitsa kwenikweni anthu awo zokhudza Ufumuwu.
Mosiyana ndi matchalitchi amenewa, a Mboni za Yehova amaphunzitsa kwambiri zokhudza Ufumu wa Mulungu. Mwachitsanzo, magazini athu a Nsanja ya Olonda, ngati imene mukuwerengayi, amamasuliridwa m’zinenero 220. Magaziniwa ndi amene amafalitsidwa kwambiri kuposa magazini ena onse padziko lonse. Mwezi uliwonse magazini pafupifupi 46 miliyoni a Nsanja ya Olonda amasindikizidwa. Koma kodi uthenga waukulu umene umapezeka m’magaziniwa ndi wotani? Dzina lonse la magaziniyi ndi lakuti: Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova.a Izi zikusonyeza kuti cholinga chachikulu cha magaziniwa ndi kulengeza za Ufumu wa Mulungu.
N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova amachita khama chonchi kulengeza za Ufumu wa Mulungu? Chifukwa timakhulupirira kuti nkhani yaikulu m’Baibulo lonse ndi yokhudza Ufumu wa Mulungu. Komanso chifukwa choti timakhulupirira kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene udzathetse mavuto onse padzikoli.
A Mboni za Yehova amayesetsa kutsatira chitsanzo cha Yesu pouza anthu za Ufumu wa Mulungu. Yesu ali padziko lapansi, ntchito yake yaikulu inali kulalikira za Ufumu wa Mulungu ndipo uthenga wake waukulu unali wokhudza zimene Ufumuwu udzachite. (Luka 4:43) N’chifukwa chiyani Yesu ankaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambiri? Nanga n’chifukwa chiyani Ufumuwu ulinso wofunika kwa inuyo? Tikukupemphani kuti muwerenge nkhani zotsatirazi kuti mupeze mayankho a m’Baibulo a mafunso amenewa.
a Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.