Kodi Mukudziwa?
Kodi amalonda amene ankagulitsa nyama kukachisi mu Yerusalemu analidi ngati “achifwamba”?
BUKU la Mateyu limanena kuti: “Yesu analowa m’kachisi ndi kuthamangitsa onse ogulitsa ndi ogula m’kachisimo, ndipo anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mabenchi a ogulitsa nkhunda. Iye anawauza kuti: ‘Malemba amati, “Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo,” koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.’”—Mat. 21:12, 13.
Mabuku a mbiri yakale ya Ayuda amasonyeza kuti amalondawa ankapeza phindu mwachinyengo pokweza kwambiri mitengo. Mwachitsanzo, buku lina limanena kuti pa nthawi ina amalondawo ankagulitsa nkhunda ziwiri zoti anthu apereke nsembe pa mtengo wa dinari imodzi yagolide. Ndalamayi ndi imene munthu wamba ankapeza akagwira ntchito kwa masiku 25. Nkhunda kapena njiwa ndi zimene anthu osauka ankaloledwa kupereka nsembe. Koma amalondawo ankagulitsanso mbalame zimenezi pa mtengo wodula kwambiri. (Lev. 1:14; 5:7; 12:6-8) Rabi wina dzina lake Simeon ben Gamaliel ataona zimene zinkachitikazi, anadandaula kwambiri. Choncho anachepetsa chiwerengero cha nsembe zimene anthu ankayenera kupereka ndipo izi zinathandiza kuti mtengo wa njiwa ziwiri utsike ndi 99 peresenti.
Malinga ndi zimene tafotokozazi, Yesu ananena zoona pamene anatchula amalonda akukachisi kuti “achifwamba.” Zili choncho chifukwa anthuwo anali achinyengo komanso adyera kwambiri.