Mafunso Ochokera Kwa Owerenga
Kodi nthawi zonse mwana woyamba kubadwa ndi amene ankakhala mumzere wa makolo a Mesiya?
M’mbuyomu tanenapo zinthu zina zosonyeza kuti zimenezi n’zoona. Tinkaona kuti mfundo imeneyi ikugwirizana ndi lemba la Aheberi 12:16. Lembali limanena kuti Esau anali “wosayamikira zinthu zopatulika” ndipo “anapereka [kwa Yakobo] udindo wake monga woyamba kubadwa pousinthanitsa ndi chakudya chodya kamodzi kokha.” Malinga ndi lembali, zinkaoneka kuti pamene Yakobo anatenga udindo “monga woyamba kubadwa” anakhalanso mumzere wa makolo a Mesiya.—Mat. 1:2, 16; Luka 3:23, 34.
Koma pambuyo pofufuza bwinobwino nkhani za m’Baibulo, taona kuti munthu sankafunikira kukhala woyamba kubadwa kuti akhale mumzere wa makolo a Mesiya. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.
M’banja la Yakobo (Isiraeli), mwana woyamba kubadwa anali wa Leya ndipo dzina lake anali Rubeni. Koma mwana woyamba kubadwa wa Rakele anali Yosefe. Ndiyeno Rubeni atalakwitsa zinthu, udindo wokhala mwana woyamba kubadwa unapita kwa Yosefe. (Gen. 29:31-35; 30:22-25; 35:22-26; 49:22-26; 1 Mbiri 5:1, 2) Koma Rubeni ndi Yosefe sanali mumzere wa makolo a Mesiya. M’malomwake amene anali mumzerewu anali mwana wa nambala 4 wa Leya, dzina lake Yuda.—Gen. 49:10.
Lemba la Luka 3:32 limatchula anthu 5 amene anali m’gulu la makolo a Mesiya ndipo zikuoneka kuti anthu 5 onsewa anali oyamba kubadwa. Lembali limasonyeza kuti Boazi anabereka Obedi ndipo Obedi anabereka Jese.—Rute 4:17, 20-22; 1 Mbiri 2:10-12.
Mwana wa Jese amene anali mumzere wa makolo a Mesiya anali Davide koma sanali woyamba kubadwa. Iye anali mwana womaliza pa ana aamuna 8 a Jese. (1 Sam. 16:10, 11; 17:12; Mat. 1:5, 6) Mwana wa Davide amene anali mumzerewu ndi Solomo ndipo nayenso sanali mwana woyamba kubadwa.—2 Sam. 3:2-5.
Komatu apa sitikutanthauza kuti kukhala mwana woyamba kubadwa kunali kopanda ntchito. Tikutero chifukwa choti mwana woyamba kubadwa ankalemekezedwa kwambiri ndipo ndi amene ankayang’anira banja lonse ngati bambo ake amwalira. Iye ankapatsidwanso magawo awiri a katundu aliyense wa m’banjalo.—Gen. 43:33; Deut. 21:17; Yos. 17:1.
Koma munthu ankatha kulandidwa udindo wokhala mwana woyamba kubadwa, udindowo n’kuupereka kwa mwana wina. Mwachitsanzo, Abulahamu anathamangitsa Isimaeli n’kupereka udindo woyamba kubadwa kwa Isaki. (Gen. 21:14-21; 22:2) Monga tanena kale, Rubeni analandidwanso udindowu ndipo unaperekedwa kwa Yosefe.
Tsopano tiyeni tikambiranenso nkhani ya pa Aheberi 12:16 ija. Lembali limati: “Muonetsetsenso kuti pasakhale wadama kapena aliyense wosayamikira zinthu zopatulika, ngati Esau, amene anapereka udindo wake monga woyamba kubadwa pousinthanitsa ndi chakudya chodya kamodzi kokha.” Kodi lembali likutanthauza chiyani?
Apa mtumwi Paulo sankafotokoza za mzere wa makolo a Mesiya. Iye ankangolimbikitsa Akhristu anzake kuti ‘awongole njira zimene ankayendamo’ n’cholinga choti ‘asalandidwe kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.’ Iwo akanafanana ndi Esau n’kulandidwa kukoma mtima kwa Mulungu ngati akanachita chiwerewere. (Aheb. 12:12-16) Paja iye ‘sanayamikire zinthu zopatulika’ ndipo anazisinthanitsa ndi zinthu zachabechabe.
Esau ayenera kuti nthawi zina ankakhala ndi mwayi wopereka nsembe kwa Yehova. (Gen. 8:20, 21; 12:7, 8; Yobu 1:4, 5) Koma popeza sankaona zinthu mmene Yehova amazionera, analolera kutaya mwayi umenewu pousinthanitsa ndi mbale ya chakudya basi. N’kutheka kuti iye ankadziwa ulosi wonena za mavuto amene mbewu ya Abulahamu idzakumane nawo ndipo ankafuna kupewa mavutowo. (Gen. 15:13) Esau anasonyezanso kuti sankakonda zinthu zauzimu chifukwa anakwatira akazi osalambira Yehova ndipo makolo ake anamva nazo chisoni kwambiri. (Gen. 26:34, 35) Izi n’zosiyana kwambiri ndi zimene Yakobo anachita. Iye anaonetsetsa kuti wakwatira mkazi amene amalambira Mulungu woona.—Gen. 28:6, 7; 29:10-12, 18.
Malinga ndi zimene takambiranazi, kodi tinganene chiyani za mzere wa makolo a Yesu yemwe ndi Mesiya? N’zoona kuti ana oyamba kubadwa ankakhala mumzerewu koma si nthawi zonse. Ayuda ankadziwa zimenezi ndipo sankadabwa nazo. Tikutero chifukwa chakuti ankavomereza zoti Khristu adzakhala mwana wa Davide, yemwe anali mwana wamwamuna womaliza wa Jese.—Mat. 22:42.