Gaŵirani Buku la Achichepere Akufunsa m’March
1 Buku la Achichepere Akufunsa nlapadera m’njira zambiri. Lalinganizidwira kuthandiza achichepere. Pakati pa zinthu zina, limapereka chitsogozo cha makhalidwe kwa achichepere kuti apeŵe tsoka pokhala osoŵa uchikulire. (Mlal. 11:10) Thandizani ena kuzindikira mmene uthenga umenewo umayambukirira ana awo mwa kugaŵira buku limeneli muutumiki m’March. Malingaliro otsatira angakhale othandiza kwa inu pokonzekera ulaliki wanu.
2 Mutapereka moni, mwina kungakukhalireni bwino kunena zonga izi:
◼ “Kukulira m’nthaŵi zino zamavuto nkovuta. Achichepere amayang’anizana ndi mikhalidwe yambiri yatsopano imene imafuna kuti apange zosankha zazikulu. ‘Kodi ndiyenera kumwa moŵa? Kumwa anamgoneka? Kodi khalidwe loyenera pakati pa asungwana ndi anyamata nlotani?’ Pamene achichepere afunsa za nkhani zazikulu zimenezi, iwo kaŵirikaŵiri amapeza mayankho ambiri owombana. Kodi muganiza nkuti kumene ambiri a iwo amapita kaamba ka thandizo? [Yembekezerani yankho.] Bukuli, Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza, limapereka chidziŵitso chothandiza. [Sonyezani mpambo wa zamkati mwake, mukumasonyeza nkhani zosiyanasiyana zofotokozedwa.] Achichepere amafuna mayankho achindunji ndi ofotokoza zenizeni. Mayankho m’bukuli amachirikizidwa ndi zimene Baibulo limanena.”
3 Nawu ulaliki wina umene mwina mungakhoze kugwiritsira ntchito:
◼ “Achichepere ali ndi zitsenderezo zambiri lerolino. Amafunikira chithandizo kuti alimbane nazo mwachipambano. Pamene tikuchita zimene tingathe kuyesa kuwathandiza, kodi sitimafuna kanthu kena kamene kamapereka chitsogozo chogwira ntchito? [Yembekezerani yankho.] Zina za zitsenderezo zovuta kwambiri zimachokera kwa achichepere ena, ausinkhu wawo. Taonani zithunzithunzi pamasamba 76 ndi 77 m’buku limeneli. [Kambani pamawu ofotokoza zithunzithunzi zimenezo ndi pandime zakanyenye patsamba 77.] Masamba otsatira m’mutu umenewu ali ndi mayankho ogwira ntchito ndi owona mtima.”
4 Zino zilidi “nthaŵi zoŵaŵitsa,” makamaka kwa achichepere. (2 Tim. 3:1) Buku la Achichepere Akufunsa lingathandizedi achichepere kuyang’anizana ndi mavuto a lerolino mwachipambano. Mitu yonse 39 ili ndi zithunzithunzi zambiri, ndipo nkhanizo zimafotokoza zinthu zenizeni ndi zogwira ntchito. Chotero panthaŵi iliyonse pamene mpata upezeka, khalani atcheru kugwiritsira ntchito buku labwino limeneli.
5 Tsimikizirani kuitanira aliyense amene asonyeza chikondwerero kupezeka pa Chikumbutso. Ndi dalitso la Yehova, mungakhoze kuthandiza anthu owona mtima, kudzutsa chikondwerero cha Baibulo ndi zifuno za Yehova.—Marko 13:10.