Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 6/95 tsamba 3-6
  • Msonkhano Wachigawo wa 1995 wa “Atamandi Achimwemwe”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Msonkhano Wachigawo wa 1995 wa “Atamandi Achimwemwe”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Msonkhano Wachigawo wa mboni za Yehova wa “Amithenga a Mtendere Waumulungu” wa 1996
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1996
  • Msonkhano Wachigawo wa 1997 wa “Kukhulupirira Mawu a Mulungu”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Zokumbutsa za Msonkhano Wachigawo wa 1998 Wakuti: “Njira ya Moyo ya Mulungu.”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Msonkhano Wachigawo Wakuti “Mantha Aumulungu” wa 1994
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1994
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 6/95 tsamba 3-6

Msonkhano Wachigawo wa 1995 wa “Atamandi Achimwemwe”

1 Kodi tili ndi zifukwa zingati zokhalira achimwemwe? Mwinamwake angapo a ife tayesa kuzindandalika zonse. Ngakhale kuti tikukhala m’dziko lachipwirikiti ndi losadalirika, tili ndi zifukwa zambiri zokhalira achimwemwe. Molingana ndi chilengezo cha mu Utumiki Wathu Waufumu wa January 1995, “Atamandi Achimwemwe” uli mutu wolimbikitsa wa misonkhano yachigawo ya 1995.

2 Timatamanda Yehova chifukwa chakuti anatiphunzitsa choonadi. (Yes. 54:13; Yoh. 8:32) Ndiyeno, ifenso timakhala achimwemwe kugaŵana choonadi ndi onse amene akufunafuna chisungiko ndi chimwemwe. (Ezek. 9:4; Mac. 20:35) Ubale wathu Wachikristu umatipatsanso chimwemwe. Banja lauzimu lachikondi limapatsa chikhutiro ndi chisangalalo. Izi ndi zifukwa zoŵerengeka chabe zimene timakhalira achimwemwe chimene chimatisonkhezera kutamanda Yehova. Nkhani za msonkhano wachigawo ndi zitsanzo zidzachititsa malingaliro athu kusumika pa zifukwa zinanso za Malemba zokhalira achimwemwe m’masiku otsiriza ano odzala ndi mavuto.

3 Msonkhano Wachigawo wa Masiku Atatu: Kodi mwakambitsirana ndi mkulu wantchito kuti adzakupatseni nthaŵi yokapezekapo pamsonkhano masiku onse atatu? Makolo amene ali ndi ana asukulu amene adzapezeka pamsonkhano mkati mwa masiku akuphunzira ayenera mwaulemu kudziŵitsa aphunzitsi kuti anawo sadzakhalako kusukulu pa Lachisanu chifukwa cha mbali yofunika kwambiri imeneyi ya kulambira kwawo. Kodi msonkhano wapafupi ndi kwanu uli kuti? Utumiki Wathu Waufumu wa April unandandalika madeti ndi malo a misonkhano isanu ndi inayi m’gawo la Malaŵi. Mlembi wa mpingo wanu ayenera kukhala atakudziŵitsani kale zofunika za mpingo wanu. Kuwonjezera pa Yachicheŵa, padzakhalanso msonkhano Wachingelezi.

4 Programu idzayamba pa Lachisanu pa 9:20 a.m. ndipo idzatha pa Sande pafupifupi 4:15 p.m. Pa Loŵeruka, programu idzayamba ndi 9:00 a.m. ndipo, pa Sande, idzayamba ndi 9:30 a.m.

5 Kodi Mudzakhalapo?: Tikulimbikitsidwa kudzakhalapo masiku onse atatu a msonkhano. Chifukwa ninji? Yehova akufuna kuti tidzakhalepo. Lerolino chikhulupiriro chathu ndi umoyo wathu wauzimu zili pachiyeso chachikulu. Paulo anapereka uphungu wonena za ‘kusaleka kusonkhana kwathu pamodzi’ panthaŵi imene Akristu mu Yudeya anakumana ndi vuto lalikulu. (Aheb. 3:12, 13; 10:25) Afilipi anali kukhala “pakati pa mbadwo wokhotakhota ndi wopotoka.” Komabe, iwo anali ‘kuonekera monga mauniko m’dziko lapansi.’ (Afil. 2:15) Kodi nchifukwa ninji Akristu a m’zaka za zana loyamba ameneŵa anali osiyana? Chifukwa chakuti momvera anatsatira zitsogozo za mzimu woyera umene unawatsogolera kukasonkhana pamodzi kuti ‘afulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino.’—Aheb. 10:24.

6 Dziko lingatisonkhezere kuleka kuchita zimenezo, likumafooketsa chikhumbo chathu cha kusonkhana pamodzi ndi abale athu ndi kutamanda Yehova. Chilimwe cha chaka chino, tikupemphedwa kulabadira mzimu wa Yehova kuti tidzasangalale ndi masiku onse atatu a msonkhanowo. Kodi tili otsimikiza mtima kudzakhalapo pamodzi ndi banja lathu lonse? Tiyenera nthaŵi zonse kumalimbitsa chikondi chathu ndi chikhulupiriro chathu. Yehova wapereka misonkhano ya chaka ndi chaka kuti itithandize kuchita zimenezo.

7 Bwererani Kunyumba ndi Chuma: Kodi ndimotani mmene mungapindulire kopambana ndi msonkhanowo? Mwachidule, yankho ndilo “kusumika maganizo.” Zimenezi nzovuta m’dziko lamakono losakhazikika ndi lotanganidwa. Kungakhale kovuta kwa anthu achichepere ndi anyonga kusumika maganizo, komanso lili vuto limene tonsefe timakhala nalo pamsonkhano wachigawo. Kusumika maganizo kudzatikhalira kosavuta ngati tikonzekera pasadakhale. Dzifunseni kuti, ‘Kodi msonkhano uli ndi mutu wotani?’ Usinkhesinkheni! ‘Kodi ndidzapitiranji, ndipo ndidzakhala ndikuchitanji pamasiku atatuwo? Kodi madzulo ndidzakhala womatanganidwa ndi zosangulutsa, kapena kodi ndalinganiza nthaŵi yokwanira ya kupumula ndi kupendanso mfundo zazikulu za msonkhano?’

8 Nkhani ya mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 1984 yakuti “Kodi Mumasinkhasinkha Kapena Kulota Masana?” inapereka malingaliro angapo osonyeza mmene mungapindulire kwambiri ndi msonkhano ndiyeno inati pomaliza: ‘Mwinamwake kulamulira maganizo ndiko mbali yofunika kopambana.’ Pamene wokamba nkhani ayamba, kaŵirikaŵiri timatchera khutu, koma mwinamwake mkati mwa nkhaniyo, timalola maganizo athu ‘kuyamba kuyendayenda.’ Kodi tingachitenji kuti zimenezi zisachitike?

9 Malingaliro operekedwa kumbuyoku ali ofunika kubwerezedwa chifukwa chakuti amathandiza. Ngati kuli kotheka, yesani kupeza mpumulo wokwanira usiku uliwonse. Zimenezi nzovuta nthaŵi zina chifukwa pangakhalenso kuyenda, ndipo ngati mukukhala m’hotela, mwina simungamagone mwamsanga kapena kupumula mmene mungachitire kunyumba kwanu. Kaŵirikaŵiri kukonzekera kwabwino kudzakuchititsani kupeza mpumulo wofunikira.

10 Kulemba nsonga zachidule kwakhalanso kothandiza kusumika maganizo. Ngati muyesa kulemba zochuluka, mungaphonye mfundo zina zofunika. Monga lingaliro, lembani nsonga ndi cholinga cha kupereka chidule cha programuyo kwa wophunzira Baibulo kapena kwa wobindikira m’nyumba. Ngakhale ngati mulibe munthu wina m’maganizo, mudzakhala ndi chifuno cholembera nsonga, ndipo pambuyo pa msonkhano mungapeze nthaŵi pamene mungafotokozere ziŵalo za banja zosakhulupirira mfundo zazikulu za programuyo monga umboni wamwamwaŵi. Mwa kulemba nsonga ndi kuuzako ena zimene munamva, simudzaiŵala msanga chidziŵitsocho. Kuzilankhula kumakulitsa chikumbukiro.

11 Ngakhale kuti chakudya sichidzaperekedwanso, padzakhalabe ndalama zina zowonongedwa zolipirira malo a msonkhano, zimene kaŵirikaŵiri zimaphatikizapo malipiro ena a ziŵiya zolankhulira, mabuku, ndi zina zotero. Kodi zowonongedwa zimenezi zimalipiriridwa motani? Mwa zopereka zathu zaufulu, kaya mwa ndalama kapena mwa cheke chokhoza kulipiriridwa kwa “Mboni za Yehova.” Zimenezi nzogwirizana ndi Salmo 96:8 ndi 2 Mbiri 31:12.

12 Atamandi Achimwemwe Amalemekeza Yehova mwa Khalidwe Laumulungu: Chaka chatha panali ndemanga zolimbikitsa zimene zinaperekedwa ndi ogwira ntchito m’mamotela ndi pamalo a msonkhano ponena za khalidwe lathu. Manijala wina wa hotela anati: “Nthaŵi zonse timakondwera kusunga Mboni chifukwa chakuti zili zoleza mtima ndi zogwirizanika ndipo zimasamalira ana awo.” Mkulu wina wa hotela anati Mboni zimaoneka kukhala zachimwemwe ndi zadongosolo kuposa magulu ena. Ngakhale kuti msonkhano wathu ndiwo unali waukulu koposa m’deralo, iye anati: “Tilibe nazo madandaulo ambiri ndipo sitinavutike nazo mofanana ndi magulu ena aang’ono kwambiri poyerekezera ndi izo.”

13 Winanso wogwira ntchito m’hotela ananena kuti msonkhano wina waposachedwa umene unachitika wathu usanachitike unawonongetsa zinthu zambiri, panalinso kuba, ngakhale kuti antchito onse analipo. Koma ponena za msonkhano wathu, iye anati: “Sitimada nkhaŵa ndi zimenezo kwa Mboni. . . . Pamene izo zili pano, timangosiyapo munthu mmodzi kapena aŵiri okonza zinthu kuti azingokonza makina ngati avuta pang’ono.”

14 Zikanakhala bwino koposa ngati malipoti onse amene timalandira anali otero, koma tsoka lake nlakuti sindimo mmene zinthu sizili. Tcheyamani wina wa msonkhano wachigawo anati: “Pambuyo pa maprogramu, achinyamata ambiri amasonkhana m’magulu aakulu m’zipinda zofikira alendo [za mahotela] nthaŵi ya usiku kwambiri, akumaseka mwaphokoso ndi kufuula. Zimenezi zimasokosera alendo ena . . . , amene amaoneka kukhala okwiya nazo. Achichepere ena amathamanga m’malikole, akumamenyetsa zitseko pamene akuchezerana m’zipinda zawo ndi kulankhula mwaphokoso kwambiri m’zipindazo.”

15 Vuto lina limene lakhalapo kwa zaka zambiri ndilo la abale ambiri omayendayenda m’malikole ndi kunja kwa malo osonkhanira mkati mwa maprogramu. Pamsonkhano wina chaka chatha, kalata ya wophunzira Baibulo wina inapezedwa m’bokosi la zopereka. Iyo inati: “Sindinaonepo za mtundu umenewu, phokoso, zochitachita, kulankhulalankhula, ndi kupulupudza m’malikole mkati mwa kukambidwa kwa nkhani . . . sindinakhalebe Mboni, ndili chabe wophunzira mantha aumulungu ndi ulemu.” Ndithudi, palibe aliyense wa ife amene angafune kupereka chithunzi chakuti sitiyamikira makonzedwe a Yehova.

16 Nthaŵi zonse tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimaimira yani, ndipo nchifukwa ninji ndili pamsonkhano uno?’ Mkhalidwe wathu wauzimu ndi kudzipereka kwathu kwaumulungu zimasonyezedwa m’kalankhulidwe kathu, khalidwe, ndi kuyamikira kwathu zinthu zauzimu. (Yak. 3:13; 1 Pet. 2:2, 3, 12) Abale amene apirira ziletso kwa zaka zambiri kaŵirikaŵiri aonedwa kukhala osumika maganizo kwambiri ndi aulemu pamisonkhano, akumakhalabe m’mipando yawo, atatchera khutu ku nkhani ndi zitsanzo.

17 Mavalidwe ndi Mapesedwe Anu Amanena za Inu: Pa 1 Samueli 16:7, timakumbutsidwa kuti “munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.” Chotero, anthu kaŵirikaŵiri amatiweruzira pa maonekedwe athu. Mavalidwe athu ndi mapesedwe amapendedwa kwambiri, makamaka pamene tili pamsonkhano wa kulambira ndi kulangiza kwa moyo Wachikristu. Ngati ndinu wachichepere amene amapita kusukulu kapena ngati ntchito yanu imakuchititsani kuyanjana kwambiri ndi anthu amene amatsatira masitayelo adziko, kungakhale kovuta kumamatira pa miyezo Yachikristu ya mavalidwe odekha.

18 Miyezo ya mavalidwe ndi mapesedwe imasiyanasiyana padziko lonse. Akristu ayenera kuvala chovala choyenera ndi cholinganizika bwino. Kodi ndani ayenera kusankha zimenezi? Makolo ayenera kutsimikizira kuti ana awo achinyamata sakuvala monga achinyamata a dziko pamasukulu. Tapatsidwa zitsogozo zotithandiza kupanga zosankha zoyenera pankhani yaikulu imeneyi.

19 Pambuyo pa Msonkhano Wachigawo wina wa “Mantha Aumulungu,” tinalandira mawu aŵa: “Abale ndi alongo awongolera kwambiri mavalidwe, mapesedwe, ndi khalidwe pamsonkhano wa chaka chino. . . . Komabe, pakali mikhalidwe ndi zizoloŵezi zina zimene zifunikira kuwongolera kwinanso.” Pambuyo pa msonkhano wina panafika lipoti lakuti mavalidwe osayenera anali oonekeratu. Lipotilo linati mavalidwe a ena anali okhumudwitsa kwa ena. Akunja ena amene analipo nawonso anaona mavalidwe osadekhawo. Mavalidwe a ena anali oonetsa thupi ndi ogwira thupi kwambiri.

20 Ngati akulu aona kuti ena ali ndi chizoloŵezi cha mavalidwe osapereka ulemu, ayenera kupereka uphungu wokoma mtima koma wamphamvu msonkhano usanafike, kusonyeza kuti mavalidwe oterowo ali osayenera, makamaka kwa nthumwi zofika pamsonkhano Wachikristu. Chonde kambitsiranani ndi ophunzira Baibulo anu amene adzapezeka pamsonkhano za malangizo a khalidwe ndi mavalidwe olongosoledwawa.

21 Malo Ogona: Kungakhale kothandiza kwambiri kuti ofalitsa aŵerengenso pamodzi ndi ophunzira nawo Baibulo mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa March 1995 ponena za malo ogona.

22 Makamera ndi Ziŵiya Zina Zojambulira: Kuli koyenera kupereka zikumbutso zoyenera ponena za makamera ndi ziŵiya zina zojambulira. Chonde kumbukirani, ngati mukufuna kudzagwiritsira ntchito makamera, kapena mtundu wina uliwonse wa chiŵiya chojambulira, sonyezani kulingalira ena okhala pafupi nanu. Kuyendayenda uku ndi uku mkati mwa maprogramu kapena ngakhale kujambula muli pampando panu kungasokoneze ena. Palibe ziŵiya zojambulira za mtundu uliwonse zimene ziyenera kulumikizidwa ku magetsi a zolankhulira, kapena kuikidwa m’njira zoyendamo. Kaya mukufuna kujambula zithunzi kapena mbali ya programu ndi tepirikoda ili nkhani yaumwini. Zithunzi ndi zojambulidwa zingakukumbutseni zinthu zabwino pamene muziona panthaŵi ina mtsogolo. Ziŵiya zonse zotero ziyenera kugwiritsiridwa ntchito mosamala, mwa njira imene siidzasokoneza ena kapena kukulepheretsani kupindula kwambiri ndi programuyo. Mutabwerera kunyumba, kodi mudzakhala ndi nthaŵi ya kumvetseranso zojambulidwazo? Mungapeze kuti kulemba nsonga kungakhale kothandiza.

23 Kakhalidwe: MIPANDO INGASUNGIDWIRE ZIŴALO ZA BANJA LANU ZOKHA NDI ALIYENSE AMENE MUNGANYAMULE M’GALIMOTO YANU. Pamalopo timakhala alendo a Sosaite. Malo osonkhanirawo amalipiriridwa ndi zopereka zaufulu. Kodi kungakhale kusonyeza chikondi ndi kulingalira ena kusunga mipando imene sitili otsimikiza ngati padzakhala munthu? Pepani kuti sikudzakhala kotheka kuti tidzapereke malo apadera opemphedwa kapena zipinda zogona kwa aja amene amadwala akayambukiridwa ndi zinthu zina.

24 Msonkhano uliwonse umakhala ndi makonzedwe osamalira amene ali ndi zosoŵa zapadera, monga okalamba ndi olemala. Chonde tsimikizirani kuti simukukhala pamipando ya m’malo otero ngati simuli oyenera. Ndiponso, khalani atcheru pa kuthandiza amene ali ndi zosoŵa zapadera kupeza mpando ngati sali ndi wina wowasamalira.

25 Kudzikonzera Chakudya Pamsonkhano: Mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa March 1995 inapereka malingaliro abwino onena za mmene aliyense angadzikonzere zakudya ndi zakumwa pamsonkhano. Kungakhale bwino kuti onse apendenso mpatika imeneyo ndi kuiŵerenganso pamodzi ndi ophunzira nawo Baibulo pamene akukonzekera msonkhano. Kuli kofunika kwambiri kuti ophunzira Baibulo akhale akudziŵa kuti onse ayenera kubwera ndi zakudya ndi zakumwa zawo pamsonkhano.

26 Kungoti tigogomezere mfundo zina, muyenera kukumbukira kubweretsa zakudya zonga zotchulidwa pano kaamba ka kupuma kwa masana. Zakudya zopepuka zomanga thupi zonga zimene anthu amapita nazo kuntchito, monga masangweji, zipatso, mtedza, masikono, ndi zina zotero. Zakumwa zingaphatikizepo kofi, zakumwa zozizira, zakumwa za zipatso, kapena madzi a m’botolo, m’chotengera chosasweka kapena m’fulasiki. Ngati zotengera zazing’ono zoziziritsa zili zofunika, zingaloledwe ngati zidzakwana pansi pa mpando wanu. Komabe, zotengera zazikulu zoziziritsa monga za ku pikiniki, moŵa, kapena zotengera za galasi siziyenera kubweretsedwa pamalo a msonkhano. Sitiyenera kudya mkati mwa programu. Zimenezi zidzasonyeza kupanda ulemu kulinga ku chakudya chauzimu chimene chikuperekedwa.

27 Ndibwinonso kukumbukira kuti nthaŵi yakupuma kwa masana yaikidwapo kuti tikhale ndi mpata wa kudya chakudya chathu chopepuka ndi kusangalala ndi mayanjano ateokratiki ndi abale ndi alongo athu. Monga anthu a Yehova, timadziŵa kuti chakudya chauzimu pamsonkhano wachigawo ndicho chofunikira koposa poyerekezera ndi zinthu zakuthupi, ndipo tiyenera kukonzekera zinthu ndi lingaliro limenelo.

28 Pa July 28, 1995, woyamba wa Misonkhano Yachigawo ya “Atamandi Achimwemwe” udzayamba. Kodi mwamaliza kukonzekera kwanu, ndipo kodi tsopano muli wokonzekera kusangalala ndi masiku atatu a mayanjano achisangalalo ndi zinthu zabwino zauzimu? Pemphero lathu loona mtima ndi lakuti Yehova adalitse zoyesayesa zanu kuti mudzakhalepo pamsonkhano wachigawo chilimwe chikudzacho pamodzi ndi abale ndi alongo anu pamene tidzakhala tikuphunzira za mmene tingakhalire atamandi achimwemwe a Yehova.

[Bokosi patsamba 6]

Zikumbutso za Msonkhano Wachigawo

Ubatizo: Oyembekezera ubatizo ayenera kukhala ali pamipando pamalo olinganizidwira iwo programu isanayambe pa Loŵeruka mmaŵa. Kwaonedwa kuti ena amavala zovala zosapereka ulemu ndi zocheukitsa pachochitikacho. Aliyense wopita ku ubatizo ayenera kunyamula chovala chomizidwa nacho choyenerera ndi thawulo. Pambuyo pa nkhani yaubatizo ndi pemphero loperekedwa ndi wokamba nkhani, tcheyamani wa gawolo adzapereka malangizo achidule kwa oyembekezera ubatizowo ndiyeno adzaitanitsa nyimbo. Nyimbo itatha, akalinde adzatsogolera oyembekezera ubatizowo kumalo omizira. Popeza kuti ubatizo wochitira chizindikiro kudzipatulira kwa munthu uli nkhani yaikulu ya munthu mwini ndi Yehova, sikuloledwa kuchita otchedwa maubatizo a paubwenzi pamene anthu aŵiri kapena oposerapo amakupatirana kapena kugwirana manja pobatizidwa.

Mabaji: Chonde valani baji la 1995 pamsonkhanopo ndiponso popita ndi pobwerako kumalo amsonkhano. Zimenezi kaŵirikaŵiri zimatikhozetsa kupereka umboni wabwino kwambiri poyenda. Makadi ndi zoikamo zake ayenera kugulidwa ku mpingo wanu, popeza kuti sizidzapezeka pamsonkhano. Kumbukirani kunyamula khadi lanu latsopano la Advance Medical Directive/Release. Ziŵalo za banja la Beteli ndi apainiya ayeneranso kunyamula makadi awo owadziŵikitsa.

Zipinda Zogona: Tikupempha kuti tikhale ogwirizana ndi aliyense amene adzagwiritsira ntchito KOKHA mndandanda wa malo ogona okonzedwa ndi msonkhano. NGATI MULI NDI VUTO, chonde dziŵitsani mwamsanga woyang’anira Dipatimenti ya Zipinda pamsonkhanopo kuti akuthandizeni kusamalira nkhaniyo mwamsanga. Alembi amipingo ayenera kutsimikizira kuti mafomu a Zosoŵa Zapadera za Pempho la Chipinda atumizidwa mwamsanga kumakeyala oyenera a msonkhano wachigawo. Ngati mufuna kufafaniza pempho la chipinda loperekedwa mwa kakonzedwe ka zosoŵa zapadera, muyenera kudziŵitsa mwamsanga Dipatimenti ya Zipinda ya msonkhano kotero kuti chipindacho chipatsidwe kwa wina.

Utumiki Wodzifunira: Kodi mungapatule nthaŵi pamsonkhano ya kuthandiza mu imodzi ya madipatimenti? Kutumikira abale athu, ngakhale kwa maola oŵerengeka okha, kungakhale kothandiza kwambiri ndi kodzetsa chikhutiro chokulira kwambiri. Ngati mukhoza kuthandiza, chonde fikani ku Dipatimenti ya Utumiki Wodzifunira pamsonkhanopo. Ana osafika usinkhu wa zaka 16 nawonso akhoza kuthandiza mwa kugwira ntchito moyang’aniridwa ndi kholo kapena wachikulire wina.

Mawu a Chenjezo: Mwa kukhala maso pa mavuto amene angabuke, tikhoza kupeŵa zovuta. Kaŵirikaŵiri mbala ndi anthu ena oipa amalondola anthu amene ali kumalo osakhala kwawo. Tsimikizirani kuti galimoto yanu ili yokhomedwa nthaŵi zonse, ndipo musasiye kanthu kalikonse koonekera kamene kangakope mbala. Mbala ndi opisa m’matumba amafuna pamene pali anthu ambiri. Sikungakhale kwanzeru kusiya zinthu zamtengo wapatali pamalo anu okhala. Simungatsimikize kuti aliyense amene ali pafupi nanu ndi Mkristu. Nkuperekeranji chiyeso? Talandira malipoti onena za anthu akunja amene ayesa kuba ana. YANG’ANIRANI ANA ANU NTHAŴI ZONSE.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena