Zilengezo
◼ Mabuku ogaŵira mu October: Masabusikripishoni a Nsanja ya Olonda kapena a Galamukani! Kumene tapeza anthu achidwi pa maulendo obwereza, tingagaŵire masabusikripishoni. Kuyambira October 12, tidzagaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 35. November: Tidzapitiriza kugaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 35. Mipingo imene iti itsirize kufola gawo lawo mwa kufikira eni nyumba ndi kope la Uthenga wa Ufumu Na. 35 panyumba iliyonse, ingagaŵire buku la Chidziŵitso pa K12.00. December: New World Translation ndi buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? January: Buku lililonse la masamba 192 lofalitsidwa 1985 isanafike lomwe mpingo uli nalo m’sitoko, pa K12.00. Mipingo yomwe ilibe mabuku amenewo ingagaŵire buku la Chidziŵitso pa K12.00.
◼ Mphatika yomwe ili m’kope lino la Utumiki Wathu Waufumu ndi “Ndandanda ya Sukulu Yautumiki Wateokratiki ya 1998” ndipo muisunge kuti muzidzayang’anamo m’chaka chonse cha 1998.
◼ Pokhala ndi mawikendi asanu athunthu, mwezi wa November ungakhale nthaŵi yabwino yoti ambiri achite upainiya wothandiza.
◼ Mipingo ingayambe kuoda makope a Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku—1998 pa oda yawo ya October yamabuku. Timabukuto tidzakhalapo m’Chicheŵa ndi m’Chingelezi. Timabukuti ndi tofuna oda yapadera ndipo pampambo wolongedzera katundu wa mipingo tidzalembapo kuti “Zoyembekezeredwa”, kenako tidzakutumizirani.
◼ M’kati mwa mlungu wa msonkhano wadera kapena msonkhano wachigawo, palibe Sukulu Yautumiki Wateokratiki kapena Msonkhano Wautumiki umene udzachitika pampingo. Zimenezi zidzapatsa abale nthaŵi yokonzekera, pakuti ambiri amafuna kuyenda ulendo. Msonkhano wokha umene udzakhalapo mkati wa mlungu wa msonkhano wadera kapena msonkhano wachigawo ndi Phunziro la Buku la Mpingo. Mkati mwa mlungu wa tsiku lamsonkhano wapadera, kuwonjezera pa Phunziro la Buku la Mpingo, mungachitinso Sukulu Yautumiki Wateokratiki ndi Msonkhano Wautumiki, ngati mikhalidwe ilola. Mulimonse mmene zingakhalire, akulu ayenera kuona zimene zidzakomera mpingo wawo ndi kulengeza pasadakhale.
◼ Tili okondwa kulengeza kuti, kuyamba ndi kope la January 1998, Sosaite idzayamba kusindikiza Utumiki Wathu Waufumu m’Chitumbuka. Zimenezi zikutanthauza kuti tidzakhala ndi Utumiki Wathu Waufumu m’zinenero ziŵiri za m’Malaŵi. Ngati mpingo wanu ukufuna makope achitumbuka a Utumiki Wathu Waufumu, Komiti Yautumiki idzakambitsirane ndi woyang’anira dera akadzachezera mpingo wanu.
◼ Zofalitsa Zomwe Zilipo:
Bukhu Lolangiza la Sukulu Yateokratiki—Chingelezi
Kukambitsirana za m’Malemba—Chicheŵa
Mapositi Khadi (Cd-10)