Kodi Ndinu Mboni Yanthaŵi Zonse?
1 Kodi mungayankhe funsoli kuti inde? Ngakhale kuti si atumiki onse odzipatulira kwa Yehova amene angachite utumiki wanthaŵi zonse, kodi si koyenera kuti tonsefe tizidziona monga Mboni zake zanthaŵi zonse? Ndithudi tiyenera kudziona motero.
2 Nkosatheka kukhala Mkristu mwa apo ndi apo. Ponena za Atate wake, Yesu anati: “Ndichita Ine zimene zimkondweretsa Iye nthaŵi zonse.” (Yoh. 8:29) Paulo, yemwenso anali ndi maganizo amodzimodziwo, anatilangiza ‘kumachita zonse ku ulemerero wa Mulungu.’ (1 Akor. 10:31) Choncho, mwa njira iliyonse tonsefe tiyenera kumadziona monga Mboni zanthaŵi zonse za Yehova. Maganizo otero nthaŵi zonse adzatisonkhezera pamene tichita chinthu chilichonse.
3 Talingalirani Umboniwu: Kaonekedwe kathu, mawu athu, ndi khalidwe lathu zingasonyeze anthu ena kuti ndithudi ndife Mboni za Yehova. Timakumbukira kufunika kwa kuvala mwaulemu, kulankhula bwino, ndi kudzisungira bwino nthaŵi zonse pamene tili mu utumiki wakumunda kapena pamisonkhano yachikristu. Komabe, kaya tili kusukulu, kaya tili pantchito yolembedwa, kapena tikuseŵera, chilichonse chokhudza ife chiyenera kuchitira umboni kuti timamvera malamulo olungama a Yehova.
4 Yesu anati: “Mudzi wokhazikika pamwamba pa phiri sungathe kubisika . . . Chomwecho muŵalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa Kumwamba.” (Mat. 5:14-16) Tiyenera kusonyeza zimenezo pa chilichonse chimene tikuchita ndiponso nthaŵi zonse. Ngati timaona kuti nthaŵi zina sitimafuna kuchitira umboni chifukwa cha kumene tili kapena chifukwa cha zimene tikuchita, tifunikira kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndikutumikira Yehova mwa apo ndi apo kapena nthaŵi zonse?’ Tisamalole mpata kutidutsa umene tikanalankhula ndi anthu za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.
5 Kumbukirani kuti timalemekeza Yehova ndi kumkondweretsa pamene timayankha funso lakuti, “Kodi ndinu Mboni yanthaŵi zonse?” ndi mawu aakulu kuti “Inde!”