Oyang’anira Amene Amatitsogolera—Woyang’anira Utumiki
1 Woyang’anira utumiki ali ndi chidwi kwambiri ndi chilichonse chokhudza kupita patsogolo kwa ntchito yolalikira m’gawo la mpingo. Motero iye amachita zambiri potithandiza kukwaniritsa ntchito yathu ya kulalikira uthenga wabwino. Monga mlengezi wachangu, amatsogolera pa kukonza zinthu zonse zokhudzana ndi utumiki. Monga mphunzitsi wabwino, amathandiza ofalitsa mmodzi ndi mmodzi kukhala ogwira mtima kwambiri mu utumiki.—Aef. 4:11, 12.
2 Mkulu ameneyu amayang’anira ntchito ya atumiki otumikira amene amasamalira mabuku, magazini, ndi magawo. Amatsimikizira kuti pali mabuku, magazini, ndi mafomu autumiki okwanira mwezi uliwonse kuti ife tizigwiritsa ntchito. Kamodzi pachaka amapenda fayelo ya gawo ya nyumba zonse zimene tinalangizidwa kuti tisakachezeko, ndipo amatumizako abale oyeneretsedwa.
3 Woyang’anira utumiki amayang’anira njira zosiyanasiyana zolalikirira, kuphatikizapo kuchitira umboni m’gawo la zamalonda, ndi mumsewu. Amakhala tcheru kupanga makonzedwe othandiza akusonkhana kaamba ka utumiki mlungu wonse, ndi pamaholide omwe. Amasonyezadi chidwi m’ntchito ya maphunziro a Baibulo. Amafunafuna njira zothandizira mwauzimu awo amene amakhala odumphadumpha kapena ofooka mu utumiki. Nthaŵi zonse amasamala za ntchito ya apainiya, ndipo amayang’anira programu ya Apainiya Athandiza Ena.
4 Monga mmodzi wa mu Komiti Yautumiki Yampingo, woyang’anira utumiki amapereka malingaliro ngati pakufunika kusintha kulikonse m’magulu a Phunziro la Buku la Mpingo. Pamene akuchezera gulu lanu, onetsetsani kuti mwapezekapo ndipo mwatsagana naye mu utumiki wakumunda.
5 Onse mumpingo ayenera kugwirizana mofunitsitsa ndi chitsogozo chimene woyang’anira utumiki amapereka. Zimenezi zidzatithandiza kukhala ogwira mtima kwambiri m’ntchito yopanga ophunzira ndi kupeza chimwemwe chachikulu mu utumiki wathu.