Tsanzirani Kupanda Tsankho kwa Yehova
1 Yehova amadera nkhawa anthu. Mosasankha amalandira aliyense wochita chifuniro chake. (Mac. 10:34, 35) Pamene Yesu anali kulalikira kwa anthu, iyenso anali wopanda tsankho. (Luka 20:21) Tiyenera kutsanzira chitsanzo chawo, monga anachitira Paulo yemwe analemba kuti: “Yemweyo ali Ambuye wa onse, nawachitira zolemera onse amene aitana pa iye.”—Aroma 10:12.
2 Kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kwa onse amene timakumana nawo kumadzetsa ulemerero kwa Mulungu. Tiyenera kupitiriza kuuza ena uthenga wabwino kwambiriwu, mosasamala kanthu za mtundu wawo, udindo umene ali nawo, maphunziro awo, chuma chawo. (Aroma 10:11-13) Izi zikutanthauza kulalikira amene angamvetsere. Amuna, akazi, ana ndi okalamba. Tiyenera kupita khomo lililonse kuti tipereke mwayi kwa mwininyumba aliyense woti amve choonadi.
3 Khalani wa Chidwi ndi Aliyense: Cholinga chathu ndicho kufikira onse amene tingathe. Pachifukwa chimenechi, ofalitsa ena achitira umboni wachipambano kwa anthu a m’maofesi a madokotala, m’zipatala, malo osungirako ana ndi anthu osowa thandizo, maofesi oona za chikhalidwe cha anthu. Kuphatikiza apo, ofalitsa achitira umboni kwa anthu oyendetsa za maliro, oyang’anira masukulu, aphungu, komanso oweruza. Polankhula ndi akuluakulu a boma, ndibwino kuwayamikira pantchito zawo zothandiza zimene akuchita m’deralo. Khalani waulemu, ndipo sankhani nkhani za panthaŵi yake zimene makamaka zimasimba zantchito yawo ndi mavuto okhudzana ndi ntchitoyo.
4 Nthaŵi ina mlongo anapeza mpata wolankhula ndi woweruza m’ofesi yake. Atatha kukambirana bwinobwino, woweruzayo ananena mawu awa: “Kodi mumadziŵa chimene chimandisangalatsa ndi Mboni za Yehova? Ali ndi mfundo zabwino zimene amazitsatira mosaphonya.” Munthu wolimbikitsa ameneyu anachitiridwa umboni wogwira mtima.
5 Sitingadziŵe za m’mitima ya anthu. Komabe, mwa kulankhula ndi aliyense amene timakumana naye, timasonyeza chikhulupiriro chathu m’mphamvu ya Mulungu kuti amatsogoza ntchito yathu. Komanso, izi zimawapatsa mwayi womva ndi kulabadira uthenga wopatsa chiyembekezo. (1 Tim. 2:3, 4) Tiyeni tigwiritse ntchito nthaŵi yathu mwanzeru ndipo tiyesetse kutsanzira kupanda tsankho kwa Yehova mwa kuuza anthu onse amene tingathe uthenga wabwino.—Aroma 2:11; Aef. 5:1, 2.