Kuthandiza Ana Athu Kukhalabe M’choonadi: Mbali Yachinayi—Mwa Kugonjetsa Zolepheretsa
1 Chofunika kwambiri pothandiza ana athu kukhalabe m’choonadi ndi phunziro la Baibulo la banja lokhazikika ndiponso latanthauzo. Mmene mungachitire phunziro limeneli kukhala logwira mtima pokhomereza choonadi m’mitima ya ana anu zinafotokozedwa m’Mbali Yachitatu ya nkhani ino. Koma mabanja ambiri sachita maphunziro okhazikika ndi ogwira mtima. Tiyeni tipende zina mwa zolepheretsazo ndi mmene tingazigonjetsere.
2 Zolepheretsa Phunziro la Banja Lokhazikika: Chimodzi mwa zolepheretsa phunziro ndi kusoŵa nthaŵi. Chifukwa cha kukwera mtengo kwa zakudya, zovala ndi zofunika zina, abambo ngakhalenso amayi angamagwire ntchito zolimba kuti apeze ndalama zokwanira kusamalira banja. Ntchito yakuthupi, malonda, ndi kukwera mtengo kwa zinthu zingasokoneze kwambiri phunziro la banja, chifukwa pamene tsiku litha makolo angakhale otopa m’thupi ndi m’maganizo. Kodi angathetse bwanji vutoli? Kwenikweni, ndi chikhulupiriro—kukhulupirira kuti Mulungu adzakwaniritsa mawu a Yesu a pa Mateyu 6:33 akuti: “Koma muthange mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzawonjezedwa kwa inu.” Ndithudi Mulungu adzakudalitsani ngati muchepetsa ntchito zakuthupi zimenezo n’kuika zinthu zauzimu patsogolo. Yehova adzakwaniritsa chilichonse chimene mukusoŵa. Pankhani yotopa, kumbukirani kuti nthaŵi zonse kukambirana zauzimu kumatitsitsimula maganizo ndi thupi. Monga mmene mumachitira mukapita ku misonkhano ngakhale muli wotopa n’kubwerako muli wotsitsimulidwa, choteronso mudzatsitsimulidwa mukatha phunziro lanu la banja. Musalephere kuchita phunziro!
3 Cholepheretsa china chingakhale chifukwa chakuti makolo ndi osaphunzira. Nthaŵi zina ana angaŵerenge bwino kuposa makolo awo. Musalole zimenezi kulepheretsa phunziro. Ngakhale abale osadziŵa kuŵerenga athandiza anthu ophunzira kuloŵa choonadi. Pa phunziro la Baibulo la banja, ngati makolo saŵerenga bwino, ana akhoza kumaŵerenga ndime. Ngakhale ngati ana angaŵerenge bwino, sizitanthauza kuti amamvetsetsa choonadi. Chifukwa chakuti makolo ndi anzeru komanso amadziŵa zambiri, ndiwo amene angauze ana awo zinthu zofunika kwambiri. Choncho, musalole kusaphunzira kwanu kukulepheretsani kuchititsa phunziro la banja nthaŵi zonse.
4 Mavuto Ofunika Kukambirana pa Phunziro la Banja: Ana ena umunthu wawo uli ndi zolakwa zazikulu zofunika kuzithetsa asanayambe kuloŵa mu utumiki. Mwina amakonda kunama, kuba, kuvala mosadzilemekeza ndi mosasamala, ndi amwano, kapena sayamikira zinthu zauzimu. Akulu amafuna kuona ana atasintha mikhalidwe imeneyi asanawavomereze kukhala ofalitsa osabatizidwa. M’malo mowalekerera, makolo afunika kuchita khama kuthandiza ana awo kuthetsa zolakwa zimenezi. Gwiritsani ntchito zofalitsa monga Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo, Achichepere Akufunsa, ndi nkhani za m’magazini zimene kwenikweni zimafotokoza mavuto amene ana angakhale nawo. Musalekerere ana anu. Kumbukirani kuleza mtima kumene kumafunika pothandiza ophunzira Baibulo kusintha umunthu wawo. Kodi simungasonyeze khama ndi kuleza mtima kofananako pa ana anu? Mwa kugwiritsa ntchito luso lanu monga mphunzitsi mudzapambana potsogolera ana anu kutumikira Yehova.
5 Kukonza Lingaliro Lolakwika: Mwina chimene chimapangitsanso kunyalanyaza maphunziro a banja ndi lingaliro lofala m’dziko lakuti ana amabadwa kaamba ka makolo awo. Ana ambiri amabadwa m’dziko kuti adzasamalire makolo awo akadzakalamba. Ena angamadzitonthoze mwa kuganiza kuti ngakhale ngati ana awo sakhala m’choonadi, makolowo adzapindulabe mwakuthupi m’tsogolo. Ndi bwino kuti ana athandize makolo awo okalamba, koma onani mfundo yachikhalidwe ya pa 2 Akorinto 12:14: “Ana sayenera kuunjikira atate ndi amayi, koma atate ndi amayi kuunjikira ana.” Ndithudi, makolo alipo kaamba ka ana awo, osati ana kaamba ka makolo awo. Kuchotsa dyera ndi malingaliro akudziko amene makolo angakhale nawo kungawathandize kudzimana, inde, kuyesetsa kwambiri m’malo mwa ana awo. Izi zimaoneka ndi khama lawo pochititsabe phunziro la Baibulo la banja nthaŵi zonse.
6 Kukonda ana athu ndiponso kuwafunira zabwino kudzatisonkhezera kuwongolera. Zimakhala zomvetsa chisoni kuona ana okulira m’choonadi akupitanso kudziko. Ngati akhalabe konko, adzawonongeka pa Armagedo. Zidzakhalatu zosangalatsa kwambiri ngati ife ndi ana athu onse tidzapulumuka Armagedo n’kupezeka pa khamu lalikulu lopyola Armagedo lotchulidwa pa Chivumbulutso chaputala 7.
7 M’nkhani yomaliza ya nkhani ino, Mbali Yachisanu, tidzapenda zimene ena angachite, monga akulu komanso abale ndi alongo okhwima pothandiza makolo makamaka a mabanja aakulu.