Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda Oct. 15
“Anthu ambiri amaona kuti m’tsogolo ndi mosapanganika moti ndi bwino kusadera nkhawa za mawa. Kodi maganizo anu ndi otani pankhani imeneyi? [Yembekezani ayankhe.] Yesu ananenapo mawu ochititsa chidwi awa. [Werengani Mateyo 6:34.] Magazini iyi ikufotokoza momwe tingakonzere bwino tsogolo lathu komanso momwe tingapewere kudera nkhawa kwambiri za tsogololo.”
Galamukani! Oct.
“Mwachionekere ife tonse tinali ndi wachibale kapena mnzathu winawake amene anamwalira. Kodi mukuganiza kuti ali kumwamba moti akutiona? [Yembekezani ayankhe.] Onani zimene Yesu ananena Lazaro atamwalira. [Werengani Yohane 11:11.] Nkhani iyi ikufotokoza ngati akufa ali ndi moyo kwinakwake kapena ngati ali mtulo kudikira kuti adzaukitsidwe.” Asonyezeni nkhani imene yayambira pa tsamba 28.
Nsanja ya Olonda Nov. 1
“Kodi mukuganiza kuti dzikoli lingakhale bwinopo ngati anthu atakhala odzichepetsa kwambiri? [Yembekezani ayankhe.] Onani zimene Yesu ananena za khalidwe limeneli. [Werengani Mateyo 23:12.] Nkhani iyi ikufotokoza kufunika kokhala wodzichepetsa m’dziko lino limene anthu amakonda kupikisana.”
Galamukani! Nov.
“Kale, anthu ankadalira Baibulo kuti liwatsogolere. Koma masiku ano ambiri amalikayikira. Kodi mukuona bwanji? [Yembekezani ayankhe. Ndiye werengani 2 Timoteyo 3:16.] Galamukani! yapadera iyi ikusonyeza umboni wamphamvu wakuti Baibulo ndi louziridwa ndi Mulungu.”