MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kuwonjezera Luso Lathu Mu Utumiki—Kulalikira Tili pa Kamera Kapena Pogwiritsa Ntchito Intakomu
KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Zipangizo zamakono komanso kuwonjezeka kwa uchigawenga zapangitsa kuti anthu ambiri azikhala ndi makamera komanso maintakomu pakhomo pawo pofuna kudzitetezera. Mwina tingamaope kulalikira munthu amene sitingamuone koma yemwe akutiona. Mfundo zotsatirazi zingatithandize kulalikira molimba mtima tikakhala pa kamera kapena tikamagwiritsa ntchito intakomu.
KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?
Tizikhala ndi maganizo abwino. Anthu ambiri amene ali ndi kamera kapena intakomu amafuna kulankhula nafe
Tizikumbukira kuti makamera ena amayamba kujambula tisanagogode kapena kuimba belu ndipo mwina mwininyumba angakhale akutiona kapena kutimvetsera tikangofika pakhomo lake
Munthuyo akatilankhula, tizilankhula pa intakomu kapena poyang’ana kamera ngati kuti tikulankhula ndi munthuyo pamasom’pamaso. Tizimwetulira komanso kugwiritsa ntchito manja polankhula ngati mmene timachitira nthawi zonse. Tizinena zimene tikananena zikanakhala kuti tikulankhula ndi munthuyo pamasom’pamaso. Ngati pali kamera, tisaiyandikire kwambiri. Ngati munthuyo sanayankhe, tisasiye uthenga uliwonse
Tisaiwale kuti tikamaliza kulankhula ndi munthuyo, iye amakhala kuti akutionabe kapena kutimvetsera