Lemba la Chaka cha 2013
“Ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu. . . . Yehova Mulungu wako ali nawe.”—Yoswa 1:9
Mu 1473 B.C.E., Aisiraeli anali okonzeka kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, koma kutsogolo kwawo kunali adani amphamvu. Choncho Mulungu analimbikitsa Yoswa kuti: “Ukhale wolimba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu.” Yoswa anafunika kumvera malamulo a Mulungu kuti zinthu zimuyendere bwino. Iye anauzidwa kuti: “Usachite mantha kapena kuopa, pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.” Zinali zoonekeratu kuti Mulungu analidi ndi Yoswa chifukwa m’zaka 6 zokha, Aisiraeli anagonjetsa adani awo onse.—Yos. 1:7-9.
Akhristu oona atsala pang’ono kulowa m’dziko latsopano lolonjezedwa, choncho akufunika kukhala olimba mtima ndiponso kuchita zinthu mwamphamvu. Mofanana ndi Yoswa, tikulimbana ndi adani amphamvu amene akufuna kutilepheretsa kutumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika. Pomenya nkhondo yathu sitikugwiritsa ntchito mikondo ndi malupanga, koma tikugwiritsa ntchito zida zauzimu, ndipo Yehova akutiphunzitsa mmene tingagwiritsire ntchito zida zimenezi mwaluso. Choncho kaya mukukumana ndi mavuto otani, dziwani kuti Yehova adzakuthandizani ndipo mudzapambana ngati muli ndi chikhulupiriro, mukakhala olimba mtima komanso mukamachita zinthu mwamphamvu.