INDONESIA
Sitinalole Kusiya Zimene Timakhulupirira
Daniel Lokollo
CHAKA CHOBADWA 1965
CHAKA CHOBATIZIDWA 1986
MBIRI YAKE Mpainiya wapadera amene anakhalabe wokhulupirika pa nthawi imene ankazunzidwa.
PA 14 April, 1989, akuluakulu a boma anandimanga pamodzi ndi anthu ena atatu. Pa nthawiyi ndinkachititsa msonkhano wa mpingo m’tauni ya Maumere pachilumba cha Flores.
Oyang’anira ndende ya m’derali anatikakamiza kuti tizichitira sailuti mbendera. Titakana, anatimenya n’kutikhazika panja kwa masiku 5, dzuwa likutentha kwambiri. Ndipo usiku, tinkazizidwa kwambiri chifukwa tinkagona pasimenti mundende zomwe zinali zazing’ono kwambiri komanso zauve. Nthawi zonse tinkakhala otopa komanso tinkamva kupweteka kwambiri chifukwa cha mabala. Woyang’anira ndendeyi ankatikakamiza kuti tingosiya zimene timakhulupirira koma tinamuuza kuti: “Tilolera kufa koma singachitire sailuti mbendera.” Ifenso tinaona kuti ndi mwayi wathu ‘kuvutika chifukwa cha chilungamo’ mofanana ndi Akhristu akale.—1 Pet. 3:14.