Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
Okondedwa Abale ndi Alongo:
M’zaka za m’ma 600 B.C.E., mneneri Ezekieli anaona masomphenya odabwitsa zedi. Iye anaona galeta lakumwamba lomwe linkayendetsedwa ndi Wolamulira wa chilengedwe chonse. Chinthu chimene chinali chodabwitsa kwambiri chinali mmene galetali linkayendera. Linkathamanga paliwiro loopsa ngati mphenzi ndipo linkachita zimenezi ngakhale likamakhota.—Ezek. 1:4, 9, 12, 14, 16-27.
Masomphenyawa akutikumbutsa kuti mbali yakumwamba ya gulu la Yehova ikuyenda mofulumira kwambiri. Koma nanga bwanji mbali ya padziko lapansi? Zimene takwanitsa kuchita chaka chapitachi zikusonyeza kuti Yehova akutsogoleranso anthu ake padziko lapansi, mofanana ndi mmene akuchitira ndi mbali yakumwamba.
Mwachitsanzo, ku United States abale a pa Beteli akhala akusamuka ku Brooklyn kupita kulikulu lathu latsopano, lomwe lili m’tauni ya Warwick ku New York, komanso kumalo ena komwe kuli maofesi athu. Abale ndi alongo ena anapemphedwa kuchoka pa Beteli kuti azikagwira ntchito yolalikira. Abale ndi alongo omwe amatumikira m’maofesi ena a nthambi padziko lonse, nawonso ndi otanganidwa kwambiri. Mwachitsanzo, chifukwa cha kusintha kwa zinthu, abale akumanganso maofesi ena, kuwakonza kapena kusamukira kwina chifukwa choti ofesi yawo ya nthambi yaphatikizidwa ndi ina. Nanga bwanji inuyo? Ngakhale kuti simunasamuke kumene mukukhala n’kutheka kuti pali zinthu zina zimene mwasintha.
Bungwe Lolamulira likuyamikira kwambiri kuona atumiki a Mulungu padziko lonse akugwira ntchito mwakhama kuti aziyendera limodzi ndi gulu la Yehova. Ena asamukira m’madera omwe kukufunika olalikira ambiri. Ena anayamba utumiki watsopano monga kulalikira kudera lomwe anthu ake amayankhula chinenero china. Komanso abale ndi alongo ambiri akhala akulalikira pogwiritsa ntchito njira zatsopano. Palinso ena omwe awonjezera utumiki wawo m’njira zina. Komanso abale ndi alongo onse okhulupirika, kuphatikizapo achikulire komanso amene amadwaladwala, akupitirizabe kuthamanga nawo mpikisano wokapeza moyo wosatha. Iwo akuyesetsa kutumikira Yehova komanso kuthandiza anthu ena kuti adziwe zoti Satana ndi wabodza.—1 Akor. 9:24
Dziwani kuti Yehova amaona zonse zimene mukuchita pomutumikira. (Aheb. 6:10) Kudzipereka kwanu kumatikumbutsa za Abulahamu ndi Sara. Abulahamu ali ndi zaka zoposa 70 anasamuka kwawo ku Uri, mzinda womwe unali wolemera n’kupita ku Kanani. Iye ndi banja lake ankakhala m’mahema ndipo anakhala kumeneku kwa zaka 100 mpaka pamene anamwalira. Pamenepatu Abulahamu ndi Sara anasonyeza kuti anali odzipereka kwambiri.—Gen. 11:31; Mac. 7:2, 3.
Tikukuthokozani chifukwa choyesetsa kutengera chitsanzo cha Abulahamu ndi Sara. Tikudziwa kuti ambirinu mukutsatira lamulo la Yesu ngakhale kuti mukukumana ndi mavuto. Iye anati: “Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga. Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera.”—Mat. 28:19.
Mawu akuti “pitani” omwe Yesu anagwiritsa ntchito akusonyeza kuti sitiyenera kungokhala n’kumadikira kuti anthu abwere. N’zochititsa chidwi kuona zimene otsatira a Khristu akwanitsa kuchita chaka chapitachi. Zikuchita kuonekeratu kuti Yehova akudalitsa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu ku mitundu yonse.—Maliko 13:10.
Anthu ambiri akumvetsera uthenga wathu. Chiwerengero cha ofalitsa cha chaka chathachi chinali 8,340,847, ndipo pa avereji tinkachititsa maphunziro a Baibulo 10,115,264 pa mwezi. Uwu ndi umboni wakuti galeta lakumwamba likuthamanga ndipo tikuyesetsa kuyenda nalo limodzi. Pitirizani kuchita khama pa nthawi imene yatsalayi chifukwa posachedwapa Yehova anena kuti ntchito yolalikira yatha.
Mpake kuti lemba la chaka cha 2017 likunena kuti: “Khulupirira Yehova ndipo chita zabwino.” (Sal. 37:3) Mukamayesetsa kutsatira mawu amenewa potumikira Yehova, mumasonyeza kuti mumamukhulupirira. Komanso muzikumbukira kuti simuli nokha. Paja Yesu anati: “Dziwani kuti ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.”—Mat. 28:20.
LEMBA LA CHAKA CHA 2017:
“Khulupirira Yehova ndipo chita zabwino”
Yehova apitirizabe kukudalitsani pamene mukumutumikira. Kaya mukuchita zambiri kapena ayi, dziwani kuti Yehova amasangalala ngati mukuchita zonse zimene mungathe komanso ndi zolinga zabwino. (2 Akor. 9:6, 7) Choncho, pitirizani kuyandikira Atate wanu wakumwamba popemphera kwa iye nthawi zonse, kuphunzira Mawu ake, kupezeka pamisonkhano komanso kulalikira mwakhama.
Satana akudziwa kuti wangotsala ndi “kanthawi kochepa” ndipo akuchita zonse zomwe angathe kuti atilepheretse kukhalabe okhulupirika kwa Yehova. (Chiv. 12:12) Koma mukamadalira kwambiri Yehova mungathe kulimbana naye. (Sal. 16:8) Dziwani kuti timakukondani kwambiri ndipo timayamikira zonse zimene mukuchita m’masiku otsiriza ano pothandiza pa zinthu zokhudza Ufumu.
Ndife abale anu,
Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova