N’chifukwa Chiyani Malo a Mboni za Yehova Opempherera Amawatchedwa Kuti “Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova”?
Dzinali ndi loyenera chifukwa:
Nyumbayo imakhala malo osonkhanira.
Timasonkhana kuti tilambire Yehova, yemwe ndi Mulungu wotchulidwa m’Baibulo, komanso kuti tichitire umboni za iye.—Salimo 83:18; Yesaya 43:12.
Timasonkhananso kuti tiphunzire za Ufumu wa Mulungu, umene Yesu ankakonda kuutchula.—Mateyu 6:9, 10; 24:14; Luka 4:43.
Ngati mungakonde mukhoza kudzasonkhana nawo mu Nyumba ya Ufumu imene muli nayo pafupi kuti mudzaone mmene a Mboni za Yehova amachitira misonkhano yawo.