Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingakupange Motani Kupita Patsogolo Kwauzimu?
“Pamene ndinapita kutchalitchi, ndinasokonezekadi. Sindinamvetsetse zimene ankayesera kunena, chotero ndinaleka kupitako. Sindiganiza kuti munthu afunikira kukhala wa chipembedzo chakutichakuti kuti akhale ndi chikhulupiriro mwa Mulungu.”—Carrie wa zaka khumi mphambu zisanu ndi ziŵiri zakubadwa.
KODI nchifukwa ninji tchalitchi chikukhumudwitsa achichepere ambiri? M’kufufuza kochitidwa ndi katswiri wa kufufuza George Gallup, achichepere anapereka zifukwa zotsatirazi: ‘Maulalikiwo amagwetsa ulesi.’ ‘Iwo samaphunzitsa za Mulungu kapena Baibulo.’ ‘Iwo nthaŵi zonse amapempha ndalama.’ ‘Matchalitchi ndi opita ku tchalitchi samatsatira zimene amanena.’ Mwachiwonekere, matchalitchi alephera kudyetsa achichepere mwauzimu.
Koma kodi mukufuna ‘kugwira moyo wosatha’? (1 Timoteo 6:12) Kodi mukufuna kulemekezedwa monga Mkristu wachikulire, amene angaikizidwe ndi mathayo? Kodi mumaufuna mwaŵi wa kukhala mmodzi wa ‘antchito anzake a Mulungu’ m’kuthandiza ena kupeza moyo wosatha? (1 Akorinto 3:9) Pamenepo muyenera kupita patsogolo mwauzimu! Mwa kugwirizana ndi Mboni za Yehova, inu mudzasangalala ndi mwaŵi umene achichepere m’Chikristu Chadziko alibe. Pezekani pa misonkhano ku Nyumba Yaufumu, kumene malangizo amphamvu a Baibulo amaperekedwa. Landirani chisamaliro chaumwini kuchokera kwa makolo anu kupyolera m’phunziro Labaibulo labanja. Yanjanani mokhazikika ndi anthu amene amayesera mowona mtima kugwiritsira ntchito Baibulo m’miyoyo yawo. Komabe, kuti mupange kupita patsogolo kwauzimu, zambiri zimafunikira. Monga mmene mtumwi Petro anafotokozera, inu muyenera kuikako ‘changu chonse.’ (2 Petro 1:5) Tiyeni tiwone chimene kuchita ichi kumaphatikiza.
Pangani Chilakolako Chauzimu
Yesu anati: “Achimwemwe ali awo ozindikira kusowa kwawo kwauzimu.” (Mateyu 5:3, NW) M’chigiriki choyambirira, mawu awa anatanthauzadi “anthu amene ali opemphapempha mzimu.” Mofanana ndi wopemphapempha wosoweratu kanthu amene akudera nkhaŵa kwabasi kusowa kwake chakudya chakuthupi, inu muyenera kuzindikira kusowa kwanu chakudya chauzimu. Yesu anati: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu.”—Yohane 17:3.
Achichepere ambiri samachita chirichonse chokwaniritsa zosowa zawo zauzimu. Bukhu lakuti The Psychology of Adolescence likunena motere za wachichepere wachikatikati: “Chidziŵitso chake cha chipembedzo chake mwinamwake nchaching’ono, ngakhale kuti nkhaŵa yake ndi chikondwerero m’chipembedzo njaikulu.” M’kufufuza kwina gulu la achichepere anafunsidwa mafunso zana limodzi a m’Baibulo. Wachichepere wachikatikati anayankha 17 okha. M’kufufuza kwina, achichepere asanu ndi aŵiri mwa khumi analephera kutchula Mauthenga Abwino anayi.
Bwanji ponena za inu? Kodi mwadzipereka nokha kuutali wotani kuphunzira Baibulo mosamalitsa? Kodi mungatsutse ziphunzitso zonyenga, monga ngati Utatu ndi kusafa kwa moyo? Kodi mungatsimikizire Mwamalemba kuti pali chiyembekezo cha moyo wosatha wa ponse paŵiri kumwamba ndi padziko lapansi? Kodi mungafotokoze kuti takhala tikukhala ‘m’masiku otsiriza’ chiyambire 1914? (2 Timoteo 3:1-5) Kapena kodi mufunikira munthu wina ‘kukuphunzitsani inu zoyamba za chiyambidwe cha maneno a Mulungu’?—Ahebri 5:12.
Ngati izi ziri tero kwa inu, ndiko kuti mufunikira “kulakalaka mkaka weniweni wa mawu, kuti mukakule nawo ndi kupulumuka.” (1 Petro 2:2, NW) Pangafunikire kuyesayesa kwamphamvu poyamba. Koma mutadzipereka nokha kwambiri kuphunzira Mawu a Mulungu, chilakolako chanu cha zinthu zauzimu chidzakulanso kwambiri.
Zikaikiro Zokhalirira
Kevin wa zaka 19 zakubadwa akuti: “Sindidziŵadi pomwe ndikuima pankhani zachipembedzo tsopano. Ndiri wosokonezekadi nacho.” Achichepere ambiri m’Chikristu Chadziko amaganizira mmenemu. Koma kodi chingakhale chifukwa chakuti kupita kwanu patsogolo kwauzimu kwatsekerezedwa mofananamo ndi zikaikiro zokhalirira?
Mwachitsanzo, kodi ndinu wokhutiritsidwiratu kuti kukhala ndi moyo momvana ndi makhalidwe abwino Abaibulo ndiko njira yabwino yokhalira ndi moyo? Kapena kodi mumadzipeza kukhala ‘wochitira nsanje oipa’? (Salmo 73:3) Kodi ndinu wokhutiritsidwa mumtima mwanu kuti tikukhala ndi moyo m’masiku otsiriza? Kapena kodi mukukonzekera ntchito modetsedwa nkhaŵa m’dongosolo lino la zinthu? Kodi ndinu wotsimikiza kuti Baibulo ndilo Mawu ouziridwa a Mulungu? Kapena kodi nthaŵi zina mumadabwa pamene nthanthi za sayansi sizikulivomereza? Ngati zikaikiro zimakuvutitsani, kumbukirani chimene Baibulo limanena pa Yakobo 1:6: ‘Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakaika konse; pakuti wokaikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.’ Zikaikiro za chikhulupiriro cha munthu zingayerekezedwenso ndi kuchucha kwa chingalawa. Zibowo zitakhala zazikulu, pamakhala kuthekera kwenikweni kwa kumira kwa chingalawacho.
Kodi ngati nthaŵi zina mumakhala ndi mafunso osayankhidwa kumatanthauza kuti chikhulupiriro chanu chiri pafupifupi “kumira”? Osati kwenikweni. Koma ngati muli ndi zikaikiro zokhalirira, inu mufunikira kugwira ntchito mwamphamvu kuzithetsa. Mwachitsanzo, ngati inu munali ndi zikaikiro zogula chovala chatsopano, kodi inu simukachisanthula mosamalitsa chovalacho, kuwona kasokedwe kake, nsalu zake, ndi mtengo musanapange chosankha? Mofananamo, zikaikiro zina zenizeni zingathetsedwe mwakusanthula Baibulo mosamalitsa kapena mwa kukambirana nkhanizo ndi Mkristu wachikulire, wokhala ndi chidziŵitso.a Miyambo 15:14 ikuti: “Mtima wa wozindikira ufunitsa kudziwa.”
Kuika Zonulirapo Zauzimu
Mtumwi Paulo anauza mwamuna wachichepere Timoteo kuti: “Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse.” Komabe, onani kuti Paulo sanalemetse Timoteo ndi chonulirapo chosatsimikizirika chapamwamba, chosafikirika. Iye anampatsa Timoteo zonulirapo zakutizakuti izi, zotsimikizirika zofunikira kugwirirapo ntchito: ‘Khala chitsanzo kwa iwo okhulupira, m’mawu, m’mayendedwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, m’kuyera mtima.’—1 Timoteo 4:12-15.
Mofanana ndi Timoteo, inu mufunikira kuika zonulirapo zauzimu zimene ziri zenizeni, zofikirika. Mwachitsanzo, talingalirani ngati munafuna kuphunzira kuphika. Kukakhala kupusa chotani nanga kuyesera kukhala katswiri wophika patsiku limodzi! Komabe, inuyo mungathe kuzolowera maluso a kaphikidwe limodzi ndi limodzi—mwinamwake poyamba mudzaphunzira mophikira ndiwo zamasamba ndikumakwerabe kufikira kuphika nyama, mikate, kugwiritsira ziwiya zophika zokha, kapena kupanga zozuna. Mofananamo, inu mungafikire bwino lomwe chonulirapo chanu cha kukula kwauzimu kwanyengo yaitali ngati inuyo muchifikira kupyolera m’zonulirapo zotsogolera ku icho kapena sitepe ndi sitepe. Izi zingatumikire monga zizindikiro za kupita kwanu patsogolo kwauzimu. Nthaŵi iriyonse mutamaliza sitepe limodzi mwachipambano, inu mudzakhala mutamanga kudzidalira kwanu. Ichi chingakusonkhezereni kugwirira pa sitepe lotsatira.
Kufikira Zonulirapo Zanu
Tsopano tiyeni tiwone zonulirapo zimene inuyo mungakhazikitse. Mwachitsanzo, kodi mwamaliza kuliŵerenga Baibulo lonse? Inde, Baibulo ndi bukhu lalikuludi, koma bwanji osaligawa m’zigawo zochepa m’kuliŵerenga kwake? (Anthu ambiri mu United States amadya zakudya makilogramu 640 chaka chirichonse. Koma kodi ndani amene angayesere kuzidya zonsezi panthaŵi imodzi?) “Mfulu” za ku Bereya ‘zinasanthula malemba masiku onse.’ (Machitidwe 17:11) Ngati inu mutsatira ndandanda ya tsiku ndi tsiku ya kuŵerenga mphindi 15 zokha patsiku—pafupifupi nthaŵi imene ingawonongedwe pomvetsera ku nyimbo zotchuka zisanu pa wailesi—inu mungamalize kuŵerenga Baibulo m’chaka chimodzi.
Inu mungakhazikitse chonulirapo cha kuŵerenga kope lirilonse la magazine a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Chidziŵitso chabwino kwambiri chopezeka mu awa chidzafulumiza kupita kwanu patsogolo mwauzimu. Inu mungachipangenso kukhala chonulirapo chanu kuimira mpingo wa Mboni za Yehova monga wofalitsa wosabatizidwa, ngati musanakhale kale. Ichi chingaphatikizepo kukhalamo ndi phande mokhazikika m’ntchito ya kulalikira kwa kukhomo ndi khomo ndi kuchitira lipoti ntchitoyo mwezi uliwonse. Mungakambirane mmene mungayenerere mwaŵi umenewu ndi makolo anu kapena akulu apampingo wa kumaloko.
Kodi palinso zonulirapo zauzimu zina? Kukhala wochenjera ndi wachikulire m’kuganiza kwanu. (Ahebri 5:14) Kupititsa patsogolo chipatso chirichonse chauzimu. (Agalatiya 5:22, 23) Kuwongolera ubwino wa mapemphero anu. (Afilipi 4:6) Kusonyeza ulemu wowonjezereka ku umutu wa makolo anu. (Aefeso 6:1) Kukhala wozoloŵerana kwenikweni ndi kuchinjiriza chikhulupiriro chanu. (1 Petro 3:15) Zonulirapozi nzopindulitsa ndipo nzofikirika!
Komabe, kumbukirani kuti, kungokhazikitsa zonulirapo nkosakwanira. Inu mufunikira kumamatirako! Monga mmene yemwe kale anali nduna yaikulu ya boma la Briteni, Benjamin Disraeli ananenera kuti: “Chinsinsi cha chipambano ndicho kukhala wokhazikika nacho chifuno.” Inde, chipangeni chilakolako chauzimu. Khazikitsani zonulirapo zanzeru zauzimu. Sonyezani kukhazikika kwa izi mwa kumamatira ku izo. Kupita patsogolo kwauzimu nkotsimikizirika kutulukapo.b
[Mawu a M’munsi]
a Mabuku awa The Bible—God’s Word or Man’s? ndi Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? (ofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.) angakuthandizeni kuthetsa mafunso anu amene mungakhale nawo ponena za kuwuziridwa kwa Baibulo.
b Nkhani zamtsogolo zidzafotokoza mbali zina zankhaniyi.
[Chithunzi patsamba 18]
Kundandalitsa mphindi zoŵerengeka kuŵerenga Baibulo tsiku lirilonse ndiyo njira ina ya kusonkhezera kupita kwanu patsogolo kwauzimu