Dziko Latsopano Lopanda Mavuto
‘Ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga.’—Yesaya 65:17, 18.
MAWU aulosi amenewo anauziridwa ndi Mulungu zaka zoposa 2,700 zapitazo. Iwo amafotokoza mwapang’ono, mmene moyo udzakhalira padziko lapansi kutsogoloku. Liti? Pamene Mulungu adzabweretsa kumapeto dongosolo lamakonoli lazinthu. Maulosi ambiri a Baibulo amachimveketsa kuti chifuniro cha Mulungu nchakuchotsa dongosolo lamakonoli la zinthu mwamsanga ndi kulilowa mmalo ndi dziko latsopano lopanda kuvutika kulikonse.
Ha moyo udzakhala wosiyana chotani nanga m’dziko latsopano limenelo utayerekezedwa ndi moyo kupyola m’mbiri yakale ya munthu! Mawu aulosi a Mulungu amatiuza kuti ilo lidzakhala lopanda nkhondo, upandu, umphaŵi, ndi chisalungamo. Matenda ndi imfa zidzakhala zitapita. Sipadzakhalanso maboma, zipembedzo, kapena madongosolo a zachuma odzetsa malekano omwe atsimikizira kukhala operewera chotero. Misozi yotuluka chifukwa cha chisangalalo idzalowa m’malo misozi yachisoni popeza kuti kuipa ndi kuvutika zidzakhala zitapitiratu.
Zochitidwiratu Chithunzi m’Maulosi Abaibulo
Onani mmene mikhalidwe yoteroyo inachitidwiratu chithunzi m’chitsanzo ichi cha maulosi a Baibulo:
Simudzakhala Nkhondo: “Aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi.” (Salmo 46:9) “Mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:4.
Chilungamo kwa Aliyense: ‘Ndipo ndidzayesa chiweruziro chingwe choongolera, ndi chilungamo chingwe cholungamitsira chiriri.’—Yesaya 28:17.
Ufulu ku Mantha: ‘Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa.’ (Mika 4:4) “Ndipo adzakhazikika m’dziko mwao.”—Ezekieli 34:27.
Njala Idzathetsedwa: ‘M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa.’ (Salmo 72:16) ‘Mitengo ya kuthengo idzapereka zobala zao, ndi nthaka idzapereka zipatso zake.’—Ezekieli 34:27.
Simudzakhala Kukalamba ndi Matenda: ‘Mnofu wake udzakhala se, woposa wa mwana; adzabwerera ku masiku a ubwana wake.’ (Yobu 33:25) “Ndipo wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.
Imfa, Kulira, ndi Kuwawa Zidzakhala Zitapita Kosatha: ‘[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.’—Chibvumbulutso 21:4.
Sadzayambukiridwa ndi Zakumbuyo
Dziko latsopano likudzalo lopangidwa ndi Mulungu lidzakhala lokhutiritsa kwenikweni kwakuti kusangalala ndi moyo kwa nzika zadziko lapansi sikudzasokonezedwa, osati ngakhale ndi zikumbukiro zoipa za kuvutika kwa kumbuyo. Malingaliro omangirira ambiri ndi ntchito zimene zidzakhala za moyo wa tsiku ndi tsiku kwa anthu m’nyengo yatsopano imeneyo zidzafuta pang’onopang’ono zikumbukiro zoipa zakale. Lonjezo la Mulungu ndi ili: “Zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.” Anthu adzakhala ‘osangalala ku nthaŵi zonse’ ndi chimene Mulungu adzayambitsa padziko lonse. “Dziko lonse lapuma, liri du; iwo ayamba kuyimba nyimbo.”—Yesaya 65:17, 18; 14:7.
Lerolino, ‘chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima,’ monga mmene Baibulo limanenera. Koma mkhalidwe udzabwezeretsedwa m’dziko latsopano. Panthaŵiyo ‘pakufika chifunirocho chidzakhala mtengo wa moyo.’ (Miyambo 13:12) Mitima sidzalemetsedwanso ndi kuvutika kapena ndi ziyembekezo zosakwaniritsidwa. Mmalo mwake, idzadzazidwa ndi kukhutiritsidwa ndi chisangalalo chifukwa cha zinthu zambiri zodabwitsa zimene Mulungu adzapereka kaamba ka banja la munthu.
Ulamuliro Wosiyana
Mmalo mwa kukhala ndi kulamulira kosakhutiritsa kwa munthu kodziimira payekha kuchoka kwa Mulungu, dziko latsopano lidzakhala ndi ulamuliro wosiyana kwenikweni. Akuluakulu olamulira maboma adzachotsedwa pa anthu. Sadzaloledwanso kulamulira modziimira paokha kwa Mulungu.
Ulosi wa Baibulo umati: ‘Ndipo masiku a mafumu aja [olamulira omwe tsopano akulamulira] Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu [m’mwamba] woti sudzaonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu [pokhala tsono palibe ulamuliro wa anthu], koma udzaphwanya ndi kutha maufumu ao onse [omwe alipo tsopano]. Nudzakhala chikhalire.’—Danieli 2:44.
Yesu anaphunzitsa atsatiri ake kupempherera ulamuliro watsopano wa padziko lapansi pamene anati: ‘Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.’—Mateyu 6:10.
Limeneli lidzakhala boma latsopano la anthu—ulamuliro wakumwamba wa Mulungu kupyolera mu Ufumu wake m’manja mwa Kristu. Ndipo padziko lapansi, atumiki aumunthu okhulupirika a Mulungu adzalamulira zinthu mogwirizana ndi chitsogozo cha Mulungu. (Yesaya 32:1) Mtumwi Petro analankhula za makonzedwe atsopano ameneŵa kuti ‘koma monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’mene mukhalitsa chilungamo.’ (2 Petro 3:13) Kulamulira kwa Ufumu kumeneko ndiko chiphunzitso chachikulu cha Baibulo.
‘Chilengedwe Chimasulidwa’
Ulamuliro watsopanowu udzaikanso magwero achibadwa a dziko lapansi pansi pa kulamulidwa kwathithithi. ‘Machitidwe achilengedwe’ onga ngati zivomezi, m’kuntho waukulu, zigumula, kapena zilala sadzachititsanso ngozi. Yesu iyemwini anasonyeza mphamvu yake ya kulamulira zinthu izi. Mwachitsanzo, nthaŵi ina, pamene ngalawa mmene munali Yesu ndi ophunzira ake inafuna kumira ndi namondwe, iye anakhalitsa bata mphepoyo ndi nyanja. Ophunzira ozizwitsidwawo analengeza kuti: “Ndiye munthu wotani uyu, pakuti ngakhale mphepo ndi nyanja zimvera iye?”—Mateyu 8:23-27.
Chotero dziko lapansi, limodzinso ndi chilengedwe chake chaumunthu, chidzapeza ufulu wosayerekezeka. ‘Cholengedwa chomwe chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi, ndi kulowa ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu. Pakuti tidziwa kuti cholengedwa chonse chibuula, ndi kugwidwa m’zowawa pamodzi kufikira tsopano.’—Aroma 8:21, 22.
Kodi tingakhale otsimikizira kuti kulamulira kwa munthu posachedwapa kudzatha ndikuti boma latsopano la Mulungu lidzatenga malo a kutsogolera zochita zonse padziko lapansi? Tingakhaledi motsimikizirika, chifukwa chakuti Mfumu ya Chilengedwe Chonse yapereka mawu ake awa: ‘Uphungu wanga udzakhala, ndipo ndidzachita zofuna zanga zonse; . . . ndanena, ndidzachionetsa; ndinatsimikiza mtima, ndidzachichitanso.’—Yesaya 46:10, 11.
“Nthaŵi Yoikika”
Kodi izi zidzabwera bwanji? Kodi zidzachitika liti? Mawu a Mulungu akuti: ‘Chinthu chirichonse chiri ndi nthaŵi yake yoikika.’ (Mlaliki 3:1) Ichi chimaphatikizapo nthaŵi yoikika ya Mulungu yoti anene kuti ‘zakwanira!’ ndikuthetsa kuipa ndi kuvutika. Danieli analozerako ku ‘nthaŵi yoikika pakutha pake.’ (Danieli 8:19) Yesu nayenso analankhula za “nthaŵi yoikika.”—Marko 13:32, 33, NW.
Inde, Mulungu wakhazikitsa nthaŵi yeniyeni yakuti iye alowereremo m’zochita za anthu ndi kuthetsa kuyesa komwe kwadzetsa tsoka kwa kulamulira kodziimira pawokha kwa anthu. ‘Mulungu adzaweruza wolungama ndi woipa; pakuti pamenepo pali mphindi ya zofuna zonse ndi ntchito zonse.’ (Mlaliki 3:17) Ndipo umboni wa kukwaniritsidwa kwaulosi wa Baibulo umasonyeza kuti nthaŵi yoikika ya Mulungu ya kulola kuvutika ili pafupi kutha. Pamene utali wa nthaŵi imeneyo watha, iye adzawononga dongosolo losakhutiritsa la kulamulira kwa anthu limene kwa zaka zikwi zambiri labweretsa kuvutika kochuluka ku banja la munthu.—Mateyu 24:3-14; 2 Timoteo 3:1-5, 13; Chibvumbulutso 19:11-21.
Pamene Mulungu adzapereka chiweruzo chake, onani chimene chidzachitika kwa amene amagonjera ku ulamuliro wake, mosiyana ndi amene samatero: ‘Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nao mtendere wochuluka.’ “Koma adzadula mbumba za oipa. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” ‘Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima! Pakuti ku matsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere. Koma olakwa adzaonongeka pamodzi: matsiriziro a oipa adzadulidwa.’—Salmo 37:10, 11, 28, 29, 37, 38; onaninso Miyambo 2:21, 22; Mateyu 5:5.
Koma bwanji ponena za anthu zikwi mamiliyoni ambiri omwe anafa kale? Kodi iwo adzapindula bwanji ndi dziko latsopanoli? Mwa kuwaukitsa, kuŵabwezeretsa ku moyo pano padziko lapansi. Iwo adzauka m’manda ndikupatsidwa mwaŵi wa kusangalala ndi moyo kosatha. Mawu a Mulungu akutsimikizira motere: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) Ndipo Yesu anakusonyeza uku mwa kuukitsa anthu akufa, monga ngati Lazaro ndi mwana wamkazi wamasiye wa ku Nayini.—Yohane 11:38-44; Luka 7:11-16.
“Zolipiridwa”
Nkodzetsa mpumulo chotani nanga kudziŵa kuti chifuno cha Mulungu nchakuthetsa kuvutika ndi kubweretsa dziko latsopano lolungama! Tangolingalirani za kukhala ndi moyo zaka mamiliyoni ambiri—ndithudi, kosatha—muumoyo wangwiro ndi chimwemwe pakati pa malo ozungulira a paradaiso, mmene kuipa ndi kuvutika zidzakhala zinthu zakale kosatha!
Kodi simungavomereze kuti “zolipiridwa” zimenezi zochoka kwa Mulungu kunka kwa anthu—kunthaŵi zosatha—zimasiyana kwambiri ndi zaka zikwi zoŵerengeka zimene Mulungu walola kuvutika kukhalapo? Ndipo kodi sizimaposanso kotheratu zaka 70 kapena 80—kapena kucheperapo—za kuvutika zimene tingakhale tavutika nazo aliyense payekha m’nthaŵi yathu yaumoyo?
Lingaliro la Nyengo Yaitali
M’lingaliro lake la nyengo yaitali ya zinthu, Mlengi amadziŵa kuti kunali kofunika kukhazikitsa choyamba nkhani zovuta za kufunikira kwake kwa kulamulira kolungama monga Mfumu ya Chilengedwe Chonse ndi kuyenerera kwa ulamuliro wake. Ndipo kunali kofunikadi kuthetsa nkhani ya kugwiritsira ntchito bwino ndi molakwa ufulu wa chosankha. Kunalinso koyenerera kusonyeza kuti chilengedwe chake nchangwiro ndikuti anthu amene amagonjera mokhulupirika ku malamulo ake olungama angasunge umphumphu kwa iye pansi pa chizunzo ndi chiyeso choperekedwa ndi olamulira adziko, chitsanzo chapadera cha ichi nkukhala Mwana wake, Yesu, pamene anali padziko lapansi.
Pokhala atathetsa nkhani zonsezi, Mulungu sadzalola kuipa ndi kuvutika kuwonekeranso ndikuipitsa chilengedwe chonse chamtendere. ‘Nsautso siidzauka kaŵiri.’—Nahumu 1:9.
Ku nthaŵi zosatha zomwe zikudzazo, Mulungu angagwiritsire ntchito zaka zikwi zambiri zapitazi monga ngati kunali kuyesedwa kwa nkhani ya m’khoti lalikulu. Chochitika chake chingagwiritsiridwe ntchito nthaŵi iriyonse yamtsogolo, kulikonse m’chilengedwe chonse, ngati pangabukenso kukaikira ufumu wa Mulungu kapena kugwiritsira ntchito molondola kwa ufulu.
Kodi Mudzasankhanji?
Tiri ndi chosankha lerolino. Tingagwiritsire ntchito ufulu wathu m’njira imodzi ya ziŵirizi: Tingasankhe kunyalanyaza zifuno za Mulungu, ndikukhala okhutiritsidwa ndi ulamuliro wa anthu, ndikugawana nawo chomwe chikuwayembekezera, kapena tingagwiritsire ntchito ufulu wathu wa kudzisankhira kuphunzira chimene zifuno za Mulungu ziri ndi chimene timafunikira kuchita kuti timkondweretse monga nzika zodzipereka za Ufumu wake.
Yesu anati kwa Mulungu m’pemphero: “Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Chotero ngati tikufuna moyo m’dziko latsopano, tiyenera kupanga kuyesayesa kuphunzira chowonadi chonena za Mulungu, zifuno zake, ndi zofuna zake. Onani mmene Baibulo limanenera: “Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.”—2 Mbiri 15:2.
Nthaŵi ikutha kaamba ka dziko lakale ili; latsopano lirikudza: ‘Dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi yonse.’ (1 Yohane 2:17) Kodi mudzasankha liti—dziko lakale lomwe likupita, kapena latsopano lomwe likudzalo?
Mawu a Mulungu amati: ‘Ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbeu zanu; kukonda Yehova Mulungu wanu, kumvera mawu ake, ndi kumamatira Iye, pakuti iye ndiye moyo wanu, ndi masiku anu ochuluka.’—Deuteronomo 30:19, 20.
Kodi nchikhumbo chanu kusangalala ndi madalitso amene Mulungu wakonzekera awo amene amagwirizana ndi zifuniro zake? Afalitsi a magazine ano kapena Mboni za Yehova kulikonse padzikoli adzakhala achimwemwe kukuthandizani, kwaulere, kuphunzira zambiri ponena za ichi.
[Mawu Otsindika patsamba 12]
Akufa adzakhala ndi mwaŵi wa kukhala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu mwa kuukitsidwa kuchoka m’manda