Achichepere Akufunsa Kuti . . .
Bwanji Ngati Makolo Anga Samandichilikiza m’Chikhulupiriro Changa?
ACHICHEPERE ambiri Achikristu ali ndi makolo osakhulupirira. “Ndine ndekha amene ndimaphunzira Baibulo m’banja mwanga,” akutero msungwana wina wazaka 12 zakubadwa. “Ndipo amayi ŵanga akufuna kuti ndileke kuliphunzira.” Ena ali ndi makolo amene amalephera kutsogolera mwauzimu. Mikhalidwe imeneyi ingakhale chiyeso chenicheni kwa wachichepere yemwe ali wofunitsitsa kutumikira Mulungu.
Kuyesayesa kukhala Mkristu wowona popanda chithandizo ndi chilimbikitso cha makolo anu nkovuta. Koma mungapambane! Zitsanzo zambirimbiri, zakale ndi zamakono, zatsimikizira chimenecho.
Achichepere Okhulupirika m’Nthaŵi za Baibulo
Talingalirani za Abele, mwana wa anthu aŵiri oyambirira, Adamu ndi Hava. Adamu ndi Hava adayenera kupereka chichilikizo chauzimu changwiro kwa ana awo. Koma anapanduka nafulatira Yehova, nawasiya ana awo kuti adzisamalire okha mwachipembedzo. M’malo modzimvera chifundo kapena kulola kupanda uzimu kwa makolo ake kuzilalitsa chiyamikiro chake cha iyemwini cha zinthu zopatulika, mwachiwonekere Abele anaphunzira zomwe anatha ponena za Mlengi. Yehova analankhula ndi ana a Adamu, Kaini ndi Abele, ndipo Abele anakulitsa unansi ndi Mulungu ndipo anakula kukhala munthu wachikhulupiriro. ‘Ndi chikhulupiriro Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yoposa ija ya Kaini, imene anachitidwa umboni nayo kuti anali wolungama.’—Ahebri 11:4; Genesis 4:2-15.
Yosiya ali chitsanzo china cha wachichepere yemwe anachita zinthu popanda chichilikizo chachipembedzo cha kholo. Atate ŵake, Mfumu Amoni wa Yuda, anaphedwa pamene Yosiya anali ndi zaka zakubadwa zisanu ndi zitatu zokha. Pamene anali ndi moyo, Mfumu Amoni ‘anachita choipa pamaso pa Yehova, monga umo anachitira Manase atate ŵake; pakuti Amoni anaphera nsembe mafano osema onse amene adawapanga Manase atate ŵake, nawatumikira. . . . Amoni amene anachulukitsa kupalamula kwake.’ (2 Mbiri 33:22, 23) Chotero, tangoyerekezerani mkhalidwe wofooketsa mwauzimu umene Yosiya, mwana wa Amoni akakuliramo.
Komabe, Yosiya ‘anachita zowongoka pamaso pa Yehova, nayenda m’njira za Davide kholo lake . . . anayamba kufuna Mulungu wa Davide kholo lake; ndipo atakhala zaka khumi ndi chimodzi [pa msinkhu wa zaka pafupifupi 20] anayamba kuyeretsa Yuda ndi Yerusalemu, kuzichotsa misanje, ndi zifanizo, ndi mafano osema, ndi mafano oyenga.’—2 Mbiri 34:2-4.
Kodi ndimotani mmene Yosiya anakulitsira nyonga yoteroyo popanda chithandizo cha tate? Iye analandira chichilikizo kwa amuna ena auzimu, monga ngati mkulu wansembe Hilikiya ndi mlembi wake Safani. Chisonkhezero chawo chabwino chauzimu pa Yosiya wachichepere chinamthandiza ‘[kuchita, NW] mawu a chilamulo.’ (2 Mafumu 23:24; 2 Mbiri 34:14-19) Chilamulo chimenecho chinafuna kuti mafumu alembe kope lawolawo ndi kuliphunzira usana ndi usiku. (Deuteronomo 17:18; Yoswa 1:8) Mosakaikira kuchita tero kunathandiza mokulira kukula kwauzimu kwa Yosiya.
Kupeza Chichilikizo Lerolino
Nanunso mungakule mwauzimu, ngakhale kuti simukulandira chichilikizo chimene mungachifune kwa makolo anu. Kaŵirikaŵiri chichilikizo chimapezedwa kwa abale ndi alongo auzimu ndi amayi ndi atate m’mipingo ya Mboni za Yehova. (Marko 10:30) Mumpingo mungakhale achichepere ena odera nkhaŵa ndi zinthu zauzimu, amene mungapalane nawo ubwenzi. Kapena pangakhale Mboni zina zachikulire zomwe zingakondwere nanu. Mwachitsanzo, wachichepere wopanda bambo wotchedwa Jerry anaitanidwa ndi mkulu wa mumpingo kutsagana naye pa phunziro Labaibulo lapanyumba. Pambuyo pa phunzirolo, kaŵirikaŵiri anali kupita kukadya ku lesitilanti ndi kulankhulana. “Iye anakhala ngati abambo ŵanga,” akukumbukira motero Jerry. Lerolino Jerry anakwatira ndipo akutumikira monga mtumiki wotumikira. Amayamikira kwambiri chichilikizo chimene mkuluyo anampatsa.
Kodi achikulire ena anadzipereka kukuthandizani mwa njira ina? Pamenepo bwanji osachitapo kanthu moyenerera? Ndipo ngati palibe amene anadzipereka, dziyambireni nokha kukulitsa mauunansi abwino. Mungayese kufikira mmodzi wa oyang’anira mumpingo wakumaloko. Mwinamwake mukufuna munthu wina kuchititsa phunziro Labaibulo lapanyumba kwa inu kapena kukuthandizani kukonzekera maasainimenti a Sukulu Yautumiki Yateokratiki.a Kapena mukungofuna kuyanjana kwabanja kwabwino. Momvekera bwino, mungachite mantha kudziŵitsa ena zosoŵa zanu mwanjirayi. Koma kumbukirani kuti akulu mumpingo anaikidwa kusamalira zosoŵa zauzimu za aliyense mumpingo—kuphatikizapo achichepere. (1 Petro 5:2) Iwo angakuthandizenidi.
Kukulitsa Chichilikizo Panyumba
Pamenepo, kodi zimenezi zikutanthauza kuti palibe chimene mungachite kuti muwongolere mkhalidwewo panyumba? Kutalitali. Mwachitsanzo, talingalirani za Joe wachichepere. Iye akulongosola mlingo wa chichilikizo chauzimu choperekedwa ndi makolo ake osakhulupirira kukhala “wochepa.” Komabe, Joe akuvomereza kuti iye angakhale anathandizira kusapereka chichilikizo kwawo. Motani? Eya, kukuwonekera kuti pamene Joe anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, anachita zochepa kugwiritsira ntchito m’moyo wake waumwini zimene anaphunzira. Chotero anapitiriza kusamvera makolo ake. Mwachibadwa, iwo sanawone chifukwa chophunzirira Baibulo iwo eni, ndipo sanawonenso chifukwa chomlimbikitsira iye kuliphunzira kwambiri Baibulo.
Bwanji nanga za inu? Ngati makolo anu sakhulupirira, kodi zochita zanu zimawapatsa chifukwa chokhulupirira kuti mukufunitsitsadi kutumikira Mulungu? Akazi Achikristu amauzidwa kupindula amuna awo osakhulupirira mwa mayendedwe awo abwino. Kodi makolo anu angapindulidwenso ‘popanda mawu’ ngati munali womvera kwambiri ndi waulemu kwa iwo? (1 Petro 3:1; Aefeso 6:1-3) Ngati ndichoncho, kodi iwo sakakuchilikizani?
Komabe, bwanji ngati makolo anu ali Akristu koma sakuchita zonse zimene ayenera kukuthandizani ndi kukulimbikitsani? Mosasamala kanthu kuti chifukwa chawo nchotani, inuyo mungachite zambiri kupititsa patsogolo mkhalidwe wabwino wauzimu m’nyumba mwanu mwakukhazikitsa chitsanzo chabwino. (1 Timoteo 4:12) Pamene nthaŵi yopita kumisonkhano Yachikristu yafika, valani ndi kukhala wokonzekera kupita. Dziperekeni modzifunira kuthandiza kuchita ntchito zina zowonjezereka zabanja kotero kuti makolo anu akonzekenso panthaŵi yake. Mudziŵa bwanji? Mwinamwake kutenthedwa maganizo kwanu ndi misonkhano kudzawayambukira bwino.
Kodi makolo anu amachititsa phunziro Labaibulo lapanyumba lamlungu ndi mlungu kwa inu? Ngati satero, bwanji osapempha mokoma mtima, osati molamula kapena modandaula. Pamene phunzirolo lichitidwa, musapangitse mbali yawo kukhala yovuta mwakukukakamizani kupereka ndemanga; khalani wokonzekera bwino lomwe kutengamo mbali. Chitani mbali yanu kuti mulipange kukhala chochitika chosangalatsa. Athokozeni chifukwa cha phunzirolo. Izi zingalimbikitse makolo anu kuchititsa phunzirolo mokhazikika.
Bwanji ngati pali chivomerezo chochepa ku zoyesayesa zanu? Musaleme. (Agalatiya 6:9) Sonyezani poyera chikondi chanu kwa Mulungu ndi chowonadi cha Baibulo. Musataye changu chanu kapena lingaliro la kufulumira pothandiza ena kuphunzira za Mulungu. Pitirizani ‘kudzimangirira nokha pa chikhulupiriro chanu choyeretsetsa, ndi kupemphera mu mzimu woyera.’ (Yuda 20) Wachichepere wotchedwa Laverne akuchita zimenezo. Iye akuti: “Ndasankha kusalola abambo ŵanga kundiletsa kuphunzira chowonadi. Choncho ndimaphunzira ndekha Nsanja ya Olonda m’malo mopenyerera TV.b Ndimaŵerenganso lemba la Baibulo m’maŵa uliwonse. Ndimakhoza kupita m’ntchito yolalikira mwakutulukira ndi abale ndi alongo ena Achikristu.”
Sonyezani kutsimikiza mtima kofananako. Musalole kusoŵeka kwa chichilikizo chapanyumba kukulefulani. Khalani olimba m’kutsimikiza mtima kwanu. Ngati nkotheka, yandikanani ndi achichepere ndi achikulire okonda zinthu zauzimu mumpingo. Koma kaya pakhale chichilikizo kapena ayi, khalani wotsimikiza mtima kusunga ubwenzi wanu ndi Mulungu. Mungamdalire kuti adzakuchilikizani.—Yerekezerani ndi Salmo 119:116.
[Mawu a M’munsi]
a Nsanja ya Olonda ili magazini inzake ya Galamukani! Mukhoza kuilandira mwakulembera afalitsi a magazini ano.
b Kuti mupeze chidziŵitso chonena za Sukulu Yautumiki Yateokratiki, onani nkhani yakuti “Kodi Misonkhano Yachikristu Ingandithandize Motani?” mu Galamukani! ya July 8, 1991.
[Chithunzi patsamba 13]
Ziŵalo zachikulire za mpingo zingathandize mwakukhala ndi chikondwerero mwa inu