Lingaliro la Baibulo
Kodi Mpikisano m’Maseŵero Ngwoipa?
AMUNA achikulire aŵiri akhala munsi mwa mtengo pa tsiku loŵala dzuŵa kwambiri, akumaseŵera nsolo. Chapafupipo pakumveka phokoso la ana amene akuthamangathamanga akumaseŵera chipako. Osati chapatali kwambiri, kagulu ka achinyamata kakusangalala ndi maseŵero a mpira. Inde, tsiku lililonse ponse pamene tili, achichepere ndi achikulire amasangalala kuchita maseŵero. Pamene atengamo mbali, anthu ambiri amene amaseŵera amayesetsa kuchita bwino kwambiri. Mwinamwake inunso mumatero.
Koma kodi kunganenedwe kuti kupikisana kwaubwenzi kotero nkoipa? Ambiri amadziŵa bwino za uphungu wa mtumwi Paulo pa Agalatiya 5:26 (NW), pamene anati Akristu sayenera kukhala ‘osonkhezera mpikisano pakati pa wina ndi mnzake.’ Mogwirizana ndi zimenezi, kodi kungakhale kosayenera kwa Akristu kupikisana m’maseŵero osangulutsa?
Kunena mosavuta, ayi. Chifukwa ninji? Tisanayankhe funsolo, tiyeni mwachidule tipende mbiri ya maseŵero.
Mbiri ya Maseŵero
Kutengamo mbali m’maseŵero kunayambira m’nthaŵi zakale ndipo kwakhala chochitika cha nthaŵi zonse m’mbiri yonse—kuphatikizapo mbiri ya anthu a Mulungu. Liwu lakuti “mpira” limapezeka ngakhale m’Baibulo. Pa Yesaya 22:18 (NW), potchula za matemberero a Yehova Mulungu kwa anthu oipa, pamati: ‘Adzawakulunga pamodzi molimba, ngati mpira.’ Mipira ina yatsopano—yonga mipira ya golf ndi ya baseball—imapangidwabe mwa kukulunga zopangira zake molimba. Baibulo la Revised Nyanja (Union) limatembenuza vesi limodzimodzili kuti: ‘adzawaponyaponya ngati mpira.’ Kuti kuyerekezera kumeneku kukhale kwanzeru, mipira iyenera kuti inagwiritsiridwa ntchito ndi awo amene anakhalako panthaŵiyo.
Ndiponso, m’Baibulo muli chochitika cha kholo Yakobo akulimbana ndi mngelo. Nkhani imeneyi ikuoneka kuti ikupereka lingaliro lakuti Yakobo anayesezapo luso limenelo pasadakhale, popeza nkovuta kunena amene anapambana pa kulimbanako kumene kunatha maola. (Genesis 32:24-26) Ndiponso, malingana ndi akatswiri ena, nkhaniyo ingasonyeze kuti Yakobo anadziŵa malamulo a kulimbana. Mwachionekere Aisrayeli anachitanso maseŵero oponya mivi—maseŵero enanso ofuna kuyeseza ndi luso. (1 Samueli 20:20; Maliro 3:12) Kuthamanga kunalinso maseŵero ena okondedwa amene amuna akale anayeseza.—2 Samueli 18:23-27; 1 Mbiri 12:8.
Maseŵero amene anafuna kulingalira—onga a kuponyerana mwambi—mwachionekere anali otchuka ndi okondedwa kwambiri. Mwinamwake chitsanzo chodziŵika koposa ndicho chimene Samsoni anachita, kuponyera mwambi Afilisti.—Oweruza 14:12-18.
M’Malemba Achigriki Achikristu, nthaŵi zina maseŵero anagwiritsiridwa ntchito monga a makhalidwe Achikristu. Mwachitsanzo, pa 1 Akorinto 9:24, 25, Paulo akutenga kuyeseza kwamphamvu kwa wothamanga ndi kukugwiritsira ntchito pakufunika kwa kudziletsa ndi kupirira kwa Mkristu. Ndiponso, nkoonekera bwino kuti Yehova anaikamo mkhalidwe wa kuseŵera m’chilengedwe chake chochuluka, popeza anthu ndi zinyama zomwe amapeza nthaŵi yoseŵera.—Yobu 40:20; Zekariya 8:5; yerekezerani ndi Ahebri 12:1.
Pamene Mpikisano Upyola Malire
Motero, kodi nchiyani chimene mtumwi Paulo analikunena kwa Akristu anzake pamene anawauza ‘kusasonkhezera mpikisano pakati pa wina ndi mnzake’? (Agalatiya 5:26) Yankho lili m’mawu ozungulira lembali. Paulo asanatchule zimenezi anachenjeza za kusakhala “odzikuza” kapena, monga mmene matembenuzidwe ena a Baibulo amanenera, kusakhala “onyang’wa,” “odzitukumula,” “okhumba ulemerero wachabe.” Kufunafuna kutchuka ndi ulemerero kunali kofala pakati pa ochita maseŵero a m’nthaŵi ya Paulo.
Moteronso m’dziko lino la ulemerero wachabe, ochita maseŵero ambiri amayamba kudzikuza ndi kudzionetsera iwo eni ndi maluso awo. Ena amapyola pamenepo ndi kunyozera ena. Kunyoza, kulozana zala, ndi kutukwana, kapena zimene amaseŵero ena amatcha “trash talking,” zikukhala mwambo mofulumira. Zonsezi zingakhale ‘kusonkhezera mpikisano,’ kotsogolera ku zimene Paulo anasonyako m’mbali yomaliza ya Agalatiya 5:26—njiru.
Ukafika poipitsitsa, mpikisano wopambanitsa umatsogolera ku ndewu ngakhale imfa. Talingalirani kukumana kwa amuna a Sauli ndi aja a Davide pa Gibeoni, pamene Abineri ndi Yoabu anavomerezana kuti “aimirire anyamata naseŵere pamaso [pawo].” (2 Samueli 2:14-32) Zimenezi zikumveka ngati kuti zikusonya ku mtundu wa kulimbana kopikisana. kaya mpikisano umenewo unali wotani, mwamsanga unakhala nkhondo yowopsa ndi yamwazi.
Lingaliro Loyenera
Maseŵero osangulutsa ayenera kukhala otsitsimula—osati okwiyitsa. Tingachite zimenezi mwa kuika zinthu m’malo ake, tikumakumbukira kuti kufunika kwathu kwa Mulungu ndi kwa anthu anzathu sikumadalira pa maluso athu m’maseŵero.
Kungakhale kupusa kulola malingaliro a kudzikuza kudzaza mwa ife chifukwa cha maluso athu akuthupi kapena nzeru zathu. Motero tiyeni tipeŵe chikhoterero chosayenera, cha kudziko cha kudzionetsera ife eni, kuti tingachititse njiru mwa ena, chikondi sichidziŵa kudzitamanda. (1 Akorinto 13:4; 1 Petro 2:1) Ndipo pamene kuli kwakuti nkoyenera kuyembekezera kuona chikondwerero, kutengeka maganizo mwadzidzidzi ndi kuyamikirana a m’gulu limodzi, sitingafune kuti malingaliro ameneŵa akhale osalamulirika ndi kukhala zodzitamandira nazo.
Sitingapime kufunika kwa ena ndi luso lawo m’maseŵero. Mofananamo, sitingafune kudziona opereŵera chifukwa cha kusoŵa maluso alionse. Kodi zimenezo zimatanthauza kuti kungakhale kulakwa kusunga zigoli? Si zimenezo kwenikweni. Koma tiyenera kukumbukira kuchepa mtengo kwa maseŵero alionse—kufunika kwenikweni kwa anthu sikumadalira pa mmene amaseŵerera. M’maseŵero a gulu, ena nthaŵi zonse amasinthasintha oseŵera m’gulu lililonse kotero kuti palibe gulu limodzi lenileni limene limapambana.
Akristu ayenera kukumbukiranso kuti pamene kuli kwakuti maseŵero amatchulidwa m’Baibulo, amangotchulidwa apo ndi apo. Kungakhale kulakwa kulingalira kuti kutchulidwa kokha kwa maseŵero m’Baibulo kumapereka chilolezo chonse cha maseŵero onse. (Yerekezerani 1 Akorinto 9:26 ndi Salmo 11:5.) Ndiponso, Paulo ananena kuti “chizoloŵezi chathupi chipindula pang’ono, koma chipembedzo chipindula zonse.”—1 Timoteo 4:8.
Motero, m’malo ake, maseŵero ngosangalatsa ndi otsitsimula. Baibulo silimatsutsa mpikisano uliwonse, koma mpikisano umene umachititsa zachabe, udani, umbombo, njiru, kapena chiwawa.