Kodi Nchifukwa Ninji Upandu Wolinganiza Ukuwonjezeka?
AL CAPONE, mpandu wovutitsayo m’Nyengo ya Kuletsa (1920-33) ku United States, ankanena kuti anali chabe wamalonda wamba wolabadira lamulo—lamulo la kupereka zofuna za anthu. Loya wa gulu lalikulu koposa la yakuza ku Japan anati: “Sungakane kuti anthu akufuna kwambiri zochitachita [za kugonana, anamgoneka, ndi kutchova juga].” Kufuna zinthuzo kumabala upandu wolinganiza. Ngakhale kuti palibe amene akufuna kuvutika ndi upandu, ena amatembenukira kwa magulu a apandu ndi kufuna thandizo lawo.
Mwachitsanzo, tinene za kunyengezera kupereka chitetezo kumene mamembala a maguluwa m’maiko ambiri amachita kuti apeze ndalama. Ngakhale nthaŵi zina amapita kwa eni masitolo oona mtima, kaŵirikaŵiri iwo amalima pamsana awo amene amachita malonda aukatangale. Mwini kasino wina ku Shinjuku, Tokyo, amene amachita malonda ake monamizira kuti ndi a maseŵero apavidiyo, anati: “Msungachuma wina anambaya mpeni, ndi kumlanda 2,000,000 [yen ($20,000)]. Koma sitikanaitana apolisi.” Chifukwa ninji? “Popeza kuti tikuchita zaukatangale (juga), sitifuna wapolisi aliyense. Ngati wodzaseŵera wina akusoŵetsa mtendere m’sitolo lathu, timaitana a yakuza.” Mwini kasino ameneyu amalipira $4,000 pamwezi kwa a yakuza, ndalama yaing’ono poilinganiza ndi phindu la $300,000 limene amapeza m’malonda ake aukatangale panthaŵi imodzimodziyo. Kodi ndalamazo zimachokera kuti? M’mathumba a amene amasangalala kutchova juga yosaloleka ndi lamulo.
Nchimodzimodzinso ndi malonda olemekezeka amene akufuna kupeŵa mavuto. Umboni wina ku New York unanena kuti wamalonda opaka utoto yemwe amapanga $15,000,000 pachaka anapulumutsa ngati $3,800,000 mwa kupseteka mamembala a m’magulu achiwawa. Zimenezi zinalola wamalondayo kulemba antchito amalipiro otsika ndi kupeŵa kulimbana ndi bungwe losonkhezeredwa ndi achiwawawo. Ku Japan, panyengo ya kutukuka kwa zachuma, anthu achuma anagula malo ndi kugwetsa nyumba zake zakale ndi masitolo ake kuti amangepo nyumba zambambande. Pamene okhalapowo anakana kuchoka kapena kugulitsa malo awo, anthu achumawo anaitana a jiageya, nthaŵi zambiri makampani ogwirizana ndi yakuza, kudzawachotsapo.
Pamene gulu la yakuza linaona kuti kukongola ndi kupanga ndalama kunalidi kosavuta m’ma 80, ilo linapanga makampani ndi kuloŵa m’malonda ogula malo ndi zigawo za makampani ndi kuzigulitsa mwanjira yotchedwa speculation (kuchita malonda malinga ndi kusintha kwa mtengo pamsika). Mabanki ndi mabungwe ena a zachuma anaikamo ndalama zawo m’makampani ameneŵa, mosakayikira ndi cholinga cha kudzipangira phindu. Koma pamene zinthu zinasintha potsirizira pake, mabanki anavutika kwambiri kupezanso ndalama zawozo. Ponena za kugwa kwa zachuma kovuta kutha ku Japan, amene kale anali mkulu wa polisi anati mu Newsweek: “Chifukwa chenicheni chimene mavuto a maloni osabwezedwa sangathetsedwe msanga nchakuti ochuluka a iwo ngogwirizana ndi upandu wolinganiza.”
Ndithudi, upandu wolinganiza umazika mizu ndi kukula kumene anthu ali ofunitsitsa kukhutiritsa zilakolako zawo zonyansa, mosasamala kuti akuzikhutiritsa motani. Umbombo wa kusanguluka, kugonana, ndi ndalama umasonkhezera kuzembetsa anamgoneka, uhule, juga, ndi ngongole zakatapira. Kuchita nawo zinthu zimenezi kambiri kumatanthauza kuchirikiza ndi kulemeretsa apandu. Zilidi zoona chotani nanga kuti upandu wolinganiza umatumikira zofuna za awo amene ali otsimikiza mtima kukhutiritsa zikhumbo zawo zoipa zakuthupi!
Mabanja Osema
Kuwonjezera pa kufuna zinthu zosaloledwa, palinso kusoŵa kwina kumene anthu ali nako kumene kukukulitsa upandu wolinganiza. Malemu amene anali mkulu wa limodzi la magulu aakulu koposa a yakuza ku Japan analimbikira kunena kuti anali kutenga ndi kusamala anthu osamvera choncho kuwaletsa kukhala anthu oipa. Iye ankanena kuti anali atate wa mamembala a gululo. Magulu ochuluka a apandu, mosasamala kanthu za mtundu wawo, amamanga magulu awo pamaunansi a mabanja osema ameneŵa.
Mwachitsanzo, tinene za Chi Sun,a amene anachokera ku banja losauka ku Hong Kong. Nthaŵi zambiri atate wake ankamumenya mwachiwawa pazifukwa zazing’ono. Chi Sun wachichepereyo anapanduka ndi kuloŵa gulu loipa la Triads pamsinkhu wa zaka 12. M’gulu la apandulo, anapeza malo amene anamva “wolandiridwa.” Chifukwa cha kulimba mtima kwake pomenyana ndi zida, mwamsanga anamkweza kukhala pamalo pamene anali kulamulira amuna angapo. Potsirizira pake, pamene anali ndi zaka 17 zokha, anaponyedwa m’ndende.
Ambiri monga Chi Sun amatembenukira ku magulu a apandu kuti apeze chomangira cha banja chimene panalibe panyumba. Mamembala ake amati ngosamala, koma kaŵirikaŵiri achichepere amagwira mwala atazindikira kuti kwenikweni membala aliyense amafuna zake za iye yekha.
Mngelo wa Kuunika
Pamene gulu laupandu lalikulu koposa ku Japan anati ndi lachiwawa malinga ndi lamulo loletsa magulu achiwawa mu 1992, mmodzi wa atsogoleri ake ananena molimba kuti gululo limadziona monga “labwino,” lolimbana ndi zoipa. Pamene chivomezi chachikulu chinakantha Kobe mu 1995, gulu limodzimodzilo linapereka chakudya, madzi, ndi zina zofunika mwamsanga kwa anansi awo. “Umataya umenewu,” inatero Asahi Evening News, “udzalimbitsadi chithunzi chakalechi cha gulu la yakuza m’Japan kuti ndi apandu olemekezeka.”
Atsogoleri a magulu a apandu nthaŵi zambiri ayesa kuvala chinyau cha anthu abwino. Kwa okhala m’mudzi wa zithando wa mumzinda mwake, mtsogoleri wambiri yoipa wa gulu lozembetsa anamgoneka la ku Medellín ku Colombia, Pablo Escobar, anali “ngati munthu wa m’nthano—mbali ina Mesiya, mbali ina Robin Hood, mbali ina Mtsogoleri m’lingaliro longa la umbuye la patrón, bwana,” analemba motero Ana Carrigan mu Newsweek. Anamangira ana nyumba yamaseŵero a nsapato zamagudumu ndi nyumba zabwino za osauka, ndipo ana a m’khwalala anawalemba ntchito. Anali ngwazi kwa awo amene anapindula ndi mataya ake.
Ngakhale zili tero, apandu amene akuoneka ngati akubisala m’magulu awo angokhala antchito a mpandu wamkulu wa m’chilengedwe chonse. Baibulo limamtchula ameneyo. “Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika. Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adzionetsa monga atumiki a chilungamo; amene chimaliziro chawo chidzakhala monga ntchito zawo.” (2 Akorinto 11:14, 15) Lerolino, anthu ochuluka samakhulupirira kuti Satana ndi munthu weniweni. Wandakatulo wina wa ku France wa m’zaka za zana la 19 anati: “Machenjera aakulu koposa a Mdyerekezi ndiwo kukukakamizani kukhulupirira kuti iye kulibe.” Iye amabisala kuseri ndi kulamulira zochitika, osati m’magulu a apandu mokha koma padziko lonse. “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo,” limafotokoza motero Baibulo. Yesu anafotokoza Satana kukhala “wambanda kuyambira pachiyambi, . . . wabodza, ndi atate wake wa bodza.”—1 Yohane 5:19; Yohane 8:44.
Maulosi a Baibulo amavumbula kuti Satana Mdyerekezi wakhala wachangu zedi kuyambira 1914. Kuyambira chakacho kumka mtsogolo, wakhala akusonkhanitsa magulu ake kuti achite nkhondo yaikulu pa anthu a Mulungu. Iye akukokera mtundu wa munthu m’chipwirikiti chachikulu. Ndiye chifukwa chachikulu chimene upandu ndi magulu a apandu akuwonjezekera lerolino.—Chivumbulutso 12:9-12.
Kodi mkulu wa magulu a apandu a padziko lapansi adzachotsedwapo konse? Kodi mtundu wa munthu udzakhalapo pamtendere ndi bata? Kodi inuyo mungawonjoke paufumu woipa umene Satana wamanga padziko lapansi lerolino?
[Mawu a M’munsi]
a Maina ena asinthidwa kutetezera otchulidwawo.
[Bokosi patsamba 7]
Mmene Mungatetezerere Banja Lanu
KUSOŴEKA kwa mkhalidwe wachikondi ndi wogwirizana m’banja kungachititse achichepere kunyengeka msanga ndi magulu a apandu. Ku United States, akuti achichepere ochuluka amene amaloŵa m’magulu opha anthu amachokera kumabanja osauka kapena osweka. “Pokhala osauka,” akutero mkulu wina wa pamalo osungira anthu amilandu ku North Carolina, “iwo amatengeka maganizo mosavuta ndi kugwirizana kolimba pakati pa bwana ndi anyamata ake ndi kugwirizana kwawo monga mamembala a gulu, zimene amaona nthaŵi yoyamba m’moyo wawo.”
Mofananamo, wachichepere wina wa yakuza Kummaŵa amene ali wofunitsitsa kukhala mtetezi wa bwana wake akuti: “Panyumba ndinkakhala ndekha nthaŵi zonse. Ngakhale kuti tinali banja, sindinaonepo monga tingakambitsirane zinthu zakukhosi. . . . Koma tsopano ndimalankhula zakukhosi ndi anyamata.” Achichepere osungulumwa amayamikira kwambiri mamembala a gulu la apandu amene amawaloŵetsa mumkhalidwe wonga banja.
“Anthu a yakuza ngosamala kwambiri,” akutero mtsogoleri wa gulu la atsikana oyendetsa njinga zamoto ku Okinawa. “Mwina ndilo tsenga lawo; koma popeza ifetu paja anthu sanatichitirepo zabwino, zimenezi zimatitenga maganizo.” Woyang’anira malo osungirapo atsikana opulupudza akuvomereza kuti anyamata a m’magulu achiwawa “alidi akatswiri pakukopa mtima wa atsikana.” Pamene atsikana osungulumwa awaimbira foni pakati pa usiku, anyamatawo amathamangirako ndi kumvetsera zimene akufuna kunena, popanda kuyesa kugonana nawo.
Chisamaliro chawo chimatha atangokopa mokwana achichepere amene akufunawo. Achicheperewo atangogwidwa mumsampha, amawawononga kotheratu—atsikana mu uhule ndi anyamata m’gulu la apandu.
Kodi Mungawatetezere Motani Okondedwa Anu?
“Atate inu, musaputa ana anu, kuti angataye mtima,” limalangiza motero Baibulo. (Akolose 3:21) Kumeneku sikulimbikitsa makolo kukhala olekerera zinthu ayi. Mwambi wina wa Baibulo umati: “Mwana womlekerera achititsa amake manyazi.” (Miyambo 29:15) M’malo mwake, Baibulo limalimbikitsa atate—ndi amayinso—kukhala ololera pochita ndi ana awo, kuwamvetsera, ndi kulankhula nawo momasuka nthaŵi iliyonse. Ndiyeno, ana adzasonkhezeredwa kuuza makolo awo zakukhosi pamene apsinjika maganizo.
Kuwonjezera pa kulankhula nawo momasuka nthaŵi iliyonse, makolo ayenera kupatsa ana awo miyezo ya m’moyo. Kodi atate angazipeze kuti zitsogozo zimenezi? Baibulo limati: “Atate inu, musamakwiyitsa ana anu, koma pitirizani kuwalera m’chilango ndi kuwongolera maganizo kwa Yehova.” (Aefeso 6:4, NW) Patulani nthaŵi yophunzira Baibulo ndi ana anu mwa maphunziro a Baibulo a banja. Ndipo zikani m’mtima mwawo mantha abwino a Yehova kuti nthaŵi zonse akatsatire zitsogozo za Yehova kaamba ka phindu la iwo eni.—Yesaya 48:17.