Lingaliro la Baibulo
Kodi Ziŵanda Zilipodi?
M’KATI mwazaka za zana la 17 ndi la 18, m’madera ambiri ku Ulaya munachitika kampeni yamphamvu yozunza mfiti. Ambiri omwe ankawaganizira kukhala mfiti anazunzidwa kwambiri. Ena omwe ankangoŵanamizira anavomereza kuti ndi mfitidi chabe kuti aleke kuwazunza. Anthu ambiri anaphedwa chifukwa cha mphekesera chabe kapena kungowaganizira.
Ngakhale kuti ankazionetsa ngati za m’Malemba, machitidwe otsutsa ufiti womwe uli wauchiŵanda, ankawachita mongotengeka maganizo. Akristu sanapatsidwe udindo wozunza kapena kupha mfiti kapena wina aliyense wochita za mizimu. (Aroma 12:19) Kodi anthu masiku ano amaiona motani nkhaniyi?
Kunyalanyaza
Masiku ano anthu ambiri m’Dziko Lachikristu saona machitachita a zamizimu monga nkhani yofunika. Chifukwa chongofuna kudziŵa, ena amayamba kupenda nyenyezi, matsenga, kuwombeza, ndi ufiti, koma saona zinthu za matsenga zimenezi monga zauchiŵanda. Nthaŵi zina, ochita za maseŵero ndi andale amavomera kuti amachitako matsenga. Mabuku ndi mafilimu ena amasonyeza mfiti ndi owombeza monga “osiririka, monga anthu odabwitsa pang’ono amene zochita zawo ndi mphamvu zawo zoposa za munthu nzosavulaza aliyense,” inatero insaikulopedia ina. Nkhani zopangidwira kusangalatsa ndi kuphunzitsa ana zikhoza kumalimbikitsa zinthu zamatsenga.
Khalidwe longonyalanyaza machitidwe auchiŵanda limeneli likhoza kupangitsa kusakhulupirira kuti kuli ziŵanda. Kodi mumakhulupirira kuti kuli ziŵanda ndipo nzotangwanika kuyesayesa kutivulaza? Ndipo masiku ano anthu ambiri akhoza kunena kuti sanaonepo ziŵanda kapena kuona zochita zawo. Kodi ziŵanda zilipodi?
Kusakhulupirira Kuli ndi Vuto
Amene amati amakhulupirira Baibulo koma amakayikira kuti ziŵanda zilipo ali ndi vuto. Ngati sakhulupirira kuti ziŵanda zilipo, ndiye kuti akusonyeza kusalikhulupirira kwenikweni Baibulo. Nchifukwa ninji? Chifukwa nkhani yakuti kuli zolengedwa zauzimu zomwe zili ndi mphamvu zoposa zomwe munthu amakhala nazo mwachibadwa imaphunzitsidwa m’Mawu a Mulungu, Baibulo.
Buku lake loyamba, Genesis, limalongosola mmene cholengedwa china chanzeru chinagwiritsirira ntchito njoka kunyenga Hava ndi kumtsogolera kupandukira Mulungu. (Genesis 3:1-5) Buku lomaliza la Baibulo, Chivumbulutso, limatcha wonyenga wochenjera ameneyu, “njoka yokalambayo,” kuti ndi “wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana wonyenga wadziko lonse.” (Chivumbulutso 12:9) Satana anapambana pa kunyenga angelo ena kuti apanduke. (Yuda 6) M’Baibulo angelo opandukaŵa amatchedwa ziŵanda. Iwo amachitira ntchito yawo padziko lapansi ndipo ndi okwiya kwambiri ndi Mulungu ndi amene amamtumikira.—Chivumbulutso 12:12.
Satana ndi ziŵanda ali ndi mphamvu yolimbikitsa, kuvulaza, ndi kulankhula ndi anthu. (Luka 8:27-33) Iwo akhala akuphunzira za chikhalidwe cha munthu kwa zaka zikwi zambiri. Amadziŵa mmene angagwiritsirire ntchito kufooka kwa munthu. Baibulo limasimba za zochitika zina pamene zinkaloŵerera, kapena kulamulira azibambo, azimayi, ndi ana. (Mateyu 15:22; Marko 5:2) Zikhoza kupangitsa matenda kapena kupundula munthu monga kumchititsa khungu. (Yobu 2:6, 7; Mateyu 9:32, 33; 12:22; 17:14-18) Zikhozanso kuchititsa khungu malingaliro a anthu. (2 Akorinto 4:4) Ziŵanda zimagwira ntchito nthaŵi zonse, monga mtsogoleri wawo, Satana, amene ali ngati “mkango wobuma, . . . kufunafuna wina akamlikwire.” (1 Petro 5:8) Baibulo lili ndi nkhani zambiri zonena zakuti ziŵanda zilipo. Ngati mumakhulupirira Baibulo, ndiye kuti mumavomerezanso kuti kuli zolengedwa zauzimu zosaoneka.
Onyenga Oipa
Koma kodi zingatheka bwanji kuti kukhale ziŵanda zamphamvu komabe osachititsa anthu padziko kukhala mwamantha? Nchifukwa chiyani kukhalapo kwawo ndi ntchito zawo sizidziŵika kwambiri? Baibulo limayankha: “Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.” (2 Akorinto 11:14) Mdyerekezi ndi wonyenga. Zochita za ziŵanda kaŵirikaŵiri zimabisidwa kukhala ngati zosavulaza mwina ngakhale zabwino. Choncho, nzovuta kuzizindikira.
Satana ndi ziŵanda zake akupitirizabe kuvutitsa anthu mwanjira zosiyanasiyana, monga mmene ankachitira m’nthaŵi za Baibulo. Ena amene tsopano ndi Akristu enieni panthaŵi ina ankachitako zamatsenga; akhoza kuchitira umboni za zochita zoopsa za ziŵanda. Mwinamwake kuposa kale lonse, lerolino ziŵanda zikugwiritsira ntchito mphamvu zawo zoposa za munthu kunyenga anthu kuchita zamatsenga. Sitiyenera kuderera mphamvu zawo. Komabe, zimakwanitsa kwambiri zolinga zawo mwa kunyenga anthu kuwachotsa kwa Mulungu koposa mwa kuwavutitsa. Satana ndi ziŵanda ‘amanyenga [anthu] dziko lonse,’ limatero Baibulo. (Chivumbulutso 12:9) Zolinga zawo ndi kuwononga chikhulupiriro cha anthu pang’onopang’ono mwamachenjera.
Ziŵanda zilipodi. Kodi tingatinso nchiyani chimene chimapangitsa kukonda kuphana ndi kuwononga zinthu koonekeratu pakati pa anthuku? Mwachibadwa anthu amafuna kumakhala mwamtendere ndi mwachimwemwe. Koma ziŵanda zimachirikiza kuipa ndipo zili ndi mphamvu zolimbikitsa ndi kusokoneza malingaliro a anthu.
Komabe, Yehova ndi Mulungu wamphamvu yonse—wamphamvu kwambiri kuposa ziŵanda. Iye amapereka mphamvu ndi chitetezo kuletsa “machenjera a Mdyerekezi.” (Aefeso 6:11-18) Sitiyenera kuopa ziŵanda monyanyira, popeza Mulungu amalonjeza kuti: “Potero mverani Mulungu; koma kanizani Mdyerekezi, ndipo adzakuthaŵani inu.”—Yakobo 4:7.
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
Sipa Icono