Kuzindikira Mulungu Woona Yekha
PAFUPIFUPI kuyambira pamene anthu anayamba kukhalako, anali ndi milungu yambiri. Milungu yakhalako yambirimbiri moti n’kovuta kutchula kuti milungu yaimuna ndi yaikazi iliko ingati, yomwe anthu amalambira padziko lonse lapansi—komabe ikukwana m’mamiliyoni.
Poti tadziŵa kuti Mulungu aliko, tingafunseno kuti, Kodi pa milungu yonse yomwe anthu akhala akulambira padziko lonse lapansi, woona ndiye uti? Zoti kuli Mulungu mmodzi yekha woona timadziŵa chifukwa Baibulo, pa Yohane 17:3 limanena momveka bwino kuti: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe Inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.”
Dzina Lomwe Amadziŵika Nalo
M’pomveka kuti mulungu aliyense wokhala ndi umunthu wakewake afune dzina lakelake lom’siyanitsa ndi milungu ina yonse yokhalanso ndi mayina awoawo. Lingakhale dzina lomwe mulunguyo wakonda, n’kudzitcha nalo yekha, osati dzina limene olambira ake am’sankhira.
Komabe, pankhani imeneyi pabukanso mfundo ina yovuta kwambiri. Ngakhale kuti zipembedzo zambiri zazikulu zimapatsa milungu yawo mayina awoawo, Ayuda ndi matchalitchi akuluakulu a m’Dziko Lachikristu alephera kupatsa mulungu amene amam’lambira dzina lakelake lom’siyanitsa ndi milungu ina. M’malo mwake, amangom’tchula ndi mayina aulemu onga akuti, Ambuye, Mulungu, Wamphamvuyonse, ndi Atate.
Mlembi wina wotchedwa David Clines, polemba m’buku lakuti Theology, ananena mawu otsatirawa: “Nthaŵi ina pakati pa zaka za zana lachisanu ndi za zana lachiŵiri B.C., ngozi inamugwera Mulungu: dzina lake linaiwalika. Zinangokhala ngati zoonadi, chifukwa Ayuda analeka kum’tchula Mulungu ndi dzina lake loti Yahweh, ndiyeno anayamba kum’tchula Yahweh ndi mayina achidule, akuti: Mulungu, Ambuye, Dzinalo, Woyerayo, Wokhalakoyo, ngakhalenso kungoti Malowo. Ngakhale kuti m’ndime zina m’Baibulo munali Yahweh, oŵerenga ena ankalitchula dzinalo kuti Adonai. Potsirizira, pamene kachisi anagwa, anthu analeka kuchita miyambo yakamodzikamodzi, ndiye poti dzinalo ankalitchula pamiyambo imeneyo, italekeka miyamboyo, anthunso anaiwala dzinalo.” Komabe, palibe aliyense amene anganenedi zenizeni zoti Ayuda osunga lamulo analeka liti kutchula dzina la Mulungu, n’kuyamba kugwiritsa ntchito mawu achihebri otanthauza Mulungu kapena kuti Ambuye Mfumu.
Choncho, zikuoneka kuti ngati munthu anafuna kudziŵa “Mulungu woona yekha” anafunikira kum’dziŵa ndi dzina lake. Kufufuza kwake sikovuta ngakhale pang’ono, chifukwa dzina la Mulungu Wamphamvuyonse, Mlengiyo, latchulidwa mosavuta pa Salmo 83:18, kuti: “Kuti adziŵe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi.”
Yehova Kapena Yahweh?
Ngakhale kuti dzina lakuti Yehova limaoneka m’Baibulo la Nyanja (Union) Version, anthu ena amakonda lakuti Yahweh osati Yehova. Dzina lenileni ndiye liti?
Mabaibulo akale kwambiri olemba pamanja analembedwa m’Chihebri. M’Malemba Achihebri, dzina la Mulungu limapezekamo nthaŵi pafupifupi 7,000 ndipo limalembedwa ndi makonsonanti anayi—YHWH kapena JHVH. Zilembo za makonsonanti anayi zimenezi n’zotchuka ndi dzina lakuti Tetragrammaton, kapena Tetragram, mawu aŵiri a Chigiriki otanthauza “zilembo zinayi.” Tsopano pabukanso vuto lakatchulidwe kabwino ka dzinalo, popeza kuti kale anthu polemba Chihebri ankalemba makonsonanti basi popanda ma vawelo othandiza woŵerenga kutchula bwino mawu. Choncho kaya munthu atchule Tetragrammaton imeneyo kuti Yahweh kapena Yehova, zidzangokhala malinga ndi mavawelo amene munthuyo wawonjezera pa makonsonanti anayiwo. Lerolino akatswiri ambiri odziŵa Chihebri amakonda kuti Yahweh chifukwa amaganiza kuti ndimo mmene liyenera kumvekera.
Komabe, zinazolowereka kulitchula dzinalo kuti Yehova. Chifukwa? Kwa zaka zambirimbiri anthu akhala akulitchula kuti Yehova m’Chicheŵa. Amene amatsutsa kuti kameneko si katchulidwe kabwino ayenera kutsutsanso katchulidwe ka Yeremiya ngakhalenso katchulidwe ka Yesu. Yeremiya akanafunikira kusintha n’kukhala Yir·meyahʹ kapena Yir·meyaʹhu, ndimo mmene Ahebri ankalitchulira kale, ndiyenso Yesu akanakhala Ye·shuʹaʽ (Chihebri) kapena I·e·sousʹ (Chigiriki). Choncho, anthu ambiri ophunzira Baibulo, kuphatikizapo a Mboni za Yehova, amaona kuti kuli bwino kumalitchula dzinalo monga mmene akhala akulitchulira m’Chicheŵa kuyambira kale, kuti “Yehova” osasinthasintha, monganso ena amalitchulira m’zinenero zawo.
Kodi Zilidi N’kanthu?
Ena anganene kuti zilibe kanthu kwenikweni ngakhale musam’tchule Mulungu Wamphamvuyonse ndi dzina lakelake, ndipo iwowo alibe nazodi kanthu, akamanena za Mulungu kapena kum’tchula, amangoti Atate kapena kungoti Mulungu basi. Komabe, mayina ameneŵa angokhala aulemu chabe, si mayina akeake omwe amam’siyanitsa ndi ena ayi. M’nthaŵi za Baibulo, liwu lakuti Mulungu (Chihebri ʼElo·himʹ), ankaligwiritsa ntchito potchula mulungu wina aliyense—ngakhale mulungu wa anthu akunja, Afilisti, wotchedwa Dagoni. (Oweruza 16:23, 24) Choncho ngati m’Hebri akanauza m’Filisti kuti iye, m’Hebriyo, amalambira “Mulungu,” mwa mawu okhawo sakanakhala atatchula Mulungu woona yemwe iyeyo ankalambira.
Buku lakuti The Imperial Bible-Dictionary la mu 1874, linanena mawu ena osangalatsa, linati: “Kulikonse dzina lakuti [Yehova] limadziŵika kuti n’dzina la munthu mmodzi, la Mulungu wokhala ndi umunthu wakewake ndipo yekhayo; pomwe Elohim lingakhale la anthu angapo, lotanthauza Wamkulu, komabe osati nthaŵi zonse. . . . M’Hebri, potchula anganene kuti Elohim wakutiwakuti, Mulungu woona, pom’siyanitsa ndi milungu yonyenga; koma potchula Yehova, sanganene kuti Yehova wakutiwakuti, ngati kuti alipo a Yehova ambiri, pomwe Yehova ndilo dzina la Mulungu woona yekha. Amabwerezabwereza kuti Mulungu wanga . . . ; koma sanena kuti Yehova wanga, chifukwa pamene akuti Mulungu wanga, akutanthauza Yehova yemweyo. Amanena kuti Mulungu wa Israyeli, koma osati Yehova wa Israyeli, chifukwa kulibenso Yehova wina. Amanena kuti Mulungu wamoyo, koma osati Yehova wamoyo, ngati kuti palinso Yehova wina wakufa.”
Mikhalidwe ya Mulungu Woona
Kungodziŵa chabe dzina la munthu wina, sizitanthauza kuti munthuyo tikum’dziŵa bwino. Ambirife timadziŵa mayina a anthu otchuka andale. Tingadziŵenso bwino ngakhale mayina a amuna ndi akazi otchuka a m’mayiko ena. Koma kungodziŵa mayina awo—ngakhale kudziŵa kutchula bwino mayina awowo—sizitanthauza kuti timawadziŵa bwino anthuwo kuti ali anthu otani. Momwemonso, kuti tidziŵe Mulungu mmodzi yekha woona, tifunikira kudziŵanso mikhalidwe yake n’kuikondanso.
Ngakhale kuti n’zoona kuti anthu sadzatha kuonana ndi Mulungu woona tsiku lina, koma mwachifundo iye anauza anthu kutilembera m’Baibulo zinthu zambiri zosonyeza umunthu wake. (Eksodo 33:20; Yohane 1:18) Ahebri ena omwe anali aneneri anaonetsedwa masomphenya a malo okhala Mulungu Wamphamvuyonse kumwamba. Akamawasimba, timaona chithunzi cha munthu wolemekezeka kwambiri ndipo waulemerero wodabwitsa ndipo munthu wamphamvu, komanso munthu wofatsa, wadongosolo, wokongola, ndipo wabwino.—Eksodo 24:9-11; Yesaya 6:1; Ezekieli 1:26-28; Danieli 7:9; Chivumbulutso 4:1-3.
Yehova Mulungu anafotokozera Mose mikhalidwe yake ina yabwino kwambiri, Moseyo n’kudzailemba pa Eksodo 34:6, 7, kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula.” Kodi simukuvomereza kuti mikhalidwe ya Mulungu imeneyi titaidziŵa tingamuyanje ndipo ingatipangitse kufuna kum’dziŵa bwino monga munthu?
Ngakhale kuti palibe munthu aliyense amene adzakhoza kuona Yehova Mulungu mu ulemerero wake wochititsa kaso, komabe kwalembedwa kuti pamene Yesu Kristu anali munthu padziko lapansi, ankasonyeza bwinobwino mmene Yehova Mulungu, Atate wake wakumwamba alilidi. Tsiku lina Yesu anati: “Sakhoza Mwana kuchita kanthu pa yekha, koma chimene aona Atate achichita, ndicho. Pakuti zimene Iye azichita, zomwezo Mwananso azichita momwemo.”—Yohane 5:19.
Choncho, mwa mawu okhawo, tingadziŵe kuti Yesu pochitira anthu ulemu, chifundo, kufatsa kwake ndi kukoma mtima kwake, ngakhalenso kukonda kwake chilungamo kwambiri koma namadana ndi choipa, inali mikhalidwe yomwe anaonera Atate wake, Yehova Mulungu, pamene Yesu anali naye kumwamba asanakhale munthu padziko lapansi pano. Ndiye kuti titafikira pakudziŵa bwino kuti dzina lakuti Yehova limatanthauzanji, m’njira iliyonse tingalikonde ndi kulidalitsa dzina limenelo, kulitamanda ndi kulikweza, ndi kulidaliranso.
Yohane 17:3 m’Baibulo la New World Translation of the Holy Scriptures, amasonyeza kuti kudziŵa Mulungu woona yekha mwa njira imeneyi ili ntchito yosatha. Panopa mawu akuti “kudziŵa” anatchulidwa bwino moti amatithandiza kwambiri kuona kuti kum’dziŵa kwake n’kwa pang’onopang’ono kosalekeza, osati kungom’dziŵa nthaŵi imodzi kwatha. Choncho, timaŵerenga kuti: “Ichi chitanthauza moyo wosatha, kuti amke nakudziŵani inu, Mulungu woona yekha, ndiponso yemwe munam’tumiza, Yesu Kristu.” Inde, kudziŵa Mulungu woona yekha, Yehova, ndi Mwana wake, Yesu Kristu, n’kopanda mapeto.
Mulungu Woona Wavumbulidwa
Choncho, Mulungu woona n’ngosiyaniratu ndi milungu yambiri yonyenga. Iye ndiye Mlengi wamphamvuyonse analenga zinthu zonse, kuphatikizapo pulaneti Dziko, limodzi ndi anthu okhalapo. Ali ndi dzina lakelake—Yehova, kapena Yahweh. Saali mmodzi mwa milungu itatu yosadziŵika bwino, kapena kuti sali Utatu. Iye ali Mulungu wachikondi, ndipo amangofuna kuti anthu omwe anawalenga zinthu ziziwayendera bwino kwambiri. Komanso ali Mulungu wachilungamo, moti sadzalekerera anthu amene saleka kuwononga dziko ndiponso okonda nkhondo ndi chiwawa.
Yehova wavumbula kuti watsimikiza kudzachotsa padziko lapansi kuipa konse ndi kulikonzanso dzikoli kuti lidzakhale paradaiso, kuti anthu amitima yabwino adzakhalemo kwamuyaya, ali achimwemwe. (Salmo 37:10, 11, 29, 34) Mulungu Wamphamvuyonse tsopano wakhazika Mwana wake, Yesu, akhale Mfumu kumwamba mu Ufumu wa Mulungu, ndipo posachedwapa Yesuyo adzayambitsa dziko latsopano lolungama ndiponso adzabwezeretsa zinthu mwakale, dziko likhalenso Paradaiso.—Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10.
Tikukhulupirira kuti tsopano mungayankhe mosavuta funso lakuti Kodi Mulungu Alikodi? ndi kutinso mungam’zindikire Mulungu woona. Tikukulimbikitsani kupitirizabe kum’dziŵa bwino, iye limodzi ndi Mwana wake, chifukwa mutawadziŵa mungapeze chimwemwe chosatha m’paradaiso padziko lapansi. Kumbukirani kuti: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munam’tuma.”
[Zithunzi patsamba 9]
Yesu Kristu anatchula Yehova kuti ndiye Mulungu woona yekha