Lingaliro la Baibulo
Ndinu Wofunika Kwambiri kwa Mulungu!
MAYI WINA WACHIKRISTU ANALEMBA KUTI: “KWA NTHAŴI YAITALI M’MOYO WANGA, NDAKHALA NDIKUDZIMVA NGATI WOPANDA NTCHITO. NGAKHALE NDIMAKONDA YEHOVA KWAMBIRI NDIPO NGAKHALE NDIMAYESETSADI KUM’TUMIKIRA, KOMABE NTHAŴI ZONSE NDIMAONA KUTI SIZIKUKWANIRA.”
KODI mukudziŵa wina aliyense amene amavutika ndi maganizo odziona ngati wopanda ntchito? Kodi kapena inunso mumamva choncho nthaŵi zina? Maganizo amenewo si achilendo, ngakhale kwa atumiki okhulupirika a Mulungu. ‘Nthaŵi tikukhala zino n’zoŵaŵitsa,’ ndipo palibe munthu amene sakhudzidwa nazo. Ambiri amanyalanyazidwa kapena kusautsidwa ndi anthu “osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino.” (2 Timoteo 3:1-5) Zimenezo zimapweteketsa mtima kwambiri, ndipo zimapangitsadi munthu kudziona ngati wopanda ntchito.
Nthaŵi zina, anthu amadzimva ngati opanda ntchito chifukwa chakuti amafuna kufikira miyezo yapamwamba kwambiri imene sangaikwanitse. Ndiyeno akalephera kuifikira miyezoyo amayamba kuganiza kuti palibe chilichonse chimene angachite bwino. Kaya pali zifukwa zotani, koma anthu amene amadzimva ngati opanda ntchitowo zimawavuta kukhulupirira kuti Mulungu—kapena wina aliyense—amawakonda. Inde, mpaka amatha kukhulupirira kuti palibe munthu amene angawakonde.
Komatu Yehova Mulungu saganiza choncho ayi! Yehova amatichenjeza kudzera m’Mawu ake, kuti tisamale “machenjera osocheretsa” a Mdani wake, Satana Mdyerekezi. (Aefeso 6:11, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono) Satana amagwiritsa ntchito machenjera ake osocheretsa kuyesa kutiletsa kulambira Mulungu. Choncho, Satana amatisonkhezera kuti tizidzimva ngati opanda ntchito, kuganiza kuti Yehova sangatikonde ngakhale pang’ono. Koma Satana ndi “wabodza”—kapena tingoti, “atate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Ndiye tisam’lole kutinyenga ndi machenjera ake! Yehova amadzinenera yekha m’Baibulo, kutiuza kuti ndife ofunika kwambiri kwa iye.
Kudziona Moyenera Monga Ofunika
Baibulo limatichenjeza kuti kudzilefula kungativulaze. Miyambo 24:10 imati: “Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa.” Tikamangokhalira kuganiza zakuti ndife opanda ntchito tingalefukedi, kufooka ndithu, ndipo tidzakhala osachedwa kudzikhumudwitsa. Dziŵani kuti Satana amadziŵanso zimenezo. N’zovutadi ngati mtima wathu umangolingalira zoti ndife opanda ntchito. Komabe, Satana naye akapezerapo mwayi, vutolo limasanduka mtolo wolemera.
N’chifukwa chake n’kofunika kuti tisadzione ngati opandiratu ntchito. Mtumwi Paulo anati: “Ndiuza munthu aliyense wa inu, kuti asadziyese koposa kumene ayenera kudziyesa; koma aganize modziletsa yekha.” (Aroma 12:3) Baibulo lina limanena motere: “Ndikuuza aliyense wa inu kuti asadzione ngati wolemekezeka kuposa mmene alilidi, koma azidziona moyenera.” (Charles B. Williams) Choncho, lembali likutilimbikitsa kumadziona moyenera. Mbali yoyamba, tiyenera kupeŵa kunyada; ndipo mbali yachiŵiri, sitiyenera kudzinyodola tokha, chifukwa pamene Paulo anati munthu aganize modziletsa, anatanthauza kuti n’kofunika kuti munthu adzione ngati munthu. Inde, mouziridwa ndi Mulungu, Paulo anasonyeza kuti aliyense n’ngwofunika kwambiri kwa Yehova.
Pamene Yesu anati: “Uzikonda mnzako monga udzikonda iwemwini,” anasonyeza kuti munthu ayenera kudziona moyenera kuti ndi wofunika. (Mateyu 22:39) Mawu akuti “monga udzikonda wekha” amasonyeza kuti tiyenera kudzimva kuti ndife ofunika, kapena kuti tiyenera kudzilemekeza. N’zoona kuti timalakwa ndipo timaphophonya. Koma ngati timayesetsa kukondweretsa Mulungu, ngatinso zolakwa zathu zimatikhumudwitsa, ndipo ngati timam’pempha kuti atikhululukire, tingadzionebe kuti ndife ofunika penapake. Mitima yathu ingatinyoze, koma kumbukirani kuti, “Mulungu ali wamkulu woposa mitima yathu.” (1 Yohane 3:20) Mwa mawu ena, Yehova amationa mosiyana ndi mmene ifeyo timadzionera.
Mitima Yosweka, Mzimu Wolapadi
Wamasalmo Davide analemba kuti: “Yehova ali pafupi ndi iwo a mtima wosweka, apulumutsa iwo a mzimu wolapadi.” (Salmo 34:18) Baibulo lotchedwa Matthew Henry’s Commentary on the Whole Bible, pothirira ndemanga pa vesi limeneli, linati: “Ndiwo mkhalidwe wa anthu olungama . . . amasweka mtima ndipo amakhala ndi mzimu wonong’oneza bondo, ndiko kuti, akachita tchimo amadzichepetsa, sadzionanso ngati kanthu; amadzipeputsa okha, ndipo sadzikhulupirira akamachita zinthu.”
Anthu amene ‘asweka mtima’ kapena a “mzimu wolapadi” angaganize kuti Yehova wawatalikira kwambiri ndi kuganizanso kuti Yehova sawaona ngati ofunika ngakhale pang’ono, motero, sangawaganizire. Koma sizili choncho ayi. Mawu a Davide akutilimbikitsa, chifukwa akutanthauza kuti Yehova sasiya anthu ‘odziona ngati opanda ntchitowo.’ Mulungu wathu wachifundo amadziŵa kuti panthaŵi zoterozo mpamene timam’funa kwambiri, ndipo nayenso amatiyandikira.
Taganizani za chitsanzo ichi. Zaka zingapo zapitazo, mayi wina anathamangira kuchipatala ndi mwana wake amene anali kukhosomola kwambiri. Pamene madokotala anam’pima mnyamatayo, anauza mayiyo kuti aganiza zoti am’goneke mwanayo m’chipatala usiku womwewo. Nanga mayiyo anagona kuti? Anagona pampando m’chipatala momwemo, pafupi ndi bedi la mwana wakeyo. Kamnyamata kake kanali kudwala, ndipo mayiyo anafunikira kukhala nako pafupi. Ndiye poti tinapangidwa m’chifanizo cha Atate wathu wachikondi wakumwamba, ndithudi iyeyo amaposa kwambiri zimene mayiyo anachita! (Genesis 1:26; Yesaya 49:15) Mawu ogwira mtima a pa Salmo 34:18 akutilonjeza kuti ngati ‘tasweka mtima,’ Yehova monga kholo lachikondi, ‘amakhala pafupi’—amayang’anitsitsa nthaŵi zonse, amakhalanso tcheru, ndi wokonzekera kuthandiza.—Salmo 147:1, 3.
“Mupambana Mpheta Zambiri”
Yesu adakali kuchita utumiki wake padziko lapansi, anali kuvumbula kwambiri za maganizo a Yehova ndi mmenenso amaonera zinthu, komanso ndi mmene Yehova amaonera atumiki Ake a padziko lapansi. Yesu anawauza ophunzira ake kangapo kuti iwowo anali ofunika kwambiri kwa Yehova.—Mateyu 6:26; 12:12.
Mwachitsanzo, Yesu, pochitira fanizo kufunika kwa aliyense wa ophunzira ake, anati: “Kodi mpheta ziŵiri sizigulidwa kakhobiri? Ndipo imodzi ya izo siigwa pansi popanda Atate wanu [kudziŵa, NW]: komatu inu, matsitsi onse a m’mutu mwanu aŵerengedwa. Chifukwa chake musamawopa; inu mupambana mpheta zambiri.” (Mateyu 10:29-31) Taganizirani mmene mawu amenewo analimbikitsira omvetsera a Yesu a m’zaka za zana loyamba.
Pa mbalame zonse zodyedwa, mpheta ndizo zinali zotsika mtengo kwambiri. Timbalame timeneti kaŵirikaŵiri tinali kukudzulidwa, kuyanikidwa pampani, ndiyeno n’kutiwamba ngati nyama yozonga. N’zosakayikitsa kuti Yesu anali ataonapo akazi ena osauka akuŵerengera ndalama zawo pamsika kuti aone kuti angagule mpheta zingati. Mbalame zimenezo zinali zotsika mtengo kwambiri moti munthu akanatha kugula mpheta ziŵiri ndi kakhobiri (monga ka assarion, kosakwana 5 tambala).
Nthaŵi inanso Yesu anadzanena fanizo lomweli—koma m’njira ina. Malinga ndi Luka 12:6, Yesu anati: “Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiŵiri?” Tangoganizani. Munthu akanatha kugula timpheta tiŵiri ndi kakhobiri chabe. Koma ngati akanafuna kupereka timakobiri tiŵiri, akanalandira mpheta zisanu osati zinayi. Mbalame yachisanuyo inali yabasela, yopanda mtengo. Ndiyeno Yesu anati: “Koma palibe imodzi ya izo iiŵalika pamaso pa Mulungu [ngakhale imodzi imene yangowonjezeredwa ngati baselayo].” Potanthauzira fanizolo, Yesu anati: “Muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.” (Luka 12:7) Tikukhulupirira kuti mawu amenewo anawalimbikitsa omvetsera ake kwambiri!
Kodi mukulimvetsetsa fanizo la Yesu lotonthoza mtimali? Ngati Yehova amaona kuti ngakhale timbalame ting’onoting’ono n’tofunika kwambiri kwa iye, nanga kuli bwanji ndi atumiki ake a padziko lapansi! Yehova amatizindikira ngakhale tili m’chigulu. Tonsefe Yehova amationa monga ofunika kwambiri kwa iye motero amayang’ana chilichonse cha ife—tsitsi lathu lenilenili, amaliŵerenga palokha palokha.
Komatu Satana azipitirizabe kuchita “machenjerero” ake—monga kutipangitsa kudzimva ngati opanda ntchito—kuti atipangitse kuleka kutumikira Yehova. Koma musalole kuti Satana akugonjetseni! Kumbukirani mkazi wachikristu amene mawu ake tawatchula pachiyambi paja. Nkhani ina ya m’magazini ya Nsanja ya Olonda ndi imene inam’thandiza, inachenjeza za Satana kuti amayesayesa kutinyenga.a Mlongoyo anati: “Inetu Sindinali kudziŵa kuti Satana amagwiritsa ntchito malingaliro anga omwe kuti andilefule. Poti ndadziŵa zimenezi, tsopano ndikhala ndi mphamvu zotha kulimbana nawo maganizo ameneŵa. Tsopano ndizilimbana nacho chi Satanachi chikamandiukira, ndili ndi chidaliro kwambiri.”
Yehova ‘amazindikira zonse.’ (1 Yohane 3:20) Inde, akudziŵa zonse zimene tikuvutika nazo tsopano lino. Amadziŵanso zimene zinatichitikira kale, zimene mwina zinatipangitsa kuyamba kudzinyoza tokha. Kumbukirani kuti, chimene chili chofunika kwambiri ndimo mmene Yehova amationera basi! Kaya timadziona ngati osakondeka kapena kudziona ngati opanda ntchito, Yehova amatitsimikizira kuti tonsefe ndife ofunika kwambiri kwa iye. Tiyeni tikhulupirire zimene Yehova amatiuza, chifukwa iye n’ngwosiyana ndi Mdani wake, chifukwa Mulungu ‘sanama.’—Tito 1:2.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Ndinu Wamtengo Wapatali Pamaso pa Mulungu!” mu Nsanja ya Olonda ya April 1, 1995, masamba 10-15.
[Mawu Otsindika patsamba 12]
Yehova ali ngati kholo lachikondi, amakhala pafupi ndi anthu okhumudwa
[Zithunzi patsamba 13]
Ngati Yehova samaiŵala mpheta, angakuiŵaleni bwanji inuyo?
[Mawu a Chithunzi]
Illustrated Natural History
Lydekker