Kodi Ndani Adzapulumutse Mapiri?
KWA masiku anayi m’chaka cha 2002, mu mzinda wa Bishkek ku Kyrgyzstan (pakati pa Asia) munachitika msonkhano woganizira za mapiri padziko lonse lapansi. Unali msonkhano woyamba wa mayiko osiyanasiyana womwe cholinga chake chinali kukambirana zinthu zokhudza mapiri. Okonza msonkhanowo anali ndi cholinga choti chaka cha 2002 chikhale “chiyambi cha nyengo yatsopano, nyengo yozindikira kufunika kwa mapiri.”
Anthu amene analipo pamsonkhanowo anagwirizana “Mfundo za ku Bishkek Zokhudza Mapiri,” zomwe zili ndi malangizo kwa aliyense amene akufuna kuteteza mapiri. Cholinga chake ndicho “kusintha miyoyo ya anthu a m’mapiri kuti ikhale yabwino kuposa kale, kuteteza malo ndi zachilengedwe za m’mapiri ndi kugwiritsa ntchito mwanzeru zinthu zachilengedwe zopezeka m’mapiri.”
Pali zinthu zothandiza zomwe zachitika zogwirizana ndi mfundo zimenezi. Padziko lonse lapansi pali malo oteteza zachilengedwe omwe amateteza malo okongola kwambiri ndiponso malo omwe ali ndi zachilengedwe zambirimbiri zosiyanasiyana. M’madera ambiri a padziko lapansi, mabungwe oteteza zachilengedwe ayesetsa ndithu kuchepetsa kuwonongeka kwa chilengedwe. Mfundo imodzi yomwe anagwirizana pa msonkhano wa ku Bishkek ndi yoti achotse zinyalala zanyukiliya zomwe zinatayidwa m’mapiri a ku Kyrgyzstan. Zinyalala zapoizoni zimenezi zinatsala pang’ono kuwononga madzi omwe anthu 20 pa anthu 100 alionse a kudera lapakati pa Asia amamwa.
Komabe, mavuto akadalipo pa ntchito yoteteza mapiri a padziko lapansili. Mwachitsanzo, mu 1995 akuluakulu a boma la Canada anakhazikitsa “Malamulo Okhudza Kadulidwe ka Mitengo” kuti ateteze nkhalango yomwe yatsala kuchigawo cha British Columbia. Koma atafufuza pambuyo pake anapeza kuti makampani odula mitengo nthawi zambiri satsatira malamulo amenewa ndipo akupitirizabe kudula mitengo yonse pamalo, ngakhale pamalo otsetsereka kwambiri. Malamulowa anasinthidwa pang’ono mu 1997, chifukwa anthu ochita malonda a mitengo anadandaula kuti anali okhwima kwambiri.
Si nkhani zachuma zokha zomwe zimalepheretsa kuteteza zachilengedwe. Mfundo yomaliza pa msonkhano wa ku Bishkek inavomereza kuti nkhondo, umphawi, ndi njala, zikuwonjezera kuti zachilengedwe za m’mapiri zipitirizebe kuwonongeka. Mapiri, limodzi ndi mbali zina zonse za dzikoli, zipitirizabe kuwonongeka mpaka mavuto onsewa, amene amayambitsa kuwonongeka kwa zachilengedwe, adzathe.
Mulungu Amadera Nkhawa Chilengedwe Chake
Ngakhale zinthu zikuoneka zoipa chonchi, tili ndi chifukwa chokhalira ndi chiyembekezo. Mulungu Wamphamvuyonse sikuti alibe nazo ntchito zomwe zikuchitikira chilengedwe chake. Baibulo limafotokoza kuti ‘chuma cha m’mapiri ndi chake.’ (Salmo 95:4) Iye amaderanso nkhawa zinyama za m’mapiri. Malinga ndi lemba la Salmo 50:10, 11, Yehova anati: “Zamoyo zonse za kuthengo ndi zanga, ndi ng’ombe za pa mapiri zikwi. Ndidziwa mbalame zonse za m’mapiri: ndipo nyama za kuthengo zili ndi Ine.”
Kodi Mulungu ali ndi njira yopulumutsira chilengedwe cha padziko lapansi chomwe chili pamavutochi? Inde, ali nayo. Baibulo limati Mulungu wakhazikitsa “ufumu woti sudzawonongeka ku nthawi zonse.” (Danieli 2:44) Yesu Kristu, Wolamulira woikidwa wa ufumu wakumwamba umenewu, ali ndi chidwi kwambiri ndi dziko lapansi ndi anthu amene amakhalamo. (Miyambo 8:31) Ulamuliro wake udzakhazikitsa mtendere padziko lapansi, udzathetsa kupanda chilungamo konse, ndipo udzakonza zinthu zomwe zawonongeka padziko lapansili.—Chivumbulutso 11:18.
Ngati mukufuna kuti zimenezi zidzachitike, mosakayikira mupitiriza kupemphera kuti ‘Ufumu wa Mulungu udze.’ (Mateyu 6:9, 10) Mapemphero oterowo sikuti sadzayankhidwa. Ufumu wa Mulungu posachedwapa udzathetsa kupanda chilungamo ndipo udzakonza zinthu zomwe zawonongeka padzikoli. Zimenezi zikadzachitika, mapiri mophiphiritsira ‘adzafuula pamodzi mokondwera.’—Salmo 98:8.