Zimene Baibulo Limanena
Kodi Tikamavutika Ndiye Kuti Mulungu Akutilanga?
Mzimayi wina wa zaka 55 atam’peza ndi matenda akhansa, anati: “Ndikuona kuti Mulungu akundilanga.” Mayiyu atakumbukira tchimo limene anachita m’mbuyomo, ananenanso kuti: “Imeneyi ndi njira yondidziwitsira kuti ndinachimwa.”
ANTHU ambiri akamavutika amaganiza kuti Mulungu akuwalanga chifukwa cha tchimo limene anachita m’mbuyomo. Akakumana ndi mavuto ambiri, iwo amadandaula kuti: “N’chifukwa chiyani zimenezi zikundichitikira? Kodi ndalakwanji?” Kodi tikamavutika tiyenera kuganiza kuti Mulungu akutilanga? Kodi ndi Mulungu amene amachititsa kuti tizivutika?
Olambira Mulungu Okhulupirika Ankavutikanso
Taganizirani zimene Baibulo limanena pankhani ya Yobu. Limafotokoza kuti chuma chake chinatha mwadzidzidzi. Kenako, ana ake onse khumi anaphedwa ndi mphepo yamkutho. Posakhalitsa, Yobu weniweniyo anadwala matenda oipa kwambiri, ofoola thupi. (Yobu 1:13-19; 2:7, 8) Mavuto amenewa anachititsa Yobu kunena kuti: “Dzanja la Mulungu landikhudza.” (Yobu 19:21) Ndipo monga amachitira anthu ambiri, Yobu anaganiza kuti Mulungu ndi amene akuchititsa mavutowo.
Komabe, Baibulo limasonyeza kuti Yobu asanayambe kuvutika, Mulungu ananena kuti Yobu anali “munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.” (Yobu 1:8) Popeza mawu amenewa akusonyeza kuti Mulungu ankamukonda Yobu, n’zoonekeratu kuti si Mulungu amene ankachititsa kuti azivutika.
Ndipotu m’Baibulo muli nkhani zambiri za anthu abwino amene anakumana ndi mavuto. Mwachitsanzo, Yosefe anakhala zaka pafupifupi ziwiri m’ndende popanda chifukwa, ngakhale kuti anali mtumiki wokhulupirika wa Mulungu. (Genesis 39:10-20; 40:15) Mkhristu wokhulupirika Timoteyo ‘ankadwaladwala.’ (1 Timoteyo 5:23) Ndiponso Yesu Khristu, amene sanachitepo tchimo, anachitidwa nkhanza zedi mpaka anaphedwa imfa yopweteka kwambiri. (1 Petulo 2:21-24) Choncho, n’kulakwitsa kuganiza kuti tikamavutika ndiye kuti Mulungu akutilanga. Komano ngati si Mulungu amene amachititsa kuti tizivutika, ndiye ndi ndani amene amachititsa zimenezi?
Zimene Zimachititsa Kuti Tizivutika
Baibulo limasonyeza kuti Satana Mdyerekezi ndi amene anachititsa kuti Yobu avutike. (Yobu 1:7-12; 2:3-8) Limasonyezanso kuti Satana yemweyo ndi amene amachititsa kuti tizivutika masiku ano, chifukwa limati: “Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ali ndi mkwiyo waukulu, podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chivumbulutso 12:12) Popeza Satana ndi “wolamulira wa dzikoli,” iye amalimbikitsa anthu kuchita zinthu zoipa zimene zimabweretsa mavuto osaneneka.—Yohane 12:31; Salmo 37:12, 14.a
Komabe, tisamafulumire kunena kuti Mdyerekezi ndi amene amachititsa mavuto onse amene timakumana nawo. Popeza kuti tinabadwa ochimwa komanso ndife opanda ungwiro, nthawi zambiri timachita zinthu mosaganiza bwino ndipo zimenezi zingatibweretsere mavuto. (Salmo 51:5; Aroma 5:12) Mwachitsanzo, taganizirani munthu amene mwadala sadya bwino komanso sapuma mokwanira. Ngati wadwala chifukwa cha zimenezi, kodi tingati ndi Mdyerekezi amene wachititsa? Ayi, zochita zake n’zimene zamubweretsera mavuto. (Agalatiya 6:7) Zimenezi zimafanana ndi zomwe mwambi wa m’Baibulo umanena kuti: “Utsiru wa munthu ukhotetsa njira yake.”—Miyambo 19:3.
Komanso tiyenera kudziwa kuti mavuto ambiriwa amachitika chifukwa cha ‘zotigwera m’nthawi yake.’ (Mlaliki 9:11) Taganizirani za munthu amene mvula yamkutho yamupezerera. Akhoza kunyowa pang’ono kapena kwambiri malinga ndi pamene mvulayo yamupezera. N’chimodzimodzinso ndi ‘m’masiku otsiriza’ ano, zinthu zoipa sizingachedwe kusanduka mavuto aakulu. (2 Timoteyo 3:1-5) Nthawi zambiri, mmene zinthu zimenezi zimatikhudzira zimadalira nthawi ndiponso mmene zinthu zilili, ndipo zimenezi sitingathe kuzilamulira. Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti tizivutika mpaka kalekale?
Mavuto Onse Atha Posachedwapa
N’zosangalatsa kuti Yehova Mulungu achotsa mavuto onse posachedwa. (Yesaya 25:8; Chivumbulutso 1:3; 21:3, 4) Pakalipano, iye akusonyeza kuti amatikonda chifukwa amatipatsa ‘malangizo’ ndi “chitonthozo cha m’Malemba” kuti tithe kupirira mavuto amene tikukumana nawo poyembekezera moyo wabwino wa m’tsogolo. (Aroma 15:4; 1 Petulo 5:7) Panthawi imeneyi, anthu onse amene Mulungu amawaona kuti ndi abwino adzasangalala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano, lopanda mavuto alionse.—Salmo 37:29, 37.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Zimene Baibulo Limanena: Kodi Satana Ndani? Kodi Alikodi?” mu Galamukani! ya February 2007.
KODI MWAGANIZIRAPO IZI?
◼ Kodi ndi ochimwa okha amene amavutika?—Yobu 1:8.
◼ Kodi Mdyerekezi ndi amene amachititsa mavuto onse?—Agalatiya 6:7.
◼ Kodi mavutowa apitirirabe mpaka kalekale?—Chivumbulutso 21:3, 4.
[Mawu Otsindika patsamba 29]
‘Yense angoona zom’gwera m’nthawi yake.’—Mlaliki 9:11.