Muziyamikira Mphatso Zimene Muli Nazo
THUPI la munthu limachita zinthu zosiyanasiyana zimene nyama sizingakwanitse kuchita. Chinthu chimodzi chomwe chimatithandiza kuti tizichita zinthu zambiri ndi chakuti timatha kuyenda ndi miyendo iwiri. Zimenezi zimathandiza kuti tizitha kuona zinthu zambiri komanso kuti manja athu azigwira ntchito zosiyanasiyana. Tikanakhala kuti anthufe timayenda ndi miyendo inayi, bwenzi tikulephera kukwanitsa kuchita zinthu zambiri zimene timachita.
Anthufe tili ndi manja, makutu, maso ndiponso ubongo, zimene zimagwira ntchito modabwitsa kwambiri. Tiyeni tikambirane mmene ziwalo zimenezi zimagwirira ntchito.
Dzanja
Manja athu amachita zinthu zogometsa kwambiri. Timatha kugwiritsa ntchito manja tikafuna kusoka, kuwaza nkhuni, kujambula chithunzi kapena kuimba piyano. Manja athu amatithandizanso kuzindikira mwachangu zinthu zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, kungokhudza chinthu popanda kuchiona timadziwa mosavuta kuti chinthucho ndi ubweya, pepala, chikopa, chitsulo, madzi kapena mtengo. Choncho, manja athu amatithandiza kuphunzira zinthu zatsopano. Timathanso kugwiritsa ntchito manja popatsana moni komanso mwamuna ndi mkazi amatha kugwirana manja posonyeza kuti amakondana.
Kodi chimachititsa n’chiyani kuti manja athu azitha kuchita zinthu zosiyanasiyana zimene tatchulazi? Pali zifukwa zambiri, koma tingokambirana zinayi zokha.
1. Manja athu onse awiri ali ndi mafupa oposa 50. Amenewa ndi mafupa ambiri zedi tikaganizira kuti thupi lonse lili ndi mafupa 206. Mafupa amenewa analumikizidwa mwaluso kwambiri moti amachititsa kuti dzanja lathu lizichita zinthu zosiyanasiyana mosavuta.
2. Dzanja lathu lili ndi chala chamanthu, chimene chili pamalo osiyana ndi zala zina. Zimenezi zimachititsa kuti chala chimenechi chikhale champhamvu komanso chizitha kupindika mosavuta.
3. Dzanja lathu lili ndi minofu yamitundu itatu imene imathandiza kuti dzanjalo lizipindika mosavuta. Mitundu iwiri yamphamvu kwambiri ili pamene panalumikizana chikhato ndi mkono. Kuti minofu imeneyi izitha kuyendetsa zala, inalumikizidwa ku timafupa ta zalazo. Ngati minofu yonseyi ikanapangidwa kuti ikhale yam’manja, bwenzi dzanjalo litangodzaza ndi minofu yokhayokha moti zikanakhala zovuta kuligwiritsa ntchito. Minofu ya mtundu wachitatu ndi yocheperapo ndipo imapezeka m’manja. Minofu imeneyi ndi imene imathandiza kuti zala zizipindika mosavuta.
4. Zala zathu zimatithandiza kuzindikira zinthu mwamsanga chifukwa kunsonga kwenikweni kwa zala zathu, kuli tinthu tambirimbiri (pafupifupi 2,500 pamalo okwana sikweya sentimita imodzi), timene timathandiza kuti tikakhudza chinthu tizidziwa mwamsanga kuti takhudza chinachake. Tinthu timeneti tilipo tamitundu yosiyanasiyana ndipo tili ndi ntchito zosiyanasiyananso. Tina timathandiza kuti munthu akagwira chinthu, azidziwa ngati chinthucho n’chotentha kapena chozizira, n’chonyowa kapena chouma, n’cholimba kapena chofewa, ndi zina zotero. Chifukwa cha zimenezi, zala zathu zimatithandiza kuzindikira zinthu mwamsanga kuposa chipangizo chilichonse chimene tingathe kugwiritsa ntchito.
Khutu
Ngakhale kuti nyama zina zikhoza kumva phokoso limene anthu sangamve, khutu lathu limamva zinthu zambiri kuposa khutu la nyama. Akatswiri amanena kuti zimenezi zili choncho chifukwa cha mmene khutulo ndi ubongo wa munthu zimagwirira ntchito pamodzi. Makutu athu amatithandiza kudziwa ngati munthu akulankhula mokweza kapena motsitsa komanso ngati akulankhula mwaukali kapena modekha. Amatithandizanso kudziwa kuti phokoso limene tikumvalo likuchokera kuti komanso n’kutali bwanji. Phokoso limayezedwa m’ma hertz (hedzi) ndipo munthu amatha kumva phokoso la mahedzi oyambira pa 20 mpaka 20,000. Munthu amamva kwambiri phokoso la mahedzi oyambira 1,000 mpaka 5,000. Komanso amatha kumva ngakhale phokoso litasintha pang’ono chabe, mwina kuchoka pa 440 hedzi kufika pa 441 hedzi.
Khutu lomwe lili bwinobwino limatha kutithandiza kuzindikira kusintha kwa phokoso ngakhale kochepa kwambiri. Malinga ndi zotsatira zakafukufuku amene anachitika payunivesite ina, “khutu la munthu lili m’gulu la zinthu zimene zimazindikira msangamsanga kusintha kwa phokoso. . . . Khutu lathu likanakhala kuti silitithandiza kuzindikira kusintha kwa phokoso, si bwenzi tikusiyanitsa phokoso la zinthu zosiyanasiyana.”
Phokoso likalowa m’makutu athu limafikira pa kanthu kenakake kokhala ngati kansalu kamene kamanjenjemera. Kenako phokosolo limatengedwa ndi timafupa tinatake titatu n’kupita mkati mwa khutu. Timafupa timeneti timathandiza kuti phokosoli likule. Nanga bwanji ngati m’khutu mwanu mutalowa phokoso lalikulu mwadzidzidzi? Mkati mwa khutu muli minofu inayake imene imagwira timafupa tija kuti phokosolo lichepe. Komabe ngati phokosolo litapitirira kwa nthawi yaitali, likhoza kuwononga makutu athu. Choncho, muziyesetsa kusamalira makutu anu, omwe ‘anapangidwa modabwitsa’ ndi Mlengi wanu.—Salimo 139:14.
Makutu athu amatithandizanso kudziwa kumene phokoso likuchokera. Pali zinthu zingapo zimene zimachititsa kuti zimenezi zitheke. Zina mwa zimenezi ndi zinthu monga mmene khutu lakunja linapangidwira, malo amene makutu awiriwo ali, komanso zimene ubongo wathu umachita ukalandira uthenga kuchokera ku makutu. Mwachitsanzo, phokoso likalowa m’khutu limodzi mofulumirirapo pang’ono kapena mocheperapo mphamvu pang’ono kusiyana ndi khutu lina, ubongo wanu umapanga masamu n’kudziwa kumene phokosolo likuchokera. Zikatero ubongo umauza maso anu kuti ayang’ane kumene phokosolo likuchokera.
Masamu onsewa amachitika inu musakudziwa. Koma mutati muzipanga masamu amenewa nokha mungafunike kukhala katswiri kwambiri pa masamu komanso mungafunike kupanga masamuwo mwachangu kwambiri kuposa kuthwanima kwa ching’aning’ani. Ngati munthu atapanga makina amene angayeseko pang’ono kufika pa zimene khutu limachita, munthu ameneyo angapatsidwe ulemu waukulu. Komabe n’zokhumudwitsa kuti anthu ambiri salemekeza Mulungu chifukwa cha zinthu zodabwitsa zimene iye anapanga.—Aroma 1:20.
Diso
Akatswiri ena amanena kuti maso amathandiza munthu kudziwa zinthu zambiri. Akuti mwina 80 peresenti ya zinthu zonse zimene munthu amadziwa, amazidziwa chifukwa chakuti anaziona. Mothandizana ndi ubongo, maso athu amatithandiza kuona zinthu zamitundu yosiyanasiyana, kuona zinthu zimene zikuyenda komanso kuona mbali zake zosiyanasiyana za chinthu pa nthawi imodzi. Timathanso kuona zinthu ngakhale mumdima.
Kodi zimatheka bwanji kuti munthu azitha kuona mumdima? Kuwala kukachepa, mwana wa diso amatamuka (kuchoka pa mamilimita 1.5 kufika pa mamilimita 8), ndipo zimenezi zimathandiza kuti pakhale malo aakulu oti kuwala kuzilowa. Kenako kuwalako kumadutsa pa kanthu kenakake kamene kamakhala ngati galasi. Galasi limeneli limatumiza kuwalako kumalo enaake mkati mwa diso, kumene kuli maselo ambiri olandirira kuwala. Galasili limachititsa kuti mphamvu ya kuwala kumene kukufika pa maselowo iwonjezereke maulendo 100,000. N’chifukwa chake n’zoopsa kwambiri kuyang’ana dzuwa popanda kuvala magalasi odziteteza chifukwa galasi la m’masolo limawonjezera kwambiri kuwala kochokera kudzuwako. Ndipo zimenezi zikhoza kuwononga maso anu.
Maselo amene amalandira mphamvu ya kuwala alipo a mitundu iwiri. Mtundu umodzi wa maselowa (omwe alipo 6 miliyoni) umathandiza kuti tizizindikira mitundu yosiyanasiyana komanso kuti tizitha kuona bwinobwino tikakhala pamalo owala kwambiri. Ndipo maselo enawo (omwe alipo pakati pa 120 miliyoni ndi 140 miliyoni) ndi amphamvu kwambiri kuposa oyambawo ndipo amathandiza kuti tizitha kuona tikakhala mumdima. Selo imodzi yokha ikhoza kuzindikira ngakhale kuwala kochepetsetsa.
Chinthu chinanso chimene chimathandiza kwambiri kuti tizitha kuona mumdima ndi minyewa imene inalumikizidwa ku maselo otithandiza kuona. Malinga ndi zimene bungwe lina la ku America loona za maso linanena, munthu akachoka pamalo owala n’kupita pamdima, minyewa imeneyi “imasintha mofulumira kwambiri, ndipo zimenezi zimachititsa kuti pambuyo pa kanthawi pang’ono munthuyo aziona bwino kwambiri, mwina kuwirikiza ka 10. Zimenezi zili ngati kukhala ndi mafilimu a mitundu iwiri mu kamera imodzi, ina yojambula bwino pamdima, ndipo ina yojambula bwino pamalo owala.”
Akatswiri akamapanga zinthu monga makamera ndi makompyuta, nthawi zambiri amapanganso mapulogalamu oyenererana ndi zinthuzo. Koma mmene zinthuzo ndi mapulogalamuwo zimagwirira ntchito pamodzi, sizingafanane ngakhale pang’ono ndi mmene ziwalo zathu monga manja, makutu, ndi maso, zimagwirira ntchito. Ndiyeno dzifunseni kuti, ‘Kodi n’zomveka kuti manja, makutu komanso maso athu, zomwe zimagwira ntchito mogometsa kwambiri, zingokhalapo zokha?’ Zimene mtumiki wakale wa Mulungu,Yobu, ankadziwa zokhudza thupi lathu n’zochepa kwambiri kusiyana ndi zimene ifeyo timadziwa masiku ano. Komabe, iye ananena kuti: “Manja anu omwe ndi amene anandiumba.”—Yobu 10:8.
Ubongo
Ubongo wathu umachita zinthu zodabwitsa kwambiri. Mwachitsanzo, umati ukalandira mauthenga kuchokera ku ziwalo zina, m’kanthawi kochepa chabe umatanthauzira mauthengawo. Ndiponso umagwirizanitsa mauthenga amene ukulandira ndi zinthu zimene ukudziwa kale. N’chifukwa chake munthu amati akangomva kafungo kenakake, nthawi yomweyo amakumbukira zinthu zinazake zimene zinachitika kalekale. Ndipo mukangoona mbali yochepa chabe ya chinthu chinachake chimene munachionapo, mumatha kuona m’maganizo mwanu chinthu chonsecho. Mwachitsanzo, kungoona mchira wa mphaka wanu, m’maganizo anu mukhoza kumuona yense.
Komabe munthu akamabadwa, sikuti ubongo wake umakhala ndi zithunzi za zinthu monga amphaka, fungo la maluwa, kapenanso phokoso la madzi. Ubongo wanu umachita kuziphunzira zinthu zimenezi. Zimenezi ndi zoona tikaganizira za anthu amene anabadwa osaona, koma pambuyo pochitidwa opaleshoni anayamba kuona. Chifukwa chakuti anali asanaonepo chilichonse, ubongo wawo umafunika kuphunzira zinthu zosiyanasiyana zimene maso awo ayamba kuona. Kodi anthu amenewa zimawathera bwanji?
M’kupita kwa nthawi anthu amenewa amayamba kudziwa mitundu yosiyanasiyana ya zinthu, kuona bwinobwino chinthu chimene chikuyenda komanso zinthu zina. Koma pakapitanso nthawi, zinthu zimasintha. Ana, makamaka aang’ono kwambiri amapitiriza kuphunzira zinthu mofulumira, pamene anthu akuluakulu amavutika. Anthu akuluakulu amalephera ngakhale kuzindikira nkhope za anthu. Ndipo chomvetsa chisoni n’chakuti, anthu achikulire amene ayamba kuona, amangosangalala m’kanthawi kochepa, koma kenako amakhumudwa ndipo amasokonezeka chifukwa cha zinthu zimene akuona. Malinga ndi zimene bungwe lina la ku America loona za maso linanena, “nthawi zambiri zimenezi zimachititsa kuti munthu ayambe kudwala matenda oopsa a maganizo.”
Mfundo zimenezi zikutithandiza kumvetsa kuti zimene Yesu Khristu anachita pochiritsa anthu zinali zodabwitsa kwambiri. Anthu osamva komanso osaona amene iye anawathandiza anayamba kuona ndi kumva bwinobwino. Koma si zokhazo. Iwo ankathanso kusiyanitsa phokoso losiyanasiyana limene ankamva komanso zinthu zosiyanasiyana zimene ankaona. Nawonso anthu osalankhula anayamba kulankhula bwinobwino, zomwe zinali zachilendo kwambiri, makamaka kwa anthu omwe anabadwa osalankhula. (Mateyu 15:30; Maliko 8:22-25; Luka 7:21, 22) Ndipo tikukhulupirira kuti palibe munthu wosaona ngakhale mmodzi pa anthu amene Yesu anawachiritsa yemwe anayamba kuvutika maganizo pambuyo pake. Ndipotu, munthu wina amene anachiritsidwa ndi Yesu, anaikira kumbuyo Yesuyo molimba mtima. Iye anauza atsogoleri a chipembedzo amene ankadana ndi Yesu kuti: “Sizinamveke n’kale lonse kuti wina watsegula maso a munthu amene anabadwa wakhungu. Munthu uyu akanapanda kuchokera kwa Mulungu, sakanatha kuchita kanthu.”—Yohane 9:1-38.
M’nkhani yotsatira, tikambirana za makhalidwe amene anthufe timasonyeza, monga kulimba mtima ndi chikondi. Kodi munayamba mwadabwapo kuti, ‘N’chifukwa chiyani anthu amatha kusonyeza makhalidwe amenewa?’ Kunena zoona, makhalidwe amenewa amasonyeza kuti anthu sanachite kusintha kuchokera ku zamoyo zina, ngati mmene anthu ena amanenera.
[Bokosi patsamba 7]
UBONGO WATHU NDI WODABWITSA KWAMBIRI
Kodi ubongo wanu umatani kuti muzitha kumva, kuona komanso kununkhiza zinthu? Asayansi samvetsa zimene zimachitika. Katswiri wina wa sayansi, dzina lake Gerald L. Schroeder, anati: “Mutati mupatsidwe mpata woona zimene zikuchitika mu ubongo wanu, simungathe kuona chimene chikuchititsa kuti muwerenge nkhaniyi.”
Iye analembanso kuti: “Zinthu zimene tapeza zokhudza ubongo, zimene m’mbuyomo tinali tisanaziganizirepo, zikusonyeza kuti n’zosatheka kuti zinthu zamoyo zingokhalapo mwangozi. Darwin akanadziwa nzeru zimene zinafunika kuti pakhale zinthu zamoyo, ndikukhulupirira kuti sakananena kuti zamoyo zinachita kusintha.”
[Zithunzi patsamba 5]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Minofu imene imayendetsa dzanja
Pamene chala chamanthu chinalumikizidwa
Timafupa ta kuzala
Kansonga ka chala kakakhudza kanthu timadziwa mwamsanga
[Chithunzi]
Kodi chimachititsa n’chiyani kuti manja athu azitha kuchita zinthu zosiyanasiyana?
[Chithunzi patsamba 7]
Ubongo ukalandira mauthenga, umatanthauzira mauthengawo, ndiponso umawagwirizanitsa ndi zinthu zimene ukudziwa kale