NKHANI YA PACHIKUTO
Kodi Mungatani Kuti Musakhale Wokonda Ndalama?
ANTHU ambiri amanena kuti chilichonse ndi ndalama. Zimenezi n’zoona chifukwa kuti munthu agule chakudya, zovala komanso kuti alipire lendi kapena kugula nyumba, zimadalira ndalama. Katswiri wina wa zachuma anati: “Ndalama zimathandiza kuti zinthu ziziyenda bwino m’dziko. Zitakhala kuti ndalama kulibe, zinthu zikhoza kusokonekera kwambiri moti mwezi sungathe anthu asanayambe kumenyana.”
Komabe pali zinthu zina zomwe sitingagule ndi ndalama. Wolemba ndakatulo wina wa ku Norway, dzina lake Arne Garborg, analemba kuti: “Ukhoza kugula chakudya, koma osati chilakolako chofuna kudya. Ukhoza kugula mankhwala, koma osati moyo wathanzi. Ukhoza kugula bedi labwino, koma sungagule tulo. Ukhoza kupita kusukulu yapamwamba, koma n’kukhala wopanda nzeru. Ukhoza kukhala wotchuka, koma n’kukhala wopanda khalidwe. Ukhoza kugula zinthu zapamwamba, koma sungagule chikondi. Ukhoza kuchita zinthu zambiri zosangalatsa, koma n’kukhala wosasangalala. Ukhoza kudziwana ndi anthu ambiri, n’kukhala wopanda anzako enieni. Ukhoza kukhala ndi antchito, koma sungawapangitse kuti akhale okhulupirika.”
Munthu amene sakonda ndalama amangoona kuti ndalamayo imamuthandiza kupeza zomwe akufuna. Cholinga chake chachikulu sichikhala kupeza ndalama koma amayesetsa kukhala wokhutira ndi zomwe ali nazo. Baibulo limanena kuti: “Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse, ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena . . . adzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.”—1 Timoteyo 6:10.
Choncho munthu amakumana ndi mavuto chifukwa chokonda ndalama, koma sikuti ndalamazo pazokha zili ndi vuto. Nthawi zambiri mabanja komanso anthu omwe amagwirizana kwambiri amasemphana maganizo pa nkhani za ndalama. Taonani zitsanzo zotsatirazi.
Daniela anati: “Ndinkaona kuti Thomas ndi mnzanga wapamtima komanso wokhulupirika. Poyamba Thomas anali mnzanga wa ponda apa m’pondepo, koma zinthu zinasokonekera atagula galimoto yanga. Pamene ndinkamugulitsa galimotoyo, sindinkadziwa kuti inali ndi vuto. Tinasainirana kuti agula galimotoyo ndipo ananena kuti adzaona zochita ngati ataipeza ndi vuto. Patangotha miyezi itatu, galimoto ija inawonongeka. Thomas anaona kuti ndinamuchita chinyengo ndipo anakwiya n’kundiuza kuti ndimubwezere ndalama zake. Nditayesa kukambirana naye, anandilalatira koopsa. Nkhaniyi itakula, Thomas anasinthiratu ndipo sanalinso munthu wabwino ngati mmene ndinkamudziwira.”
Esin anati: “Nesrim ndi mchemwali wanga ndipo tinabadwa awiri m’banja mwathu. Poyamba tinkagwirizana kwambiri ndipo sindinkaganiza kuti tingayambane pa nkhani za ndalama. Koma ndi zomwe zinachitikadi. Makolo athu atamwalira, anatisiyira ndalama ndipo asanamwalire ananena kuti tidzagawane ndalamazo mofanana. Koma m’bale wangayo anakakamira kuti atenge ndalama zambiri kuposa ineyo. Ataona kuti sindinagwirizane nazo, anakwiya kwambiri ndipo anayamba kundiopseza. Panopa zinthu zinasokonekera ndipo sitigwirizananso.”
NDALAMA ZIMACHITITSA KUTI ANTHU AZISANKHANA
Nthawi zina nkhani za ndalama zimachititsa kuti anthu ena aziona ena molakwika. Mwachitsanzo munthu yemwe ndi wolemera akhoza kumaganiza kuti anthu osauka ndi aulesi. Ndipo munthu wosauka akhoza kumaganiza kuti anthu olemera ndi odzikonda komanso adyera. Mtsikana wina wochokera m’banja lolemera, dzina lake Leanne ananena kuti anthu amamusala.
M’Baibulo muli malangizo abwino okhudza ndalama ndipo malangizowo ndi othandiza kwambiri mofanana ndi mmene zinalili pamene ankalembedwa
Leanne anati: “Anthu a kusukulu kwathu ankanena kuti bambo anga ndi mpondamakwacha. Ndipo ankakonda kunena kuti: ‘Si paja anzathu mukafuna chinachake mumangowauza adadi anu kuti akugulireni.’ Nthawi zina ankanenanso kuti: ‘Banja lakwathu n’losauka ndipo sitingakwanitse kugula galimoto yodula ngati yakwanu ija.’ Tsiku lina ndinauza anzangawo kuti asamanene zimenezo. Ndinawauzanso kuti zimene amanenazo sizindisangalatsa. Ndinkafuna kuti ndizidziwika ngati munthu amene amachitira ena zabwino osati ngati munthu wochokera kubanja lolemera.”
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
Baibulo silinena kuti ndalama ndi zoipa. Silinenanso kuti munthu amene ali ndi ndalama ndi woipa, ngakhale munthuyo atakhala nazo migolomigolo. Choncho nkhani si kuchuluka kwa ndalama zimene munthu ali nazo, koma mmene amaonera ndalamazo komanso zimene amachita kuti azipeze. M’Baibulo muli malangizo abwino okhudza ndalama ndipo malangizowo ndi othandiza kwambiri mofanana ndi mmene zinalili pamene ankalembedwa. Taonani zitsanzo zotsatirazi.
BAIBULO LIMATI: “Usamadzitopetse ndi ntchito kuti upeze chuma.”—Miyambo 23:4.
Buku lina limanena kuti, anthu omwe amangokhalira kufunafuna chuma “amadwala matenda a maganizo, zilonda zapakhosi, kupweteka kwa msana komanso mutu. Amakondanso kumwa kwambiri mowa komanso kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.” (The Narcissism Epidemic) Apatu n’zoonekeratu kuti anthu amene amangokhalira kufunafuna chuma amakumana ndi mavuto osaneneka.
BAIBULO LIMATI: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.”—Aheberi 13:5.
Nthawi zina, munthu amene amakhutira ndi zomwe ali nazo amathabe kukhala ndi nkhawa pa nkhani za ndalama. Komabe sikuti nthawi zonse amangokhalira kuganizira za ndalama n’kuiwala kuti palinso zinthu zina zofunika kwambiri. Mwachitsanzo, munthu yemwe amakhutira ndi zomwe ali nazo, samakhumudwa kwambiri akakumana ndi mavuto a zachuma. Amayesetsa kutengera chitsanzo cha mtumwi Paulo, yemwe anati: “Ndithudi, kukhala wosowa ndimakudziwa, kukhala ndi zochuluka ndimakudziwanso. M’zinthu zonse ndi m’zochitika zosiyanasiyana, ndaphunzira chinsinsi chokhala wokhuta ndi chokhala wanjala. Ndaphunziranso chinsinsi chokhala ndi zochuluka, ndi chokhala wosowa.”—Afilipi 4:12.
BAIBULO LIMATI: “Wodalira chuma chake adzagwa.”—Miyambo 11:28.
Akatswiri amanena kuti nkhani za ndalama ndi zimene zimachititsa kuti mabanja ambiri asamayende bwino komanso kuti athe. Ndalama zimachititsanso kuti anthu ena adziphe. N’zomvetsatu chisoni kuti anthu ena akumaona kuti ndalama n’zofunika kwambiri kuposa banja lawo ngakhalenso moyo wawo. Koma anthu omwe sakonda ndalama amadziwa kuti pali zinthu zina zofunika kwambiri. Amaona kuti zimene Yesu ananena pa Luka 12:15 n’zoona. Yesu anati: “Ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera m’zinthu zimene ali nazo.”
KODI MUMAONA KUTI NDALAMA N’ZOFUNIKA KUPOSA CHILICHONSE?
Kuti mudziwe ngati mumakonda ndalama kapena ayi, mungachite bwino kudzifufuza. Mwachitsanzo mungadzifunse mafunso otsatirawa.
Kodi ndimafuna kupeza ndalama zambiri m’kanthawi kochepa?
Kodi sindifuna kugawirako ena ndalama zanga?
Kodi ndimakonda kucheza ndi anthu omwe amakonda kunena za ndalama komanso zinthu zomwe ali nazo?
Kodi ndimalolera kunama kapena kuchita zinthu zina zolakwika kuti ndipeze ndalama?
Kodi ndimaona kuti ndalama ndi zimene zimapangitsa kuti anthu aziona kuti ndine wofunika?
Kodi nthawi zonse ndimangokhalira kuganizira za ndalama?
Kodi ndimangokhalira kufunafuna ndalama n’kumanyalanyaza thanzi langa komanso banja langa?
Muzigawira ena zomwe muli nazo
Ngati pali funso lina limene mwayankha kuti “Inde,” muyenera kuyesetsa kuti musamangoganizira zopeza ndalama komanso katundu wambiri. Muzipewa kucheza ndi anthu omwe amaona kuti ndalama komanso kupeza zinthu zambiri n’kofunika kuposa chilichonse. Muzikonda kucheza ndi anthu omwe amaona kuti kukhala ndi khalidwe labwino n’kofunika kwambiri kuposa kukhala ndi zinthu zambiri.
Musalole kuti mtima wanu ukhale wokonda ndalama. M’malo momangokhalira kufunafuna ndalama, mungachite bwino kumapeza nthawi yocheza ndi banja lanu, anzanu komanso yosamalira thanzi lanu. Kuchita zimenezi kungasonyeze kuti simukonda ndalama.
a Tasintha mayina m’nkhaniyi.