Mutu 4
Cifukwa Cace Timakalamba ndi Kufa
1. (a) Kodi nciani cimene ciri cikhumbo ca anthu ambiri ponena za thanzi labwino ndi moyo? (b) Cifukwa cakuti matenda ndi imfa ziri paliponse, kodi ndi mafunso otani amene amabuka ponena za cifuno ca Mulungu kaamba ka munthu?
MUNTHU aliyense wolongosoka amakhumba moyo ndi thanzi labwino. Timafunafuna citonthozo pa ululu ndi kubvutika zimene matenda amazibweretsa ndipo timaikhumba njira ya kucipewera ciyambukiro cofoola cimene ukalamba umacidzetsa pa matupi athu. Kumatipwetekanso ife, pamene tiwaona awo amene timawakonda akumakanthidwa ndi zinthu zimenezi. Cifukwa ca ici, anthu ambiri amafunsa kuti, “Kodi zinthu zonsezi zinali mbali ya cifuno coyambiriraco ca Mulungu? Pamene Mulungu anamlenga munthu, kodi cinali cifuno cace kuti munthu azikalamba, ndi kufikira kukhala wogontha kapena wakhungu? Kodi iye anafuna kuti khungu la munthu lizicita makwinya cifukwa ca ukalamba, mtima wace kugwidwa matenda ndiponso ziwalo zace zina kufooka? Kwenikwenidi, kodi Mulungu anampanga munthu kuti azifa?”
2. (a) Kodi Mulungu anamlenga munthu ali ndi cirema ciriconse? (b) Pamenepo, kodi ndi ciyembekezo cotani cimene Adamu ndi Hava anapatsidwa ndi Mulungu?
2 Ai, Yehova Mulungu sanamlenge munthu kaamba ka mtsogolo mwatsoka moteromo. Baibulo limatiuza ife kuti Yehova anaupereka munda wosangalatsa kwambiri kuti ukhale kwao kwa anthu awiri oyambirirawo, ndipo iye anawadalitsa iwo. Pomaipenda ncito yace ya kulenga, Mulungu moyenerera anaicha iyo kukhala ‘yabwino kwambiri.’ (Genesis 1:28, 31) Ici cikutanthauza kuti Adamu ndi Hava analengedwa ali angwiro, popanda cirema ca m’maganizo kapena thupi. (Deuteronomo 32:4; Miyambo 10:22) Iwo anali ndi ciyembekezo ca kukhala kosatha.
3. Kodi nciani cimene asayansi amanena ponena za mphamvu ya moyo wa anthu?
3 Mokondweretsa, asayansi amakono amadziwa kuti thupi laumunthu limadzikonza lokha mosalekeza, ndipo amanena kuti, m’mikhalidwe yoyenera, ilo liri lokhoza kukhala kosatha. Wolandira Mfupo wochuka, Dr. Linus Pauling, analongosola kuti mphamvu ya thupi la munthu imadzibwezeretsa yokha ndipo, mwa kutero, liyenera kutero kosatha. William Beck amene ali Biochemist ananenanso kuti: “Sindikuciona cifukwa cace cimene imfa, mu mkhalidwe wa zinthu, ifunikira kukhala yosapeweka.” Komabe, mosasamala za kukhala opangidwa motero, anthu amapitirizabe kumakalamba ndi kufa. Cifukwa ninji? Mau a Mulungu Baibulo amatipatsa ife yankho lokhutiritsa.
ZOTURUKAPO ZA KUSAMVERA
4. Kodi ndi ciyeso cotani cimene Mulungu anacipereka pa Adamu ndi Hava, kumakugogomezera kuopsa kwace kwa kusamvera?
4 Pamene Yehova anamlenga Adamu ndi Hava, iwo anafikira kukhala mbali ya pa dziko lapansi ya banja lalikuru la Mulungu, limene linaphatikizapo kale ciwerengero cacikuru ca zolengedwa zauzimu kumiyamba. Mulungu anali Atate wa anthu awiri amenewo, popeza kuti iye anawapatsa iwo moyo. Komabe, mphatso ya moyo imeneyo inali yodalira pa kanthu kena; ndiko kuti, iyo ikanapitirizabe kukhala yao kokha ku utali umene iwo akanapitiriza kuukwaniritsa mkhalidwe wa kumvera kwacikondi kwa atate wao wakumwamba. Kumvera lamulo kuli koyenera kaamba ka mtendere ndi cilongosoko cabwino cosalekeza, cotero iwo anayenera kumzindikira Mulungu kukhala Wolamulira wao Wamkuru. Kodi iwo anacidziwa ici? Inde, cifukwa cakuti Yehova anaika pa iwo ciyeso cimene cinakugogomezera kufunika kwace kwa kuvera. Iye anamuuza Adamu kuti: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; cifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.”—Genesis 2:16, 17.
5. (a) Kodi ciyeso ca pa kumvera kwa Adamu ndi Hava cinacipereka cizunzo pa iwo? (b) Kodi ncifukwa ninji ‘zipatso zokanizidwazo’ sizinali kugonana?
5 Ciyeso ca kumvera cimeneci sicinali cobvuta. Iwo sanamanidwe cakudya cofunikaco, ndipo iwo sanayesedwe mokupitirira kukhoza kwao. Komabe, kumvera kwaoko kunali kusonyeza kuti iwo anauzindikira unansi wao ndi Mulungu. (1 Yohane 5:3) Ngakhale kuli kwakuti anthu ena ali ndi lingaliro lakuti ‘cipatso cokanizidwaco’ cinali kunena za kugonana kwa pakati pa mwamuna ndi mkaziyo, sizinali conco. Mulungu mwiniyo anali atawauza iwo kale kuti “mubalane, mucuruke, mudzaze dziko lapansi.” (Genesis 1:28) Pamene Mulungu anawalamulira iwo kusadya zipatso za mtengo wakuti wakuti kunangotanthauza kokha kuti Mulungu anaupatula mtengo umodzi wokha pakati pa mitengo yazipatso yambiri ya mu Edene ndipo anawalamulira anthu awiriwo kusadya zipatso zace.
6. (a) Kodi ncifukwa ninji mtengowo unali kuchedwa “mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa”? (b) Pamene Adamu ndi Hava anadya zipatsozo, kodi ndi cinthu coipa cotani cimene iwo anali kucicita kwa Atate wao wakumwamba?
6 Kodi ncifukwa ninji mtengowo unali kuchedwa “mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa”? Cifukwa cakuti, Monga coturukapo ca lamulo la Mulungu, zipatso zace zinaphiphiritsira kuyenera kwa Mulungu kwa kuzisankhira zolengedwa zace zimene zinali “zabwino” ndi zimene zinali “zoipa” kaamba ka iwo. Cotero, kwa anthu awiriwo kudya cipatso ici kunatanthauza kuti iwo anali kufufunuka kwa Atate wao wakumwambayo ndi kumacikana citsogozo cace caumulungu ndi cifuniro cangwiro. Pamene cinali cosabvuta, ciyesoco cinaphatikizapo zambiri. Cinaphatikizapo kudalira kwa munthu pa Mlengi wace ndi kuuzindikira ufumu waumulungu kwa munthuyo. Kumbukiraninso kuti, Yesu Kristu analipereka kwa anthu opanda ungwiro lamulo lakuti “iye amene akhulupirika m’cacing’onong’ono alinso wokhulupirika m’cacikuru.” (Luka 16:10) Ndi motani nanga mmene icico cinagwirira nchito kwa zolengedwa zangwirozo!
7. (a) Kodi nciani cimene colengedwa cosaoneka, cimene cinali kulankhula kupyolera mwa cinjoka, cinamuuza Hava ponena za zipatso za mtengowo? (b) Pamenepo kodi nciani cimene Hava anacicita, ndipo pamene mwamuna wace anadziwa za ico, kodi iye anacitanji?
7 Ncifukwa ninji Hava analiswa lamulo la Mulungu ndi kudya cipatsoco? Lingalirolo silinayambike ndi iyeyo koma linaperekedwa kwa iyeyo ndi colengedwa cauzimu comagwiritsira nchito cinjoka copanda nzeru cimene cinalankhula kupyolera mwa ico. Colengedwa cauzimu cimeneco, cimene cadziwikitsidwa m’Baibulo kukhala Satana Mdierekezi, cifukwa ca cimeneco cikuchedwa “njoka yakaleyo.” (Cibvumubulutso 12:9) colengedwa cosaoneka cimene cinali kulankhula kupyolera mwa cinjokaco mwapoyera cinacikana coonadi ca lamulo la Mulungu limene Hava anligwira mau. Iye anazisonyeza zipatso za mtengowo kukhala zokhoza kumpangitsa mkaziyo kukhala wofanana ndi Mulungu akumadzisankhira yekha zimene zinali “zabwino” ndi zimene zinali “zoipa.” Pamenepo Hava anayamba kuzilingalira zipatsozo kukhala ngati zokhumbika ndipo iye sanamvere Mulungu mwa kumazidya izo. Adamu, mwamuna wace ndi mutu wace, atacizindikira cimene mkaziyo anacicita, sanakatsutse kacitedwe ka mkaziyo koma anagwirizana naye.—Genesis 3:2-6; Yakobo 1:14, 15; 1 Akorinto 11:3.
8. (a) Mwa kacitidwe kao kakusamverako, kodi Adamu ndi Hava anali ocimwa pa ciani? (b) Kodi ncifukwa ninji sitiyenera kukuona kuopsa kwace kwa cimene Adamu ndi Hava anacicita mu njira imene anthu amalingalirira za kusamvera ndi kuba lerolino?
8 Mwa kacitidwe kosamvera kameneka iwo anapezeka kukhala ocimwa, ndipo anadzidzetsera cilango ca ucimo. (1 Yohane 3:4) M’kumakulingalira kuyenera kwa cosankha ca Mulungu sitiyenera kucipanga colakwa ca kumakuona kuopsa kwace kwa cimene Adamu ndi Hava anacicita mwa njira imene anthu ambiri amazionera zinthu mu nthawi yathu. Lerolino kusamvera makolo kuli kofala, kawirikawiri akumangokhala osalangidwa. Kubanso kuli kofala, ndipo ambiri amalingalira kuti, ngati cimene cabedwaco ciri cacing’ono, kubako sikuli kodetsa nkhawa. Kupanduka ndi kulankhula motsutsana ndi olamulira zirinso zofala lerolino. Koma zimenezo sizimaziongolera zinthu izi! Zocuruka za zipatso zobvunda zimene timaziona lerolino mu mpangidwe wa kukulakula kwa kupulupudza kwa anyamata ndi upandu kuli cifukwa ca kulephera kwa makolo ndi ena a mu ulamuliro kwa kuziongolera zinthu pakuyamba pace.—Miyambo 13:24; Mlaliki 8:11.
9. (a) Pomacilingalira cimene Adamu ndi Hava anacicitadi, kodi ncifukwa ninji Mulungu anali wokakamizika limodzi ndi banja lace la mu cilengedwe caponseponse kuti alicirikize lamulo? (b) Kodi ndi cilango cotani cimene awiri okwatirana osamverawo anapatsidwa kaamba ka cimo lao?
9 Mulungu sanati akulimbikitse kulakwa mwa kulephera kwa kulipangitsa lamulo lace kukhala logwira nchito. Mwa kusamvera kwao Adamu ndi Hava anasonyeza kusakhala ndi cikondi kwakukuru ca pa Uyo amene anawapatsa iwo zocuruka kopambana modabwitsa. Iwo analakwa mwa kuba, cifukwa cakuti anacitenga cimene Mlengi wao ananena kuti sicinali cao. Coipanso kwambiri ndico cakuti iwo anagwirizana ndi mdani wa Mulungu ndipo, mwa macitidwe ao, anamucha Mulungu kukhala wabodza. Yehova anakuona kukhala koyenera kwa iye ndi ku banja lace la mu cilengedwe caponseponse kulisunga lamulo. Iye anacicitadi ici. Monga coturukapo ca kucimwa kwace kwadala anthu awiri okwatirana osasunga lamulowo anaturutsidwa m’munda wa Edenewo kuti akafe.—Genesis 3:22-24.
10. Kodi ndi motani mmene ciyambukiro ca ucimo cingafaniziridwire ndi makina, ndipo kodi ucimo unatsogolera Adamu ndi Hava kuti?
10 Cotsatirapo ca ucimo pa iwo cingayerekezedwe ndi cimene cimacitikira pa makina abwino pamene sakugwiritsiridwa nchito moyenera, mogwirizana ndi malangizo a wopanga makinayo. Makinawo adzayamba kukhala ndi zirema ndipo, mu nthawi yace, adzathyoka. Cimodzimodzinso, monga coturukapo ca kuwanyalanyaza malangizo a Mpangi wao, Adamu ndi Hava anayamba kufooka, ndipo potsirizira pace analeka kugwira nchito, mu imfa. Cimeneco ndico cimene kusamvera ndi kutaya ciyanjo ca Mulungu kunatanthauza kwa iwo. (Genesis 3:16-19) Adamu ataigwiritsira nchito yocuruka ya nthawi yace mphamvu ya thupi lace limene pa nthawi yina linali langwirolo, iye anamwalira pa usinkhu wa zaka 930. Ici cinacitika mkati mwa “tsiku lophiphiritsira la zaka cikwi cimodzi limene Mulungu anali atalikhazikitsa.—Genesis 5:5; 2 Petro 3:8.
CIYAMBUKIRO PA MBADWA
11. Kodi ndi motani mmene Baibulo limalongosolera cifukwa cace timadwala ndi kufa?
11 Koma, popeza kuti ife lerolino sitinalimvere lamulo limenelo mu Edene, kodi ncifukwa ninji kulinso kwakuti timadwala ndi kufa? Kuli cifukwa ca ici: Mbadwa zonse za Adamu zinabadwa iye atacimwa kale. Motero mbadwa zace zinakhala ndi ucimo wa colowa ndi imfa kucokera kwa iye. Anthu onse amakhala ndi kupanda ungwiro kwa colowa, cifukwa cakuti onse amacokera kwa Adamu ndi Hava. Monga momwe bukhu la Baibulo la Yobu limatiuzira ife: “Adzaturutsa coyera m’cinthu codetsa ndani? Nnena mmodzi yense.” (Yobu 14:4) Ndiponso, pa Aroma 5:12 Baibulo limalongosola kuti: “Ucimo unalowa m’dziko lapansi mwa [Adamu] munthu mmodzi, ndi imfa mwa ucimo; cotero imfa inafikira anthu onse.” Monga momwe makina angwiro sangaumbidwe kucokera mu cikombole coipa, cotero Adamu pa kukhala kwace wopanda ungwiro sakanatha kuwabereka ana angwiro, osalakwa. Salmo 51:5 [50:7, Dy].
12. Kodi ndi motani mmene ciyambukiro ca ucimo wa Adamu ndi Hava cingayerekezedwere ndi cimene cimacitika pamene anthu amene amakhala mwacisembwere amawabala ana?
12 Ciyambukiro ca ucimo wa Adamu ndi Hava pa mbadwa zao cingayerekezedwe ndi cimene cimacitika kawirikawiri pamene anthu amene amalinyalanyaza lamulo la Mulungu ndi kumakhala ndi moyo mwacisembwere amawabalira ana. Anthu oterowo angatenge matenda ku ziwalo zao zogonanira zimene Mulungu anawapatsa kuti abalire ana ao. Ana a makolo “aucisi” oterowo angabadwe ali opunduka mwakuthupi kapena mwa maganizo cifukwa ca ucimo wa makolo ao. Coteronso, makolo athu oyambirira anafikira kukhala “aucisi,” opanda ungwiro, okhoza kumadwala, ndipo potsirizira pace kufa. Iwo akanacipereka kwa ana ao cokha cimene anali naco: kupanda ungwiro, limodzi ndi ciyembekezo ca kudwala ndi kufa. Cimeneco ndico cifukwa cace ife tonse timakalamba ndi kufa, ndiponso cifukwa cace ife mosabvuta timacicita cimene ciri colakwika.
13. Kodi pali kusiyana pakati pa ucimo wadala ndi ucimo wa mwadzidzidzi? Motani?
13 Komabe, kucita zolakwa za mwadzidzidzi cifukwa ca ucimo wa colowa kuli kosiyana kotheratu ndi kumazicitacita mwadala zinthu zimene munthuyo amazidziwa kukhala zolakwika. (1 Yohane 5:16) Ngati munthu alidi wolapa moona mtima cifukwa ca zofooka zace zacolowa, iye angaciyembekezere cikhululukiro cacifundo kucokera kwa Mulungu. (Miyambo 28:13) Koma iye ayenera kukhala wosamala kuti, iye atacidziwa cimene ciri coyenera, iye asasankhe mwadala kukatsatira kacitidwe kamene kali kosiyana ndi cifuniro ca Mulungu. Kuteroko kukatanthauza kutaya ciyanjo ca Mulungu ndi ca moyo weniweniwo.—Deuteronomo 30:15-20; Ahebri 10:26, 27.
14. Kodi ndi makonzedwe otani amene Mulungu wawapanga a kuupulumutsa mtundu wa anthu ku ucimo ndi imfa?
14 Mwacimwemwe, Yehova wawapanga makonzedwe acikondi a kuwapulumutsa olapawo kucokera ku ziyambukiro zoipa za ucimo wa colowa ndi imfa. Citonthozo cabwino cotereci cidzadza kupyolera mu nsembe ya dipo ya Yesu Kristu. Ponena za makonzedwe amenewa Baibulo limati: “Mulungu anamtuma Mwana wace wobadwa yekha, alowe m’dziko lapansi, kuti tikhale ndi moyo mwa iye.” (1 Yohane 4:9) Cotero, mu nthawi yokwanira ya Mulungu, m’kulamulira kwa Ufumu wa Mwana wace, kupanda ungwiro kwaumunthu kwa colowa mwapang’onopang’ono kudzacotsedwa, ndipo mtundu wa anthu sudzakhala nazo ziyambukiro za ucimo wa Adamu. Eya, ngakhale imfa imene tinailandira mwa colowa kucokera kwa Adamu sidzakhalanso ndi mphamvu pa ife! (Cibvumbulutso 21:3, 4) Mungakhale mmodzi wa awo amene angasangalale ndi madalitso oterowo. Motani? Mwa kumagwiritsira nchito zogawira zimene Yehova wazipereka ndi kumacitsimikizira cikondi canu pa iye mwa kumasunga malamulo ace.—Mlaliki 12:13.
[Chithunzi patsamba 30]
Adamu analiswa mwadala lamulo lolongosoledwa momvekera bwino la Mulungu