Mutu 2
Kalata Yochokera kwa Mulungu
TANDIUZANI, kodi ndi bukhu liti limene mumalikonda kwambiri mwa onse?—Ana ena akasankha lina limene limasimba za nyama. Ena akasankha bukhu lokhala ndi zithunzithunzi zochuruka mu ilo. Kungathe kukhala kosangalatsa kuwawerenga mabukhu amenewo.
Koma mabukhu abwino kopambana m’dziko lonse lapansi ali amene amatiuza ife choonadi chonena za Mulungu. Ndipo limodzi la mabukhu amenewo liri lamtengo wapatali koposa ena onse. Kodi mukulidziwa limenelo?—Baibulo.
Kodi nchifukwa ninji Baibulo liri lofunika kwambiri?—Chifukwa chakuti ilo linachokera kwa Mulungu. Ilo limatiuza ife ponena za iye ndi ponena za zinthu zimene iye adzatichitira ife. Ndipo limatisonyeza ife chimene tiyenera kuchichita m’malo mwakuti timkondweretse iye. Ilo liri ngati kalata yochokera kwa Mulungu.
Tsopano, Mulungu akadatha kulilemba Baibulo lonse kumwamba ndipo kenaka kulipereka ilo kwa munthu. Koma iye sanatero. Malingalirowo anachokera kwa Mulungu. Koma iye anawagwiritsira nchito atumiki ache pa dziko lapansi kukuchita kochuruka kwa kulembako.
Kodi ndi motani mmene iye anakuchitira kumeneko?—Chitsanzo chingatithandize ife kuzindikira. Pamene anthu awamva mau pa wailesi iwo ali ochokera kwa munthu wina amene ali kutali kwambiri. Iwo sangathe kumuona iye, koma iwo angathe kumva chimene iye akuchinena, kodi sichoncho?
Anthu angathe kupitadi kukafika ku mwezi mu zombo zao zouluka kutali m’mlengalenga, ndipo iwo angathe kutumiza mauthenga ku dziko lapansi ali kumeneko. Kodi munachidziwa chimenecho?—Ngati anthu angathe kuchita chimenecho, kodi Mulungu angathe kutumiza mauthenga kuchokera kumwamba?—Ndithudi iye angathe! Ndipo iyo anachichita icho kalekale anthu asankhale ndi wailesi ndi wailesi yakanema.
Mose anali munthu wina amene Mulungu analankhula naye. Mose sanathe kumuona Mulungu, koma iye anatha kumva mau. Mamiliyoni ambiri a anthu analipo pamene ichi chinachitika. Iwo anachiona icho pamene Mulungu analichititsa phiri lonse kugwedezeka, ndipo panali bingu ndi mphezi. Iwo anamva pamene mau anachokera kumwamba. Iwo anadziwa kuti Mulungu anali atalankhula. Mulungu analankhula ndi Mose kachiwiri pambuyo pache, ndipo Mose anazilemba zinthu zimene Mulungu anazinena. Zimene iye anazilemba ziri m’Baibulo.—Eksodo 19:3-20:21.
Sanali Mose yekha amene analemba. Mulungu anawagwiritsira nchito amuna pafupifupi makumi anai kuzilemba mbali za Baibulo. Iwo analemba zinthu zimene Mulungu anali kudzazichita mtsogolo. Kodi ndi motani mmene iwo anazidziwira zinthu zimenezo izo zisanachitike nkomwe?—Mulungu anali atalankhula nawo.
Pomafikira pa nthawi imene Yesu, Mphunzitsi Wamkuruyo, anali pa dziko lapansi, mbali yaikuru ya Baibulo inali italembedwa. Tsopano, kumbukirani kuti, Mphunzitsi Wamkuruyo anali kumwamba. Iye anazidziwa zimene Mulungu anali atazichita. Kodi iye anakhulupilira kuti Baibulo linachokera kwa Mulungu?—Inde, iye anatero.
Pamene Yesu analankhula ndi anthu ponena za nchito za Mulungu, iye anawerenga kuchokera m’Baibulo. Nthawi zina iye anawauza iwo kuchokera m’chikumbu mtima zimene ilo linanena.
Yesu anatitengeranso ife chidziwitso chochuruka kuchokera kwa Mulungu. Iye anati: ‘Zinthu zenizenizo zimene ndinazimva kuchokera kwa Mulungu ine ndiri kumazilankhula m’dziko.’ Yesu anali atamva zinthu zambiri kuchokera kwa Mulungu chifukwa chakuti iye anali atakhala ndi Mulungu. Ndipo kodi nkuti kumene ife tingathe kuziwerenga zinthu zimenezo zimene Yesu anazinena?—M’Baibulo. Zonse zinalembedwa kaamba ka ife kuti tiziwerenge.—Yoh. 8:26, NW.
Ndithudi, pamene Mulungu anawagwiritsira nchito anthu kulemba, iwo analemba m’chinenero chimene iwo anachigwiritsira nchito tsiku liri lonse. Chotero mbali ya Baibulo inalembedwa m’Chihebri, ina m’Chiaramu, ndipo yochepera kwambiri m’Chigriki. Anthu ochuruka lero lino sakudziwa kuziwerenga zinenero zimenezo. Kodi inu mukuzidziwa?—
Chimenecho ndicho chifukwa chache chimene Baibulo lakopedwera m’zinenero zina. Lero lino pali mbali za Baibulo m’zinenero zopitilira chikwi chimodzi kudza mazana anai. Tangoganizirani za chimenecho! Baibulo liri kalata ya Mulungu kwa anthu kuli konse. Chotero ilo liyenera kukhala m’zinerero zambiri. Koma mosasamala kanthu kaya ilo lakopedwa kangati, uthengawo uli wochokera kwa Mulungu.
Chimene Baibulo limachinena chiri chofunika kaamba ka ife. Ilo linalembedwa kale kwambiri. Koma ilo limasimba zinthu zimene ziri kumachitika lero lino. Ndipo ilo limatiuza ife chimene Mulungu adzachichita posachedwapa mtsogolomu. Chimene ilo limanena chiri chokondweretsa! Ilo limatipatsa ife chiyembekezo chodabwitsa.
Baibulo limatiuzanso ife mmene Mulungu amatifunira ife kukhala ndi moyo. Ilo limatiuza ife chimene chiri choyenera ndi chimene chiri cholakwa. Inu mufunikira kuchidziwa chimenechi ndi inenso chimodzimodzi. Ilo limatiuza ife za anthu amene anachita zinthu zoipa, ndi chimene chinawachitikira iwo. Chotero ife tingathe kulipewa bvuto limene iwo anali nalo. Ilonso limatiuza ife za anthu amene anachita choyenera, ndi zoturukapo zabwino zimene zinadza kwa iwo. Zonsezo zinalembedwa kaamba ka ubwino wathu.
Koma kuti tipindule nalo kopambana Baibulolo, ife tifunikira kulidziwa yankho la funso lina. Funsolo ndilo ili: “Kodi ndani amene anatipatsa ife Baibulo?” Kodi inuyo mukanati chiani?—Inde, lonselo liri lochokera kwa Mulungu.
Koma anthu ena samamvetsera chimene Mulungu amachinena m’Baibulo. Iwo amangokhala momwe iwo afunira. Kodi mukuganiza kuti zimenezo ziri bwino?—Kodi mukuganiza kuti munthu ali yense amadziwa zochuruka koposa mmene. Mulungu amadziwira?—Njira ya kusonyezera kuti ife tiridi anzeru ndiyo kumumvetsera Mulungu. Ndiyeno ife tifunikira kuchita zimene iye amazinena.
Chotero ife tifunikira kukhala ndi nthawi kuliwerenga Baibulo pamodzi. Pamene ife tilandira kalata kuchokera kwa munthu wina amene ife timamkonda kwambiri, ife timaiwerenga iyo mobwerezabwereza. Iyo iri yamtengo wapatali kwa ife. Imeneyo ndiyo njira imene Baibulo liyenera kukhalira kwa ife, chifukwa chakuti ndilo kalata yochokera kwa Uyo amene amatikonda ife koposa. Ilo liri kalata yochokera kwa Mulungu.
(Khalani ndi mphindi zina zowerengeka tsopano ndi kuwawerenga malemba awa amene amasonyeza kuti Baibulo liridi Mau a Mulungu, olembedwa kaamba ka phindu lathu: 2 Timoteo 3:16, 17; 2 Petro 1:20, 21; Aroma 15:4.)