Mutu 4
Mulungu Ali ndi Dzina
KODI dzina lako ndani?—Iwe uli ndi dzina. Inenso chimodzimodzi. Mwamuna woyambayo pa dziko lapansi anali ndi dzina. Mulungu anamcha iye Adamu. Mkazi woyambayo anachedwa Hava. Mwamuna, mkazi ndi mwana ali yense ali ndi dzina.—
Tatukulani mutu muyang’ane nyenyezi zambirimbirizo, usiku. Kodi mukuganiza kuti izo ziri ndi maina?—Inde, Mulungu anaipatsa dzina nyenyezi iri yonse m’mlengalengamo. Baibulo limatiuza ife kuti: “Awerenga nyenyezi momwe ziri; azicha maina zonsezi.”—Salmo 147:4.
Anthu ndi nyenyezi zonse ziri ndi maina. Nanga kodi mukuganiza kuti Mulungu ali ndi dzina?—Mphunzitsi Wamkuruyo ananena kuti iye ali nalo. Iye pa nthawi ina anati kwa Mulungu m’pemphero: ‘Ndalidziwikitsa dzina lanu kwa atsatiri anga’.—Yohane 17:26.
Kodi mukulidziwa dzina la Mulungu?—Mulungu mwiniyo amatiuza ife chimene ilo liri. Iye amati: “Ine ndine Yehova. Limenelo ndilo dzina langa.” Chotero dzina la Mulungu ndilo YEHOVA—Yesaya 42:8, NW.
Kodi mumakonda pamene ena alikumbukira dzina lanu?—Anthu amakonda kuitanidwa ndi dzina lao. Ndipo Yehova amawafuna anthu kulidziwanso dzina lache. Chotero ife tiyenera kuligwiritsira nchito dzinalo Yehova pamene ife tilankhula za Mulungu.
Mphunzitsi Wamkuruyo analigwiritsira nchito dzina la Mulungu Yehova pamene iye analankhula kwa anthu. Nthawi ina iye anati: “Inu muyenera kumkonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse.”—Marko 12:30, NW.
Yesu anadziwa kuti “Yehova” liri dzina lofunika kwambiri. Chotero iye anawaphunzitsa atsatiri ache kuligwiritsira nchito dzina la Mulungu. Iye anawamphunzitsadi iwo kulankhula za dzina la Mulungu m’mapemphero ao.
Kalekale Mulungu anakusonyeza kufunika kwa dzina lache kwa munthuyo Mose. Mose anali mmodzi wa ana a Israyeli. Ana a Israyeli anakhala m’dziko lochedwa Igupto. Aiguptowo anawapanga ana a Israyeli kukhala akapolo ndipo anali ankhanza kwambiri kwa iwo. Pamene Mose anakula, iye anayesayesa kumthandiza mmodzi wa anthu ache. Ichi chinaipangitsa mfumu ya Igupto kukwiya. Iyo inafuna kumupha Mose! Chotero Mose anathawa mu Igupto.
Mose anapita ku dziko lina. Ilo linali dziko la Midyani. Kumene iye anagwira nchito monga mbusa, kumaweta nkhosa. Tsiku lina iye anaona chinthu chodabwitsa. Chitsamba cha minga chinali kuyaka, koma icho sichinali kupsya! Mose anapita chapafupi kuti aonetsetse bwino.
Kodi mukuchidziwa chimene chinachitika?—Mose anamva mau kuchokera pakati pa chitsamba choyaka chimenecho. Mauwo anaitana kuti, “Mose! Mose!”
Kodi ndani amene anali kumanena choncho?—Anali Mulungu amene anali kulankhula! Mulungu anali ndi nchito yaikuru yakuti Mose aichite. Mulungu anati: ‘Idza ndikutume kwa Farao, mfumu ya Igupto, ndipo uturutse anthu anga ana a Israyeli mu Igupto.’ Mulungu analonjeza kumthandiza Mose.
Koma Mose anati kwa Mulungu: ‘Bwanji nditafika kwa ana a Israyeli mu Igupto ndi kunena kwa iwo kuti Mulungu anandituma. Bwanji ngati iwo andifunsa ine kuti, Kodi dzina lache ndani? Kodi ndidzati chiani?’ Mulungu anamuuza Mose kukawauza ana a Israyeli kuti: ‘Yehova wandituma ine kwa inu. Yehova ndilo dzina langa kosatha.’—Eksodo 3:1-15.
Ichi chimasonyeza kuti Mulungu akalisungabe dzinalo Yehova. Mulungu anafuna kudziwika ndi dzina lakuti Yehova kosatha.
Mose anabwelera ku Igupto. Aiguptowo kumeneko sanamdziwedi Yehova. Iwo anaganizira kuti iye sanali chabe kamulungu ka ana a Israyeli. Aiguptowo sanaganizire kuti Yehova anali Mulungu wa dziko lonse lapansi. Chotero Yehova anaiuza mfumu ya Igupto kuti: ‘Ndidzalidziwikitsa dzina langa m’dziko lonse lapansi.’ —Eksodo 9:16.
Yehova analidziwikitsadi dzina lache m’dziko lonse lapansi. Iye anamlamulira Mose kuwatsogolera ana a Israyeli kuturuka mu Igupto. Ndipo anthu m’dziko lonse lapansi mwamsanga anamva za Yehova.
Lero lino anthu ambiri ali ofananadi ndi mmene Aiguptowo analiri. Iwo samakhulupilira kuti Yehova ali Mulungu wa dziko lonse lapansi. Chotero Yehova amawafuna anthu ache kuwauza ena za iye. Ichi ndicho chimene Yesu anachichita.
Kodi inuyo mukufuna kukhala ngati Yesu?—Pamenepo auzeni ena kuti dzina la Mulungu ndilo Yehova. Inu mudzapeza kuti anthu ambiri sakulidziwa ilo. Chotero mwinamwache inu mungathe kuwasonyeza iwo lemba m’Baibulo pa Salmo 83:18, NW. Tiyeni titenge Baibulo nthawi yomwe ino ndi kulipeza lemba limenelo pamodzi. Ilo limati: “Kuti anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu liri Yehova, inu nokha muli Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.”
“Yehova” ndilo dzina lofunika koposa limene liripo. Ilo ndilo dzina la Uyo amene anapanga zinthu zonse. Ndipo kumbukirani kuti, Yesu ananena kuti ife tiyenera kumkonda Yehova ndi mtima wathu wonse. Kodi inu mumamkonda Yehova? -
Kodi ife tingasonyeze motani kuti timamkonda iye?—Njira imodzi ndiyo kuwauza ena dzina lachelo Yehova. Tingawauzenso iwo ponena za zinthu zodabwitsa zimene iye wazichita. Ichi chidzamkondweretsa Yehova, chifukwa chakuti iye amadziwa kuti anthu afunikira kudziwa za iye. Ife tingathe kukhala ndi phande m’kumachichita chimenecho, ati?-
Si munthu ali yense amene adzafuna kumvetsera pamene ife tilankhula za Yehova. Anthu ambiri sanamvetsere ngakhale pamene Yesu analankhula ponena za Iye. Koma chimenecho sichinamletse Yesu kumalankhula za Yehova.
Chotero tiyeni tikhale ngati Yesu. Tiyeni tipitirizebe kumalankhula za Yehova. Ngati ife titero, Yehova Mulungu adzakondweretsedwa nafe chifukwa chakuti ife tikusonyeza chikondi kaamba ka dzina lache.
(Tsopano werengani pamodzi kuchokera m’Baibulo malemba ena angapo amasonyeza kufunika kwa dzina la Mulungu: Yohane 17:26; Yesaya 12:4, 5; Aroma 10:13.)