Mutu 10
Wakhate Mmodzi Analemekeza Mulungu
KODI mai wanu anakukonzerani inu chakudya chabwino lero?—Kunali kukoma kwao mtima kuchita chimenecho, ati?—Kodi munawathokoza iwo?—Nthawi zina ife timaiwala kunena kuti “Zikomo” pamene ena atichitira ife zinthu zokoma mtima, sichoncho kodi? Pamene Mphunzitsi Wamkuruyo anali pa dziko lapansi, panali akhate ena amene amaiwala kunena kuti “Zikomo.”
Kodi mukuchidziwa chimene wakhate ali?—Wakhate ndiye munthu amene ali ndi nthenda yochedwa khate. Nthenda imeneyo ingathedi kuchititsa mnofu wa munthu kulakatika. Pamene Yesu anakhala ndi moyo pa dziko lapansi, akhate anali kukhala kotalikirana ndi anthu ena. Ndipo ngati wakhate anamuona munthu wina alinkudza, iye analinkukuwa kuti: ‘Ndine wakhate. Usafike kuno!’ Mwinamwache anthuwo akanaitenga nthenda ya wakhateyo.
Yesu anali wokoma mtima kwambiri kwa akhate. Tsiku lina, pamene iye anali pa ulendo wache wopita ku Yerusalemu, Yesu anafika pafupi ndi tauni ina yaing’ono. Akhate khumi anaturuka kuti amuone iye.
Akhatewo sanafike pafupi ndi Yesu. Iwo anaima kutali. Koma iwo anali atamva kuti Yesu anali ndi mphamvu yochokera kwa Mulungu ya kuchiritsira nthenda za mitundu yonse, ngakhale khate. Chotero iwo anamfuulira iye kuti, ‘Yesu, Mphunzitsi, tithandizeni!’
Kodi inuyo mumawamvera chisoni anthu amene ali kudwala?—Yesu anawamvera chisoni. Iye anadziwa mmene kunaliri kosakondweretsa kukhala wakhate. Chotero iye anawayankha iwo, nati: ‘Pitani ndi kukadzisonyeza kwa ansembe a Mulungu.’
Kodi nchifukwa ninji Yesu anawauza iwo kuchita chimenechi?—Chinali chifukwa cha lamulo limene Yehova analipereka kwa anthu ache. Lamulo limeneli linanena kuti wansembe wa Mulungu anafunikira kuyang’ana thupi la wakhateyo. Wansembeyo ankamuuza wakhateyo pamene nthenda yache yonse inachokera iye. Pamenepo iye ankatha kukhaliranso limodzi ndi anthu opanda khate.—Levitiko 13:16, 17.
Koma akhate khumi amenewa anali nayobe nthenda yao. Chotero kodi iwo akanapita ndi kukamuona wansembeyo monga momwe Yesu ananenera?—Inde, iwo anapita nthawi yomweyo. Amuna amenewa ayenera kukhala atakhulupilira kuti Yesu akaichotsa nthenda yao.
Nanga kodi nchiani chimene chinachitika?—Eya, pamene iwo anali pa ulendo wao wopita kwa wansembeyo, nthenda yao inawachokera. Thupi lao linachiritsidwa. Iwo anachiritsidwa! Chikhulupiliro chao mu mphamvu ya Yesu chinafupidwa. Ha, ndi chisangalalo chotani nanga chimene iwo anali nacho!
Koma, tsopano, kodi nchiani chimene iwo akanayenera kuchichita kuti asonyeze chiyamikiro chao? Kodi inuyo mukanachitanji?—
Mmodzi wa amuna ochiritsidwawo anabwelera kwa Yesu. Iye anayamba kumamlemekeza Yehova, akumanena zinthu zabwino ponena za Mulungu. Chimenecho chinali chinthu choyenera kuchichita, chifukwa chakuti mphamvu ya kumchiritsira iye inachokera kwa Mulungu. Munthuyonso anagwa pa mapazi a Mphunzitsi Wamkuruyo namthokoza iye. Iye anali woyamikira kwambiri kaamba ka zimene Yesu anazichita.
Koma bwanji ponena za amuna asanu ndi anai enawo? Yesu anafunsa kuti: ‘Panali akhate khumi amene anachiritsidwa, kodi sichoncho? Kodi asanu ndi anai enawo ali kuti? Kodi mmodzi yekha anabwelera kudzamlemekeza Mulungu?’
Inde, nzoona, Mmodzi yekha mwa khumiwo anamlemekeza Mulungu, ndipo anabwelera kudzamthokoza Yesu. Ndipo munthu ameneyu anali Msamariya, munthu wochokera ku dziko lina. Amuna ena asanu ndi anaiwo sanamthokoze Mulungu; iwo sanamthokoze nkomwe Yesu.—Luka 17:11-19.
Kodi inuyo muli ngati uti wa amuna amenewo?—Ife tonse tikufuna kukhala ngati munthu Wachisamariyayo, ati?—Chotero, pamene munthu wina atichitira ife chinthu chokoma mtima, kodi nchiani chimene ife tiyenera kukumbukira kuchichita?—Tifunikira kusonyeza kuyamikira kwathu.
Anthu kwirikawiri amaiwala kunena kuti “Zikomo.” Koma kuli bwino kunena kuti “Zikomo.” Chiri chinthu choyenera kuchichita. Ndipo pamene inu muchichita icho, Yehova Mulungu ndi Mwana wache Yesu amakondwera.
Ngati muganizira za icho, mudzakumbukira kuti anthu akuchitirani inu zinthu zambiri. Kodi mukukumbukira kukhala mutadwala?—Inuyo mungakhale musanadwale mofanana ndi akhate khumi amenewo. Koma inuyo mungakhale mutadwala chimfine choipa, kapena kupota kwa m’mimba mwanu. Kodi mai wanu kapena atate wanu anakusamalirani?—Kodi inu muli okondwa kuti iwo anakuthandizani kuti mupeze bwino?—
Munthu Wachisamariyayo anamthokoza Yesu kaamba ka kumamchiritsa iye, ndipo ichi chinamkondweretsa Yesu. Kodi mukuganizira kuti mai wanu kapena atate wanu adzakondwa ngati inu munena kuti “Zikomo” pamene iwo akuchitirani zinthu?—Inde, iwo adzakondwa.
Nthawi zina anthu amatichitira ife zinthu tsiku ndi tsiku kapena mlungu ndi mlungu. Ingakhale nchito yao kuchita ichi. Iwo angakhaledi okondwa kuichita iyo. Koma ife tingaiwale kuwathokoza iwo.
Mphunzitsi wanu wa ku sukulu angagwire nchito zolimba kukuthandizani inu kuphunzira zinthu zambiri. Imeneyi ndiyo nchito yache. Koma iye adzakhala wokondwera ngati inu mumthokoza iye kaamba ka kumakuthandizani inu kuti muphunzire.
Nthawi zina anthu amangokuchitirani zinthu zazing’ono. Kodi munthu wina anayamba wakugwirizirani chitseko?—Kapena kodi munthu wina anakupatsirani chakudya pa thebulo lodyera?—Kuli bwino kunena kuti “Zikomo” ngakhale kaamba ka zinthu zazing’ono zimenezi.
Ngati ife tikumbukira kunena kuti “Zikomo” kwa anthu pa dziko lapansi, pamenepo ife tiri osakaikiradi kukumbukira kunena kuti “Zikomo” kwa Atate wathu wa kumwamba. Ndipo, ha, ndi zinthu zochuruka zotani nanga zimene ziripo zimene tingamthokozere Yehova! Iye anatipatsa ife moyo wathu, ndi zinthu zonse zabwino zimene zimaupangitsa moyo kukhala wokondweretsa. Chotero tiri ndi chifukwa chiri chonse cha kumlemekezera Mulungu mwa kumalankhula zinthu zabwino ponena za iye tsiku liri lonse.
(Ponena za kusonyezedwa kwa zithokozo, werenganinso Salmo 92:1 [91:1,MO] ndi Aefeso 5:20.)