Mutu 7
“Chilengedwe Chatsopano” Chiyamba Kugwira Ntchito!
1, 2. (a) Kodi ndi chilengedwe chotani, cha m’zaka zosakwanira zikwi ziwiri zapita’zo, chimene chinali chodabwitsa kwambiri koposa chija cha mwamuna ndi mkazi? (b) Monga mwa kunena kwa mau a Yesu mu Luka 24:46-48 ndi Machitidwe 1:8 kodi kudzozedwa kwa “chilengedwe chatsopano” kunali kaamba ka chifuno chotani?
KULENGEDWA kwa mwamuna ndi mkazi oyamba pafupifupi zaka zikwi zisanu ndi chimodzi zapita’zo kunali kodabwitsa. (Genesis 1:26-28) Kubadwa kwa “chilengedwe chatsopano” zosakwanira zaka zikwi ziwiri zapita’zo kunali chikhalirebe kodabwitsa kwambiri, kwatanthauzobe kwambiri kwa mtundu wonse wa anthu. Kubadwa’ko kunachitika pa tsiku la Pentekoste wa 33 C.E. pa kubadwa kwa mpingo wa ophunzira a Kristu, iwo onse odzozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu kaamba ka kulengeza ufumu Waumesiya.
2 Yosakwana milungu iwiri tsiku la mu mbiri la Pentekoste limene’lo lisanakwane, Yesu Kristu woukitsidwa’yo anati kwa ophunzira ake:
“Kotero kwalembedwa, kuti Kristu amve zowawa, nauke kwa akufa tsiku lachitatu; ndi kuti kulalikidwe m’dzina lake kulapa ndi kukhululukidwa kwa machimo kwa mitundu yonse, kuyambira ku Yerusalemu. Inu ndinu mboni za izi.” (Luka 24:46-48) “Mudzalandira mphamvu pamene mzimu woyera ufika pa inu, ndipo mudzakhala mboni zanga ponse pawiri m’Yerusalemu ndi m’Yudeya monse ndi Samariya ndi kufikira ku malekezero a dziko lapansi.” Machitidwe 1:8, NW.
3. Kodi gawo logawiridwa limene’lo linali lalikulu motani, ndipo kodi ndi liti pamene opunzira’wo anayamba kuchitiramo umboni ndipo kuyambira kuti?
3 Kodi pakakhala gawo liri lonse logawiridwa lochitiramo umboni lalikulu kwambiri koposa limene’li? Linali la pa dziko lonse. Bwanji ponena za kufikira gawo lonse’li ndi umboni Waumesiya? Kumene’ku kukafunikira nthawi, inde, kuyesayesa kwakhama ndi kolimba mtima. Komabe, mwamsanga mzimu woyera wolonjezedwa’wo utafika pa iwo pa tsiku la Pentekoste iwo anayamba ntchito monga mboni kwa ena pa Yerusalemu, choyamba.
4. Kodi zinthu zinayamba kuchitika motani pa tsiku la Pentekoste limene’lo monga momwe’di Yoweli 2:28, 29 ananeneratu?
4 Zinthu zinachitika monga momwe’di Yoweli 2:28, 29 ananeneratu: ophunzira odzazidwa ndi mzimu’wo anayamba kunenera, ngakhale m’zinenero zachilendo, mozizwitsa! Ayuda zikwi zambiri amene anali m’Yerusalemu kukachita phwando la Pentekoste anasonkhana kudzaona chochitika’cho. Iwo anamva mpingo waung’ono’wo wa ohunzira a Kristu ‘ukulankhula,’ monga momwe iwo ananenera “m’malirime athu zazikulu za Mulungu.”—Machitidwe 2:11.
5. Kodi ndi motani m’mene Petro anagwiritsirira ntchito ‘mfungulo ya ufumu wa kumwamba’ pa tsiku la Pentekoste limene’lo?
5 M’malo mwakuti alongosole chochitika’cho, mtumwi Petro anagwiritsira ntchito “mafungulo a Ufumu Kumwamba” mwa kutsogolera m’kukambira nkhani khamu lofunsa’lo “(Mateayu 16:19) Iye anachitira umboni za Yesu monga Mesiya, uyo wokanidwa ndi kuphedwa ndi atsogoleri Achiyuda koma woukitsidwa pa tsiku lachitatu ndipo tsopano wolemekezedwa pa dzanja lamanja la Mulungu. Ayuda okanthidwa ndi chikumbu mtima’wo tsopano anafunsa kuti: “Amuna inu, abale, Tidzachita chiani?” Yankho la Petro linali lakuti: “Lapani, batizidwani yense wa inu m’dzina la Yesu Kristu kuloza ku chikhululukiro cha machimo; ndipo mudzalandira mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti lonjezano [la Yoweli 2:28, 29] liri kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.”—Machitidwe 2:14-39.
6. Kodi Ayuda olapa’wo amene anabatizidwa anachitikiridwa chiani, ndipo kodi iwo anapulumutsidwa ku chiani?
6 Awo olandira Yesu monga Mesiya kapena Kristu momvera anabatizidwa m’madzi, Motero pa tsiku limodzi limene’lo anthu okwanira zikwi zitatu anaonjezedwa. Yesu Kristu wolemekezedwa’yo anawabatiza ndi mzimu woyera, ndipo iwo anabadwa’nso monga ana auzimu a Mulungu. Iwo anasamutsidwa kuchoka m’pangano la Chilamulo cha Mose kulowa m’pangano latsopano lochitiridwa unkhoswe ndi Yesu Kristu. M’njira imene’yi iwo analabadira chilangizo chofulumira cha Petro cha ‘kudzipulumutsa kwa mbadwo uno wokhotakhota.’ Pochita zimene’zi, iwo anapulumuka ku kubatizidwa ndi moto pa chionongeko cha Yerusalemu m’chaka cha 70 C.E. chochitidwa ndi ozinga Achiroma otsogozedwa ndi Kazembe Tito.—Machitidwe 2:40; Luka 3:16, 17.
7. Kodi odzozedwa’wo anayenera kutsanzira Yesu Kristu m’njira yotani, ndipo kodi kuchitidwa kwa ntchito imene iye anaineneratu kunatsegula khomo la ku chiani kwa okhulupirira?
7 Kuyambira pa tsiku la Pentekoste limene’lo kumkabe m’tsogolo, kudzoza ndi mzimu woyera kunadza pa oonjezerekaonjezereka a awo okhulupirira Yesu monga Mesiya. Adzichitanji tsopano? Monga odzozedwa, iwo anali ndi thayo la kutsanzira chitsanzo cha Yesu Kristu. Kodi iye anachitanji pambuyo pa kudzozedwa kwake pa Mtsinje wa Yordano? Iye anayendayenda m’dziko’lo ndipo analalikira ufumu wa Mulungu. (Mateyu 4:12-17) Kulalikidwa kwa ufumu wa Mulungu sikukalekera pa imfa yake. Masiku owerengeka imfa yake yophedwera chikhulupiriro isanachitike pa Yerusalemu, iye ananereratu chionongeko cha mzinda’wo chochitidwa ndi Aroma koma ananena kuti, ngakhale tsoka la mtundu wonse limene’lo lisanachitike, “mbiri yabwino imene’yi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse.” (Mateyu 24:14-22, NW) Atadza Pentekoste, wotsagana ndi kudzozedwa kwao ndi mzimu woyera, odzozedwa’wo sanataye nthawi m’kuyamba kugwira ntchito! Kulalikira ufumu kumene’ku kunatsegula njira kwa okhulupirira kukhala olowa nyumba limodzi ndi Yesu Kristu mu ufumu wake wakumwamba.
8. Kodi ndi motani m’mene kulalikira Ufumu kunamkera ku Samariya, ndipo limodzi ndi zotulukapo zotani?
8 Chizunzu chachiwawa chinaulika. Ophunzira anabalalitsidwa kuchoka m’Yerusalemu. Koma kubalalika kwa mpingo kumene’ku kunangochititsa kufalikira kwa kulengezedwa kwa Ufumu. Monga momwe kunanenedweratu, kuchitira umboni’ko kunalowetsedwa m’chigawo cha Samariya. Atakakamizidwa kutuluka mu Yerusalemu, wophunzira Filipo anatembenuzira chisamaliro chake kwa Asamariya “Pamene anakhulupirira Filipo wakulalikira Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi dzina la Yesu Kristu, anabatizidwa, amuna ndi akazi.” Pambuyo pake, pa ulendo wa Petro ndi Yohane wa ku Samariya, Asamariya obatizidwa’wo analandira kupyolera mwa atumwi amene’wa mzimu woyera.—Machitidwe 8:1-17.
9. (a) Kodi ndi kutembenuka kosayembekezeredwa kotani pakati pa Ayuda kumene kunachitika tsopano? (b) Kodi ndi motani m’mene Petro anagwiritsirira ntchito yachiwiri ya “zofungulira ufumu wa kumwamba”?
9 Mwadzidzidzi tsopano, zodabwitsa kwambiri! M’tsogoleri wa ozunza akusanduka Mkristu. Saulo wa kuTariso akutembenuziridwa ku Chikristu. Iye akukhala wolengeza wamkulu wa ufumu wa Mulungu wokhala m’manja mwa Yesu Mesiya. (Machitidwe 9:1-30) Dzina lake lakale, Saulo, likusiyidwa ndipo akufikira pa kuchedwa Paulo mtumwi. Pambuyo pa kutembenuzidwa kwapadera kumene’ko, panadza kutembenuka kwa mtundu wina kwapadera. Kunali kutembenuzidwa kwa wa Amitundu wosadulidwa kapena wosakhala Myuda. Zimene’zi zinachitika pamene mzimu woyera unatsogoza mtumwi Petro kugwiritsira ntchito ina ya “mfungulo za ufumu wakumwamba” zimene’zo (Mateyu 16:19) Petro anatero mwa kulalikira m’nyumba ya mkulu wankhondo Wachitaliyana Korneliyo mu Kaisareya. Pa Machitidwe 10:44-48 timawerenga kuti:
“Petro ali chilankhulire, Mzimu Woyera anagwa pa onse akumva mau’wo. Ndipo anadabwa okhulupirira’wo akumdulidwe onse amene anadza ndi Petro, chifukwa pa amitundu’nso panathiridwa mphatso ya Mzimu Woyera. Pakuti anawamva iwo alikulankhula ndi malirime, ndi kum’kuza Mulungu. Pamenepo Petro anayankha, Kodi pali munthu akhoza kuletsa madzi, kuti asabatizidwe awa, amene alandira Mzimu Woyera ngati’nso ife? Ndipo analamulira iwo abatizidwe m’dzina la Yesu Kristu.”
10, 11. (a) Kuchokera ku nyumba ya Korneliyo, kodi kulalikira Ufumu kunafalikira mpaka kuti, ndipo kaamba ka phindu la yani? (b) Ngakhale kuli kwakuti Petro anatsegula njira yolowera m’maiko a Amitundu, kodi ndi motani ndipo n’chifukwa ninji Paulo anam’posa?
10 Kuchokera ku nyumba ya kenturiyo Korneliyo wa Amitundu’yo kulalikidwa kwa mbiri yabwino kunafalikira mpaka “ku malekezero a dziko lapansi.” Kumene’ku kunali kopindulitsa Amitundu kudza’nso kwa Ayuda achibadwidwe.
11 Pamene kuli kwakuti Petro anatsegula njira yolowera m’maiko a Amitundu, mtum’wi Paulo anaposa onse m’kulalikira Mau a Mulungu kwa Amitundu osadulidwa, m’nthawi yake. Iye sanachite manyazi kudzicha “mtumwi wa anthu amitundu [Akunja].” Iye sanachepetse chenicheni chimene’chi. Iye analemekeza utumiki wake ndipo chotero anaulimbikira kwambiri.—Aroma 11:13.
12. Kodi Paulo anafuna kukafika kutali kuti kukalalikira, koma kodi iye anafika pati ku mbali imene’yo ndipo kodi iye anachitanji kumene’ko?
12 Paulo anafuna kutengera mbiri yabwino ngakhale m’Spanya, koma kumva za iye kotsirizira kuli m’kati mwa kubindikiritsidwa kwake m’Roma, Italiya. Ponena za kugwidwa kwake koyamba ndi kubindikiritsidwa kwake m’nyumba yake yobewereka mu Roma, timawerenga za Paulo kuti: “Ndipo anakhala zaka ziwiri zamphumphu m’nyumba yake yobwereka, nalandira onse akufika kwa iye, ndi kulalikira Ufumu wa Mulungu, ndi kuphunzitsa za Ambuye Yesu Kristu ndi kulimbika konse, wosam’letsa munthu.”—Machitidwe 28:30, 31; Aroma 15:24, 28.
KUCHHITIRA UMBONI CHOLENGEDWA CHONSE 70 C.E. ISANAFIKE
13. Chifukwa chakuti iwo anachita mogwirizana ndi kudzozedwa kwao, kodi Paulo akanatha kulembera chiani Akristu mu Kolose, pokwana pafupifupi 60-61 C.E.?
13 Panali Akristu ochuluka amene anatsanzira mtumwi Paulo ndi atumwi ena m’kulalikira mbiri yabwino ya ufumu Waumesiya. Mpingo wobadwa ndi mzimu’wo monga “chilengedwe chatsopano” unadzozedwera kuchita kulalikira kotero’ko. (Yesaya 61:1-3; 2 Akorinto 1:21, 22) Iwo anadzazidwa changu ndipo anapitirizabe kumka nawanditsa mbiri yabwino kopambana pa dziko lapansi kwa ena ochuluka monga momwe kungathekere. Pamenepa, n’kosadabwitsa, kuti pafupifupi m’chake cha 60-61 C.E. kapena zaka zingapo Aroma asanaononge Yerusalemu ndi kachisi wake wokongola’yo mu 70 C.E., mtumwi Paulo anatha kulemba ali m’nyumba yake yakaidi m’Roma kalata yomka kwa Akristu m’Kolose, Asia Minor, ndi kunena kuti, pa nthawi imene’yo: ‘Mbiri yabwino . . . [inali] italalikidwa kale cholengedwa chonse pansi pa thambo; umene ine Paulo ndakhala mtumiki wake.’—Akolose 1:23.
14. Kodi ntchito ya mpingo wa m’zaka za zana loyamba imatumikira monga chitsanzo kwa yani lero lino, polingalira thayo lotani kwa amene’wo lero lino?
14 Kulengezedwa kwa cholengedwa chonse kwa ufumu Waumesiya wa Mulungu kumene’ko kochitidwa ndi mpingo wa m’zaka za zana loyamba wa ophunzira odzozedwa a Kristu kumatumikira monga chitsanzo chabwino kwa mpingo wodzozedwa wa m’zaka zathu za zana la makumi awiri. Mpingo wodzozedwa ndi mzimu umene’wu monga “cholengedwa chatsopano” cha Mulungu, ufunikira kutsiriza kuchitira umboni kwa pa dziko lonse ufumu wa Mulungu wokhazikitsidwa’wo “chisautso chachikulu””chisanadze pa dziko lonse, ndipo Chikristu cha Dziko chonyenga’cho chisanabatizidwe ndi moto wa chionongeko limodzi ndi mbali ina yotsala ya dongosolo iri loipa la zinthu.—Mateyu 24:14-22; NW; Marko 13:10.
UMBONI WA MZIMU WONENA ZA UMWANA
15. Kodi Paulo analemberanji mpingo Wachiroma ponena za umboni wa mzimu, ndipo kodi ndi funso lotani limene tsopano limabuka ponena za awo amene lero lino amayembekezera kupita kumwamba?
15 Kale’lo m’zaka za zana loyamba C.E., olemba Baibulo Achikristu ndi ophunzira anzao sanali okaikira ponena za unansi wao ndi Mulungu ndi thayo lao kwa Iye. Iwo anali’di ndi chikhulupiriro chakuti iwo anali ana auzimu a Mulungu, ndipo iwo anali ndi chiyembekezo cha cholowa chakumwamba. Chotero, mtumwi Paulo asanafike ndi kufika komwe ku Roma, iye anatha, osati mosatsimikizira, kulembera kalata mpingo wa kumene’ko ndi kunena mau achidaliro awa: “Inu munalandira mzimu wa kulandiridwa monga ana, mwa umene ife timapfuula: ‘Abba Atate!’ Mzimu uwo wokha umachitira umboni ndi mzimu wathu kuti ife tiri ana a Mulungu. Pamenepa, ngati, ife tiri ana, ife tiri’nso olowa nyumba ogwirizana limodzi ndi Kristu, malinga ngati tibvutika limodzi kuti tikalemekezedwe’nso limodzi.” (Aroma 8:15-17, NW) Kodi ndani lero lino, amene amanena kuti akuyembekezera kupita kumwamba, ali ndi umboni wa mzimu wa Mulungu wotero’wo limodzi ndi wa mzimu wa iye mwini?
16. Kodi ndi mtundu wotani wa kachitidwe umene unalipo pakati pa mzimu wa Mulugu ndi mzimu wa mpingo Wachikristu wa m’zaka za zana loyamba?
16 Ndithudi mzimu wa Mulungu sukanachita umboni wotero’wo kwa wongodzicha kukhala Mkristu amene sali kwenikweni wolowa nyumba wa Mulungu ndi wolowa nyumba limozi ndi Yesu Kristu. Kaamba ka kachitidwe kali konse pamakhala yankho. Yankho’lo lingakhale kaya lobvomereza kapena lotsutsa, loipidwa. Mu Aroma 8:15-17, mtumwi Paulo amanena za yankho lobvomereza. Iye amalongosola kachitidwe kogwirizana pakati pa mzimu wa Mulungu. Tsopano, chabwino, kodi ndi motani m’mene mzimu wa Mulungu unachitirira umboni ndi mzimu wa ziwalo za mpingo Wachikristu woyamba wa m’zaka za zana loyamba, “chilengedwe chatsopano” chimene’cho?
17. (a) Kodi mpingo wa m’zaka za zana loyamba unatsutsa umboni wa mzimu wa Mulungu kwa iwo kupyolera mwa atumiki ake ouziridwa? (b) Chotero kodi ndi motani m’mene mpingo wa mu Tesalonika unalingalirira uthenga woperekedwa ndi Paulo?
17 Ngati mzimu wa Mulungu umachitira umboni kwa ife ponena za kudziwika Kwachikristu ndi kugwirizana kwathu ndi Mulungu ndi makonzedwe ake kaamba ka ife, pamenepo ife tifunikira kubvomerezana ndi mzimu umene’wo ndipo osati kuutsutsa. Chotero, pamene Akristu a m’zaka za zana loyamba anali ndi kalata yochokera kwa mtumwi kapena wophunzira wouziridwa wa Kristu yowerengeredwa ku mpingo umene iwo anali ziwalo zake zobatizidwa, iwo analandira zimene kalata imene’yo inanena kwa iwo ndi ponena za iwo ponena za kaimidwe kao, mathayo ao, ziyembekezo zao za m’tsogolo m’kakonzedwe ka Mulungu. Iwo anazindikira kuti mzimu wa Mulungu unali kugwira ntchito mwa atumwi ndi ophunzira okhala ndi ulamuliro otero’wo ndi kuti uwo unachita ndi kulemba mwa njira ya zipangizo zaumunthu. Kalata ya mtumwi Paulo ku mpingo Wachikristu wa m’zaka za zana loyamba m’Tesalonika, Makedoniya, ikuchitira umboni chenicheni chimene’chi. Iwo anadziwa choonadi chake pamene Paulo analemba kuti: “Pakulandira mau Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amene’nso achita mwa inu okhulupirira.”—1 Atesalonika 2:13.
18. Kuti akhale onena chimodzi, kodi ndi motani m’mene Akristu Achitesalonika amene’wo anayenera kulandirira mau olembedwa a Paulo, ndipo kodi n’chifukwa ninji Mulungu anawasankha, malinga ndi zimene Paulo ananena?
18 Chotero kukakhala kogwirizana kwa okhulupirira amene’wa kulandira’nso mau olembedwa a Paulo kukhala mofananamo “mau a Mulungu.” M’kalata imene’yi Paulo analembera kalata okhulupirira Achitesalonika ponena za ‘kuwasankha’ kwa Mulungu. Kodi n’chifukwa ninji iwo ‘anasankhidwa’? “Kuti Uthenga Wabwino wathu sunadza kwa inu m’mau mokha, komatu’nso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m’kuchuluka kwakukulu; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu chifukwa cha inu. Ndipo munayamba kukhala akutsanza anthu, ndi a Ambuye, m’mene mudalandira mau’wo m’chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha Mzimu Woyera.”—1 Atesalonika 1:4-6.
19. Kodi kuperekedwa kwa mphatso za mzimu mwa njira ya atumwi kukatanthauza unansi wotani wa olandira’wo kwa Mulungu?
19 Iwo anadziwa kuti, mwa njira ya mzimu woyera, Mulungu walankhula kwa anthu ake osankhika m’nthawi za Chikristu chisanakhale. Mofananamo, m’zaka zao za iwo eni za zana oyamba C.E., Mulungu akanatha kulankhula mwa njira ya mphamvu yogwira ntchito imodzimodzi’yo kupyolera mwa atumwi ouziridwa a Yesu Kristu. Ndipo’nso, Mulungu anali kugwiritsira ntchito atumwi amenewo’wo kupereka kwa okhulupirira obatizidwa’wo mphatso zosiyanasiyana za mzimu woyera. Ndithudi kulandiridwa kwa mphatso zimene’zo kukasonyeza kwa olandira’wo kuti iwo apangidwa kukhala ana auzimu a Mulungu.—Machitidwe 8:15-18; 19:2-6.
20. Kodi ndi motani m’mene, kupyolera mwa makalata a olemba Baibulo Achikristu, mzimu woyera unali kuchitirira umboni ku mpingo wa m’zaka za zana loyamba kuti unansi wao kwa Mulungu unali wa mtundu wapadera?
20 Kodi atumwi amene’wo ndi olemba Baibulo ena Achikristu anali kuika pamaso pa okhulupirira obatizidwa’wo chiyembekezo cha pa dziko lapansi, chiyembekezo cha kukhala ana a Atate Wosatha, Yesu Kristu, ndi kukhala pa paradaiso wa pa dziko lapansi kosatha? Ai! Iwo anali kuika pamaso pa awo amene iwo anali kuwalalikira ndi kuwalembera chiyembekezo pa nthawi imene’yo cha awo obalidwa monga ana a Mulungu, ana a Yehova. (Yesaya 9:6, 7) M’zolembedwa zouziridwa Zachikristu ophunzira a pa nthawi’yo anatsimikiziridwa kuti iwo anali ndi chiitano cha ku ufumu umene unali wakumwamba ndi kuti chiyembekezo chao chinali chija cha kukhala olowa nyumba limodzi ndi Yesu Kristu kumwamba. (Akolose 1:13; 1 Akorinto 1:26-31; (2 Petro 1:10, 11) Chinthu chimodzi chokha chinaikidwa pamaso pao; iwo sanasiyidwe m’chikaikiro chiri chonse. M’njira imene’yi mzimu woyera unali kichitira umboni kwa ophunzira a m’zaka za zana loyamba wakuti iwo anali ana a Mulungu, olowa nyumba a Mulungu. Zimene’zi zinatanthauza kuti, pa nthawi imodzimodzi’yo, iwo anali olowa nyumba limodzi ndi Yesu Kristu wolemekezedwa’yo.
21. Kodi ndi motani mzimu wa Akristu a m’zaka za zana loyamba limene’lo unachitira ndi mzimu wa Mulungu wochitira umboni’wo, limodzi ndi zotulukapo zotani kwa iwo?
21 Chisonkhezero cha iwo eni cha m’kati, mzimu wao wa iwo eni, unabvomereza mogwirizana ku umboni woperekedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu umene’wo. Mzimu wa Atate wakumwamba unali kuwafulumiza ndi kuwalimbikitsa iwo monga ana ake auzimu ndi olawa nyumba. Iye anika mwa iwo, osati lingaliro la umwana kwa atate ao a pa dziko lapansi, koma lingaliro la umwana kwa Atate wao wakumwamba, umwana wauzimu.
22. (a) Kodi Ayuda opangidwa kukhala Akristu’wo sanadzionenso kukhala ali pansi pa pangano lotani, mu mkhalidwe wotani? (b) Moyankha mzimu wa Mulungu, kodi ndi motani m’mene mzimu wa Akristu unawasonkhezerera kusonyeza kuti iwo anali ana auzimu a Mulungu?
22 Ayuda kapena Aisrayeli opangidwa kukhala Akristu’wo sanalingalire’nso kuti iwo anali akapolo okhala pansi pa pangano la Chilamulo cha Mose ndi kumayembekezerabe Mesiya. Iwo anaona, iwo anadziwa kuti iwo anali ana auzimu a Mulungu amene iwo anam’lambira mogwirizana ndi pangano latsopano. Mzimu wa iwo eni, mphamvu yosonkhezera imene inatuluka m’mitima yao, inawasonkhezera kuchitapo kanthu pa nchito za mzimu wa Mulungu. Onse pamodzi, monga ana, iwo anapfuula kwa Mulungu kuti, “Abba, Atate!” Malalamulo a Atate wao kaamba ka ana ake auzimu iwo anawagwiritsira ntchito kwa iwo eni. Nchito yake yoperekedwa kwa ana ake iwo anaichita mwachikondi. Malonjezo ake akumwamba kwa ana ake auzimu iwo anawalandira ndipo anayesayesa kuwatsimikizira kukhala oyenerera kukwaniritsidwa kwa iwo. Chiyembekezo chakumwamba chimene iye anachiika pamaso pa ana ake iwo anachisunga, ndipo chiyembekezo chimene’chi iwo amayesayesa kukhala ndi moyo mogwirizana nacho. Mofunitsitsa iwo anabvutika ndi kuchitiridwa moipa ndi dziko lino.
23. Kodi iwo anali ofunitsitsa kubvutikira chiyembekezo chotani limodzi ndi Kristu ndi kufa yofanana ndi imfa yake?
23 Iwo anadziwa kuti iwo anayenera kukhala ana olemekezedwa a Mulungu limodzi ndi Yesu Kristu, “malinga ngati tibvutika limodzi.” (Aroma 8:17, NW) Chotero iwo anali ofunitsitsa ku bvutika kaamba ka kukhala ndi moyo mobwirizana ndi chiyembekezo chakumwamba. Iwo analandira chenicheni chakuti iwo ayenera kufa mofanana ndi Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, m’malo mwakuti akhale ndi phande m’chifanefane cha chiukiriro chake.—Aroma 6:5-8.
24. (a) Kodi mzimu wao ndi mzimu wa Mulungu unagwirizana mu umboni wogwirizana pa chenicheni chotani? (b) Kodi mapemphero ndi miyoyo yao zinagwirizanitsidwa ndi chiyembekezo chotani, ngakhale mpaka kufika ku chotulukapo chotani?
24 M’jira imene’yo ana auzimu a Mulungu a m’zaka za zana loyamba amene’wo anagwirizana ndi mzimu wake woyera mu umboni wogwirizana wakuti iwo anali ana a Mulungu, mwa kubadwa’nso ndipo limodzi ndi cholowa chosungidwira iwo kumwamba. Chifukwa cha chimene’cho mzimu wa iwo eni unagwira ntchito monga mphamvu yosonkhezera m’miyoyo yao kotero kuti agwirizanitse mapemphero ao ndi Atate wao wakumwamba mogwirizana kotheratu ndi umboni umene mzimu Wake ukupereka kwa iwo ndi wosasemphana nawo. Iwo anagwirizanitsa Malemba amene amanena za cholowa chao chakumwamba ndi mapemphero ao kwa Mulungu. Mapemphero otero’wo anawalitsa chiyembekezo chao cha kulowa m’cholowa chakumwamba. Chotero iwo anakhala ndi moyo, kulingalira, kulankhula ndi kuchita mogwirizana ndi mapemphero ao ndi chiyembekezo chao. Mapemphero ao anawalimbikitsa kupirira chiyeso ndi chizunzo m’malo mwakuti apeze kaimidwe kobvomerezeka ndi Mulungu; ndipo iwo anadziwa kuti kaimidwe kobvomerezeka kamene’ka ndi Iye kamakulitsa chiyembekezo chimene sichidzalepheretsedwa. Iwo anadziwa kuti, m’malo mwakuti afikire chiyembekezo chao chakumwamba, iwo ayenera kudzitsimikizira kukhala “okhulupirika kufikira imfa.”—Aroma 5:3-5; Chibvumbulutso 2:10.
25. Kodi n’chifukwa ninji zapita’zo ziyenera kutumikira monga chitsogozo kwa Mkristu wodzipereka ndi wobatizidwa m’kutsimikizira unansi wake kwa Mulungu, makamaka kuyambira m’ngululu ya 1935 C.E.?
25 Zonse zapamwambapo’zo ziyenera kutumikira monga chitsogozo lero lino kaamba ka kuti Akristu odzipereka ndi obatizidwa atsimikizire kaya ngati mzimu woyera wa Mulungu ukuchitira umboni limodzi ndi mzimu wao kuti iwo ali ana Ake auzimu ndi olowa nyumba ake, kudza’nso olowa nyumba limodzi ndi mzimu wao kuti iwo ali ana Ake auzimu ndi olowa nyumba ake, kudza’nso olowa nyumba limodzi ndiYesu Kristu mu ufumu wake wakumwamba. Zimene’zi ziyenera kukhala choncho, makamaka chiyambire m’ngululu ya 1935 C.E. Kodi n’chifukwa ninji kuyambira pa nthawi imene’yo? Chifukwa chakuti pa nthawi imene’yo “khamu lalikulu” lolongosoledwa m’Chibvumbulutso 7:9-17 linalongosoledwa kukhala kagulu ka pa dziko lapansi kamene ‘sikakubadwa’nso.’ M’malo mwake, kaika pamaso pake chiyembekezo cha kupulumuka”chisautso chachikulu”cha dziko lapansi chimene chiri patsogolo’pa ndipo chikupulumuka kulowa m’dongosolo latsopano lolungama la Mulungu, kukasangalala kumene’ko ndi paradaiso wa pa dziko lapansi wokhala pansi pa ufumu wakumwamba wa Yesu Kristu ndi olowa nyumba ake144, 000. (Luka 23:43) Mwa kukhala omvera ku Ufumu’wo ndi kutsimikizira kudzipereka kwao kwa mfumu ya m’chilengedwe chaponseponse cha Yehova Mulungu pansi pa chiyeso chotsirizira, iwo satofunikira kufa m’thupi kuchokera pa dziko lapansi. Iwo alo a “nkhosa zina” zimene Mbusa Wabwino Yesu Kristu anazinena mu Yohane 10:16.
MZIMU WOYERA MONGA WOPEMPHERERA
26. Malinga ndi kunena kwa Aroma 8:23-27, kodi ndi ntchito ina yotani imene mzimu woyera umachitira “oyera mtima’wo”?
26 Kuphatikiza pa kukhala wochitira umboni ana auzimu a Mulungu, mphamvu yogwira ntchito yoyera imene’yi imagwira ntchito ina. Mtumwi Paulo akusonyeza ntchito imene’yi m’kalata yake yolembera mpingo wa mu Roma, umene, Paulo akuti, unali ndi Akristu “oitanidwa kuti akhale oyera mtima,” amene’wa akumakhala’nso “olowa nyumba; “inde, olowa nyumba ake a Mulungu, ndi olowa anzake a Kristu.” (Aroma 1:7; 8:16, 17) Paulo akulemba kuti:
“Ndipo si chotero chokha, koma ife tomwe, tiri nazo zoundukula za Mzimu, inde ife’nso tibuula m’kati mwathu, ndi kulindirira umwana wathu, ndiwo chiomboledwe cha thupi lathu. Pakuti ife tinapulumutsidwa ndi chiyembekezo: koma chiyembekezo chimene chioneka si chiri chiyembekezo ai; pakuti ayembekezera ndani chimene achipenya? Koma ngati tiyembekezera chimene sitichipenya, pomwepo tichilindirira ndi chipiriro.
“Ndipo momwemo’nso Mzumu athandiza kufoka kwathu; pakuti chimene tizipempha monga chiyenera, sitidziwa; koma Mzimu mwini atipempherera ndi zobuula zosatheka kuneneka; ndipo Iye amene asanthula m’mitima adziwa chimene achisamalira Mzimu, chifukwa apempherera oyera mtima monga mwa chifuno cha Mulungu.”—Aroma 8:23-27.
27. Kodi ndi m’mikhalidwe yotani imene Akristu amafuna mzimu woyera monga wodandaulira?
27 Mogwirizana ndi zimene’zi mau a Miyambo 13:12 ali oyenerera kwambiri: “Chiyembekezo chozengereza chidwalitsa mtima.” M’kati mwa chilengedwe chaumunthu chomabuula chimene’chi, Akristu amene ali ana auzimu a Mulungu akuyembekezera chimasuko chao ku thupi lopanda ungwiro laumunthu ndi kulowa kwao m’cholowa chao chakumwamba. Nthawi zina kumakhala kobvuta kwa iwo kutulutsa za kukhosi kwao m’pemphero kwa Mulungu, osadziwa kwenikweni chochipempha m’mikhalidwa yotsendereza. Panopa ndipo pamene iwo amafunikira wopempherera, ndiko kuti, mzimu woyera wa Mulungu, monga wopembedzera.
28, 29. (a) Ponena za olemba a Malemba Achihebri, kodi n’chifukwa ninji kuli monga ngati kuti mzimu woyera unali kulankhula ndi kulemba? (b) Kodi ndi motani m’mene olemba Baibulo Achihebri amene’wa aliri poyerekezera ndi ziwalo za mpingo Wachikristu ponena za malingaliro ndi zofooka?
28 Mtumwi Paulo amanena kuti “ife tomwe,” ndiko kuti, Paulo ndi abale ake Achikristu amene abadwa ndi mzimu wa Mulungu, “tiri nazo zoundukula za mzimu.” (Aroma 8:23) Paulo pano akutanthauza kukhala ndi mphamvu yogwira ntchito yoyera yosaoneka ya Mulungu. Mphamvu yogwira ntchito imene’yi yasonkhezera anthu kulankhula ndipo’nso kulemba zimene iwo alankhula. Kunali monga ngati kuti mzimu weniweni unali kulankhula ndi kulemba. Mogwirizana ndi chenicheni chimene’chi, timawerenga kuti:”Palibe chinenero cha lembo chitanthauzidwa pa chokha, pakuti kale lonse chinenero sichinadza ndi chifuniro cha munthu; koma anthu a Mulungu, ogidwa ndi Mzimu Woyera, analankhula.” (2 Petro 1:20-21) Malemba Achihebri ouziridwa amene anagwidwa mau ndi Paulo mochirikiza Chikristu analembedwa ndi zolengedwa zaumunthu chabe. Iwo anali ndi malingaliro ndi zofooka zakuthupi zofanana ndi zija zimene ziwalo za mpingo Wachikristu ziri nazo. Chotero tingaone kukhala ogwirizana nawo m’mbali zimene’zi.
29 “Ife’nso tiri anthu a mkhalidwe wathu umodzimodzi ndi wanu.” Anatero mtumwi Paulo ndi mmishonale mnzake Barnaba kwa akunja olambira mafano amene molakwa anawaona kukhala oposa anthu, milungu yoonekera m’thupi lanyama kwa anthu.—Machitidwe14:15.
30. (a) Kodi zolembedwa za Baibulo ziri kwenikweni mau a mphamvu yotani ndipo chotero za phindu lotani? (b) Kodi mikhalidwe ndi zochitika za anthu a m’Baibulo zinalowetsamo nbali zotani zofunikira chithandizo choposa cha anthu?
30 Zolembedwa za Baibulo zouziridwa’zo zinali kweni kweni mau a mzimu woyera wa Mulungu. Chifukwa cha chimene’cho zolembedwa zouziridwa zimene’zo ‘zipindulitsa pa chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iri yonse yabwino.’ (2 Timoteo 3:16, 17) Zophatikizidwa m’zolembedwa ‘zopindulitsa’ pali mapemphero operekedwa kwa Mulungu, osati ndi olemba Baibulo okha, koma’nso ndi anthu ena amene anali odzipereka kwa Yehova Mulugu. Pansi pa mikhalidwe ya mtundu uli wonse mapemphero amene’wo aperekedwa kwa Mulungu. Anthu amene’wo okhala ndi zofooka zofala kwa anthu tonsefe anaona zitsenderezo za mikhalidwe yapadera ndi mikhalidwe yoopsya imene inalipo. Mikhalidwe yao yosowa inali yosiyanasiyana kwambiri kuti ifanane ndi mikhalidwe imene Akristu ona ngakhale lero lino nthawi zina amadzipezamo. Zimene’zi zimafikira kukhala zochitika m’zimene choposa chithandizo chaumunthu chikufunika. Pamenepa, kodi ndi motani m’mene tiyenera kupempherera?
31, 32. (a) Motero kodi Akristu ali operewera ku mlingo wotani ponena za m’mene angapempherere? (b) Pamenepa, kodi ndi motani m’mene mzimu umene unauzira zolembedwa za Baibulo umadandaulira Akristu, ndipo kodi ndi motani m’mene Mulungu amamvera ndi kuyankha?
31 Mu kupanda chithandizo ndi kusokonezeka kwathu “ife’nso tibula m’kati mwathu.” (Aroma 8:23) Sitimadziwa kwenikweni m’mene tingapempherere kapena kupembedzera Mulungu ndi ziganizo oyenera kapena mau oti tinene kwa Wothandiza wathu wakumwamba. Komabe, Mulungu amazindikira mkhalidwe wathu ndipo amazindikira chenicheni chimene moonadi tikafuna kukhala nacho.
32 Ngati ife enife sitingathe kuumba mapemphero, chabwino, mapemphero aumbidwa kale kaamba ka ife. Kuti? M’Malemba Oyera olosera amene anauziridwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. Mulungu amadziwa bwino kwambiri mapemphero olembedwa m’Mau ake. Iye amadziwa “tanthauzo” lao. Iye amadziwa amene amatiyenerera ife amene timafuna kupemphera moyenera. Chotero Mulungu amalingalira mapemphero oyenera olembedwa amene’wo monga ngati kuti anali kuperekedwa ndi Akristu omabuula iwo eni’wo. Mapemphero otero’wo sanaperekedwe ndi Akristu osowa iwo eniwo, koma Mulungu amamva monga ngati kuti mzimu woyera unali kum’dandaulira mogwirizana ndi mapemphero ouziridwa ndi mzimu amene ali m”Baibulo. Mosakaikira iye amayankha m’njira yofanana ndi m’mene iye anayankhira pemphero olembedwa lakale’lo, m’nthawi za Baibulo.
33. Chotero kodi ndi motani m’mene mzimu umalowetsedwera, m’kuthandiza kaamba ka zofooka zathu, ndipo limodzi ndi chipambano chotani?
33 Popeza kuti mzimu woyera unauzira kulembedwa kwa mapemphero oyambirira m’mene kudandaulira Mulungu kukuchitidwa, kungathe kunenedwa kuti mzimu ukudandaulira “monga mwa chifuno cha Mulungu.” Mwa njira imene’yi “mzimu athandiza kufoka kwathu.” (Aroma 8:26, 27) Mulungu samalephera kuyankha zodandaula zotero zochitidwa ndi mzimu wake woyera monga wopempherera.
34. Kodi tikupezanji ponena za chimene chikunenedwa m’mapemphero olembedwa m’Baibulo, ndipo kodi n’chifukwa ninji ‘zobuula zathu zosaneneka, siziri zopanda pake?
34 Chotero si kodabwitsa kuti, ngati Akristu apenda mapemphero ouziridwa amene alembedwa m’Masalmo nd mbali zina za Malemba Oyera iwo adzafika pa mapemphero amene amanena monga momwe’di iwo analingalirira, mapemphero amene amanena kwenikweni chimene iwo anafuna kupempha kwa Mulungu kaya kaamba ka iwo eni’wo kapena gulu monga mpingo Wachikristu. Iwo amasonkhezeredwa m’katikati mwa mitima yao pa kupeza mapemphero otero’wo amene anachititsidwa ndi mzimu woyera kunena zinthu ndi kuyenerera kwa ndendende kotero’ko. “Zobuula” zao za iwo eni sizinakhale zopanda pake, sizinamvedwe molakwa kapena kunyalanyazidwa. Chotero kuchokera m’Malemba ouziridwa ndi mzimu iwo amafikira pa kudziwa kachulidwe ka mau kabwino kamene “mzimu” wawadandaulira nawo pamaso pa Mulungu. Iwo eni’wo amalimbikitsidwa m’chikhulupiriro cholongosoledwa ndi mtumwi Paulo pamene iye akupitiriza kunena kuti: “Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino.”—Aroma 8:22.
35, 36. (a) Kodi ndi mphamvu yotani imene ikugwira ntchito mwamphamvu pamene Mulungu akupangitsa ntchito zake zonse kugwirizana kaamba ka om’konda? (b) Kodi ndi chimasuko chotani chimene chiri pafupi kaamba ka “chilengedwe chatsopano,” ndipo kodi chimene’chi chimasonyeza’nso chiani kaamba ka mtundu wa anthu womabuula’wo?
35 Wogwira ntchito mwamphamvu mogwirizanitsa ntchito zonse za Mulungu kaamba ka ubwino wamuyaya wa awo amene amakonda Mulungu ndiwo mzimu wake woyera. Ha, ndi makonzedwe abwino kwambiri chotani nanga m’mene mphamvu yoyera yogwira ntchito yochokera kwa Mulungu iriri! Mzimu wa Mulungu, umene umadzisonyeza mwamphamvu kwambiri kupyolera mwa Baibulo louzidwa, uli wamphamvu kopambana koposa mkombero wa pemphero liri lonse lachikunja kapena bukhu lina liri lonse la mapemphero lolembedwa ndi atsogoleri achipembedzo a Chikristu cha Dziko okhala ndi mapemphero a mau oumbidwa mwapadera kuti awerengedwe kaamba ka zochitika zapadera, mikhalidwe kapena anthu.
36 Chilengedwe chaumunthu chakale cha mtundu wa anthu chiribe mzimu umene’wu, ndipo m’zaka zino za zana la makumi awiri chikubuula koposa kale lonse, chikumafunafuna m’njira ina kumasulidwa ku ukapolo wa chibvundi pansi pa dongosolo lakale la zinthu. Koma zaka mazana khumi ndi asanu ndi anai zapita’zo “chilengedwe chatsopano” cha Mulungu chinakhala ndi moyo ndipo chinayamba kugwira ntchito. Icho chinatero pansi pa mphamvu yopereka nyonga ya mzimu woyera wa Mulungu, imene inayamba kutsanulidwa pa tsiku la phwando la Pentekoste wa 33 C.E. Zosaphula kanthu zinakhala zoyesayesa za aunyinji wa chilengedwe chakale chaumunthu kuononga “chilengedwe chatsopano” cha Mulungu, mpingo Wachikristu wabadwa ndi mzimu. Lero lino “chilengedwe chatsopano” chimene’cho chikuyandikira nthawi yake ya chimasuko ku thupi lake la pa dziko lapansi la chibvundi. Kuyandikira kwa chimasuko chake chaulemerero kumasonyeza ubwino waukulu kwa mtundu wonse wa anthu. Kumasonyeza kuti kulanditsidwa kjwa mtundu wa anthu womabuula’wo kuli’nso pafupi. Kumasonyeza kuti tsopano pali dongosolo latsopano lolungama lochirikizidwa ndi mzimu woyera wa Mulungu.