NKHANI 83
Malinga a Yerusalemu
TAONANI ntchito imene ikuchitika pano. Aisrayeli ali otanganistidwa kumanga malinga a Yerusalemu. Pamene Mfumu Nebukadinezara anaononga Yerusalemu zaka 152 zapita’zo, iye anagwetsa malinga awa naocha zitseko za zipata za mzinda’wo. Aisrayeli sanamange’nso malinga’wo pamene iwo anangofika kumene kuchokera ku Babulo.
Kodi muganiza kuti anthu’wo anali kumva bwanji kukhala muno kwa zaka zonse’zi popanda malinga ozungulira mzinda’wo? Iwo sanaone kukhala osungika. Adani ao akanadza mosabvuta n’kuwaukira. Koma tsopano mwamuna’yu Nehemiya potsirizira akuthandiza anthu kumanga’nso malinga’wo. Kodi mukudziwa kuti Nehemiya ndani?
Iye ndi Muisrayeli amene akudza kuchokera ku mzinda wa Susani, kumene Mordekai ndi Estere amakhala. Iye anagwira ntchito m’mphala ya mfumu, chotero iye angakhale bwenzi labwino la Mordekai ndi Mkazi wa Mfumu Estere. Koma Baibulo silimanena kuti Nehemiya anagwirira ntchito mwamuna wa Estere, Mfumu Ahaswero. Iye anagwirira ntchito mfumu yotsatirapo, Mfumu Aritasasta.
Pajatu, Aritasasta ndi mfumu yabwino imene inapatsa Ezara ndalama zonse zobwerera nazo ku Yerusalemu kukakonzera kachisi wa Yehova. Koma Ezara sanamange malinga a mzinda ogamuka’wo. Tiyeni tione m’mene zinachitikira kuti Nehemiya anachita ntchito’yi.
Papita zaka 13 chiyambire pamene Aritasasta anapatsa Ezara ndalama zokakonzera kachisi. Nehemiya tsopano ndi woperekera chikho wa Mfumu Aritasasta. Izi zikutanthauza kuti amapatsira mfumu vinyo wake, ndi kutsimikizira kuti palibe ali yense akum’patsa mankhwala akupha. Ndi ntchito yofunika kwambiri.
Eya, tsiku lina mbale wa Nehemiya Hanani ndi amuna ena a ku Israyeli akudza kudzaona Nehemiya. Iwo akumuuza za bvuto limene Aisrayeli akukumana nalo, ndi m’mene malinga a Yerusalemu aliri chigamukire. Izi zikupangitsa Nehemiya kukhala wachisoni kwambiri, ndipo akupemphera kwa Yehova za izo.
Tsiku lina ikumuona ali wachisoni kwambiri, nifunsa kuti: ‘Kodi n’chifukwa ninji ukuoneka kukhala wachisoni kwambiri?’ Nehemiya akuiuza kuti n’chifukwa chakuti Yerusalemu ali mu mkhalidwe woipa ndipo malinga ake ngogamuka. Mfumu inafunsa kuti, ‘Ukufunanji?’
‘Ndiloleni ndimke ku Yerusalemu,’ akutero Nehemiya, ‘kuti ndikamange’nso malinga’wo.’ Mfumu’yo iri yokoma mtima kwambiri. Iyo ikunena kuti Nehemiya angamuke, ndipo ikum’thandiza kupeza matabwa okamangira. Posakhalitsa atangofika ku Yerusalemu, akuuza anthu za malinganizidwe ake. Iwo akukonda lingaliro’lo, nati: ‘Tiyeni tiyambe kumanga.’
Adani ao poona malinga akukwera, akuti: ‘Tiyeni timke tikawaphe, ndi kuletsa kumanga’ko.’ Koma Nehemiya akumva za izi, ndipo akupatsa antchito’wo malupanga ndi mikondo. Nati: ‘Musaope adani athu. Menyerani nkhondo abale anu, ana anu, akazi anu ndi nyumba zanu.’
Anthu’wo ali olimba mtima kwambiri. Akukhala ndi zida zao chire usana ndi usiku, napitirizabe kumanga. Chotero m’masiku 52 okha malinga’wo akutsirizidwa. Tsopano anthu’wo akuona kukhala osungika mu mzinda’wo. Nehemiya ndi Ezara akuphunzitsa anthu’wo chilamulo cha Mulungu, ndipo anthu’wo ali achimwemwe.
Koma zinthu siziri chimodzi-modzi monga momwe zinaliri Aisrayeli asanatengedwe ukapolo kumka ku Babulo. Anthu’wo akulamuliridwa ndi mfumu ya Perisiya ndipo ayenera kum’tumikira. Koma Yehova walonjeza kuti iye adzawatumizira mfumu yatsopano, ndi kuti mfumu’yi idzadzetsa mtendere kwa anthu’wo. Kodi mfumu’yi ndani? Kodi ndi motani m’mene iyo ikadzetsera mtendere pa dziko? Pafupi-fupi zaka 450 zinapitapo kali konse kasanamvedwe ponena za izi. Ndiyeno pali kubadwa kwa mwana wofunika. Koma iye n’nkhani ina.