Mutu 9
Mphamvu ya Chiyembekezo cha Chiukiriro
1. Kodi nziyembekezo zodabwitsa zotani zimene zimatheketsedwa ndi chiukiriro?
POPANDA chiukiriro, palibe chiyembekezo cha moyo uliwonse wamtsogolo kaamba ka anthu akufa. Koma Yehova, mwakukoma mtima kwachifundo, watsegula mwayi wamtengo wapatali kaamba ka mabiliyoni amene anafa kusangalala ndi moyo wamuyaya. Chifukwa chachimenecho, ifenso tiri ndi chiyembekezo chokondweretsa mtima cha kugwirizananso ndi okondedwa amene anagona mu imfa.—Yerekezerani ndiMarko 5:35, 41, 42; Machitidwe 9:36-41.
2. (a) Kodi chiukiriro chatsimikizirira kukhala chofunika m’njira zotani m’kuchitidwa kwa chifuno cha Yehova? (b) Kodi ndiliti makamaka pamene chiyembekezo cha chiukiriro chiri magwero odabwitsa opereka nyonga kwa ife?
2 Chifukwa cha chiukiriro Yehova angakhoze, popanda chivulazo chosatha pa atumiki ake okhulupirika, kulola Satana kufika mpaka, pamene angafike m’kuyesa kutsimikizira chinenezo chake cha njiru chakuti, “Khungu kulipa khungu, inde munthu adzapereka zonse ali nazo kuombola moyo wake.” (Yobu 2:4) Chifukwa chakuti Yesu anaukitsidwa kuchokera kwa akufa anali wokhoza kupereka mtengo wansembe yake yaumunthu pamaso pa mpando wachifumu wakumwamba wa Atate wake, limodzi ndi phindu lopulumutsa moyo kwa ife. Kupyolera mwa chiukiriro awo amene ali olowa nyumba anzake a Kristu amagwirizanitsidwa naye mu Ufumu wakumwamba. Ndipo kwa ife tonse amene tiri ndi chikhulupiriro, chiukirirocho chiri magwero anyonga yoposa yachibadwa pamene tikomana ndi ziyeso zimene zimatichititsa kuyang’anizana ndi imfa.
Chifukwa Chake Chiri Chofunika Kwambiri ku Chikhulupiriro Chachikristu
3. (a) Kodi chiukiriro chiri “chiphunzitso choyamba” mulingaliro lotani? (b) Kodi chiukiriro chimatanthauzanji kudziko lonseli?
3 Monga momwe kwalongosoledwera pa Ahebri 6:1, 2, chiukiriro ndicho, “chiphunzitso choyambirira,” chiri mbali ya maziko a chikhulupiriro chimene ngati tiribe sitingakhale konse Akristu okula msinkhu. Koma nchosadziwika m’maganizo mwa dziko lonse. Chifukwa cha kupanda mkhalidwe wauzimu, anthu owonjezerekawonjezereka amakhala ndi moyo molondola chikondwerero. Amangowona moyo uno kukhala weniweni. (1 Akor. 15:32) Awo amene amamamatira ku zipembedzo zamakolo, ponse pawiri mkati ndi kunja kwa Dziko Lachikristu, amalingalira kuti ali ndi moyo wosakhoza kufa, umene ungachititse chiukiriro kukhala chosafunikira. Aliyense amene amayesayesa kugwirizanitsa mfundo ziwiri zimenezi amapeza kukhala kosokoneza maganizo m’malo mwa kukhala kopereka chiyembekezo. Kodi ndimotani mmene tingathandizire awo amene ali ofunitsitsa kumvetsera?—Mac. 17:32.
4. (a) Munthu asanazindikire chiukiriro, kodi nchiyani chimene tifunikira kukambitsirana naye? (b) Kodi ndimalemba ati amene mukagwiritsira ntchito kulongosola chimene moyo uli? Mkhalidwe wa akufa? (c) Koma bwanji ngati munthu wina agwiritsira ntchito matembenuzidwe a Baibulo amene amawonekera kukhala akuphimba chowonadi chopezedwa m’malemba amenewo?
4 Anthu otere asanazindikire mmene makonzedwe a chiukiriro aliri odabwitsa, afunikira kumvetsetsa chimene moyo uli ndi mkhalidwe wa akufa. Kawirikawiri, malemba owerengeka chabe ali okwanira kuchititsa nkhani izi kumvekera kwa munthu wofunafuna chowonadi. (Gen. 2:7; Ezek. 18:4; Sal. 146:3, 4) Koma matembenuzidwe ena amakono ndi mabukhu a ndemanga za Baibulo amaphimba chowonadi chimenechi. Chotero kungakhale kofunikira kupenda mawu ogwiritsiridwa ntchito m’zinenero zoyambirira za Baibulo.
5. Kodi ndimotani mmene mukanathandizira munthu wotero kuzindikira chimene moyo uli?
5 Makamaka New World Translation iri (yofunikadi kwambiri m’kuchita izi, chifukwa chakuti mosasintha) imatembenuza liwu Lachihebri neʹphesh ndi liwu lofanana nalo Lachigriki psy·kheʹ monga “moyo,” ndipo m’mphatika yake mwandandalikidwa malemba kumene mawu awa akupezeka. Matembenuzidwe ena amakono angapereke mawu oyambirira ofananawo osati kokha monga “moyo” komanso monga “cholengedwa,” “chamoyo,” “munthu” ndi “umoyo”; “neʹphesh yanga” ingatembenuzidwe “ine,” ndi “neʹphesh yanu” monga “inu.” Kuyerekezera kwa Mabaibulo amenewa ndi matembenuzidwe akalepo kapena ndi New World Translation kudzathandiza wophunzira wowona mtima kuzindikira kuti mawu a m’chinenero choyambirira otembenuzidwa kukhala “moyo” amanena (1) anthu, (2) zinyama ndi (3) umoyo umene amasangalala nawo monga wotero. Koma samapereka konse lingaliro lakuti moyo uli chinthu chosawoneka, chosakhudzika chimene chingatuluke m’thupi pa imfa ndi kupitirizabe kukhalapo mozindikira kwina kwake.
6. (a) Kodi nchifukwa ninji matembenuzidwe ena amakono amasiya owerenga ali osokonezeka ponena za tanthauzo la Sheol, Hade ndi Gehena? (b) Kodi mukanalongosola bwanji kuchokera m’Baibulo mkhalidwe wa anthu m’Sheol, kapena Hade? M’Gehena?
6 Mofananamo, New World Translation sirimasinthasintha m’kugwiritsira ntchito kwake Sheol kuchita supelo ya mawu Achihebri sheōlʹ ndi kugwiritsira ntchito kwake Hade kaamba ka liwu Lachigriki haʹdes ndi Gehena kaamba ka geʹen·na. Koma matembunuzidwe ena amakono ndi ndemanga za Baibulo amasokoneza wowerenga mwakutembenuza mawu ONSE AWIRI haʹdes ndi geʹen·na kukhala “helo,” kuphatikiza pa kugwiritsira ntchito “manda” ndi “dziko la akufa” monga matembenuzidwe ena a sheōlʹ ndi haʹdes. Mwakuyerekezera matembenuzidwe, pamene kuli kofunika, kungasonyezedwe kuti Sheol ali wofanana ndi Hade. (Sal. 16:10; Mac. 2:27) Baibulo limakumveketsa bwino kuti Sheoli, kapena Hade, manda a anthu onse, ali ogwirizanitsidwa ndi imfa, osati moyo. (Sal. 89:48; Chiv. 20:13) Limasonyanso ku chiyembekezo cha kutulukako mwa chiukiriro. (Yobu 14:13; Mac. 2:31) Mosiyana, palibe chiyembekezo cha moyo wamtsogolo chimene chikuperekedwa kwa awo opita ku Gehena, ndipo, ndithudi, moyo sumanenedwa kukhala ndi kukhalako kozindikira.—Mat. 18:9; 10:28.
7. Chitazindikiridwa bwino lomwe, kodi ndimotani mmene chiukiriro chingasonkhezerere mkhalidwe ndi zochita za munthu?
7 Pamene nkhani zotero zimveketsedwa, imfa ndi chiukiriro cha Kristu imakhala ndi tanthauzo lenileni. Munthuyo tsopano angakhoze kuthandizidwa kuzindikira chimene chiukiriro chingatanthauze kwa iye ndipo angayambe kuzindikira chikondi cha Yehova m’kupanga makonzedwe odabwitsa otero. Chisoni chimene chiri ndi otaikiridwa okondedwa awo mu imfa tsopanolino chingalowedwe mmalo ndi chiyembekezo chosangalatsa cha kugwirizanitsidwanso m’Dongosolo Latsopano la Mulungu. Akristu a m’zaka za zana loyamba anazindikira kuti chiukiriro cha Yesu Kristu chinali maziko a chikhulupiriro Chachikristu. Mwachangu anachichitira umboni kwa ena ndi chiyembekezo chimene icho chinatsimikizira. Choteronso, awo amene amachizindikira lerolino ali ofunitsitsa kugawira ena chowonadi chamtengo wapatali ichi.—Mac. 5:30-32; 10:40-43; 13:32-39; 17:31.
Kugwiritsira Ntchito Mfungulo za Hade
8. Kodi kugwiritsira ntchito “zofungulira za imfa ndi Hade” kwa Yesu kumatanthauzanji kwa otsatira ake odzodzedwa ndi mzimu?
8 Onse amene adzagwirizanitsidwa ndi Kristu mu Ufumu wake wakumwamba potsirizira pake ayenera kufa. Koma amadziwa bwino chitsimikiziro chimene anapereka pamene anati kwa mtumwi Yohane: “Ndinali wakufa, ndipo tawona, ndiri wamoyo kufikira nthawi zanthawi, ndipo ndirinazo zofungulira za imfa ndi hade.” (Chiv. 1:18) Kodi iye anatanthauzanji? Anali kusonyeza chokumana nacho cha iyemwini. Iyenso, anali atafa. Koma Mulungu sanamsiya m’Hade. Patsiku lachitatu Yehova iyemwiniyo anamuukitsira kumoyo wauzimu nampatsa kusakhoza kufa. Sizokhazo, koma Mulungu anampatsa “zofungulira za imfa ndi Hade” kugwiritsira ntchito m’kuonjolera ena kuchokera kumanda a anthu onse ndi ku ziyambukiro za uchimo wa Adamu. Chifukwa cha kukhala ndi mfungulo zimenezo, Yesu ali wokhoza kuukitsa otsatira ake okhulupirika kwa akufa. Pamene atero, iye amapatsa ziwalo za odzozedwa ndi mzimu zampingo wake mphatso yamtengo wapatali ya moyo wosakhoza kufa wakumwamba, monga momwe Atate anachitira kwa iye.—Aroma 6:5; Afil. 3:20, 21.
9. Kodi ndiliti pamene chiukiriro cha Akristu odzodzedwa okhulupirika chimachitika?
9 Kodi ndiliti pamene Akristu odzodzedwa okhulupirika amenewo akalandira chiukiriro chimenecho? Icho chayamba kale. Mtumwi Paulo akulongosola kuti iwo akaukitsidwa ‘m’nthawi ya kukhalapo kwa Kristu,’ kukhalapo kumene kunayamba mu 1914 C.E. (1 Akor. 15:23) Tsopano, pamene amenewa atsiriza njira yawo ya padziko lapansi, samafunikira kuyembekezera kubwereranso kwa Mbuye wawo ali mu imfa. Mwamsanga pamene afa amaukitsidwa mu mzimu, ‘akumasandulidwa, m’kamphindi, m’kuthwanima kwa diso.’ Ha ndi chawo chotani nanga chimene chifukwa chakuti “ntchito zawo zikutsagana nawo pamodzi”!—1 Akor. 15:51, 52; Chiv. 14:13.
10. Kodi nchiukiriro china chiti chidzakhalako, ndipo kodi ndiliti pamene chidzayamba?
10 Koma chawocho sindicho chiukiriro chokha. Chenicheni chakuti icho chikutchedwa “kuuka koyamba” chikusonyeza kuti china chiyenera kutsatira. (Chiv. 20:6) Awo opindula ndi chiukiriro chapambuyochi adzakhala ndi chiyembekezo chachimwemwe cha moyo wosatha padziko lapansi la Paradaiso. Kodi chimenecho chidzachitika liti? Bukhu la Chivumbulutso limasonyeza kuti chidzakhalako pambuyo pa kuchotsedwa kwa “dziko lapansi ndi miyamba” za dongosolo loipa lamakonoli lazinthu. Mapeto amenewo a dongosolo lakale ayandikira kwambiri. Pambuyo pake, panthawi yokwanira ya Mulungu, chiukiriro cha padziko lapansi chidzayamba.—Chiv. 20:11, 12.
11. Kodi ndani amene adzaphatikizidwa pakati pa okhulupirika oukitsidwira kumoyo padziko lapansi, ndipo chifukwa ninji chimenecho chiri chiyembekezo chochititsa chidwi?
11 Kodi ndani amene adzaphatikizidwamo? Atumiki okhulupirika a Yehova kuyambira kunthawi zakale. Pakati pawo padzakhala amuna amene, chifukwa cha chikhulupiriro chawo champhamvu m’chiukiriro, “sanalola kuomboledwa”—ndiko kuti sanataye umphumphu wawo kwa Mulungu kuchitira kuti apewe imfa yachiwawa. (Aheb. 11:35) Ha ndichikondwerero chotani nanga mmene chidzakhalira kuwadziwa mwachindunji ndi kumva mawu, ochokera pakamwa pawo, mawu atsatane tsatane onena za zochitika zimene zasimbidwa kokha mwachidule m’Baibulo! Pakati pa ena, padzakhala Abele, mboni yoyamba yokhulupirika ya Yehova. Enoke ndi Nowa, alengezi opanda mantha a uthenga wa Mulungu wa chenjezo Chigumula chisanadze. Abrahamu, amene anachereza angelo. Mose, kupyolera mwa amene Chilamulo chinaperekedwa pa Phiri la Sinai. Aneneri olimba mtima onga Yeremiya, amene anawona chiwonongeko cha Yerusalemu mu 607 B.C.E. Ndi Yohane Mbatizi, amene anamva Mulungu iyemwiniyo akudziwikitsa Yesu monga Mwana wake. Padzakhalanso okhulupirika ena amene anafa mkati mwa masiku otsiriza a dongosolo liripoli lazinthu.—Aheb. 11:4-38; Mat. 11:11.
12. (a) Kodi ndiangati a akufa mu Hade adzaukitsidwa? (b) Chotero kodi ndani adzaphatikizidwa, ndipo chifukwa ninji?
12 M’nthawi yokwanira, enanso, adzaukitsidwa. Mlingo umene Yesu adzagwiritsira ntchito ‘mfungulo za Hade’ kuukitsa anthu wasonyezedwa m’masomphenya operekedwa kwa mtumwi Yohane mu amene anawona Hade “akuponyedwa m’nyanja yamoto.” Kodi kumeneko kukutanthauzanji? Kuti ikuwonongedwa; kulibeko chifukwa cha kukhutulidwa kotheratu. Chotero, m’kuwonjezera pa kuukitsa olambira okhulupirika a Yehova, Yesu mwachifundo adzaukitsa kuchokera ku Hade, kapena Sheoli, ngakhale anthu osalungama. Palibe aliyense wa oukitsidwawo adzangoweruzidwa kokha kuyenerera imfa kachiwirinso. M’chitaganya cholungama pansi pa Ufumu wa Mulungu adzathandizidwa kuchititsa miyoyo yawo kukhala yogwirizana ndi njira za Yehova. Masomphenyawo anasonyeza “mpukutu wa moyo” ukutsegulidwa, ndipo iwo adzakhala ndi mwayi wakulembedwa maina awo m’menemo. Anthu “adzaweruzidwa mwa zolembedwa m’mabukhu, monga mwantchito zawo” zochitidwa pambuyo pa chiukiriro chawo. (Chiv. 20:14; Mac. 24:15) Chotero, chitawonedwa mwa lingaliro la chimene potsirizira pake chidzakhala chotulukapo, chawocho chingatsimikizire kukhala “kuuka kwa moyo” ndipo sichidzakhala “kuuka kwa kuweruza” (kutsutsidwa) mosapeweka.—Yoh. 5:28, 29.
13. (a) Kodi ndani amene sadzaukitsidwa? (b) Kodi ndimotani mmene chidziwitso cha chowonadi chonena za chiukiriro chiyenera kuyambukirira miyoyo yathu?
13 Ndithudi, siwonse amene anakhalapo ndi moyo adzaukitsidwa. Ena anachita machimo amene kukhululukira kuli kosatheka. Ophedwa mu “chisautso chachikulu,” chimene tsopano chayandikira, adzaphatikizidwa pakati pa awo okomana ndi chionongeko chosatha. (Mat. 12:31, 32; 23:33; 24:21, 22; 25:41, 46; 2 Ates. 1:6-9) Chotero, pamene chifundo chapadera chikusonyezedwa m’kuwonjola onse amene ali mu Hade, chiukiriro sichikupereka maziko a kukhala kwathu amphwayi ponena za mmene tikukhalira ndi moyo tsopano. M’malo mwake, chiyenera kutisonkhezera kusonyeza mmene tikuyamikirira kwambiri za kukoma mtima kwachifundo kowona kwa Mulungu kumeneku.
Kulimbikitsidwa ndi Chiyembekezo cha Chiukiriro
14. Kodi ndimotani mmene chiukiriro chingakhalire magwero a nyonga yaikulu kwa munthu amene akuyandikira mapeto a moyo wanthawi ino?
14 Awo amene apanga chiyembekezo cha chiukiriro kukhala cha iwo eni ali okhoza kupezako nyonga. Pamene ali pafupi ndi mapeto a moyo wawo, amadziwa kuti iwo sangakankhire patsogolo imfa kunthawi yosadziwika, mosasamala kanthu za mankhwala amene angagwiritsiridwe ntchito. (Mlal. 8:8) Ngati iwo akhala otanganitsidwa m’ntchito ya Ambuye ndipo anatumikira mokhulupirika ndi gulu lake, angakhoze kuyang’ana mtsogolo ndi chitsimikiziro chodzala. Amadziwa kuti mwa chiukiriro panthawi yokwanira ya Mulungu adzasangalalanso ndi moyo. Ndipo ha udzakhala moyo wokondweretsa chotani nanga! “Moyo weniweni,” monga momwe mtumwi Paulo akuutchera.—1 Tim. 6:19; 1 Akor. 15:58; Aheb. 6:10-12.
15. Ngati tithupsidwa ndi ozunza achiwawa, kodi nchiyani chimene chingatithandize kusunga umphumphu kwa Yehova?
15 Sikudziwa kokha kuti chiukiriro chiriko, koma kudziwa Munthuyo amene ali Magwero amakonzedwe amenewa kumatikhozetsa kukhala olimba. Izi zimatilimbikitsa kukhala okhulupirika kwa Mulungu ngakhale ngati tathupsidwa ndi imfa ndi ozunza achiwawa. Kwanthawi yaitali Satana wagwiritsira ntchito kuopa imfa ya mwamsanga monga njira yosungira anthu mu ukapolo. Koma Yesu sanagonjere ku mantha otero; anatsimikizira kukhala wokhulupirika kwa Yehova mpaka pa imfa penipenipo. Kupyolera mwa chimene imfa yake inakwaniritsa anapereka njira ya kumasulira ena kuchokera ku mantha otero. (Aheb. 2:14, 15) Monga chotulukapo cha chikhulupiriro chawo m’makonzedwe amenewo, otsatira ake owona apanga cholembedwa chapadera monga osunga umphumphu. Pamene atsenderezedwa, atsimikizira kuti ‘samakonda miyoyo ya iwo eni’ koposa mmene amakondera Yehova. (Chiv. 12:11) Mwanzeru, iwo samayesa kupulumutsa moyo wawo wamakono mwa kuswa malamulo a makhalidwe abwino Achikristu, ndi kutaikiridwa ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya. (Luka 9:24, 25) Kodi inu muli ndi mtundu umenewo wa chikhulupiriro? Mudzatero ngati mukondadi Yehova ndipo mwazindikira chimene chiyembekezo cha chiukiriro chimatanthauza kwa inu.
Makambitsirano Openda
● Kodi nchifukwa ninji munthu afunikira kumvetsetsa chimene moyo uli ndi mkhalidwe wa akufa asanazindikire chiukiriro?
● Kodi ndani adzaukitsidwa kwa akufa? Kodi chidziwitso ichi chiyenera kutiyambukira motani?
● Kodi ndimotani mmene chiyembekezo cha chiukiriro chimatilimbikitsira?