Chaputala 2
“Kalonga wa Mtendere” Ayang’anizana ndi Armagedo
1, 2. (a) Kodi ndimawu ochititsa chidwi otani amene Mulungu anauzira mneneri Yesaya kulankhula? (b) Kodi ndiliti pamene mawu ameneŵa anayamba kukwaniritsidwa?
M’ZAKA za zana lachisanu ndi chitatu za Nyengo Yathu isanakhale, mneneri Yesaya anauziridwa kunena kwa anthu a Mulungu: “Kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala papheŵa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa Mtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pampando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kumkabe nthaŵi zonse.”—Yesaya 9:6, 7.
2 Mawu ochititsa chidwi amenewo anayamba kukwaniritsidwa m’mbali yotsirizira ya chaka cha 2 B.C.E. Imeneyi inali nthaŵi pamene Yesu anabadwa monga mbadwa ya Mfumu Davide, amene analamulira mu mzinda wa Yerusalemu pa mafuko 12 a Israyeli.
Pangano la Ufumu la Mtendere Wosatha
3. (a) Kodi ndipangano lotani limene Mulungu anachita ndi Mfumu Davide? (b) Kodi ndipambadwa ya Mfumu Davide iti pamene Yehova anaika dzina laulemu lakuti “Kalonga wa Mtendere”?
3 Chifukwa cha changu cha Davide kaamba ka kulambiridwa kwa Mulungu wa Israyaeli, Yehova anachita naye pangano la Ufumu wosatha mu mzera wa mbadwa zake. (2 Samueli 7:1-16) Pangano limenelo linachirikizidwa ndi lumbiro la Mulungu. (Salmo 132:11, 12) Mogwirizana ndi pangano limenelo, ufumu wa Davide unali kudzapereka maziko a Ufumu ulinkudza wa “Kalonga wa Mtendere.” “Yesu Kristu, mwana wa Davide,” ndiye amene Yehova anaperekako dzina laulemu lakuti “Kalonga wa Mtendere.”—Mateyu 1:1.
4. (a) Kodi ndani amene anakhala mayi wapadziko lapansi wa Yesu? (b) Kodi nchiyani chimene mngelo Gabrieli ananena kwa iye pamfundoyi?
4 Amayi ŵa Yesu anali mkazi wobadwira mu mzera wachifumu wa Mfumu Davide. Iye anali namwali pamene anali ndi pakati pa mwana wake wamwamuna wolonjezedwayo, amene akakhala woloŵa nyumba wachikhalire pampando wachifumu wa Davide. Mkaziyo anakhala ndi pakati Yosefe asanamtenge kukhala mkazi wake. (Mateyu 1:18-25) Mngelo Gabrieli anali atauza namwali Mariya kuti: “Tawona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu. Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa iye mpando wachifumu wa Davide atate wake: ndipo iye adzachita ufumu pabanja la Yakobo kunthaŵi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha.”—Luka 1:31-33.
5. Kodi nchiyani chimene mneneri Yesaya adaneneratu ponena za ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”?
5 Ndicho chifukwa chake mneneri Yesaya adaneneratu ponena za “Kalonga wa Mtendere” kuti “ulamuliro wake ngwaukulu mu mtendere umene ulibe mapeto, kaamba ka mpando wachifumu wa Davide ndi kaamba ka ulamuliro wake wachifumu.” (Yesaya 9:6, 7, The Jerusalem Bible) Motero, mogwirizana ndi pangano lokhazikitsidwa ndi Davide, Ufumu umenewu ukakhala boma losatha la mtendere wopanda mapeto. Mpando wake wachifumu uyenera kukhalako “kosatha”!
6. (a) Kukwaniritsa pangano la Ufumu, kodi Mulungu anachitanji patsiku lachitatu la imfa ya Yesu? (b) Kodi ndiliti pamene Yesu anayamba kulamulira monga “Kalonga wa Mtendere”?
6 Kuti pangano la Ufumu limeneli likwaniritsidwe, Mulungu Wamphamvuyonse anaukitsa Yesu kwa akufa patsiku lachitatu la imfa yake yophedwera chikhulupiriro. Limeneli linali tsiku la 16 la mwezi Wachiyuda wa Nisani, m’chaka cha 33 cha Nyengo Yathu. Monga mboni yowona ndi maso ya Mwana wa Mulungu woukitsidwayo, mtumwi Petro ananena kuti “wophedwatu m’thupi, koma wopatsidwa moyo mu mzimu.” (1 Petro 3:18) Mulungu Wam’mwambamwamba anamkwezera Iye kudzanja lake lamanja. Kumeneko, chiyambire kutha kwa Nthaŵi za Akunja, kapena “nthaŵi zoikidwiratu za mitundu,” kuchiyambiyambi kwa October wa chaka cha 1914, iye wakhala akulamulira monga “Kalonga wa Mtendere.”—Luka 21:24.
7. (a) Kodi nchiyani chimene Yesu anayang’anizana nacho kuyambira pachiyambi pa ulamuliro wake? (b) Kodi ndani amene akulengeza ufumu wa Yesu kumitundu yonse, ndipo m’kukwaniritsidwa kwa chiyani?
7 Kuyambira pachiyambi pa ulamuliro wake wakumwamba, iye wakhala akuyang’anizana ndi dziko laudani, monga momwe kwatsimikizidwira ndi nkhondo za dziko ziŵiri zomenyedwera nkhani yakuti ndani amene adzalamulira dziko lapansi. Iye tsopano wayang’anizana ndi gulu la Mitundu Yogwirizana. Mwa chilengezo chokweteza dziko cha mbiri yabwino ya Ufumu yolengezedwa ndi Mboni za Yehova, zimene zikulalikira m’maiko oposa 200, ufumu wake wogwira ntchito kumwamba ukusonyezedwa kumitundu yonse. Zimenezi ndizo kukwaniritsidwa kwa chimene “Kalonga wa Mtendere” mwiniyo adaneneratu, monga mwomwe timaŵerengera pa Mataeyu 24:14, NW: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kumitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.”
8. Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti tiri mkati mwenimweni mwa “mapeto a dongosolo la zinthu” ameneŵa?
8 Nkhani ya ulamuliro wa dziko iyenera kuthetsedwa msanga. Tsopano, zoposa zaka 70 pambuyo pa mapeto a “nthaŵi zoikidwiratu za amitundu” mu 1914, tiri mkati mwenimweni mwa ‘mapeto ameneŵa a dongosolo la zinthu.’ Mbadwo wa 1914 unawona chiyambi cha zochitika zopereka tanthauzo za dziko zonenedweratu ndi Yesu. (Mateyu 24:3-14) Yesu anati, mbadwo umenewo, sukapita konse kufikira zinthu zonse zimenezi zikakwaniritsidwa. Tsopano uli pafupi kwambiri ndi kumaliza njira yake.—Mateyu 24:34.
9, 10. (a) Kodi ndimotani mmene mawu olosera m’bukhu la Chivumbulutso anafikitsidwira kwa ife? (b) Kodi nchiyani chimene Chivumbulutso 16:13, 14, 16 chimaneneratu ponena za Harmagedo, kapena Armagedo?
9 Chifukwa chake, kodi nchiyani chimene chiri mtsogolo pafupipa, ndipo kodi “Kalonga wa Mtendere” akuyang’anizana ndi chiyani? Iye mwiniyo anagwiritsiridwa ntchito kuneneratu zimenezi m’bukhu lomalizira lenileni la Baibulo, Chivumbulutso, limene Mulungu anampatsa ndi limene anapereka kwa mtumwi Yohane wokalambayo kupyolera mwa mngelo. (Chivumbulutso 1:1, 2) Zimenezo zinachitika pafupifupi cha kumapeto kwa zaka zana loyamba la Nyengo Yathu. Pa Chivumbulutso 16:13, 14, 16, Yesu anachititsa mtumwi Yohane kulemba mawu aŵa ofunika ponena za Harmagedo kapena Armagedo:
10 “Ndipo ndinawona motuluka mkamwa mwa chinjoka, ndi mkamwa mwa chirombo, ndi mkamwa mwa mneneri wonyenga mizimu itatu yonyansa, ngati achule; pakuti ali mizimu ya ziŵanda zakuchita zizindikiro; zimene zituluka kumka kwa mafumu a dziko lonse, kuwasonkhanitsira kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse. Ndipo anawasonkhanitsira kumalo otchedwa m’Chihebri Harmagedo.”
“Phiri la Megido” Lophiphiritsira
11. (a) Kodi dzinalo Armagedo limatanthauzanji, ndipo kodi panali malo enieni otchedwa motero? (b) Kodi nchifukwa ninji mzinda wakale wa Megido unali wofunika m’mbiri? (c) Kodi nditanthauzo la paŵiri lotani limene dzina lakuti Megido linakhala nalo?
11 Dzina Lachihebri lakuti Harmagedo, kapena Armagedo, limatanthauza “Phiri la Megido.” Palibe malo enieni m’nthaŵi zakale kapena zamakono amene amatchedwa Phiri la Megido. Motero m’bukhu longa la Chivumbulutso lodzala ndi mawu okuluŵika, liwulo liri ndi tanthauzo lophiphiritsira. Kodi limenelo liyenera kukhala chiyani? Eya, mzinda wokwezeka wa Megido, dzina limene malo ake amatanthauza “msonkhano wa magulu a nkhondo,” unali ndi tanthauzo lapadera m’mbiri. M’mbiri ya dziko ndi ya Baibulo dzinali linakumbutsa za nkhondo zothetsera mkangano. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti panthaŵiyo mzindawo unamangidwa panjira yoyenda magaleta ankhondo imene inali pakati pa Ulaya, Asiya, ndi Afirika, ndipo nzika zake zinali ndi mwaŵi wabwino wa kupereka chitokoso kwa oukira panthaŵi yomweyo ndi kuimikidwa ndi okhalamo ake. Chifukwa chake liwu lakutilo Megido linali ndi matanthauzo aŵiri—kumbali ina linatanthauza kugonjetsedwa kochititsa manyazi ndipo kumbali inayo chipambano chaulemerero.
12, 13. (a) Kodi ndimotani mmene Mulungu wa Baibulo anagwirizanitsidwira ndi Megido ndi mtsinje wake wapafupi m’masiku a Woweruza Baraki? (b) Kodi ndimotani mmene nyimbo yachipambano ya Baraki ndi Debora imalongosolera mbali ya Mulungu m’chilakikocho?
12 Mulungu Wabaibulo anafikira pakugwirizanitsidwa ndi Megido limodzi ndi mtsinje wapafupi wa Kisoni mkati mwa nyengo ya oweruza a Israyeli. M’masiku a Woweruza Baraki ndi a mneneri wachikazi Debora, Mulungu anapereka chizindikiro cha kugonjetsa kwa anthu ake osankhidwa m’malo oyandikana ndi Megido. Woweruza Baraki anali ndi amuna 10 000 okha, pamene kuli kwakuti mdaniyo motsogozedwa ndi Kazembe Wankhondo Sisera anali ndi magaleta ankhondo okokedwa ndi akavalo 900, kuwonjezera pamagulu ankhondo oyenda pansi. Yehova analoŵerera m’nkhondo kumenyera anthu ake osankhidwa nachititsa liyambwe lokokolola kuti lidodometse magaleta ankhondo owopsa a mdani. M’nyimbo yachipambano imene Baraki ndi Debora anaimbira Mulungu pambuyo pa kugonjetsa mozizwitsa magulu ankhondo a Sisera, iwo anatchula mbali ya Mulungu m’kugubuduzidwa kumeneku kwa mdani:
13 “Anadza mafumu, nathira nkhondo; pamenepo anathira nkhondo mafumu a Kanani. M’Taanaki, kumadzi a Megido; osatengako phindu la ndalama. Nyenyezi zinathira nkhondo yochokera kumwamba, m’mipata mwawo zinathirana ndi Sisera. Mtsinje wa Kisoni unawakokolola, mtsinje uja wakale, mtsinje wa Kisoni.”—Oweruza 5:12, 19-21.
14. Kodi ndimawu omaliza ati a nyimbo youziridwa yachilakiko imeneyo amene mosakaikira ali pemphero lonena za nkhondo irinkudza pa Armagedo?
14 Mosakaikira, mawu ouziridwa amene Baraki ndi Debora anatseka nawo nyimbo yawo pambuyo pa chilakiko chakale chimenecho pa Megido amagwira ntchito monga pemphero ponena za nkhondo imene irinkudza pa Armagedo. Iwo anaimba kuti: “Adani anu onse, Yehova, atayike momwemo. Koma iwo akukonda inu akhale ngati dzuŵa lotuluka mu mphamvu yake.”—Oweruza 5:31.a
Mitundu Isonkhanitsidwira ku Armagedo
15. (a) Pamenepa, kodi Armagedo, ali malo amtundu wotani? (b) Kodi ndiati amene ali amodzi a magwero a mawu okopa onyansa amene amasonkhanitsa mitundu kunkhondo pa Armagedo?
15 Motero Megido anali malo kumene nkhondo zothetsa mkangano zinamenyedwera. Pamenepa, mwachiwonekere, Armagedo ikakhala bwalo la nkhondo ku limene mitundu yonse yaudziko lerolino ikagubirako motsogozedwa ndi magulu osonkhezera olongosoledwa pa Chivumbulutso 16:13, 14. “Mizimu ya ziŵanda” imene imasonkhanitsa mitundu ndiyo mawu okopa amene lerolino akunenedwa, ofanana ndi achule onyansa mogwirizana ndi kunena kwa Baibulo. Amodzi a magwero a mawu okopa onyansa otero ndiwo “chinjoka chachikulu chofiira.” Chivumbulutso 12:1-9 chimafotokoza “chinjoka” kukhala Satana Mdyerekezi.
16. Pa Chivumbulutso 16:13, kodi “chirombo” chimaphiphiritsira chiyani?
16 Magwero ena a mawu ena okopa onyansa ndiwo “chirombo.” Pa Chivumbulutso 16:13 ‘chirombo chophiphiritsira chimenechi’ chadziŵikitsidwa kukhala “chinjoka” chauchiŵanda. Mogwirizana ndi kunena kwa Chivumbulutso 20:10, “chirombo” chimenechi chidzawonongedwa kosatha chifukwa cha kugwirizana kwake ndi “chinjoka” chophiphiritsira. “Chirombo” chimaphiphiritsira dongosolo lonse la ndale zadziko za dziko lino limene “chinjoka” chiri mulungu wake. (2 Akorinto 4:4) Chimaphatikizapo maboma osiyanasiyana andale zadziko onse a dziko lino.—Yerekezerani ndi Danieli 7:17; 8:20, 22.
17. Kodi nchiyani chimene chiri chiyambukiro cha mawu okopa otuluka ku “chirombo”?
17 Dongosolo la ulamuliro wandale zadziko lotero liri ndi mawu ake okopa odziŵika. Ndipo kunenedwa kumeneku kwa mawu okopa onga achule ndiko mawu ouziridwa amene amatumikira limodzi ndi mawu ouziridwa a “chinjoka” kusonkhanitsira “mafumu,” kapena olamulira andale zadziko a dziko, ku “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” imene idzamenyedwera pa Armagedo.
18. (a) Kodi dzinalo Harmagedo limatanthauza chiyani (b) Kodi phirilo lingatanthauze chiyani?
18 Motero Harmagedo imatanthauza mkhalidwe wa dziko umene umaloŵetsamo nkhondo yothetsera mkangano. Imatanthauza mkhalidwe wothetsera mkangano pamene zochitika za dziko zimafika pamkhalidwe umene olamulira andale zadziko mogwirizana amatsutsa chifuniro cha Mulungu, kotero kuti Mulungu ayenera kuchitapo kanthu mwamphamvu mogwirizana ndi chifuno chake. Motero mtsogolo mudzatsimikiziridwa ndi zimene zidzakhala zotulukapo za mkangano umenewu. Pa Megido penipenipo, malo enieni, panalibe phiri. Koma phiri lingaphiphiritsire malo odziŵika okomanako amene akadziŵika mosavuta kuchokera patali ndi magulu onse ankhondo osonkhanitsidwa kumeneko.
19, 20. Kodi ndiluso lankhondo lotani limene Kazembe wa magulu ankhondo akumwamba a Yehova adzagwiritsira ntchito pa Armagedo ndipo nzotulukapo zotani?
19 Patapita zaka zingapo Yesu Kristu Kazembe wankhondo wa magulu ankhondo a Yehova, wawonerera kusonkhana kwa olamulira adziko ndi magulu awo ankhondo pa Armagedo. Koma sanayese kusankha mfumu imodzi iriyonse ndi magulu ake ankhondo kuti agonjetse magulu ankhondo a mdani ali yekha ndipo motero kuwatha pang’onopang’ono. Mmalo mwake, iye akuŵapatsa nthaŵi yokwanira ya kusonkhana pamodzi ndi kugwirizanitsa magulu awo ankhondo kukhala amphamvu kwambiri m’zankhondo monga momwe kungathekere kwa iwo. Chifuno chake chachikulu ndicho kumenyana nawo onse panthaŵi imodzimodzi!
20 Motero adzaŵalaka mwa chilakiko chachikulu, kukhale ulemerero kwa Kazembe wake wankhondo Wamkulu Yehova Mulungu, ndi kutsimikiziridwa kwa iyemwini monga “Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye,” wopanda womtsutsa.—Chivumbulutso 19:16.
[Mawu a M’munsi]
a Maumboni ena onena za Megido akupezeka pa 2 Mafumu 9:27; 23:29, 30; 2 Mbiri 35:22; Zekariya 12:11.