Chaputala 18
Kukhulupirika ku Gulu Lowoneka la Mulungu Lerolino
1, 2. Kodi lemba la Salmo 50:5 lingazindikiridwe motani?
M’SALMO 16:10 mwalembedwa: “Simudzasiya moyo wanga kumanda; simudzalola wokondedwa wanu avunde.” Ndipo m’Salmo 50:5 mwalembedwa kuti: “Mundisonkhanitsire okondedwa anga; amene anapangana ndi Ine ndi nsembe.” Kodi amene amachita pangano la Yehova ndiwo amene amapereka “nsembe”? Ayi, okhulupirika ameneŵa samadzipereka aliyense payekha kukhala “nsembe,” akumapereka matupi awo anyama kuti achite pangano ndi Mulungu.
2 Pamenepa, kodi ndimotani mmene pangano limachitidwira? Mwa “nsembe” ya “wokhulupirika” amene moyo wake suunasiyidwe m’Sheoli koma amene anaukitsidwa kwa akufa. Mtumwi Petro anagwiritsira ntchito mawu a Salmo 16:10 kwa Yesu Kristu napitirizabe kunena kuti: “Iye [Davide] pa kuwona ichi kale, analankhula za kuuka kwa Kristu, kuti sanasiyidwa m’Hade, ndi thupi lake silinawona chivundi. Yesu ameneyo, Mulungu anamuukitsa.”—Machitidwe 2:25, 27, 31, 32.
3. Kodi ndani amene ali osonkhanitsidwa mogwirizana ndi lamulo la Salmo 50:5, ndipo ndichifukwa ninji tiyenera kusonkhezeredwa kutsimikizira kukhala okhulupirika kwa Mulungu?
3 Yesu woukitsidwa ameneyo ndiye Mtetezi wa pangano latsopano, ndipo kuli pamaziko a nsembe yake kuti pangano latsopano linayamba kugwira ntchito. (Ahebri 9:15, 17) Motero kodi ndani amene akasonkhanitsidwa mogwirizana ndi lamulo la m’Salmo 50:5? Iwo ndiwo ophunzira a Yesu amene ali m’pangano latsopano kupyolera mwa nsembe yake. Mwa chiyamikiro kwa Yehova kaamba ka nsembe yake yosayerekezereka, ayenera kusonkhezeredwa kutsimikizira kukhala okhulupirika kwa iye.
4, 5. (a) Kodi ndichipambano chotani chimene Satana Mdyerekezi anali nacho mkati mwa nkhondo yoyamba ya dziko m’kuyesayesa kwake kuwononga gulu lowoneka la Yehova? (b) Kodi nkuti kumene malikulu a Sosaite anasamutsidwira, ndipo chifukwa ninji? (c) M’zochitika zofanana zamakono za Salmo 137:1, kodi mkhalidwe wa maganizo, kapena khalidwe, wa otsalira okhulupirika pamene anasinkhasinkha mkhalidwe wovulazika wa gulu la Mulungu unali wotani?
4 Pamene Ufumu wa Yehova unakhazikitsidwa m’miyamba mu 1914, mitundu inakwiya motsutsana ndi Ufumu umenewo mwa kuphatikizidwa m’nkhondo yoyamba yadziko, ndipo Mulungu analola zimenezi. (Salmo 2:1, 2) Satana Mdyerekezi anayesayesa kugwiritsira ntchito nkhondo yadziko imeneyo kuwononga mbali yowoneka ya gulu la Yehova. Iye anapeza chipambano m’kuchititsa prezidenti wa Watch Tower Bible and Tract Society kuikidwa m’ndende yachitaganya yokhaulitsira mu Atlanta, Georgia. Oimira ena asanu ndi aŵiri a Sosaite anaikidwa m’ndende limodzi naye.
5 Chifukwa cha chizunzo, malikulu a Sosaite m’Brooklyn, New York, anasamutsidwira kunyumba yobwereka m’Pittsburgh, Pennsylvania. Zimenezi zinachitidwira kufalitsidwa kwa magazine a Nsanja ya Olonda. Kuvekedwa ulemerero wakumwamba kwa okhulupirika kunayembekezeredwa mwamsanga. Koma otsalirawo anali ndi chikhoterero cha kulira pamene analingalira za mkhalidwe wotsedereza, wa kuvulazika wa gulu la Yehova.—Salmo 137:1.
Kukhulupirika Mkati mwa Nthaŵi ya Kuikidwa m’Ndende
6-8. M’nthaŵi ya kuikidwa kwake m’ndende, kodi ndimotani mmene prezidenti wa Sosaite J. F. Rutherford anasonyezera kukhulupirika kugulu la Yehova?
6 Kusonyeza kukhulupirika kugulu la Yehova mkati mwa nthaŵi ya kuikidwa kwake m’ndende, prezidenti wa Watch Tower Society, J. F. Rutherford, pa December 25, 1918, analemba kalata yapadera kwa J. A. Bohnet, mtumiki mnzake wokhulupirika wa Yehova. Inalunjikitsidwa kwa iye pa ofesi ya Sosaite m’Pittsburgh. Rutherford analemba zotsatirazi:
7 “Chifukwa chakuti ndinakana kugonjera ku Babulo, koma ndinayesa mokhulupirika kutumikira Mbuye wanga, ndiri m’ndende, chinthu chimene ndikuchiyamikira. . . . Ndithudi ndikasankha kuvomerezedwa ndi kuyanjidwa ndi iye ndi kukhala m’ndende, kuposa kulolera molakwa kapena kugonjera ku Chirombo ndi kumasulidwa ndi kutamandidwa ndi dziko lonse. Chiri chokumana nacho cha dalitso, ndi chokondweretsa kuvutika kaamba ka utumiki wokhulupirika kwa Ambuye. Koposa zinthu zonse tidzakhala ndi chivomerezo cha Atate mu Ufumu. Zimenezi ziyenera kukhala zinthu zofunika kwambiri m’maganizo a ana onse a Mulungu. Tikulakalaka kupeza mgwirizano umene udzatipangitsa ife kukhala amodzi kumeneko. Ndiri wachimwemwe, komabe ndiri ndi chikhumbo cha kukuwonaninso inu nonse. Msonkhano waukulu ndi msonkhano wa chaka ndi chaka ukuyandikira. Mzimu wa Kristu udzazetu mitima ya alionse ofikapo . . .
8 “Kukali chikhalirebe zambiri za kuzichita. Chidzakhala chisomo chachikulu kugaŵanamo. Ali awo okha omkonda Iye kwakukulu ndi okhulupirika amene adzakhala ndi mwaŵi umenewo. . . . Tsiku limenelo la chikondwerero lisanafike payenera kuperekedwa umboni wachangu. . . . Njira zakale ndi maluso sizingathe kukwaniritsa zofunika, koma Ambuye m’njira Yake yabwino adzagaŵira. . . . Ndiri wokondwera kuti chokumana nacho cha ndende chimenechi chinasungidwira ife mmalo mwa Mbale Russell. Ndi kalelonse sindinanyansidwe motere ndi chisalungamo ndi kukonda chilungamo ndipo kulakalaka kuthandiza ena. . . . Chipambano cha Ziyoni chayandikira.”
Gulu la Mulungu ‘Magwero Achimwemwe Chawo Chopambana’
9. Kodi ndimkhalidwe wotani wa wamasalmo umene oimira a Sosaite oikidwa m’ndende anasonyeza?
9 Ngakhale kuli kwakuti atumiki a Yehova anawonedwa m’dziko kukhala osakhulupirika, opereka, osakonda dziko lawo, iwo sanakane gulu la Yehova. Iwo anakana kugonjera pansi pa chipsinjo chimenecho. Iwo anasankha kutayikiridwa ndi kugwiritsiridwa ntchito kwa dzanja lawo lamanja kapena kukhala mbeŵeŵe kuposa kuiŵala gulu la Mulungu ndi kusalilolanso kukhala ‘magwero a chimwemwe chawo chopambana.’—Salmo 137:5, 6.
10, 11. (a) Kodi otsalira okhulupirika anapempherera chiyani, ndipo ndimawu a wamasalmo ati onena za Edomu amene iwo anawatenga kukhala awo? (b) Kodi ndichiyani chimene adani a gulu lowoneka la Yehova akhala akuchita, ndipo kodi adani amenewo sanayembekezere chiyani?
10 Adani a Yehova mwankhalwe anakondwera pa chochikitika chotsutsana ndi oimira a padziko lapansi a gulu lake la chilengedwe chonse. Koma atumiki a Yehova anapempherera kudza kwa tsiku lake la kulipsira chifukwa cha mtonzo wonsewo wounjikidwa pagulu lake. Iwo anatenga mawu amene wamasalmo analankhula ponena za Edomu wakale kukhala awo: “Yehova, kumbukirani ana a Edomu tsiku la Yerusalemu; amene adati, gamulani, gamulani, kufikira maziko ake.” (Salmo 137:7; Agalatiya 4:26) Aha, inde, Yehova amakonda kwambirimbiri gulu lake longa mkazi kotero kuti sakanaiŵala zimene awo amene ali mbali ya gulu la Mdyerekezi amanena ndi kuchita motsutsana ndi okhulupirika a gulu lake la padziko lapansi.
11 Mwa kuwona mkhalidwe wawo wonse wakunja panthaŵiyo, andale zadziko amene anali kumverana chifundo ndi Babulo Wamkulu anawononga gulu lowoneka la Yehova ‘kufikira pamaziko ake enieni.’ Iwo sanayembekezere konse kuliwona likudzuka kuchokera kufumbi ku kukhala gulu la padziko lonse lapansi mmene liriri lerolino.
Chimwemwe cha Wolipsira Wake
12. (a) Ndani amene anali mpulumutsi wa anthu otengedwa ndende a Yehova m’Babulo wakale, ndipo kodi Salmo 137:8, 9 imamtchula mwa lingaliro lokwanira koposa? (b) Kodi mavesi ameneŵa ananeneratu za chiyani ponena za wolipsira wa gulu la padziko lapansi la Mulungu?
12 Yehova anagwiritsira ntchito wolamulira wa Aperesi Koresi kulanditsa anthu ake kuchokera ku ulamuliro wadziko wakale wa Babulo. Koma m’lingaliro lokwanira koposa, Koresi sindiye amene anatanthauzidwa m’mawu omalizira a Salmo 137, limene limasonya ku Babulo Wamkulu, ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga: “Mwana wamkazi wa ku Babulo, iwe amene udzapasulidwa; wodala iye amene adzakubwezera chilango monga umo unachitira ife. Wodala iye amene adzagwira makanda ako, ndi kuwaphwanya pathanthwe.”—Salmo 137:8, 9.
13, 14. Kodi ndichifukwa ninji “wodala” wa pa Salmo 137:8, 9 sakusonya kwa olamulira andale zadziko amene amawononga Babulo Wamkulu?
13 Kodi ndani amene adzakhala “wodala” ameneyo? Kodi “wodala” ameneyo akuimira “nyanga khumi” zophiphiritsira zimene ziri pamutu wa “chirombo,” chimene monyang’wa pamsana pake pakwera dongosolo la hule lakale lachipembedzo kwanthaŵi yaitali motero? Ayi, Chifukwa chakuti owononga andale zadziko a ulamuliro wadziko wa chipembedzo chonama samaliwononga kuti alambule njira ya kulambira kwangwiro kwa Mulungu wowona. Iwo samachita zimenezo kaamba ka ulemerero wa Mulungu wa Baibulo. Pamenepa, kodi ndimotani mmene kwenikweni otchulidwa ndi wamasalmo amenewo angakhalire “odala”?
14 Maulamuliro andale zadziko za dziko lino samakwaniritsa ntchito yotsutsana ndi chipembedzo imeneyi mwa kukonda olambira a Yehova. Kulekeranji? Chifukwa chakuti Mboni za Yehova zidzalepheretsa kupangika kwa dziko losapembedza kotheratu. Motero maulamuliro andale za dziko ali kokha ziŵiya zogwiritsiridwa ntchito ndi Mulungu wa Mboni kukwaniritsa chifuno cha iyemwini—Chivumbulutso 17:17.
15. Kodi ndani amene kwenikweni amasonkhezera olamulira andale zadziko, ndipo kupyolera mwa yani?
15 Motero, ngakhale kuli kwakuti olamulira andale zadziko ameneŵa angagwiritsiridwe ntchito mwachindunji m’kuwonongedwa kwa ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, alidi Yehova Mulungu amene akuwasonkhezera. Motani? Iye amagwiritsira ntchito Mwana wake wolandira mphamvu yachifumu, Koresi Wamkulu, Yesu Kristu. Motero, Yesu Kristu m’mphamvu ya Ufumu ali “wodalayo” wonenedweratu m’Salmo!
16. Kodi ndimotani mmene Yehova amawonongera “ana” a Babulo?
16 Pamene kuli kwakuti Yehova adzatetezera okhulupirika ake, iye, mophiphiritsira adzagwira “ana onse” achipembedzo a dongosolo longa hule la chiphunzitso chonyenga ndi kuwaphwanyira pa chimene chimawonekera mofanana ndi ‘thanthwe’—Ufumu wosagonjetseka wa Yehova Mulungu kudzera mwa Yesu Kristu.
17. (a) Mogwirizana ndi kunena kwa Yesaya 61:1, 2, kodi Yesu anali kudzalengeza chiyani pambuyo pa kudzozedwa ndi mzimu wa Mulungu? (b) Kodi ndimotani mmene chilengezocho chikuchitidwira lerolino?
17 Pamene anali padziko lapansi, Yesu anadzozedwa ndi mzimu wa Mchirikizi wake waumulungu osati kokha kuti ‘alengeze chaka chokomera Yehova’ komanso kulengeza ‘tsiku la kulipsira kwa Mulungu wathu.’ (Yesaya 61:1, 2; Luka 4:16-21) M’nthaŵi yathu, mkati mwa “masiku otsiriza” a dongosolo lino la zinthu, Yehova akuchititsa akapolo ake okhulupirika kulengeza ‘tsiku la kubwezera la Mulungu wathu’ m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka chenjezo kumitundu yonse. M’chilengezo chimenechi otsalira agwirizana ndi “khamu lalikulu” lomakulakula la ophunzira onga nkhosa a Yesu Kristu, monga momwe anawonedweratu m’masomphenya a m’Chivumbulutso 7:9-17.
18. Kodi ndim’chimwemwe chotani chimene okhulupirika a Mulungu adzagaŵanamo?
18 Onseŵa, otsalira ndi “khamu lalikulu,” amvera lamulo la mngelo la pa Chivumbulutso 18:4. Iwo atuluka m’Babulo Wamkulu. Kodi ndichifukwa ninji kuchitapo kanthu kotero kuli kofulumira? Chifukwa chakuti ayenera kutuluka m’Babulo Wamkulu “ana” ake achipembedzo asanaphwanyidwe ndi kuwonongedwa kupyolera mwa “chirombo” ndi ‘nyanga zake khumi’ mwamsanga Armagedo isanakanthe. Okhulupirika amenewa adzakhala ndi phande m’chimwemwe cha Koresi Wamkulu, Yesu Kristu. Iwo adzagwirizana ndi miyamba m’kunena kuti: “Haleluya; chipulumutso, ndi ulemerero, ndi mphamvu nza Mulungu wathu; pakuti maweruzo ake ali owona ndi olungama; ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake.”—Chivumbulutso 19:1, 2; yerekezerani ndi Yeremiya 51:8-11.
19. Kodi ndichimwemwe chotani chimene otsalira okhulupirika tsopano akusangalala nacho, ndipo kodi ndichimwemwe chachikulukulu kwambiri chotani chimene chikuwayembekezera?
19 Chiyambire 1919 Yehova wachitira anthu ake “zazikulu.” (Salmo 126:1-3) Chifukwa cha kukuzidwa kumeneku kwa mphamvu zake zomasula, zimene zimasonyeza kuti iye ali “Mulungu wokhulupirika,” otsalira owomboledwa akali okondwerabe mu mtima. (Deuteronomo 7:9) Iwo ali ndi chimwemwe chachikulu, koma pali chimwemwe chokulirapo chimene chikuwayembekezera. Chimenechi chidzakhala pamene akhala ndi mbali m’chimwemwe cha Koresi Wamkulu, Mfumu yolamulira, Yesu Kristu, panthaŵi imene awononga “ana” onse agulu lauchiŵanda limenelo.
20. Kodi ndani ena amene akugaŵanamo m’chimwemwe cha otsalira odzozedwa, ndipo chifukwa ninji?
20 Mamiliyoni a amene poyamba anali “andende” a Babulo Wamkulu athandizidwa kale kuthaŵa gulu lachipembedzo loweruziridwa ku chiwonongeko limenelo lisanawonongedwe mwachiwawa. Chotulukapo chakhala “khamu lalikulu” la “nkhosa zina.” Iwo tsopano ali ndi chiŵerengero, cha padziko lonse lapansi, cha oposa 3 000 000, ndipo sikukudziŵika chiŵerengero cha amene ati awonjoledwebe pakuwonongedwa kwa ulamuliro wa dziko lonse wachipembedo chonyenga. Mokhulupirika kugulu la Yehova, iwo akugaŵana chimwemwe cha otsalira mwa kugwirizana nawo m’kulengeza tsiku la kubwezera la Yehova pa Babulo Wamkulu wachipembedzo.
21. Kodi mkhalidwe wathu kulinga ku Babulo Wamkulu ndi andende ake uyenera kukhala wotani?
21 Pamenepa, tisadzigwirizanitse ndi ulamuliro wa chipembedzo chabodza umenewo. Pasakhalenso obwerera kwa iye m’masiku ano a kugwa kwake. Tipitirizetu kuthandiza andende ambiri monga momwe tingathere a Babulo Wamkulu kutuluka m’dongosolo limenelo loweruzidwira ku chiwonongeko Koresi Wamkulu asanapeze chilakiko chake chokondweretsa.