Moyo m’Dziko Latsopano Lamtendere
Pamene muyang’ana chithunzithunzi cha katrakiti kano, kodi muli ndi maganizo otani? Kodi mtima wanu sukulakalaka mtendere, chimwemwe, ndi kulemerera zowonedwa panopa? Ndithudi umatero. Koma kodi ndilo loto wamba, kapena zam’khutu, kukhulupirira kuti mikhalidwe imeneyi idzakhalapo padziko lapansi?
Mwinamwake anthu ambiri amalingalira motero. Lerolino zochitika ndizo nkhondo, upandu, njala, matenda, ukalamba—kungotchulapo zochepekera. Komabe pali chifukwa cha kukhalira ndi chiyembekezo. Poyang’ana mtsogolo, Baibulo limasimba za ‘miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene tikuyembekezera mogwirizana ndi lonjezo [la Mulungu], ndipo m’menemo mukhalitsa chilungamo.’—2 Petro 3:13, (New World Translation); Yesaya 65:17.
“Miyamba yatsopano” imeneyi ndi “dziko lapansi latsopano,” mogwirizana ndi kunena kwa Baibulo, sindiyo miyamba yeniyeni yatsopano kapena dziko lapansi latsopano lenileni. Mbulumbwayi dziko lapansi, ndi miyamba yeniyeni zinapangidwa mwanjira yangwiro, ndipo Baibulo limasonyeza kuti zidzakhala kosatha. (Salmo 89:36, 37; 104:5) “Dziko lapansi latsopano” lidzakhala chimangidwe chatsopano cha anthu olungama okhala padziko lapansi, ndipo “miyamba yatsopano” idzakhala ufumu wakumwamba wangwiro, kapena boma, limene lidzalamulira pachimangidwe chimenechi cha anthu padziko lapansi. Koma kodi kuli kwanzeru kukhulupirira kuti “dziko lapansi latsopano,” kapena dziko latsopano laulemerero, liri lothekera?
Eya, talingalirani chenicheni chakuti mikhalidwe yokondweretsa yotero inali mbali ya chifuno choyambirira cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi limeneli. Iye anaika aŵiri okwatirana oyambirira aumunthu m’Paradaiso wa padziko lapansi wa Edene nawapatsa gawo lokondweretsa lakuti: “Mubalane, muchuluke mudzaze dziko lapansi muligonjetse.” (Genesis 1:28) Inde, chifuno cha Mulungu chinali chakuti iwo abale ana ndipo potsirizira pake afutukulire Paradaiso wawo padziko lonse lapansi. Ngakhale kuli kwakuti pambuyo pake iwo anasankha kusamvera Mulungu, motero kutsimikizira kukhala osayenerera kukhala ndi moyo kosatha, chifuno choyambirira cha Mulungu sichinasinthe. Ndipo chiyenera kukwaniritsidwa m’dziko latsopano!—Yesaya 55:11.
Kwenikweni, pamene mupemphera pemphero la Ambuye, kapena la Atate Wathu, mukumapempha Ufumu wa Mulungu kuti udze, mukupempherera boma lake lakumwamba kuti lichotse kuipa padziko lapansi ndi kulamulira padziko latsopano limeneli. (Mateyu 6:9) Ndipo tingathe kukhala ndi chidaliro chakuti Mulungu adzayankha pemphero limenelo, chifukwa chakuti Mawu ake amalonjeza kuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.
Moyo m’Dziko Latsopano la Mulungu
Ufumu wa Mulungu udzabweretsa mapindu osayerekezereka padziko lapansi, ukumakwaniritsa kanthu kalikonse kabwino kamene Mulungu poyambirirapo analinganizira anthu ake kusangalala nako padziko lapansi. Maudani ndi tsankhu zidzatha, ndipo potsirizira pake aliyense padziko lapansi adzakhala bwenzi lowona la munthu aliyense. M’Baibulo, Mulungu amalonjeza kuti ‘adzathetsa nkhondo kumalekezero a dziko lapansi.’ “Mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Salmo 46:9; Yesaya 2:4.
Potsirizira pake dziko lonse lapansi lidzaloŵetsedwa mu mkhalidwe wonga munda wa paradaiso. Baibulo limati: “Chipululu ndi malo ouma adzakondwa ndipo dziko loti see lidzasangalala ndi kuphuka ngati duŵa. . . . Pakuti m’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti see. Ndipo mchenga wong’azimira udzasanduka thamanda, ndi nthaka yopanda madzi idzasanduka zitsime zamadzi.”—Yesaya 35:1, 6, 7.
Padzakhala chifukwa chabwino chokhalira wachimwemwe m’dziko lapansi Laparadaiso. Anthu sadzamvanso njala chifukwa cha kusoŵeka kwa chakudya. “Dziko lapansi lapereka zipatso zake,” limatero Baibulo. (Salmo 67:6; 72:16) Onse adzasangalala ndi zipatso za ntchito yawo, monga momwe Mlengi wathu amalonjezera: “Iwo adzawoka minda ya mphesa, ndi kudya zipatso zake. . . . Iwo sadzawoka, ndi wina kudya.”—Yesaya 65:21, 22.
M’dziko latsopano la Mulungu, simudzakhalanso anthu amene adzapanikizana m’nyumba zazikulu zamidadada kapena m’nyumba zosasamalidwa zauve, chifukwa chakuti Mulungu walinganiza kuti: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo . . . iwo sadzamanga, ndi wina kukhalamo.” Baibulo limalonjezanso kuti: “Iwo sadzagwira ntchito mwachabe.” (Yesaya 65:21-23) Motero anthu adzakhala ndi ntchito yopindulitsa, ndi yokhutiritsa. Moyo sudzakhala wonyong’onya.
M’nthaŵi yokwanira, Ufumu wa Mulungu udzabwezeretsa ngakhale maunansi amtendere amene anali m’munda wa Edene pakati pa zinyama, ndi pakati pa zinyama ndi anthu. Baibulo limati: “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choŵeta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera.”—Yesaya 11:6-9; Hoseya 2:18.
Tangoyerekezerani, m’dziko lapansi la Paradaiso matenda onse ndi utenda wakuthupi zidzachiritsidwanso! Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti: “Wokhalamo sadzanena ine ndidwala.” (Yesaya 33:24) “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.
Mmene Ziriri Zotheka kwa Inu
Ndithudi mtima wanu uyenera kusonkhezeredwa ndi malonjezo a Mulungu onena za moyo m’dziko lake latsopano lachilungamo. Ndipo pamene kuli kwakuti ena angalingalire kukwaniritsidwa kwa madalitso otero kukhala abwino mopambanitsa kuti nkukhala owona, iwo saali abwino mopambanitsa kuti sangachokere m’dzanja la Mlengi wathu wachikondi.—Salmo 145:16; Mika 4:4.
Ndithudi, pali ziyeneretso zofunikira kufikiridwa ngati titi tikhale ndi moyo kosatha m’dziko lapansi la Paradaiso lirinkudzalo. Yesu anasonyeza chachikulu, akumati m’pemphero kwa Mulungu: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”—Yohane 17:3.
Chotero ngati ife tikufunadi kukhala ndi moyo m’dziko latsopano la Mulungu, choyamba tiyenera kuphunzira chifuniro cha Mulungu ndiyeno kuchichita. Chifukwa chakuti chowonadi ndicho chakuti: ‘Dziko lino lapansi lipita ndi chilakolako chake, koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthaŵi yonse,’ kusangalala kosatha madalitso amene adzatsanuliridwa ndi Mlengi wathu wachikondi.—1 Yohane 2:17.
Kusiyapo ngati kwasonyezedwa mwanjira ina, mawu onse a Baibulo ogwidwa muno ngochokera mu Revised Union Nyanja Version.