Mutu 4
Mulungu—Kodi Iye Ndani?
1. (a) Kodi ndimilungu yotani imene yalambiridwa ndi anthu? (b) Kodi ndikusiyanitsa kotani kumene Baibulo limapanga pakati pa “milungu” ndi Mulungu”?
PADZIKO LONSE LAPANSI pali milungu yambiri yolambiridwa. M’Chishinto, Chibuda, Chihindu ndi zipembedzo zafuko muli mamiliyoni ambiri a milungu. Milungu yonga ngati Zeu ndi Herme inalambiridwa m’nthawi ya atumwi a Yesu. (Machitidwe 14:11 ,12) Motero Baibulo limavomereza kuti “pali ‘milungu’ yambiri,” koma limanenanso kuti “kwenikweni kwa ife kuli Mulungu mmodzi Atate, kwa amene zinthu zonse zichokera.” (1 Akorinto 8:5, 6, NW) Ngati mukanafunsidwa kuti, ‘Kodi Mulungu ameneyu ndani?’ kodi mukanati bwanji?
2. Kodi ndimalingaliro osiyanasiyana otani amene anthu ali nawo ponena za Mulungu?
2 ‘Iye ndiAmbuye,’ ambiri amatero. Kapena iwo angati: ‘Iye ndi Mzimu kumwamba.’ Bukhu lina lotanthauzira mawu limatcha Mulungu: “Wokhalako Wamkulu.” Atafunsidwa kuti: ‘Kodi dzina la Mulungu ndani?’ anthu ena amayankha kuti, ‘Yesu.’ Ena samaganizira Mulungu kukhala munthu, koma monga nyonga yamphamvu imene iri yopezeka kulikonse. Ndipo ena amakayikiradi ngati kuli Mulungu. Kodi tingatsimikizire kuti aliko?
MULUNGU ALIKODI
3. Kodi nyumba imakhalapo motani?
3 Pamene muyang’ana nyumba yokongola, kodi munayamba mwadabwa amene womangayo anali? Ngati munthu wina akanakuuzani kuti palibe aliyense adamanga nyumbayo, koma kuti inangokhalako yokha, kodi mukanakhulupirira? Ndithudi ayi! Monga momwe wolemba Baibulo wina ananenera: “Nyumba iriyonse iri naye wina woimanga.” Aliyense akudziwa zimenezo. Chabwino, pamenepa, kodi sitingavomereze lingaliro lomveka la wolemba Baibuloyo: “Wozimanga zonse ndiye Mulungu”? —Ahebri 3:4.
4. Kodi mabiliyoni ambiri a nyenyezi anakhalapo motani?
4 Lingalirani chilengedwe chonse limodzi ndi mabiliyoni a mabiliyoni ake a nyenyezi. Komabe onsewo amayenda m’mlengalenga mogwirizana ndi malamulo amene akuwasunga mogwirizana kwambiri ndi ina ndi inzake. “Kodi ndani amene walenga zinthu zimenezi?” linali funso lofunsidwa kalekale. Yankho loperekedwalo limamveka: “Amene atulutsa khamu lawo ndi kuziwerenga; azitcha zonse maina awo.” (Yesaya 40:26) Ndithudi kukakhala kopusa kuganizirakuti mabiliyoni a nyenyezi anangodzipanga, ndipo popanda chitsogozo chirichonse, anapanga magulu aakulu anyenyezi amene amayenda mwadongosolo lodabwitsa loterolo!—Salmo 14:1.
5. (a) Kodi pali kuthekera kotani kwakuti, mwa iwo okha, mapatsi angagwirizane kupanga chochekera nyama? (b) Kodi zimenezi zimasonyezanji ponena za chilengedwe chathu?
5 Chilengedwe chonse cholinganizidwa kwambiri chimenechi sichikanangokhalako chokha. Mlengi wanzeru wokhala ndi mphamvu yaikulu anafunika. (Salmo 19:1, 2) Wabizinesi wina amene anafunsidwa chifukwa chake anakhulupirira Mulungu anafotokoza kuti mufakitale yake kumatenga masiku awiri kwa msungwana kuphunzira kulumikiza mapatsi 17 a chochekera nyama. “Ine ndine wopanga masupuni ndi mafoloko chabe,” iye anatero. “Koma izi ndikudziwadi, kuti mungathe kukhutchumuza mapatsi 17 a chochekera nyamawo m’chotsukira kwa zaka zotsatirapo mabiliyoni 17 ndipo inu simudzakhala ndi chochekera nyama.” Chilengedwe chino, kuphatikizapo mitundu yambiri ya moyo padziko lapansi, nchocholowanacholowana kwambirimbiri koposa chochekera nyama. Ngati makina oterowo amafuna wopanga waluso, tingakhale otsimikizira kuti Mulungu Wamphamvuyonse anafunika kulenga zinthu zonse. Kodi ulemu suyenera kupita kwa iye kaamba ka zimene wachita?—Chivumbulutso 4:11; Machitidwe 14:15-17; 17:24-26.
MULUNGU MUNTHU WENIWENI
6. Kodi nchifukwa ninji tingakhalire otsimikiza kuti Mulungu ndimunthu weniweni?
6 Pamene anthu ochuluka amati iwo amakhulupirira Mulungu, ambiri samamganizira kukhala munthu weniweni. Kodi iye ndiyedi? Eya, kungawonedwe kuti kumene kuli nzeru kuli maganizo. Mwa chitsanzo, tinganene kuti, ‘Sindingasinthe maganizo anga.’ Ndipo tikudziwa kuti kumene kuli maganizo kuli ubongo m’thupi la mpangidwe wotsimikizirika. Motero, pamenepa, maganizo akulu ochititsa zolengedwa zonse ngaMunthu wamkulu, Mulungu Wamphamvuyonse. Ngakhale kuli kwakuti iye alibe thupi lowoneka, iye ali ndi lauzimu. Kodi munthu wauzimu ali ndi thupi? Inde, Baibulo limati: “Ngati pali thupi lachibadwidwe, palinso lauzimu.”—1 Akorinto 15:44; Yohane 4:24.
7. (a) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Mulungu ali ndi malo kumene amakhala? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti iye ali ndi thupi?
7 Popeza kuti Mulungu ndimunthu wokhala ndi thupi lauzimu, iye ayenera kukhala ndi malo okhala. Baibulo limatiuza kuti kumwamba ndiko “malo okhazikitsidwa okhala” a Mulungu. (1 Mafumu 8:43, NW) Ndiponso, tikuuzidwa kuti “Kristu analowa. . . m’mwamba mwenimwenimo, tsopano kukawonekera pamaso pa nkhope ya Mulungu kaamba kaife.” (Ahebri 9:24, NW) Anthu ena adzafupidwa moyo kumwamba limodzi ndi Mulungu, pa nthawi imeneyo iwo adzalandira matupi auzimu. Iwo pa nthawi imeneyo adzawona Mulungu, Baibulo limatero, ndi kukhalanso onga iye. (1 Yohane 3:2) Zimenezinso, zimasonyeza kuti, Mulungu ndimunthu, ndi kuti ali ndi thupi.
8, 9. (a) Kodi ndimotani mmene chitsanzo cha nyumba yamagetsi chimasonyezera mphamvu ya Mulungu yofika kutali? (b) Kodi nchiyani chimene chiri mzimu woyera wa Mulungu, ndipo kodi ungachitenji?
8 Koma munthu wina angafunse kuti: ‘Ngati Mulungu ali munthu weniweni amene amakhala pamalo ena kumwamba, kodi iye angawone motani chinthu chirichonse chimene chimachitika kulikonse? Ndipo ndimotani mmene mphamvu yake ingamvedwere m’mbali iriyonse ya chilengedwe?’ (2 Mbiri 16:9) Chenicheni chakuti Mulungu ndimunthu m’njira iriyonse sichimachepetsa mphamvu yake kapena ukulu. Ndiponso sichiyenera kuchepetsa ulemu wathu kwa Iye. (1 Mbiri 29:11-13) Kutithandiza kuzindikira zimenezi, lingalirani ziyambukiro zofika kutali za nyumba yamagetsi.
9 Nyumba yamagetsi imakhala ndi malo ena mumzinda kapena pafupi nawo. Koma nyesi yake imagawidwa m’dera lonse limenelo, ikumapereka magetsi ndi mphamvu. Nkofanana ndi Mulungu. Iye ali kumwamba. (Yesaya 57:15; Salmo 123:1) Komabe mzimu wake woyera, umene uli mphamvu yake yogwira ntchito, ungamvedwe kulikonse, m’chilengedwe chonse. Mwa njira ya mzimu wake woyera Mulungu analenga kumwamba, dziko lapansi ndi zinthu zamoyo zonse. (Salmo 33:6; Genesis 1:2; Salmo 104:30) Kuti alenge zinthu zimenezi, Mulungu sanafunikire kukhalapo m’thupi. Iye angatumize mzimu wake, mphamvu yake yogwira ntchito, kuchita chirichonse chimene akufuna ngakhale kuli kwakuti iye ali kutali. Ha, ndiMulungu wodabwitsa chotani nanga! —Yeremiya 10:12; Danieli 4:35.
MTUNDU WA MUNTHU UMENE MULUNGU ALI
10. Kodi njira imodzi njotani mu imene ife tingafikire pa kudziwa Mulungu?
10 Kodi Mulungu ndi mtundu wa munthu amene tikafika pa kumkonda ngati titamdziwa bwino? ‘Mwina mwakedi,’ mungatero, ‘koma popeza kuti sitingawone Mulungu, kodi tingafike pa kumdziwa motani?’ (Yohane 1:18) Baibulo limasonyeza njira imodzi pamene limati: “Pakuti mikhalidwe yake yosawoneka ikuwoneka bwino lomwe kuyambira pa kulengedwa kwa dziko kumkabe mtsogolo, chifukwa chakuti iyo ikuzindikiridwa ndi zinthu zopangidwa, ngakhale mphamvu yake yamuyaya ndi Umulungu.” (Aroma 1:20, NW) Motero zinthu zimene Mulungu walenga zingatithandize kuzindikira chimene Mulungu ali, ngati tizipendadi ndi kuziganizira.
11. Kodi tingaphunzirenji ponena za Mulungu mwa zinthu zimene walenga?
11Monga momwe tawonera, kuyang’ana kuthambo lanyenyezi kumatiuzadi ukulu ndi mphamvu yaikulu za Mulungu! (Salmo 8:3, 4; Yesaya 40:26) Ndiyeno talingalirani dziko lapansi. Mulungu analiika m’mlengalenga motero limapeza kuchuluka koyenera kwa kutentha ndi kuwunika kochokera kudzuwa. Ndipo talingalirani zungulirezungulire wamadzi. Mvula imagwa kuthirira dziko lapansi. Madzi amalowa m’mitsinje, imene imalowa m’nyanja. Dzuwa limanyamula madzi kuchokera m’nyanja monga nkhungu, imene imagwa monga mvula kuthiriranso dziko lapansi. (Mlaliki 1:7) Pali zungulurezungulire wochuluka kwambiri wodabwitsa amene Mulungu anayambitsa kugwira ntchito kupereka chakudya, mthunzi ndi zinthu zonse zimene munthu ndi nyama zikufuna! Ndipo kodi zinthu zodabwitsa zonsezi zimatiuzanji ponena za mtundu wa munthu amene Mulungu ali? Kuti iye ndiMulungu wa nzeru yaikulu ndi kuti iye ngwaufulu koposa ndipo amasamalira zolengedwa zake.—Miyambo 3:19, 20; Salmo 104:13-15, 24, 25.
12. Kodi thupi lanu limakuphunzitsani chiyani ponena za Mulungu?
12 Talingalirani thupi lanu la inu mwini. Ilo mwachiwonekere linapangidwa kuti lichite zambiri koposa kukhala ndi moyo chabe. Ilo linalinganizidwa modabwitsa kwenikweni kusangalala ndi moyo. (Salmo 139:14) Maso athu angawone osati zakuda ndi zoyera zokha komanso mawonekedwe, ndipo dziko lapansi ladzaza mawonekedwe ochuluka oti tisangalale nawo. Tinganunkhize ndi kulawa. Motero kudya sikuli chabe ntchito yofunika; kungakhale kosangalatsa. Motero mphamvu zoterozo siziri chofunika kotheratu cha moyo, koma izo ziri mphatso yochokera kwa Mulungu wachikondi, waufulu ndi wolingalira.—Genesis 2:9; 1 Yohane 4:8.
13. Kodi mukuphunziranji ponena za Mulungu mwa njira yake yochitira ndi anthu?
13 Kupenda zochita za Mulungu ndi anthu kumasonyezanso mtundu wa Mulungu umene iye ali. Iye ali ndi lingaliro lamphamvu la chilungamo. Iye samasonyeza tsankho ku mitundu ina ya anthu. (Machitidwe 10:34, 35) Iye alinso wachifundo ndi wokoma mtima. Baibulo ponena za zochita zake ndi mtundu wa Israyeli, umene iye anaulanditsa mu ukapolo mu Igupto, limati: “Iye anali wachifundo; . . .iye anapitiriza kukumbukira kuti iwo anali anthu.” Komabe Aisrayeli kawirikawiri anali osamvera, ndipo zimenezo zinapangitsa Mulungu kukwiya. Monga momwe Baibulo likunenera: “Iwo ankampangitsa kumva ululu. . . ndipo iwo anapweteka ngakhale Woyera wa Israyeli.” (Salmo 78:38-41; 103:8, 13, 14, NW) Ndiponso, pamene atumiki ake ali omvera malamulo ake, Mulungu amakondwera. (Miyambo 27:11) Ndiponso Mulunguamafotokoza mmene amamvera pamene atumiki ake amavutitsidwa ndi adani: “Iye amene akukhudza inu akukhudza diso langa.” (Zekariya 2:8, NW) Kodi inu simukusonkhezereka kukonda Mulungu amene ali ndi chikondi choterocho kwa anthu onyozeka ndi osanunkha kanthu a mafuko ndi mitundu yonse?—Yesaya 40:22; Yohane 3:16.
KODI MULUNGU NDIYESU KAPENA UTATU?
14. Kodi chiphunzitso Chautatu nchotani?
14 Kodi Mulungu wodabwitsa ameneyu ndani? Anthu ena amati dzina lake ndiYesu. Ena amati iye ndiUtatu, ngakhale kuli kwakuti liwulo “utatu” silimawoneka m’Baibulo. Malinga ndi kunena kwa chiphunzitso cha Utatu, muli anthu atatu mwa Mulungu mmodzi, ndiko kuti, pali “Mulungu mmodzi, Atate, Mwana nd Mzimu Woyera.” Magulu ambiri achipembedzo amaphunzitsa zimenezi, ngakhale kuli kwakuti iwo amavomereza kuti ndicho “chinsinsi.” Kodi malingaliro a Mulungu oterowo ngolondola?
15. Kodi ndimotani mmene Baibulo limasonyezera kuti Mulungu ndi Yesu ali anthu awiri osiyana amene sali olingana?
15 Eya, kodi Yesu anayamba wanena kuti iye anali Mulungu? Ayi, sanatero. M’malo mwake, m’Baibulo iye amatchedwa “Mwana wa Mulungu.” Ndipo iye anati: “Atate ali wamkulu ndi ine.” (Yohane 10:34-36; 14:28) Ndiponso, Yesu anafotokoza kuti panali zinthu zina zimene iye ngakhale angelo sanadziwe koma zimene Mulungu yekha anadziwa. (Marko 13:32) Kuwonjezerapo, pa nthawi ina Yesu anapemphera kwa Mulungu, kuti: “Sikufuna kwanga ayi, komatu kwanu kuchitike.” (Luka 22:42) Ngati Yesu akanakhala Mulungu Wamphamvuyonse, iye sakanapemphera kwa iye yekha, kodi akanatero? Kunena zowona, motsatizana ndi imfa ya Yesu, Malemba amati: “Yesu ameneyu Mulungu anamuukitsa.” (Machitidwe 2:32, NW) Motero Mulungu Wamphamvuyonse ndi Yesu ali mwachiwonekere anthu awiri osiyana. Ngakhale pambuyo pa imfa ndi chiukiriro ndi kukwera kwakekumwamba, Yesu anali chikhalirebe wosalingana ndi Atate wake.—1 Akorinto 11:3; 15:28.
16. Ngakhale kuli kwakuti Yesu akutchedwa kukhala “Mulungu,” kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti iye sali Mulungu Wamphamvuyonse?
16 ‘Koma kodi Yesu sakutchedwa mulungu m’Baibulo?’ wina angatero. Zimenezi nzowona. Komabe Satana akutchedwanso mulungu. (2 Akorinto 4:4) Pa Yohane 1:1, amene amatchula Yesu kukhala “Mawu,” matembenuzidwe ena Abaibulo amati: “Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawuyo anali ndi Mulungu, ndipo Mawuyo anali Mulungu.” Koma wonani, vesi 2 limanena kuti Mawuyo anali “pachiyambi ndi Mulungu.” Ndipo ngakhale kuli kwakuti anthu awona Yesu, vesi 18 limanena kuti “palibe munthu wawona Mulungu pa nthawi iriyonse.” (Authorized kapena King James Version) Motero tikuwona kuti matembenuzidwe ena a vesi 1 amapereka lingaliro loyenera la chinenero choyamba pamene iwo amati: “Mawuyo anali ndi Mulungu, ndipo Mawuyo anali wonga mulungu,” kapena anali “mulungu” ndiko kuti, Mawuyo anali wamphamvu wonga mulungu. (An American Translation) Mwachiwonekere, Yesu sali Mulungu Wamphamvuyonse. Kunena zowona, Yesu anatchula Atate wake kukhala “Mulungu wanga” ndipo monga “Mulungu wowona yekha.”—Yohane 20:17; 17:3.
17. Kodi ndimotani mmene kutsanuliridwa kwa mzimu woyera pa atsatiri a Yesu kumatsimikizirira kuti suli munthu?
17 Ponena za “Mzimu Woyera,” wotchedwa Munthu wachitatu wa Utatu, tawona kale kuti umenewu suli munthu koma mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu. Yohane Mbatizi ananena kuti Yesu akabatiza ndi mzimu woyera, monga momwedi Yohane anali kubatizira ndi madzi. Chifukwa cha chimenecho, m’njira imodzimodziyo imene madzi saliri munthu, mzimu woyera suli munthu. (Mateyu 3:11) Chimene Yohane ananeneratu chinakwaniritsidwa pamene, motsatizana ndi imfa ndi kuukitsidwa kwa Yesu, mzimu woyera unatsanuliridwa pa atsatire ake osonkhana m’Yerusalemu. Baibulo limati: “Anadzazidwa onse ndi mzimu woyera.” (Machitidwe 2:4) Kodi iwo “anadzazidwa” ndi munthu? Ayi, koma iwo anadzazidwa ndi mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu. Motero maumboni amamveketsa bwino lomwe kuti Utatu suli chiphunzitso Chabaibulo. Kwenikweni, kalekale Yesu asanafike padziko lapansi milungu inalambiridwa m’magulu a atatu, kapena mautatu, m’malo onga ngati Igupto ndi Babulo wakale.
DZINA LA MULUNGU
18. (a) Kodi “Mulungu” ndidzina lenileni la Mulungu Wamphamvuyonse? (b) Kodi dzina lake lenileni ndani?
18 Mosakayikira aliyense amene mukumdziwa ali ndi dzina. Mulungu alinso ndi dzina lake kuti limlekanitse ndi ina yonse. ‘Kodi “Mulungu” sidzina lake?’ ena angatero. Ayi, pakuti “Mulungu” liri chabe dzina laulemu, monga momwedi “Pulezidenti,” “Mfumu” ndi “Woweruza” aliri maina aulemu. Timamva dzina la Mulungu kuchokera m’Baibulo, mmene limapezeka pafupifupi nthawi 7,000. Mwa chitsanzo, mu Revised Nyanja (Union) Version, Salmo 83:18 limati: “Kuti adziwe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi.” Ndiponso, dzina la Mulungu likupezeka m’Mabaibulo ochuluka pa Chivumbulutso 19:1-6 monga mbali ya mawuwo “Aleluya.”Amenewa amatanthauza “tamandani Ya,” mpangidwe wofupikitsidwa wa Yehova.
19. (a) Kodi nchifukwa ninji anthu ena amadabwa kuwona dzina la Mulungu m’Baibulo mwawo? (b) Kodi dzinalo limapezeka pati mu King James Version?
19 Anthu ena amadabwa kuwona dzina la Mulungu m’Baibulo mwawo. Zimenezi kawirikawiri ziri chifukwa chakuti Baibulo lawo ndilo limene silimagwiritsira ntchito kawirikawiri dzina la Mulungu. Mwa chitsanzo, King James Version, imagwiritsira ntchito dzinalo “Yehova” mwa ilo lokha kokha pa Eksodo 6:3, Salmo 83:18 ndi Yesaya 12:2 ndi 26:4. Komabe, pamene Baibulo limeneli limasulira dzina la Mulungu mwa dzina laulemulo “Ambuye” kapena “Mulungu,” ilo nthawi zonse limalemba dzina laulemu limeneli m’zilembo zazikulu, monga “AMBUYE’ ndi “MULUNGU,” kumene kumalilekanitsa ndi mawu awambawo “Ambuye” ndi “Mulungu.” Wonani zimenezi pa Salmo 110:1.
20. (a) Kodi nchifukwa ninji dzina la Mulungu silinagwiritsidwe ntchito nthawi zonse? (b) Kodi liyenera?
20 ‘Koma kodi nchifukwa ninji,’ mungatero, ‘dzina la Mulungu silikugwiritsiridwa ntchito m’malo alionse amene likupezeka m’bukhu Labaibulo loyambirira? Kodi nchifukwa ninji maina aulemuwo AMBUYE ndi MULUNGU anagwiritsiridwa ntchito mofala m’malo mwake?’ M’mawu ake oyamba American Standard Version limafotokoza chifukwa chake limagwiritsira ntchito dzina la Mulungu Yehova, ndi chifukwa chake kwa nthawi yaitali dzina limenelo silinagwiritsiridwe ntchito: “Okonzetsera Achimereka, pambuyo pa kulingalira kosamala, anafikitsidwa ku lingaliro limodzi lakuti mwambo Wachiyuda, umene unawona Dzina la Mulungu kukhala lopatulika kwambiri kuti litchulidwe, suyeneranso kulamulira m’Chingelezi kapena m’bukhu lina lirilonse. . . Dzina lake limeneli, lomodzi ndi kuchuluka kwake kwa zigwirizano zopatulika, tsopano labwezeretsedwa kumalowo m’bukhu lopatulika ku limene liri ndi kuyenera kosafunsidwa.” Inde, amuna amene anatembenuza Baibulo limenelo kulowa m’Chingelezi analingalirakuti zifukwa zimene dzina la Mulungu linasiyidwira sizinali zabwino. Motero iwo analibwezeretsa m’Baibulo m’malo ake oyenera.
21. Kodi nchiyani chimene Catholic Douay Version limanena ponena za dzinalo Yehova?
21 Komabe, pali awo amene amatsutsa kuti liwulo “Yehova” siliyenera kugwiritsiridwa ntchito chifukwa chakuti siliri kwenikweni dzina la Mulungu. Mwa chitsanzo, Catholic Douay Version, limene silimagwiritsira ntchito dzina la Mulungu m’bukhu lake lonse, imati m’mawu ake amtside ofotokoza Eksodo 6:3: “Amakono ena apanga dzinalo Yehova . . . kutchulidwa kwenikweni kwa dzinalo, kumene kuli m’bukhu Lachihebri, mwa kusagwiritsiridwa ntchito kwa nthawi yaitali, tsopano kwatayika kotheratu.”
22. (a) Kodi ndimotani mmene dzina la Mulungu likuimiridwira m’chinenero Chachihebri? (b) Kodi nchifukwa ninji pali vuto la kudziwa mmene dzina la Mulungu linatchulidwira poyambirira?
22 Inde, monga Baibulo Lachikatolikalo likunenera pano, dzina la Mulungu limapezekadi m’bukhu Lachihebri, Chihebri chikumakhala chinenero chimene mabukhu a Baibulo oyambirira 39 analembedwamo. Dzinalo likusonyezedwa m’menemo ndi zilembo zinai Zachihebri, YHWH. M’thawi zakale chinenero Chachihebri chinalembedwa popanda mavaulo, zilembo zonga ngati a, e, i, o ndi u, zimene zimatithandiza kupereka kutchula koyenera ku mawu. Chifukwa cha chimenecho, vuto lerolino nlakuti tiribe njira yodziwira kwenikweni mavaulo amene Ahebri anagwiritsira ntchito limodzi ndi makonsonantiwo YHWH.
23. Kodi ndimotani mmene sipeloyo “nymb” yotanthauza “nyumba” ingatithandizire kuzindikira vuto la kutchula dzina la Mulungu?
23 Kuti atithandize kumvetsetsa vutolo, lingalirani liwulo “nyumba.” Tinene kuti ilo linayamba nthawi zonse kulembedwa “nymb,” ndi kuti, m’kupita kwa nthawi, liwulo silinali kutchulidwa. Pamenepa, kodi ndimotani mmene munthu, wokhala ndi moyo zaka 1,00 kuchokera tsopano akadziwira kutchula “nymb” pamene ataliwona litalembedwa? Popeza kuti iye sadalimve likutchulidwa ndipo sanadziwe mavaulo amene anali m’liwulo, iye ndithudi sakadziwa. Nkofanana ndi dzina la Mulungu. Sikukudziwidwa kwenikweni mmene linatchulidwira, ngakhale kuli kwakuti asikolala ena amaganiza kuti “Yahweh” nkolondola. Komabe, mpangidwewo “Yehova” wakhala ukugwiritsiridwa ntchito kwa zaka mazana ambiri ndipo ngwodziwika mofala kwambiri.
24. (a) Kuti tikhale onena chimodzi, kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kuti tigwiritsire ntchito dzina la Mulungu? (b) Polingalira Machitidwe 15:14, kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu?
24 Komabe, kodi tiyenera kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu, ngakhale kuli kwakuti tingakhale tisakulitchula kwenikweni m’njira imene linatchulidwira poyambirira? Eya, timagwiritsira ntchito maina a anthu ena m’Baibulo, ngakhale kuli kwakuti sitikuwatchula m’njira imene mainawo anatchulidwira m’Chihebri choyambirira. Mwa chitsanzo, dzina la Yesu limatchulidwa “Yesh’ua” m’Chihebri. Momwemonso, nkoyenera kugwiritsira ntchito dzina la Mulungu, limene lavumbulidwa m’Baibulo, kaya tikulitchula “Yahweh,” “Yehova,” kapena m’njira inanso yofala m’chinenero chathu. Chimene chiri cholakwa ndicho kulephera kugwiritsira ntchito dzina limenelo. Kodi nchifukwa ninji? Nchifukwa chakuti awo amene sakuligwiritsira ntchito sakagwirizanitsidwa ndi anthu amene Mulungu akutenga kuti akhale “anthu a dzina lake.” (Machitidwe 15:14, NW) Sitiyenera kudziwa kokha dzina la Mulungu komanso kulitamanda pamaso pa ena, monga momwe anachitira Yesu pamene anali padziko lapansi.—Mateyu 6:9; Yohane 17:6, 26.
MULUNGU WA CHIFUNO
25. (a) Kodi ndizinthu zotani zonena za Mulungu kungakhale kovuta kwa ife kumvetsetsa? (b) Kodi nchiyani chimene chinasonkhezera Yehova kuyamba kulenga?
25 Ngakhale kungakhale kovuta kwa maganizo athu kumvetsetsa, Yehova analibe chiyambi ndipo sadzakhala ndi mapeto. Iye ndiye “Mfumu ya muyaya.” (Salmo 90:2; 1 Timoteo 1:17, NW) Asanayambe kulenga, Yehova anali yekhayekha kumwamba. Komabe iye sanakhale wosungulumwa, pakuti iye ngokwanira mwa iye yekha ndipo samasowa kanthu. Chinali chikondi chimene chinamsonkhezera kuyamba kulenga, kupereka moyo kwa ena kuti asangalale nawo. Zolengedwa zoyamba za Mulungu zinali anthu auzimu onga iye mwini. Iye anali ndi gulu lalikulu la ana amuna akumwamba ngakhale dziko lapansi lisanalinganizidwire anthu. Yehova analinganiza kuti iwo apeze chikondwerero chachikulu m’moyo ndi m’ntchito imene iye anawapatsa kuti achite.—Yobu 38:4, 7.
26. Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikizira kuti chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi chidzakwaniritsidwa?
26 Pamene dziko lapansi linalinganizidwa, Yehova anaika awiriwo, Adamu ndi Hava, m’mbali ina ya dziko lapansi yopangidwa kale kukhala paradaiso. Chinali chifuno chake kuti iwo akhale ndi ana amene akamvera ndi kumlambira, ndi amene akafutukulira paradaiso ameneyo padziko lonse lapansi. (Genesis 1:27, 28) Komabe, monga momwe tamvera, chifuno chabwino kwambiri chimenecho chinadodometsedwa. Adamu ndi Hava anasankha kusamvera Mulungu, ndipo chifuno chake sichinakwaniritsidwe. Koma chidzakwaniritsidwa, pakuti kungakhale kuvomereza kugonjetsedwa kwa Yehova kusachita zimene amalinganiza. Ndipo sangachite zimenezo! “Chirichonse chimene ndikondwera nacho ndizachita, iye akutero. “Ndachinenadi; ndidzachibweretsa.”—Yesaya 46:10, 11, NW.
27. (a) Kodi nchifukwa ninji tiri ndi mlandu kwa Mulungu? (b) Motero kodi ndifunso lotani limene tiyenera kuganizira kwambiri?
27 Kodi mukuwona pamene mungalowere m’chifuno cha Mulungu? Sikuli chabe mwa kuchita chirichonse chimene mukufuna popanda kulingalira chimene chiri chifuniro cha Mulungu. Zimenezo ndizo zimene Satana ndi Adamu ndi Hava anachita. Iwo anadziwa chimene chinali chifuniro cha Mulungu koma iwo sanachichite. Ndipo Mulungu anawaimba mlandu. Kodi nafenso, tiri ndi mlandu, kwa Mulungu? Inde, chifukwa chakuti Mulungu ndiye Magwero a moyo wathu. Moyo wathu ngwodalira pa iye. (Salmo 36:9; Mateyu 5:45) Pamenepa, kodi ndikufikira pati pamene timakhalira ndi miyoyo yathu mogwirizana ndi chifuno cha Mulungu kwa ife? Tiyenera kuganizira mwamphamvu ponena za zimenezi, chifukwa chakuti mwayi wathu wa moyo wosatha umadalirapo.
KULAMBIRA KWAKE YEHOVA
28. Kodi ndizothandiza zotani zimene anthu ena agwiritsira ntchito kulambira Mulungu?
28 Mmene tikulambirira Yehova nkofunika. Tiyenera kulambira m’njira imene iye amanena, ngakhale kuli kwakuti imeneyi ingakhale yosiyana ndi njira imene taphunzitsidwa. Mwa chitsanzo, chakhala chizolowezi kwa anthu ena kugwiritsira ntchito mafano m’kulambira kwawo. Iwo anganene kuti sakulambira fano, koma kuti kuchiwona ndi kuchikhudza kumawathandiza kulambira Mulungu. Komabe kodi Mulungu akutifuna kuti timlambire mothandizidwa ndi mafano?
29. Kodi ndimotani mmene Baibulo limasonyezera kuti nkolakwa kugwiritsira ntchito mafano m’kulambira?
29 Ayi, iye sakutero. Ndipo kaamba ka chifukwa chimenechichi Mose anauza Aisrayeli kuti Mulungu sanawonekere kwa iwo mu mpangidwe uliwonse wowoneka. (Deuteronomo 4:15-19) Kunena zowona, limodzi la Malamulo Khumi limati: “Musadzadzipangire fano losema kapena chifaniziro chirichonse cha chinthu chirichonse. . . musadzazigwadire kapena kuzitumikira.” (Eksodo 20:4, 5, Catholic Jerusalem Bible) Yehova yekha ayenera kulambiridwa. Baibulo limasonyeza mobwerezabwereza mmene kuliri kolakwa kupanga fano kapena kuligwadira, kapena kulambira munthu aliyense kapena chinthu chirichonse kusiyapo Yehova.—Yesaya 44:14-20; 46:6, 7; Salmo 115:4-8.
30. (a) Kodi nchiyani chimene Yesu ndi atumwi ake ananena chimene chimasonyeza kuti kugwiritsiridwa ntchito kwa mafano nkolakwa? (b) Malinga ndi kunena kwa Deuteronomo 7:25, kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa ndi mafano?
30 Pamenepa, monga momwe tingakhale titayembekezerera, Yesu sanagwiritsire ntchito mafano m’kulambira. “Mulungu ndiye Mzimu,” iye anatero, “ndipo awo omlambira ayenera kulambira ndi mzimu ndi chowonadi.” (Yohane 4:24, NW) Pochita mogwirizana ndi uphungu umenewu, palibe aliyense wa atsatiri oyambirira a Yesu anagwiritsira ntchito mafano monga zithandizo m’kulambira. Kunena zowona, mtumwi wake Paulo analemba kuti: “Tiyendayenda mwa chikhulupiriro si mwa chiwonekedwe.” (2 Akorinto 5:7) Ndipo mtumwi wake Yohane anachenjeza kuti: “Dzisungireni nokha kupewa mafano.” (1 Yohane 5:21) Bwanji osaunguzaunguza m’nyumba mwanu ndi kudzifunsa kaya ngati mukutsatira chilangizo chimenechi?—Deuteronomo 7:25.
31. (a) Ngakhale ngati sitingamvetsetse chifukwa cha lamulo lina la Mulungu, kodi nchiyani chimene chidzatisonkhezera kulimvera? (b) Kodi nchiyani chimene tiyenera kuyesa kuchita, ndipo kodi ndi chiitano chotani chimene tiyenera kulandira?
31 Kulambira Yehova, Mlengi, m’njira imene iye amasonyeza nkotsimikizirika kutipatsa chimwemwe chenicheni. (Yeremiya 14:22) Baibulo limasonyeza kuti zofuna zake ziri kaamba ka ubwino wathu, limodzi ndi cholinga cha thanzi lamuyaya. Nzowona kuti pangakhale nthawi zina, chifukwa cha chidziwitso ndi nzeru zathu zochepa, kuti sitikuzindikira mokwanira chifukwa chake lamulo lina loperekedwa ndi Mulungu liri lofunika kwambiri, kapena mmene limagwiriradi ntchito kaamba ka ubwino wathu. Komabe chikhulupiriro chathu champhamvu chakuti Mulungu amadziwa kwambiri koposa mmene tikudziwira chiyenera kutisonkhezera kumumvera ndi mtima wofunitsitsa. (Salmo 19:7-11) Pamenepa, tiyeni tipange kuyesayesa kulikonse kuti tiphunzire zonse zimene tingathe ponena za Yehova, tikulamalandira chiitanocho: “Tiyeni, tipembedze tiwerame; tigwade pamaso pa Yehova, amene anatilenga: pakuti iye ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za m’dzanja mwake.”—Salmo 95:6, 7.
[Bokosi patsamba 42]
Malo anai m’mene dzina la Mulungu limapezeka mu King James Version akuwoneka pano
3 Ndipo ndinawonekera kwa Abrahamu, kwa Isake, ndi kwa Yakobo ndi dzina lakuti Mulungu Wamphamvuyonse, koma ndi dzina langa YEHOVA sindinadziwike kwa iwo.
18 Kuti anthu akadziwe kuti inu, amene dzina lanu lokha ndinu YEHOVA, ndinu wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi.
2 Tawonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzadalira ndi kusachita mantha: pakuti AMBUYE YEHOVA ndiye nyonga yanga ndi nyimbo yanga; iyenso wakhala chipulumutso changa.
4 Khulupirirani AMBUYE kosatha pakuti mwa AMBUYE YEHOVA muli nyonga yosatha.
[Zithunzi pamasamba 34, 35]
Ngati nyumba iri ndi womanga,. . . ndithudi chilengedwe chocholowanacholowana kwambiricho chiyenera kukhalanso ndi Mlengi
[Chithunzi patsamba 39]
Popeza kuti Yesu anapemphera kwa Mulungu, akumapempha kuti chifuniro cha Mulungu, osati chake, chichitidwe, awiriwo sangakhale munthu mmodzimodziyo
[Chithunzi pamasamba 40, 41]
Kodi ndimotani mmene mzimu woyera ungakhalire munthu, pamene unadzaza ophunzira okwanira 120 pa nthawi imodzimodziyo?
[Chithunzi patsamba 45]
Kodi nkoyenera kugwiritsira ntchito mafano m’kulambira?