Chikhulupiriro
Tanthauzo: “Chikhulupiriro ndicho chiyembekezo chotsimikiziridwa cha zinthu zoyembekezeredwa, chisonyezero chowonekera bwino cha zenizeni ngakhale sizinapenyedwe.” (Aheb. 11:1, NW) Chikhulupiriro chowona sichiri chonyengeka, ndiko kuti, chokonzekera kukhulupirira chinthu popanda umboni wabwino kapena kokha chifukwa chakuti munthuyo afuna kuti zikhalire momwemo. Chikhulupiriro chowona chimafikira maziko kapena chidziŵitso chachikulu, kuzolowerana ndi umboni, kuphatikizapo chiyamikiro chochokera pansi pa mtima cha zimene umboniwo ukusonyeza. Chotero, ngakhale kuti kuli kosatheka kukhala ndi chikhulupiriro chenicheni popanda chidziŵitso cholongosoka, Baibulo limanena kuti “ndi mtima” munthu amasonyeza chikhulupiriro.—Aroma 10:10.
Kodi nchifukwa ninji anthu ambiri alibe chikhulupiriro?
Chikhulupiriro ndicho chipatso cha mzimu wa Mulungu, ndipo Mulungu amapereka mzimu wake mokondwera kwa awo owufunafuna. (Agal. 5:22; Luka 11:13) Chotero anthu opanda chikhulupiriro sakufunafuna mzimu umenewo, kapena akutero kaamba ka chifuno cholakwa kapena akukamiza kugwira kwake ntchito m’miyoyo yawo. Zinthu zambiri zimasonkhezera zimenezi:
Kupanda chidziŵitso cholongosoka Chabaibulo: Baibulo liri chipatso chamzimu wa Mulungu, pokhala louziridwa ndi Mulungu. (2 Tim. 3:16, 17; 2 Sam. 23:2) Kulephera kuliphunzira kumalepheretsa kukhalapo kulikonse kwa chikhulupiriro chowona. Ngakhale kuli kwakuti ziŵalo zamatchalitchi zingakhale nawo Mabaibulo, ngati iwo aphunzitsidwa malingaliro a anthu mmalo mwa Mawu a Mulungu, adzakhala opanda chikhulupiriro chenicheni mwa Mulungu ndi chifuno chake. Kuti athetse mavuto a moyo, iwo adzakhala ndi chikhoterero cha kudalira pamalingaliro a iwo eni ndi a anthu ena.—Yerekezerani ndi Mateyu 15:3-9.
Kugwiritsidwa mwala ndi chipembedzo: Ochuluka agwiritsidwa mwala ndi chinyengo cha matchalitchi a Dziko Lachikristu, amene amanena kuti amaphunzitsa Mawu a Mulungu koma nalephera kukhala ndi moyo mogwirizana ndi zimene amanena. Ena anali ziŵalo za chipembedzo chosakhala Chachikristu, koma anawona chipatso choipa chochokera m’zizolowezi zake kapena anapeza kuti zikhulupiriro zawo sizinawathandizedi kulaka mavuto a moyo. Chifukwa cha kupanda chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu wowona, anthu otero amafufunuka ku chinthu chirichonse chogwirizana ndi chipembedzo.—Yerekezerani ndi Aroma 3:3, 4; Mateyu 7:21-23.
Samamvetsetsa chimene Mulungu walolezera kuipa: Anthu ambiri samazindikira chifukwa chake Mulungu amaloleza kuipa ndipo chotero amati ndiye wochititsa zinthu zonse zoipa zimene zikuchitika. Samazindikira kuti chikhoterero cha munthu cha kuchita zoipa sichiri chifukwa cha chifuniro cha Mulungu koma chifukwa cha uchimo wa Adamu. (Aroma 5:12) Iwo angakhale osazindikira za kukhalapo kwa Satana Mdyerekezi ndi za chisonkhezero chake m’nkhani za dziko, chotero amapaka Mulungu liwongo la kuchita zoipa zochitidwa ndi Satana. (1 Yoh. 5:19; Chiv. 12:12) Ngati iwo akuzindikira zinthu zimenezi kumlingo waung’ono, angalingalire kuti Mulungu ngochedwa m’kuchitapo kanthu, chifukwa chakuti samawona bwino lomwe nkhani ya ulamuliro wachilengedwe chonse ndipo samazindikira chenicheni chakuti kuleza mtima kwa Mulungu kufikira nthaŵi ino kumawapatsa mpata wapadera wa kupeza chipulumutso. (Aroma 2:4; 2 Pet. 3:9) Ndiponso, samazindikira mokwanira kuti Mulungu ali ndi nthaŵi yoikidwiratu pamene adzawononga kosatha onse amene amachita zoipa.—Chiv. 22:10-12; 11:18; Habak. 2:3.
Miyoyo njolamulidwa ndi zikhumbo ndi malingaliro akuthupi: Kaŵirikaŵiri, anthu opanda chikhulupiriro chenicheni adzipereka kukulondola zinthu zina. Ena anganene kuti amakhulupirira Baibulo koma iwo angakhale asanaliphunzire mosamalitsa kapena angakhale atalephera kusinkhasinkha moyamikira zimene amaŵerenga, pa zifukwa zake, ndi mmene limagwirira ntchito m’moyo watsiku ndi tsiku. (Yerekezerani ndi 1 Mbiri 28:9.) M’zochitika zina, analephera kulimbikitsa chikhulupiriro chimene anali nacho, koma mmalo mwake, analola chikhumbo cha zinthu zosalungama kulamulira chikhoterero cha mtima wawo kotero kuti anafufunuka kwa Mulungu ndi njira zake.—Aheb. 3:12.
Kodi ndimotani mmene munthu angapezere chikhulupiriro?
Aroma 10:17: “Chikhulupiriro chidza ndi mbiri.” (Yerekezerani ndi Machitidwe 17:11, 12; Yohane 4:39-42; 2 Mbiri 9:5-8. Choyamba munthuyo ayenera kufufuza zimene Baibulo limanena, ndipo adzalimbikitsa chikhutiro chake ngati alipenda mosamalitsa kotero kuti akhale ndi chikhutiro cha kudalirika.)
Aroma 10:10: “Ndi mtima munthu akhulupira.” (Mwa kusinkhasinakha pa zinthu zaumulungu kuti akulitse kuziyamikira kwake, munthuyo amakhomereza mumtima wake wophiphiritsira.)
Chikhulupiriro chimalimbikitsidwa pamene munthuyo achitapo kanthu pamalonjezo a Mulungu ndiyeno nawona umboni wa dalitso la Mulungu pa zimene wachita.—Wonani Salmo 106:9-12.
Chitsanzo: Mwinamwake inu muli ndi bwenzi limene mukananena za iro kuti: ‘Mwamuna uja ndimamkhulupirira. Ndingamdalire kuti adzasunga mawu ake; ndipo ndidziŵa kuti ngati ndiri ndi vuto, adzandithandiza.’ Sikukuwonekera ngati kuti mungakhale mukunena zimenezo ponena za munthu aliyense amene munakumana naye dzulo kwanthaŵi yoyamba, kodi sichoncho? Akafunikira kukhala munthu wina amene munakhala naye kwanthaŵi yaitali, munthu amene watsimikizira kudalirika kwake mobwerezabwereza. Nzofanana ndi chikhulupiriro cha chipembedzo. Kuti mukhale ndi chikhulupiriro, mufunikira kupeza nthaŵi ya kudziŵa Yehova ndi njira yake yochitira zinthu.
Chikhulupiriro chakuti kuli Mulungu
Wonani tsamba 306-313, pamutu waukulu wakuti “Mulungu.”
Chikhulupiriro m’chiyembekezo cha dongosolo latsopano lolungama lazinthu
Pamene munthu afikira kukhala wozoloŵerana bwino ndi cholembedwa cha ntchito za Mulungu ndi atumiki ake, amakhala ndi lingaliro lofanana ndi la Yoswa, amene anati: “Mudziŵa mitima yanu yonse, ndi m’moyo mwa inu nonse, kuti pamawu okoma onse Yehova Mulungu wanu anawanena za inu sanagwa padera mawu amodzi; onse anachitikira inu, sanasowapo mawu amodzi.”—Yos. 23:14.
Malonjezo a Baibulo athanzi lokonzedwanso, chiukiriro cha akufa, ndi zina zotero, amatsimikiziridwa ndi cholembedwa cha zozizwitsa zochitika ndi Yesu Kristu. Zimenezi siziri nthano. Ŵerengani zolembedwa za Mauthenga Abwino ndi kuwona umboni wakuti ziri ndi chitsimikiziro chonse cha kukhala chowonadi cha zochitika za m’mbiri. Malo a kumene zinachitikira atchulidwa, maina a olamulira adziko a panthaŵiyo aperekedwa; cholembedwa choposa mboni yowona ndi maso imodzi chasungidwa. Kusinkhasinkha paumboni umenewu kungathe kulimbikitsa chikhulupiriro chanu m’malonjezo a Baibulo.
Pitani ku Nyumba Zaufumu za Mboni za Yehova ndi kumisonkhano yawo yaikulu yotsegukira anthu onse, ndipo mungadziwonere nokha umboni wakuti kugwiritsiridwa ntchito kwa uphungu wa Baibulo kumasanduliza miyoyo, kuti kungakhoze kupangitsa anthu kukhala owona mtima ndi olungama mwa makhalidwe, kuti kungakhozetse anthu a mafuko onse ndi mitundu kukhalira ndi moyo ndi kugwirira ntchito pamodzi mu mzimu waubale wopanda chinyengo wowona.
Kodi ntchito ziridi zofunika ngati munthu ali ndi chikhulupiriro?
Yak. 2:17, 18, 21, 22, 26: “Chikhulupiriro, chikapanda kukhala ndi ntchito, chikhala chakufa mkati mwakemo. Koma wina akati, Iwe uli nacho chikhulupiriro, ndipo ine ndiri nazo ntchito; undiwonetse ine chikhulupiriro chako chopanda ntchito zako, ndipo ine ndidzakuwonetsa iwe chikhulupiriro changa chotuluka m’ntchito zanga. Abrahamu kholo lathu, sanayesedwe wolungama ndi ntchito kodi, paja adapereka mwana wake Isake nsembe paguwa lansembe? Upenya kuti chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro; pakuti monga thupi lopanda mzimu liri lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa.”
Chitsanzo: Mnyamata angapalane chibwenzi ndi msungwana, akumamuuza kuti amamkonda. Koma ngati mnyamatayo safunsira msungwanayo kuti akwatirane, kodi iye akusonyezadi kuti chikondi chake nchowona? Mofananamo, ntchito ndizo njira yosonyezera kutsimikizirika kwa chikhulupiriro chathu ndi chikondi. Ngati sitimvera Mulungu sitimamkondadi kapena kukhala ndi chikhulupiriro m’kulungama kwa njira zake. (1 Yoh. 5:3, 4) Komatu sitingalipidwe chipulumutso mosasamala kanthu za ntchito zimene timachita. Moyo wamuyaya uli mphatso yochokera kwa Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu, sichiri malipiro a ntchito zathu.—Aef. 2:8, 9.