Mutu 24
Chifukwa Chake Yesu Anadza Kudziko Lapansi
TSIKU la Yesu mu Kapernao ndi ophunzira ake anayi lakhala lotanganitsidwa, pomaliza anthu a ku Kapernao akubweretsa odwala awo onse kuti achiritsidwe mkati mwa madzulowo. Pakhala palibe nthaŵi yokhala yekha.
Tsopano ndi mmaŵa tsiku lotsatira. Pamene kudakali mbandakucha, Yesu akudzuka napita kunja ali yekha. Iye akupita kumalo a yekhayekha kumene angapemphere kwa Atate wake mtseri. Koma kukhala kwamtseri kwa Yesu nkosakhalitsa chifukwa pamene Petro ndi ena azindikira kuti iye palibe, iwo akukamfunafuna.
Pamene apeza Yesu, Petro akuti: “Akufunani inu anthu onse.” Anthu a ku Kapernao akufuna kuti Yesu akhale nawo. Ndithudi iwo akuyamikira zimene wawachitira! Koma kodi Yesu anadza kudziko lapansi kwakukulukulu kudzachita machiritso ozizwitsa otero? Kodi iye akunenanji za zimenezi?
Malinga ndi cholembedwa chimodzi cha Baibulo, Yesu akuyankha ophunzira ake kuti: “Tiyeni kwina, kumidzi iri pafupi apa, kuti ndilalikire komwekonso; pakuti chifukwa ndadzera ntchito imeneyi.” Ngakhale kuti anthu akumuumiriza Yesu kukhala, iye akuwauza kuti: “Kundiyenera ine ndilalikire uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumidzi inanso: chifukwa ndinatumidwa kudzatero.”
Inde, Yesu anadza kudziko lapansi makamaka kudzalalikira Ufumu wa Mulungu, umene udzalengeza za dzina la Atate wake ndi kuchotsa kosatha mavuto onse a anthu. Komabe, kupereka umboni wakuti iye anatumidwa ndi Mulungu, Yesu akuchita machiritso ozizwitsa. M’njira imodzimodziyo imene Mose, zaka mazana ambiri zapitazo, anachitira zozizwitsa kukhazikitsa kuyenera kwake monga mtumiki wa Mulungu.
Tsopano, pamene Yesu akuchoka ku Kapernao kukalalikira kumizinda ina, ophunzira ake anayi akupita naye. Anayi ameneŵa ndiwo Petro ndi mbale wake Andreya, ndi Yohane ndi mbale wake Yakobo. Mudzakumbukira kuti mlungu wapitawo, anaitanidwa kukhala anzake a Yesu ogwira naye ntchito oyamba oyenda nawo.
Ulendo waulaliki wa Yesu wa ku Galileya ndi ophunzira ake anayi ndiwo chipambano chodabwitsa! Kwenikweni, lipoti la ntchito yake likufalikira ngakhale ku Suriya. Makamu aakulu ochokera ku Galileya, Yudeya, ndi kutsidya kwa Mtsinje wa Yordano akutsatira Yesu ndi ophunzira ake. Marko 1:35-39; Luka 4:42, 43; Mateyu 4:23-25; Eksodo 4:1-9, 30, 31.
▪ Kodi chikuchitika nchiyani mmaŵa pambuyo pa tsiku la Yesu lotanganitsidwa mu Kapernao?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu anatumizidwa kudziko lapansi, ndipo ndichifuno chotani chimene zozizwitsa zake zikutumikira?
▪ Kodi ndani akupita ndi Yesu paulendo wake wolalikira ku Galileya, ndipo kodi nchiyani chiri chilabadiro kuntchito ya Yesu?