Mutu 31
Kubudula Ngala pa Sabata
MWAMSANGA Yesu ndi ophunzira ake akuchoka m’Yerusalemu kubwerera ku Galileya. Ndinthaŵi ya ngululu, ndipo m’minda muli ngala za tirigu pamatsamvu ake. Ophunzirawo ali ndi njala. Chotero iwo akubudula ngalazo nadya. Koma popeza kuti nditsiku la Sabata, mchitidwe wawo ukuwonedwa.
Atsogoleri achipembedzo m’Yerusalemu anali atangotha kumene kufunafuna kupha Yesu kaamba ka kuswa Sabata. Tsopano Afarisi akudzetsa chinenezo. “Tapenyani, ophunzira anu achita chosaloleka tsiku la sabata,” iwo akuwaneneza motero.
Afarisi amanena kuti kubudula ngala za tirigu ndi kuzifikisa m’manja kuti zidyedwe ndiko kututa ndi kupuntha. Koma kutanthauzira kwawo chimene chimapanga ntchito kwapangitsa tsiku la Sabata kukhala lolemetsa, pamene kuli kwakuti inayenera kukhala nthaŵi yosangalatsa, ndi yolimbikitsa mwauzimu. Chotero Yesu akupereka zitsanzo Zamalemba kusonyeza kuti Yehova Mulungu sanalinganize kugwiritsira ntchito koletsa kosafunikira kotero lamulo Lake la Sabata.
Yesu akunena kuti pamene Davide ndi anthu ake anali ndi njala, analoŵa m’nyumba ya Mulungu nadya mikate yowonetsera. Mikate imeneyo inali itachotsedwa kale pamaso pa Yehova ndi kuloŵedwa mmalo ndi yatsopano, ndipo mwachizoloŵezi inali itasungidwira ansembe kuti adye. Komabe, pansi pa mikhalidweyo, Davide ndi anthu ake sanatsutsidwe kaamba ka kuidya.
Popereka chitsanzo china, Yesu akuti: “Simunaŵerenga kodi m’Chilamulo, kuti tsiku la Sabata ansembe m’kachisi amaipitsa tsiku la sabata, nakhala opanda tchimo?” Inde, ngakhale tsiku la Sabata ansembe amapitiriza kupha nyama ndi ntchito zina pakachisi pokonzekera nsembe za nyama! “Koma ndinena kwa inu,” Yesu akutero, “kuti wakuposa kachisiyo ali pompano.”
Polangiza Afarisiwo, Yesu akupitiriza kuti: “Mukadadziŵa nchiyani ichi, Ndifuna chifundo, sinsembe ayi; simukadaŵeruza olakwa iwo osachimwa.” Pamenepo akumaliza kuti: “Pakuti Mwana wa munthu ali Mwini tsiku la Sabata.” Kodi Yesu akutanthauzanji mwakutero? Yesu akusonyeza za ulamuliro wake Waufumu wamtendere wa zaka chikwi.
Kwa zaka 6,000 tsopano, mtundu wa anthu wakhala ukuvutika mu ukapolo wowawa pansi pa Satana Mdyerekezi, ndi chiwawa ndi nkhondo zokhala chinthu cha tsiku ndi tsiku. Kumbali ina, ulamuliro wa Sabata lalikulu wa Kristu udzakhala nthaŵi ya mpumulo kumavuto onse amenewo ndi chitsenderezo. Mateyu 12:1-8; Levitiko 24:5-9; 1 Samueli 21:1-6; Numeri 28:9; Hoseya 6:6.
▪ Kodi nchinenezo chotani chimene chikupangidwa pa ophunzira a Yesu, ndipo kodi Yesu akuyankha motani?
▪ Kodi ndikulephera kotani kwa Afarisi kumene Yesu akuvumbula?
▪ Kodi ndimnjira yotani imene Yesu aliri “Mwini tsiku la Sabata”?