Mutu 39
Onyada ndi Odzichepetsa
ATATCHULA ubwino wa Yohane Mbatizi, Yesu akutembenukira kwa anthu onyada, osinthasintha omzingawo. “Obadwa awa,” iye akulengeza motero, “ali ofanana ndi ana akukhala m’mabwalo a malonda, amene alikuitana anzawo. ndi kuti, Tinakulizirani inu zitoliro, ndipo inu simunavina; tinabuma maliro, ndipo inu simunalira.”
Kodi Yesu akutanthauzanji? Iye akufotokoza kuti: “Yohane anadza wosadya, wosamwa, ndipo iwo amati, Ali nchiwanda; Mwana wa munthu anadza wakudya ndi wakumwa, ndipo iwo amati, Wonani! Munthu wosusuka ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la okhometsa misonkho ndi ochimwa.”
Nkosatheka kukhutiritsa anthu. Palibe chimene chikuwakondweretsa. Yohane wakhala ndi moyo wokhweka wodzimana monga Mnaziri, mogwirizana ndi chilengezo cha mngelo chakuti ‘sayenera konse kumwa vinyo ndi chakumwa chaukali.’ Ndipo komabe anthu akuti iye ali nchiwanda. Kumbali ina, Yesu akukhala ndi moyo monga anthu ena, wosadzimana kwambiri, ndipo iye akunenezedwa kukhala wonkitsa.
Nkovuta chotani nanga mmene kukondweretsa anthuwo kuliri! Iwo ali ngati ana oseŵera, amene ena a iwo akukana kuvina pamene ana enawo akuliza chitoliro kapena kumva chisoni pamene anzawo akulira maliro. Komabe, Yesu akunena kuti: “Nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.” Inde, umboni—ntchito—zimasonyeza bwino lomwe kuti chinenezo chochitidwa pa onse aŵiriwo Yohane ndi Yesu nchonama.
Yesu akupitiriza kusonyeza themberero pamizinda itatu ya Korazini, Betsaida, ndi Kapernao, kumene wachitako zochuluka za ntchito zake zamphamvu. Ngati akadachita ntchito zimenezo mumzinda wa Foinike wa Turo ndi Sidon, Yesu akutero, mizinda imeneyi ikanalapa m’chiguduli ndi m’mapulusa. Potsutsa Kapernao, amene mwachiwonekere wakhala malikulu a kwawo mkati mwa nyengo ya uminisitala wake, Yesu akulengeza kuti: “Dzuŵa la kuweruza, mlandu wake wa Sodomu udzachepa ndi wako.”
Kenako Yesu mwapoyera akutamanda Atate wake wakumwamba. Iye akusonkhezeredwa kutero chifukwa chakuti Mulungu amabisira chowonadi chamtengo wapatali chauzimu kwa anzeru ndi ophunzira koma amavumbulira zinthu zodabwitsazi kwa anthu odzichepetsa, kwa makanda, kunena kwake titero.
Pomaliza, Yesu akupereka chiitano chokopa chakuti: “Idzani kuno kwa ine nonsenu akulema ndi akuthodwa, ndipo ndidzakupumulitsani inu. Senzani goli langa, ndipo phunzirani kwa ine; chifukwa ndiri wofatsa ndi wodzichepetsa mtima: ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu. Pakuti goli langa liri lofeŵa, ndi katundu wanga ali wopepuka.”
Kodi ndimotani mmene Yesu amaperekera mpumulo? Iye amatero mwa kugaŵira ufulu kuchokera kumiyambo yomanga ukapolo imene atsogoleri achipembedzo alemetsa nayo anthu, mwachitsanzo, kuphatikizapo, kusunga malamulo a Sabata koumirizako. Iye amasonyezanso njira yachitonthozo kwa awo amene amalemetsedwa ndi ulamuliro wochitidwa ndi maboma a ndale za dziko ndi kwa awo amene amalemedwa ndi machimo awo kupyolera mwa chikumbumtima chovulazidwa. Iye amavumbula kwa anthu ovulazidwa otero za mmene machimo awo angakhululukidwire ndi mmene angakhalire ndi unansi wamtengo wapatali ndi Mulungu.
Goli lofeŵa limene Yesu amapereka ndilo lija la kudzipatulira kotheratu kwa Mulungu, kukhala wokhoza kutumikira Atate wathu wakumwamba wachikondi, wachifundoyo. Ndipo katundu wopepuka amene Yesu amapereka kwa awo amene amadza kwa iye ndiye uja wa kumvera zofunika za Mulungu kaamba ka moyo, zimene ziri malamulo Ake olembedwa m’Baibulo. Ndipo kumvera ameneŵa sikuli kolemetsa konse. Mateyu 11:16-30; Luka 1:15; 7:31-35; 1 Yohane 5:3.
▪ Kodi anthu onyada, osinthasintha a mbadwo wa Yesu ngofanana ndi ana motani?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akusonkhezeredwera kutamanda Atate wake Wakumwamba?
▪ Kodi ndim’njira zotani mmene anthu alemetsedwera, ndipo kodi ndimpumulo wotani umene Yesu amapereka?