Mutu 43
Kuphunzitsa mwa Mafanizo
YESU mwachiwonekere ali ku Kapernao pamene akudzudzula Afarisi. Pambuyo pake tsiku lomwelo, iye akuchoka m’nyumba napita ku Nyanja ya Galileya imene ili pafupipo, kumene makamu a anthu asonkhanako. Kumeneko iye akukwera ngalaŵa, nasuntha pang’ono, ndipo ayamba kuphunzitsa anthu cha m’mphepete mwa nyanja ponena za Ufumu wakumwamba. Iye akutero mwamipambo yamafanizo, kapena zoyerekezera, lirilonse lokhala ndi zochitika zozoloŵereka kwa anthuwo.
Choyamba, Yesu akusimba za wofesa amene akufesa mbewu. Mbewu zina zikugwera panjira ndipo zikudyedwa ndi mbalame. Mbewu zina zikugwera panthaka imene pansi pake pali thanthwe. Popeza kuti mizu sinazame, mbewu zatsopanozo zikufota ndi dzuŵa loŵawula. Ndipo mbewu zina zikugwera paminga, imene itsamwitsa mmera pamene utuluka. Potsirizira pake, mbewu zina zikugwera panthaka yabwino ndipo zikubala zipatso kuŵirikiza zana limodzi, zina kuŵirikiza makumi asanu ndi limodzi, ndipo zina kuŵirikiza makumi atatu.
Mufanizo lina, Yesu akuyerekezera Ufumu wa Mulungu ndi munthu amene amafesa mbewu. M’kupita kwa masiku, pamene munthuyo agona ndi pamene iye adzuka, mbewuzo zikukula. Munthuyo sadziŵa mmene zikuyendera. Mbewuzo zikukula mwa izo zokha ndipo zikubala zipatso. Pamene zipatsozo zicha, munthuyo azituta.
Yesu akusimba fanizo lachitatu la munthu wofesa mbewu yabwino, koma “mmene anthu analinkugona,” mdani adza nafesa namsongole pakati pa tirigu. Atumiki a munthuyo akufunsa ngati iwo ayenera kudzula namsongoleyo. Koma iye akuyankha kuti: ‘Ayi, ngati mutero inu mudzadzula wina wa tiriguyo. Ziloleni zonse ziŵiri zikulire pamodzi kufikira kututa. Pamenepo ndidzauza otutawo kusonkhanitsa namsongole ndi kumutentha ndi kuika tirigu munkhokwe.’
Popitiriza nkhani yake kwa makamuwo pamphepete pa nyanjayo, Yesu akusimba mafanizo ena aŵiri. Iye akusimba kuti “ufumu wakumwamba” uli wofanana ndi kambewu ka mpiru kamene munthu amafesa. Ngakhale kuti iko kali kochepetsetsa pambewu zonse, iye akutero, kamakula kukhala chitsamba chachikulu koposa zitsamba zonse. Kamafikira kukhala mtengo umene mbalame zimadzapo, kupeza mthunzi pakati pa nthambi zake.
Lerolino ena amatsutsa akumati pali mbewu zina zochepa kwambiri kuposa mbewu za mpiru. Koma Yesu panopa sakuphunzitsa maphunziro a zolima dimba. Pambewu zonse zimene Agalileya a m’tsiku lake anali ozoloŵerana nazo, mbewu ya mpiru iridi yochepetsetsa koposa zonse. Chotero iwo akuzindikira nkhani ya kukula kochititsa chidwi imene Yesu akufotokoza mwafanizo.
Potsirizira pake, Yesu akuyerekezera “ufumu wakumwamba” ndi chotupitsa chimene mkazi atenga nachisakaniza ndi miyeso yaikulu itatu ya ufa. M’kupita kwa nthaŵi, iye akuti, chimafikira mbali iriyonse yamtandawo.
Atapereka mafanizo asanu ameneŵa, Yesu akuuza makamuwo kumuka ndipo akubwerera kunyumba kumene amakhala. Mwamsanga atumwi ake 12 ndi ena akufika kwa iye kumeneko.
Kupindula Kuchokera Kumafanizo a Yesu
Pamene ophunzira adza kwa Yesu pambuyo pakulankhula kwake ndi makamu pagombe, iwo akuchita chidwi ndi njira yake yophunzitsa yatsopano. Mwawona nanga, iwo anamumva akugwiritsira ntchito mafanizo kalero, koma osati mokulira chotero. Chotero iwo akufunsa kuti: “Chifukwa chanji muphiphiritsira iwo m’mafanizo?”
Chifukwa chimodzi chimene iye akuchitira motere ndicho kukwaniritsa mawu a mneneri akuti: “Ndidzatsegula pakamwa panga ndimafanizo; ndipo ndidzaulula zinthu zobisika chiyambire kukhazikidwa kwake kwa dziko lapansi.” Komatu pali zambiri zophatikizidwa kuposa izi. Kugwiritsira ntchito kwake mafanizo kumatumikira chifuno cha kuthandiza kuvumbula mkhalidwe wa mtima wa anthuwo.
Kwenikweni, anthu ambiri amasangalalira Yesu kokha monga katswiri wowauza nthano ndi wochita zozizwitsa, osati monga woyenerera kutumikiridwa monga Ambuye ndi kutsatiridwa popanda dyera. Iwo safuna kudodometsedwa m’lingaliro lawo pa zinthu kapena njira yawo yamoyo. Iwo safuna kuti uthengawo ufunge kumlingo umenewu.
Chotero Yesu akuti: “Chifukwa chake ndiphiphiritsira iwo m’mafanizo; chifukwa kuti akuwona samawona, ndi akumva samamva, kapena samadziŵitsa. Ndipo adzachitidwa kwa iwo mawu adanenera Yesaya, amene amati . . . Chifukwa unalemera mtima wa anthu awa.”
“Koma,” Yesu akupitiriza kunena, “ali odala maso anu chifukwa apenya; ndi makutu anu chifukwa amva. Pakuti indetu ndinena ndi inu, kuti aneneri ambiri ndi anthu olungama analakalaka kupenya zimene muziwona, koma sanaziwona, ndi kumva zimene muzimva, koma sanazimva.”
Inde, atumwi 12 ndi awo amene ali nawo ali ndi mitima yolabadira. Chifukwa chake Yesu akuti: “Chifukwa kwa inu kwapatsidwa zinsinsi za ufumu wakumwamba, koma sikunapatsidwa kwa iwo.” Chifukwa cha chikhumbo chawo cha kufuna kuzindikira, Yesu akupereka kwa ophunzira ake tanthauzo la wofesa.
“Mbewuzo ndizo mawu a Mulungu,” Yesu akutero, ndipo nthaka ndiyo mtima. Ponena za mbewu yofesedwa panthaka youma m’mphepete mwanjira, iye akufotokoza kuti: “Akudza Mdyerekezi, nachotsa mawu m’mitima yawo, kuti angakhulupirire ndi kupulumuka.”
Kumbali ina, mbewu yofesedwa panthaka yokhala ndi thanthwe pansi pake imatanthauza mitima ya anthu amene amalandira mawuwo ndi chisangalalo. Komabe, chifukwa chakuti mawuwo sangathe kuzika mizu m’mitima yotero, anthu ameneŵa amakhumudwa pamene nthawi ya chiyeso kapena chizunzo ifika.
Ponena za mbewu imene inagwera paminga, Yesu akupitiriza kuti, iyi ikutanthauza anthu amene amva mawuwo. Komabe, ameneŵa, amatengeka ndi nkhaŵa ndi chuma ndi zikondwerero za moyo uno, chotero iwo amatsamwitsidwa kotheratu ndipo samaphula kanthu kalikonse.
Potsirizira, ponena za mbewu yofesedwa panthaka yabwino, Yesu akuti, ameneŵa ndiwo awo amene, pambuyo pakumva mawu pokhala ndi mtima wabwino ndi wolabadira, amawasunga ndipo amabala zipatso ndi chipiriro.
Ngodalitsidwa chotani nanga ophunzira ameneŵa amene afunafuna Yesu kuti apeze tanthauzo la ziphunzitso zake! Yesu akufuna kuti mafanizo ake amveketsedwe kutsata kuti apereke chowonadi kwa ena. “Kodi atenga nyali kuti akaivundikire m’mbiya, kapena akaike pansi pa kama?” iye akufunsa. Ayi, ‘amaiika pachoikapo nyali.’ Motero Yesu akuwonjezera kuti: ‘Chifukwa chake, perekani chisamaliro ponena za mmene mumvetserera.’
Odalitsidwa ndi Malangizo Owonjezereka
Atalandira mafotokozedwe a Yesu a fanizo la wofesa, ophunzirawo akufuna kuphunzira zowonjezereka. “Mutitanthauzire,” iwo akupempha motero, “fanizo lija la namsongole wa m’munda.”
Mkhalidwe wa ophunzirawa ngwosiyana chotani nanga ndi wakhamu lonse limene linali pagombelo! Anthu ameneŵo alibe chikhumbo chowona mtima cha kuphunzira tanthauzo la mafanizo, akumakhutira kokha ndi zinthu zotchulidwamo. Akumasiyanitsa omvetsera a m’mphepete mwa nyanja amenewo ndi ophunzira ake ofunsawo amene adza kwa iye m’nyumbamo, Yesu akuti:
‘Muyeso umene muyeza nawo, mudzayesedwa nawo inunso, inde, mudzakhala ndi zambiri zowonjezeredwa kwa inu.’ Ophunzirawo akuyeza chikondwerero cha changu cha Yesu ndi chisamaliro, ndipo chotero akudalitsidwa mwa kulandira malangizo owonjezereka. Motero, poyankha funso la ophunzira ake, Yesu akufotokoza kuti:
“Wofesa mbewu yabwino ndiye Mwana wa munthu; ndipo munda ndiwo dziko lapansi; ndi mbewu yabwino ndiyo ana a ufumuwo; ndi namsongole ndiye ana a woipayo; ndipo mdani amene anafesa uwu, ndiye Mdyerekezi: ndi kututa ndiko chimaliziro cha nthaŵi ya pansi pano; ndi otutawo ndiwo angelo.”
Atatchula mbali iriyonse yafanizo, Yesu akufotokoza chotulukapo chake. Pamapeto a dongosolo la zinthu, iye akunena kuti otutawa, kapena angelo, adzalekanitsa Akristu oyerekezera onga namsongole kuchokera kwa owonawo “ana aufumuwo.” Pamenepo “ana a woipa” adzaperekedwa kuchiwonongeko, koma ana a Ufumu wa Mulungu, “olungamawo,” adzaŵalitsa mu Ufumu wa Atate wawo.
Kenako Yesu akudalitsa ophunzira ake ofunitsitsawo ndi mafanizo ena atatu. Choyamba, iye akuti: “Ufumu wakumwamba uli wofanana ndi chuma chobisika m’munda; chimene munthu anachipeza, nachibisa; ndipo m’kuchikonda kwake achoka, nagulitsa zonse ali nazo, nagula munda umenewu.”
“Ndiponso,” iye akupitirizabe, “ufumu wakumwamba uli wofanana ndi munthu wamalonda, wakufuna ngale zabwino: ndipo mmene anaipeza ngale imodzi ya mtengo wapatali, anapita nakagulitsa zonse anali nazo, naigula.”
Yesu mwiniyo ali wofanana ndi munthu wopeza chuma chobisika ndipo ngwofanana ndi wamalonda amene apeza ngale yamtengo wapatali. Iye anagulitsa zonse, titero kunena kwake, akumasiya malo ake olemekezeka kumwamba kukakhala munthu wotsika. Ndiyeno, monga munthu padziko lapansi, iye akuvutika ndi mtonzo ndi chizunzo chaudani, akumatsimikizira kuyenerera kwake kukhala Wolamulira mu Ufumu wa Mulungu.
Chitokoso chikuikidwa pamaso pa ophunzira a Yesu kuti nawonso agulitse chirichonse kuti apeze mphoto yaikulu ya kukhala olamulira ndi Kristu kapena nzika za padziko lapansi za Ufumuwo. Kodi ife tidzalingalira kukhala ndi phande mu Ufumu wa Mulungu monga kanthu kena ka mtengo wapatali kuposa chirichonse m’moyo, monga chuma cha mtengo wapatali wosayerekezeka kapena ngale ya mtengo wapatali?
Potsirizira pake, Yesu akuyerekezera “ufumu wakumwamba” ndi khoka limene limasonkhanitsa nsomba za mtundu uliwonse. Pamene nsomba zilekanitsidwa, zosayenerera zimatayidwa koma zabwino zimasungidwa. Chotero, Yesu akunena kuti kudzatero pamapeto a dongosolo iri la zinthu; angelo adzalekanitsa oipa kuchokera kwa abwino, akumasungira oipawo chiwonongeko.
Yesu mwiniyo akuyamba ntchito iyi yakusodza, akumaitana ophunzira ake oyamba kukhala “asodzi a anthu.” Moyang’aniridwa ndi angelo, ntchito yosodza ikupitirizabe mkati mwa zaka mazana ambiri. Potsirizira pake nthaŵi ikudza ya kukoka “khoka,” limene limaphiphiritsira magulu apadziko lapansi odzitcha kukhala Akristu.
Ngakhale kuti nsomba zosayenera zikuponyedwa m’chiwonongeko, moyamikira tingathe kuŵerengeredwa pakati pa ‘nsomba zabwino’ zimene zikusungidwa. Mwakusonyeza changu chofanana ndi chimene ophunzira a Yesu anali nacho cha kufunafuna chidziŵitso chowonjezereka ndi luntha, tidzadalitsidwa osati kokha mwa kulandira malangizo owonjezereka koma ndi dalitso la Mulungu la moyo wosatha. Mateyu 13:1-52; Marko 4:1-34; Luka 8:4-18; Salmo 78:2; Yesaya 6:9, 10.
▪ Kodi ndiliti ndipo ndikuti kumene Yesu akulankhulira mafanizo kwa makamuwo?
▪ Kodi ndimafanizo asanu otani amene Yesu tsopano akusimbira makamuwo?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akuti mbewu ya mpiru njaing’ono koposa mbewu zonse?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akulankhula mwamafanizo?
▪ Kodi ndimotani mmene ophunzira a Yesu akudzisonyezera kukhala osiyana ndi makamuwo?
▪ Kodi ndimafotokozedwe otani amene Yesu akupereka ponena za fanizo la wofesa?
▪ Kodi ndimotani mmene ophunzira asiyanira ndi makamu apagombe?
▪ Kodi ndani kapena nchiyani chimene chikuimiridwa ndi wofesa, munda, mbewu yabwino, mdani, kututa, ndi otuta?
▪ Kodi ndimafanizo owonjezereka atatu otani amene Yesu akupereka, ndipo tingaphunzirenji kwa iwo?